Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Yesu—Kodi Anachokera Kuti?

Yesu—Kodi Anachokera Kuti?

“[Pilato] analowanso m’nyumba ya bwanamkubwa ndi kufunsa Yesu kuti: ‘Kodi umachokera kuti?’ Koma Yesu sanamuyankhe.”​—YOHANE 19:9.

PONTIYO PILATO, yemwe anali bwanamkubwa wachiroma, anafunsa funso limeneli pamene Yesu ankazengedwa mlandu umene anaweruzidwa kuti aphedwe. * Pilato ankadziwa dera la ku Isiraeli limene Yesu ankachokera. (Luka 23:6, 7) Iye ankadziwanso kuti Yesu sanali munthu wamba. Kodi pamenepa Pilato ankafuna kudziwa ngati Yesu anakhalapo kwinakwake? Kodi wolamulira ameneyu, amene sankalambira Mulungu, ankafunadi kudziwa zoona zake kuti achite mogwirizana ndi zimene wadziwazo? Mulimonse mmene zinalili, Yesu sanamuuze kumene anachokera ndipo pasanapite nthawi zinadziwika kuti Pilato ankadera nkhawa kwambiri udindo wake, osati kuchita zinthu mwachilungamo kapena mogwirizana ndi choonadi.​—Mateyu 27:11-26.

Koma n’zosangalatsa kuti anthu amene amafunadi kudziwa kumene Yesu anachokera angathedi kudziwa. Baibulo limafotokoza mosapita m’mbali kumene Yesu Khristu anachokera. Taonani mfundo zotsatirazi.

Kumene anabadwira

Malinga ndi kawerengedwe ka masiku ano, Yesu anabadwa cha kumayambiriro kwa chaka chimene chimatchedwa 2 B.C.E. Iye anabadwira m’banja losauka, m’mudzi wina wotchedwa Betelehemu ku Yudeya. Lamulo limene Augusito Kaisara anapereka, loti anthu onse akalembetse m’kaundula linachititsa kuti Yosefe ndi mkazi wake Mariya, yemwe pa nthawiyi anali “wotopa ndi pakati,” ayende ulendo wopita ku Betelehemu kumene kunali kumudzi kwa Yosefe. Banjali silinapeze malo ogona chifukwa mumzindawu munali anthu ambiri. Choncho iwo anagona m’khola moti Yesu anabadwira m’kholamo ndipo anamugoneka modyera ziweto.​—Luka 2:1-7.

Zaka zambiri Yesu asanabwere padziko lapansi, Baibulo linali litalosera kale kumene iye adzabadwire. Ulosiwu unati: “Iwe Betelehemu Efurata, ndiwe mzinda waung’ono kwambiri moti sungawerengedwe ngati umodzi mwa mizinda ya fuko la Yuda. Komabe mwa iwe mudzatuluka munthu amene adzakhale wolamulira mu Isiraeli.” * (Mika 5:2) Betelehemu, unali mzinda waung’ono kwambiri moti sankauyika m’gulu la mizinda ikuluikulu ya m’dziko la Yuda. Komabe ulosi unanena kuti mumzinda waung’ono umenewu mudzachitika chinthu chapadera. Mesiya wolonjezedwa kapena kuti Khristu anali kudzachokera mu mzindawu.​—Mateyu 2:3-6; Yohane 7:40-42.

Kumene anakulira

Yosefe ndi banja lake atakhala ku Iguputo nthawi yochepa, anasamukira ku Nazareti, mzinda womwe unali m’chigawo cha Galileya, makilomita 96 kumpoto kwa Yerusalemu. Pa nthawiyi n’kuti Yesu asanakwanitse zaka zitatu. Yesu anakulira m’dera limeneli, lomwe linali lokongola ndipo anthu ambiri anali alimi, abusa komanso asodzi. Makolo a Yesu anali ndi ana ambiri ndipo zikuoneka kuti banjali linali losauka.​—Mateyu 13:55, 56.

Zaka zambiri zimenezi zisanachitike, Baibulo linali litalosera kuti Mesiya adzakhala “Mnazareti.” Mateyu, yemwe analemba nawo Uthenga Wabwino ananena kuti, banja la Yesu lidzasamukira ku “Nazareti kuti akwaniritsidwe mawu onenedwa kudzera mwa aneneri kuti: ‘Iye adzatchedwa Mnazareti.’” (Mateyu 2:19-23) Zikuoneka kuti dzina lakuti Mnazareti ndi logwirizana ndi mawu achiheberi amene anawamasulira kuti “mphukira.” Mateyu ayenera kuti ankanena za ulosi wa Yesaya umene unanena kuti Mesiya ndi “mphukira” yotuluka mwa Jese. Kutanthauza kuti Mesiya adzakhala mbadwa ya Jese, bambo ake a Mfumu Davide. (Yesaya 11:1) N’zoona kuti Yesu analidi mbadwa ya Jese kudzera mwa Davide.​—Mateyu 1:6, 16; Luka 3:23, 31, 32.

Kumene anachokera

Baibulo limaphunzitsa kuti Yesu anali kwinakwake asanadzabadwe m’khola la ziweto ku Betelehemu. Ulosi wa Mika umene tautchula poyamba uja umanena za Yesu kuti: “Wakhala alipo kuyambira nthawi zoyambirira, wakhala alipo kuyambira masiku akalekale.” (Mika 5:2) Monga Mwana woyamba wa Mulungu, Yesu anali mngelo kumwamba asanadzabadwe ngati munthu padziko lapansi. Yesu anati: “Ndinatsika kuchokera kumwamba.” (Yohane 6:38; 8:23) Kodi zimenezo zinatheka bwanji?

Yehova Mulungu anagwiritsa ntchito mzimu woyera kuchita chozizwitsa. * Iye anasamutsa moyo wa Mwana wake kumwamba n’kuuika m’mimba mwa namwali wachiyuda dzina lake Mariya. Zimenezi zinachititsa kuti Yesu abadwe wopanda uchimo. Kuchita chozizwitsa chimenechi sikunali kovuta kwa Mulungu Wamphamvuyonse. Monga mmene mngelo amene anafotokoza nkhaniyi kwa Mariya ananenera, “zimene Mulungu wanena, sizilephereka.”​—Luka 1:30-35, 37.

Komabe Baibulo silimangotiuza kumene Yesu anachokera. Mauthenga Abwino onse anayi, Mateyu, Maliko, Luka, ndi Yohane amatiuza zinanso zokhudza moyo wa Yesu.

^ ndime 3 Kuti mudziwe zambiri za kumangidwa ndiponso mayesero amene Yesu anakumana nawo, onani nkhani yakuti “Mlandu Umene Unaweruzidwa Mopanda Chilungamo Kuposa Milandu Yonse,” patsamba 18 mpaka 22 m’magazini ino.

^ ndime 6 Zikuoneka kuti Betelehemu poyamba ankatchedwa Efurata (kapena kuti Efurati).​—Genesis 35:19.

^ ndime 10 Baibulo limanena kuti dzina la Mulungu ndi Yehova.