Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mulungu Analengeranji Dziko Lapansili?

Kodi Mulungu Analengeranji Dziko Lapansili?

Phunzirani Zimene Mawu a Mulungu Amanena

Kodi Mulungu Analengeranji Dziko Lapansili?

Nkhani ino ili ndi mafunso amene mwina mumafuna mutadziwa mayankho ake ndipo ikusonyeza mavesi a m’Baibulo amene mungapezeko mayankhowo. A Mboni za Yehova ndi okonzeka kukambirana nanu mafunso amenewa.

1. Kodi Mulungu analengeranji dziko lapansili?

Dziko lapansi ndi kwawo kwa anthu. Mulungu analenga angelo kuti azikhala kumwamba ndipo kenako analenga anthu kuti azikhala padziko lapansi. (Yobu 38:4, 7) Choncho, Yehova anaika munthu woyamba m’paradaiso wokongola wotchedwa Edeni ndipo anakonza zoti iye ndi ana ake amene anali kudzabadwa mtsogolo adzakhale ndi moyo wosatha padziko lapansi.​—Genesis 2:15-17; werengani Salimo 115:16.

Munda wa Edeni unali kadera kochepa chabe ka dziko lapansi. Adamu ndi Hava anayenera kubereka ana. Mulungu anafuna kuti anthu achuluke, azilimamo zinthu ndiponso kulikonza kuti likhale paradaiso. (Genesis 1:28) Dziko lapansili silidzawonongedwa.​—Werengani Salimo 104:5.

2. N’chifukwa chiyani dziko lapansili silili paradaiso panopa?

Adamu ndi Hava anathamangitsidwa m’munda wa Edeni chifukwa sanamvere Mulungu. Paradaiso anathera pompo ndipo palibe munthu aliyense amene angathe kubwezeretsa dzikoli kukhala paradaiso. Baibulo limati: “Dziko lapansi laperekedwa m’manja mwa woipa.”​—Yobu 9:24; werengani Genesis 3:23, 24.

Koma Yehova Mulungu sanaiwale chifukwa chimene analengera anthu ndipo cholinga chake chidzakwaniritsidwa. (Yesaya 45:18) Yehova adzaonetsetsa kuti anthu akukhala mmene iye anafunira poyamba.​—Werengani Salimo 37:11.

3. Kodi Mulungu adzabwezeretsa bwanji mtendere padziko lapansi?

Kuti padziko lapansi pakhale mtendere, Mulungu ayenera kuchotsa kaye anthu oipa. Pa nkhondo ya Aramagedo angelo a Mulungu adzawononga anthu onse amene samvera Mulungu. Satana adzaikidwa m’ndende kwa zaka 1,000. Koma anthu amene amakonda Mulungu adzapulumuka pa nkhondo imeneyi ndipo adzakhala m’dziko lapansi latsopano.​—Werengani Chivumbulutso 16:14, 16; 20:1-3; 21:3, 4.

4. Kodi mavuto adzatha liti?

Kwa zaka 1,000, Yesu adzalamulira dziko lapansi ali kumwamba ndipo adzalisandutsa paradaiso. Komanso adzakhululukira machimo a anthu amene amakonda Mulungu. Zimenezi zidzachititsa kuti Yesu athetse matenda, ukalamba ndi imfa.​—Werengani Yesaya 11:9; 25:8; 33:24; 35:1.

Kodi Mulungu adzathetsa liti zoipa padzikoli? Yesu anapereka “chizindikiro” chothandiza anthu kudziwa kuti mapeto ali pafupi. Masiku ano anthu padzikoli akukhala mwamantha ndipo zimenezi zikusonyeza kuti tikukhala m’nthawi ya “mapeto.”​—Werengani Mateyu 24:3, 7-14, 21, 22; 2 Timoteyo 3:1-5.

5. Kodi ndani adzakhale m’Paradaiso?

Yesu anauza otsatira ake kuti aziphunzitsa anthu kuti akhale ophunzira ake komanso aziwaphunzitsa kuti Mulungu amachita zinthu mwachikondi. (Mateyu 28:19, 20) Padziko lonse, Yehova akukonzekeretsa anthu ambirimbiri kuti adzapeze moyo m’dziko latsopano. (Zefaniya 2:3) Ku Nyumba ya Ufumu ya Mboni za Yehova anthu amaphunzira zimene angachite kuti akhale amuna komanso abambo abwino. Amaphunziranso zimene angachite kuti akhale akazi komanso amayi abwino. Ana ndiponso makolo amaphunzira mfundo zimene zingawathandize kuti azikhulupirira kuti kutsogoloku kuli zinthu zabwino.​—Werengani Mika 4:1-4.

Ku Nyumba ya Ufumu mungapezeko anthu amene amakonda Mulungu ndiponso amene akufuna kuphunzira zimene angachite kuti azimusangalatsa.​—Werengani Aheberi 10:24, 25.

Kuti mudziwe zambiri, werengani mutu 3 m’buku ili Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?, lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.