Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Baibulo Limasintha Anthu

Baibulo Limasintha Anthu

 Baibulo Limasintha Anthu

KODI n’chiyani chinathandiza munthu wina yemwe anali wovuta, yemwenso ankaimba nyimbo zaphokoso kwambiri, kuyamba kukonda anthu ndiponso kuwathandiza? N’chiyani chinathandiza mwamuna wina wa ku Mexico kuti asiye khalidwe logona ndi amuna anzake? Nanga n’chiyani chinapangitsa kuti katswiri wina wa mpikisano wopalasa njinga wa ku Japan asiye masewerawa n’kuyamba kutumikira Mulungu? Werengani kuti mumve zimene anthu amenewa ananena.

“Ndinali wamwano, wonyada komanso wosachedwa kupsa mtima.”​—DENNIS O’BEIRNE

CHAKA CHOBADWA: 1958

DZIKO: ENGLAND

POYAMBA: SINDINKAFUNA KUCHEZA NDI WINA ALIYENSE KOMANSO NDINKAIMBA NYIMBO ZAPHOKOSO KWAMBIRI

KALE LANGA: Bambo anga anali wochokera ku Ireland, ndipo ndinakulira m’banja lachikatolika. Nthawi zambiri ndinkapita ndekha kutchalitchi ngakhale kuti sindinkasangalala ndi zopita kutchalitchi. Komabe, ndinkaona kuti zosowa zanga zauzimu sizikukwaniritsidwa. Nthawi zambiri ndinkapemphera Pemphero la Ambuye ndipo ndikukumbukira kuti nthawi zina usiku ndinkagona pabedi n’kumaganizira tanthauzo la pempheroli. Ndinkagawagawa pempheroli mbali zingapo kuti ndimvetse tanthauzo la mbali iliyonse.

Ndili mnyamata ndinalowa chipembedzo cha Marasi. Ndinayambanso kuchita chidwi ndi zandale. Mwachitsanzo ndinayamba kuchita chidwi ndi gulu lina lodana ndi chipani cha Nazi. (Anti-Nazi League) Koma chimene ndinkakonda kwambiri ndi gulu la anthu akhalidwe loipa oimba nyimbo zaphokoso ndipo ndinali munthu wosamvera malamulo. Ndinkakonda mankhwala osokoneza bongo makamaka chamba chimene ndinkasuta pafupifupi tsiku lililonse. Sindinkasamala za munthu ndipo ndinkamwa mwauchidakwa. Nthawi zambiri ndinkachita zinthu zoika moyo wanga pachiswe komanso sindinkasamala kwenikweni za moyo wa munthu. Ndinali munthu wosafuna kucheza ndi anthu ndipo ngati ndalankhula ndi munthu ndiye kuti ndaona kuti zimene ndilankhule nayezo zindithandiza. Ndinafika mpaka pomakana kujambulidwa. Panopa ndikaganiza moyo umene ndinkakhala nthawi imeneyo, ndimaona kuti ndinali munthu wamwano, wonyada komanso wosachedwa kupsa mtima. Anthu amene ndinkawachitira zinthu mokoma mtima kapena kuwathandiza anali amene ndinkagwirizana nawo basi.

Ndili ndi zaka 20, ndinayamba kuchita chidwi ndi Baibulo. Mnzanga wina amene anamangidwa chifukwa chogulitsa mankhwala osokoneza bongo anayamba kuwerenga Baibulo ali kundende. Atatuluka, tinkakambirana nthawi yaitali nkhani za chipembedzo, Tchalitchi komanso zimene Satana akuchita padzikoli. Kenako ndinagula Baibulo ndipo ndinayamba kuliphunzira pandekha. Ineyo ndi mnzangayo tikawerenga Baibulo tinkakumana n’kumakambirana zimene tawerengazo ndipo kenako tinkapeza tanthauzo lake. Tinachita zimenezi kwa miyezi yambiri.

