Yesu—N’chifukwa Chiyani Anafa?
‘Mwana wa munthu anabwera . . . kudzapereka moyo wake dipo kuwombola anthu ambiri.’—MALIKO 10:45.
YESU ankadziwa zimene zidzamuchitikire ndipo ankadziwa kuti pa moyo wake adzakumana ndi mavuto. Ankadziwanso kuti adzaphedwa ali ndi zaka 30 chakuti, ndipo sankaopa imfa imeneyi.
Baibulo limasonyeza kuti imfa ya Yesu ndi yofunika kwambiri. Buku lina linanena kuti Malemba Achikhristu Achigiriki, omwe ena amati Chipangano Chatsopano, amatchula za imfa ya Yesu ka 175. Komano n’chifukwa chiyani Yesu anayenera kuvutika ndi kufa? Tifunika kudziwa chifukwa chake popeza kuti imfa ya Yesu ingakhudze kwambiri moyo wathu.
Zimene Yesu ankayembekezera
M’chaka chimene anamwalira, Yesu anauza ophunzira ake mobwerezabwereza kuti iye ankayembekezera kuzunzidwa ndiponso kuphedwa. Mwachitsanzo, nthawi ina Yesu ali pa ulendo wa ku Yerusalemu kukachita Pasika wake womaliza, anauza atumwi ake 12 kuti: “Mwana wa munthu akaperekedwa kwa ansembe aakulu ndi alembi, ndipo akamuweruza kuti aphedwe, ndipo akam’pereka kwa anthu amitundu. Iwo akam’chitira chipongwe, kum’lavulira, kum’kwapula ndi kumupha.” * (Maliko 10:33, 34) Kodi n’chifukwa chiyani Yesu sankakayikira kuti zimenezi zimuchitikira?
Yesu ankadziwa bwino maulosi a m’Baibulo opezeka m’Malemba Achiheberi amene analosera mmene iye adzafere. (Luka 18:31-33) Taonani ena mwa maulosi amenewa limodzi ndi malemba amene akufotokoza mmene ulosiwo unakwaniritsidwira.
Mesiya . . .
-
Adzaperekedwa ndi ndalama 30 zasiliva.—ZEKARIYA 11:12; MATEYU 26:14-16.
-
Adzamenyedwa ndi kulavuliridwa malovu.—YESAYA 50:6; MATEYU 26:67; 27:26, 30.
-
Adzapachikidwa.—SALIMO 22:16; MALIKO 15:24, 25.
-
Adzanyozedwa ali pamtengo wozunzikirapo.—SALIMO 22:7, 8; MATEYU 27:39-43.
-
Adzaphedwa koma mafupa ake sadzathyoledwa ngakhale limodzi.—SALIMO 34:20; YOHANE 19:33, 36.
Maulosi amenewa ndiponso ena ambiri anakwaniritsidwa pa Yesu. Sizikanatheka kuti zimenezi zingochitika mwangozi. Ndipo kukwaniritsiwa kwa maulosi amenewa kunatsimikizira kuti Yesu anatumizidwadi ndi Mulungu. *
Komabe n’chifukwa chiyani Yesu anafunika kuvutika ndi kufa?
Yesu anafa kuti athetse nkhani zofunika kwambiri
Yesu ankadziwa kuti pali nkhani zofunika kwambiri zokhudza chilengedwe chonse zimene zinayambira m’munda wa Edeni. Adamu ndi Hava anasankha kusamvera Mulungu ndipo iwo anachita zimenezi chifukwa chomvera mngelo wopanduka. Kupanduka kwa Adamu ndi Hava kunachititsa kuti zolengedwa zina ziyambe kukaikira ngati Mulungu alidi woyenera kulamulira chilengedwe chonse komanso ngati amalamuliradi bwino. Komanso kuchimwa kwawo kunayambitsa funso lakuti, kodi pangapezeke munthu amene angakhale wokhulupirika kwa Mulungu ngakhale atayesedwa?—Genesis 3:1-6; Yobu 2:1-5.
