Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Yesu Khristu Ndani Kwenikweni?

Kodi Yesu Khristu Ndani Kwenikweni?

“Tsopano atalowa mu Yerusalemu, mzinda wonse unagwedezeka. Ena anali kufunsa kuti: ‘Kodi ameneyu ndani?’ Khamu la anthulo linali kuyankha kuti: ‘Ameneyu ndi mneneri Yesu, wochokera ku Nazareti, ku Galileya!’”​—MATEYU 21:10, 11.

KODI n’chifukwa chiyani Yesu Khristu * atalowa mu Yerusalemu m’chaka cha 33 C.E mzindawu unagwedezeka choncho? Chinali chifukwa chakuti anthu ambiri mumzindawu anali atamva za Yesu komanso zinthu zodabwitsa zimene iye anachita. Choncho anthuwa ankakambirana zokhudza Yesu. (Yohane 12:17-19) Koma anthuwa sanadziwe kuti zochita ndiponso zolankhula za Yesu zidzakhudza anthu ambiri padziko lonse komanso zidzakhudza anthu mpaka nthawi yathu ino.

Tiyeni tione zitsanzo zochepa za mmene moyo wa Yesu wakhudzira anthu ambiri padziko lonse.

  • Kalendala imene anthu ambiri amagwiritsa ntchito padziko lonse inapangidwa motsatira chaka chimene anthu ambiri amakhulupirira kuti n’chimene Yesu anabadwa.

  • Anthu 2 biliyoni, omwe ndi pafupifupi hafu ya anthu onse padziko lapansi, amanena kuti ndi Akhristu.

  • Asilamu, omwe alipo oposa 1 biliyoni padziko lonse, amaphunzitsa kuti Yesu ndi “mneneri wamkulu kuposa Abulahamu, Nowa ndi Mose.”

  • Masiku ano anthu ambiri polankhula, amatchula ena mwa mawu anzeru amene Yesu ananena monga akuti:

    ‘Umutembenuzire tsaya lina.’​MATEYU 5:39.

    ‘Umunyamulirenso mtunda wina.’​MATEYU 5:41.

    ‘Munthu sangatumikire ambuye awiri.’​MATEYU 6:24.

    ‘Musamaponyere nkhumba ngale zanu.’​MATEYU 7:6.

    “Zinthu zonse zimene mukufuna kuti anthu akuchitireni, inunso muwachitire zomwezo.”​MATEYU 7:12.

    Muziwerengera kaye mtengo wake.’​LUKA 14:28.

N’zoonekeratu kuti zonena za Yesu zakhudza kwambiri anthu. Komabe anthu padziko lonse amaganiza ndiponso kukhulupirira zosiyanasiyana ponena za Yesu. Choncho mwina mungamadzifunse kuti, ‘Kodi Yesu Khristu ndani kwenikweni?’ Baibulo lokha ndi limene lingatiuze zoona zokhudza Yesu. Lingatiuze kumene anachokera, zimene anachita pa moyo wake komanso chifukwa chake anafa. Kudziwa zoona za Yesu kungakuthandizeni kwambiri panopa komanso m’tsogolo.

^ ndime 3 Dzina la mneneri wochokera ku Nazareti ameneyu lakuti “Yesu” limatanthauza “Yehova Ndiye Chipulumutso.” Mawu akuti “Khristu” amatanthauza “Wodzozedwa.” Zimenezi zikusonyeza kuti Yesu anadzozedwa kapena kuti anapatsidwa udindo wapadera ndi Mulungu.