Zina mwa mfundo zimene tinaona kuti taziphunzira kuchokera pa zimene tinawerenga ndi izi: Tikukhala m’masiku otsiriza, Akhristu ayenera kumalalikira uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu, Akhristu sayenera kukhala mbali ya dzikoli ndipo sayenera kuchita ndale. Tinaonanso kuti Baibulo limapereka malangizo othandiza pa nkhani ya makhalidwe abwino. Mfundo zimenezi zinatithandiza kuzindikira kuti Baibulo limanena zoona ndiponso kuti payenera kukhala chipembedzo chinachake choona. Koma tinkadzifunsa kuti chipembedzo chake n’chiti? Tinaganizira za  matchalitchi osiyanasiyana otchuka, miyambo yawo komanso kulowerera kwawo ndale ndipo tinaona kuti zimenezi zinali zosiyana ndi zimene Yesu ankaphunzitsa. Tinkadziwa kuti Mulungu sangagwiritse ntchito anthu ochita zimenezo. Choncho tinaganiza zofufuza zipembedzo zina zosatchuka kwenikweni kuti tione zimene amaphunzitsa.

Kawirikawiri tinkakumana ndi anthu a m’zipembedzo zimenezi n’kumawafunsa mafunso osiyanasiyana. Ifeyo tinkadziwa mayankho a m’Baibulo a mafunsowo, choncho tinkadziwa ngati atiyankha zogwirizana ndi Mawu a Mulungu kapena ayi. Nthawi iliyonse tikamaliza kukambirana ndi anthuwa mafunso a m’Baibulo ndinkapemphera kwa Mulungu kuti, ‘Ngati chipembedzo cha anthu amenewa ndi choona, ndithandizeni kuti ndifune kudzaonana nawonso nthawi ina.’ Panapita miyezi yambiri ndikumakumana ndi anthuwa, komabe sindinapeze anthu amene anayankha mafunso athu pogwiritsa ntchito Baibulo. Komanso ndikakambirana nawo sindinkalakalaka kudzaonananso ndi aliyense wa anthu amenewa.

Tsiku lina ine ndi mnzanga uja tinakumana ndi a Mboni za Yehova. Titawafunsa mafunso omwe aja anatiyankha pogwiritsa ntchito Baibulo. Zimene ananena zinagwirizana ndendende ndi zimene tinali titawerenga m’Baibulo zija. Choncho tinawafunsa mafunso ena amene tinali tisanapeze mayankho ake m’Baibulo. Mwachitsanzo tinkafuna kudziwa kuti Mulungu amaona bwanji kusuta komanso kumwa mankhwala osokoneza bongo. Apanso iwo anatiyankha funso limeneli pogwiritsa ntchito Mawu a Mulungu. Tinavomera kupita nawo ku misonkhano yawo ku Nyumba ya Ufumu.

Koma kupita kumisonkhano kunali kondivuta kwambiri. Ndinali munthu wosakonda kucheza ndi anthu moti sindinkafuna kuti anthu ansangala komanso ovala bwino amene ndinawapeza ku Nyumba ya Ufumu azindipatsa moni. Ndinkaganiza kuti ena mwa anthu amenewa ankandilankhula kuti anditole zifukwa. Choncho sindinafune kudzapitanso kukasonkhana ndi anthu amenewa. Koma monga mwa masiku onse, ndinapemphera kwa Mulungu kuti andipatse chidwi chodzapitanso kukasonkhana ndi anthu amenewa ngati chipembedzo chawo chilidi choona. Ndinadabwa kuona kuti ndinayamba kulakalaka kwambiri kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova.

MMENE BAIBULO LINASINTHIRA MOYO WANGA: Ndinazindikira kuti ndinafunika kusiya mankhwala osokoneza bongo ndipo ndinasiyadi mosavutikira. Koma nkhani inali pa kusuta fodya. Ndinayesetsa kuti ndisiye koma ndinkalephera. Nditamva za anthu ena amene sizinawavute kusiya kusuta moti atasiya sanasutenso moyo wawo wonse, ndinapemphera kwa Yehova kuti andithandize. Kuyambira nthawi imene ndinapempherayo Yehova anandithandiza kuti ndisiye fodya. Zimenezi zinandithandiza kuona kufunika komuuza Yehova m’pemphero vuto lenileni limene ukufuna kuti akuthandize.