Yesu anapereka mayankho ogwira mtima pa nkhani ziwiri zonsezi, zomwe ndi nkhani yokhudza ulamuliro wa Yehova ndiponso nkhani yokhudza Afilipi 2:8) Yesu anasonyezanso kuti munthu wangwiro angathe kukhalabe wokhulupirika kwa Yehova ngakhale atayesedwa chotani.
kukhulupirika kwa anthu. Pomvera mokhulupirika “mpaka imfa . . . ya pamtengo wozunzikirapo,” Yesu anasonyeza kuti Mulungu ndi woyenera kulamulira chilengedwe chonse. (Yesu anafa kuti awombole anthu
Mneneri Yesaya analosera kuti mavuto amene Mesiya wolonjezedwa adzakumane nawo ndiponso imfa yake, zidzachititsa kuti anthu atetezedwe ku machimo awo. (Yesaya 53:5, 10) Yesu ankadziwa bwino mfundo imeneyi ndipo mofunitsitsa anapereka “moyo wake dipo kuwombola anthu ambiri.” (Mateyu 20:28) Imfa yake yansembe inachititsa kuti anthu opanda ungwiro akhale pa ubwenzi ndi Yehova komanso kuti awomboledwe ku uchimo ndi imfa. Inachititsanso kuti anthufe tipezenso zimene Adamu ndi Hava anataya, zomwe ndi chiyembekezo cha moyo wosatha padziko lapansi lopanda mavuto. *—Chivumbulutso 21:3, 4.
Zimene mungachite
Kuyambira nkhani yoyamba ija, takambirana zimene Baibulo limanena zokhudza Yesu. Takambirana mafunso akuti, kodi anachokera kuti? Anachita zotani pa moyo wake? Komanso kodi n’chifukwa chiyani anafa? Kudziwa mayankho amafunso amenewa kungakuthandizeni kudziwa zoona zokhudza Yesu. Komanso kungakuthandizeni kuchita zinthu mogwirizana ndi zimene mwadziwazo. Zimenezi zingakuthandizeni kuti muzikhala wosangalala panopo ndiponso kuti mudzapeze moyo wosatha. Ndipo Baibulo limatiuza zimene tiyenera kuchita ngati tikufuna kupeza madalitso amenewa.
-
Phunzirani zambiri za Yesu komanso udindo umene ali nawo pokwaniritsa chifuniro cha Yehova.—YOHANE 17:3.
-
Sonyezani kuti mumakhulupirira Yesu mwa kuchita zinthu zoonetsa kuti mumakhulupirira kuti iye ndi Mpulumutsi wanu.—YOHANE 3:36; MACHITIDWE 5:31.
A Mboni za Yehova ndi okonzeka kukuthandizani kuphunzira zambiri zokhudza Yesu Khristu, ‘Mwana wobadwa yekha’ wa Mulungu, amene kudzera mwa iye tingapeze mphatso ya “moyo wosatha.”—Yohane 3:16.
^ ndime 5 Nthawi zambiri Yesu ankadzitchula kuti “Mwana wa munthu.” (Mateyu 8:20) Mawu amenewa akusonyeza kuti pa nthawi imene anali padziko lapansi, iye anali munthu weniweni komanso kuti anali “mwana wa munthu” amene amatchulidwa mu ulosi wa m’Baibulo.—Danieli 7:13, 14.
^ ndime 13 Kuti mudziwe zambiri za maulosi ena amene anakwaniritsidwa pa Yesu, onani zakumapeto mutu wakuti “Mesiya Wolonjezedwayo Anali Yesu” m’buku la Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.
^ ndime 17 Kuti mudziwe zambiri zokhudza kufunika kwa nsembe ya imfa ya Yesu, werengani mutu 5 wakuti “Dipo la Yesu Ndilo Mphatso ya Mulungu ya Mtengo Wapatali Koposa Zonse” m’buku la Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?