Chinanso chachikulu chimene ndinasintha pa moyo wanga ndi kavalidwe. Nthawi yanga yoyamba kupita kukasonkhana ku Nyumba ya Ufumu, tsitsi langa linali lanyankhalala ndipo linali lodaya mzera wa buluu. Kenako ndinalidaya kuti lizioneka lachikasu. Ndinkakonda kuvala majinzi ndi masukumba achikopa olembalemba. Ndinkaona kuti panalibe chifukwa chosinthira kavalidwe kanga ngakhale kuti a Mboni ankandithandiza mwachifundo kuti ndisinthe. Komabe kenako ndinaganizira kwambiri lemba la 1 Yohane 2:15-17 limene limati: “Musamakonde dziko kapena zinthu za m’dziko. Ngati wina akukonda dziko, ndiye kuti sakonda Atate.” Ndinazindikira kuti kavalidwe kanga kankasonyeza kuti ndimakonda za m’dziko. Choncho kuti ndisonyeze kuti ndimakonda Mulungu ndinafunika kusintha kavalidwe ndipo ndinachitadi zimenezo.

Patapita nthawi ndinazindikiranso kuti si a Mboni okha amene ankafuna kuti ndizipita ku misonkhano yachikhristu. Lemba la Aheberi 10:24, 25 linandithandiza kuona kuti kwenikweni Mulungu ndi amene amafuna kuti ndizipita kukasonkhana. Nditayamba kupita kumisonkhano yonse n’kudziwana bwino ndi anthu, ndinaganiza zobatizidwa posonyeza kuti ndadzipereka kwa Yehova.

PHINDU LIMENE NDAPEZA: Ndakhudzidwa mtima kwambiri ndi mmene Yehova amachitira zinthu n’cholinga chakuti tikhale naye pa ubwenzi. Chifundo komanso chikondi chake zandilimbikitsa kwambiri kuti nditengere chitsanzo cha Mwana wake, Yesu Khristu komanso kumutsatira pa moyo wanga. (1 Petulo 2:21) Ndaphunzira kuti pamene ndikuyesetsa kukhala ndi makhalidwe abwino monga Mkhristu, ndingathebe kukhala ndi umunthu wosiyana ndi ena. Ndikuyesetsanso kuti ndizikonda ena komanso kuwachitira chifundo. Ndikuyesetsa kutsanzira Khristu pochita zinthu ndi mkazi komanso mwana wanga. Ndipo ndimakonda kwambiri abale ndi alongo anga mumpingo. Kutsatira chitsanzo cha Khristu kwachititsa kuti anthu azindilemekeza, ndidzizipatsa ulemu komanso kwandithandiza kuti ndizikonda anthu.

 “Anandilandira Mwaulemu Kwambiri.”​—GUADALUPE VILLARREAL

CHAKA CHOBADWA: 1964

DZIKO: MEXICO

POYAMBA: NDINKAKONDA ZACHIWEREWERE

KALE LANGA: Ndinakulira mumzinda wa Hermosillo, m’dera la Sonora ku Mexico ndipo m’banja lathu tinalipo ana 7. Anthu ambiri m’derali anali osauka kwambiri. Bambo anga anamwalira ndili mwana ndipo zimenezi zinachititsa kuti mayi afunefune ntchito n’cholinga choti azitha kutisamalira. Ndinkayenda opanda nsapato chifukwa mayi sakanakwanitsa kundigulira nsapato. Ndinayamba kugwira ntchito ndili wamng’ono n’cholinga choti ndizithandiza banja lathu. Monga zinalili ndi anthu ena, banja lathu linkakhala m’nyumba mopanikizana.

Popeza kuti mayi ankapita kuntchito tsiku lililonse, nthawi zambiri tinkakhala tokha. Kenako ndili ndi zaka 6 mnyamata wina wazaka 15 anayamba kuchita nane zachiwerewere. Zimenezi zinakhala zikuchitika kwa zaka zambiri. Zimenezi zinachititsa kuti ndisokonekere maganizo kwambiri pa nkhani za kugonana. Choncho ndinayamba kuona kuti palibe vuto lililonse kugonana ndi amuna anzanga. Ndikafotokozera adokotala kapena abusa zimenezi, ankandiuza kuti ndilibe vuto lililonse chifukwa zimenezo zimachitikira aliyense.

Kenako ndili ndi zaka 14 ndinayamba kuvala komanso kuchita zinthu ngati mmene anthu ogona ndi amuna anzawo amachitira. Ndinakhala ndikuchita zimenezi kwa zaka 11 zotsatira ndipo ndinali ndi amuna anzanga ambirimbiri amene ndinkagona nawo. Kenako ndinaphunzira kukonza anthu tsitsi ndipo ndinatsegula saluni. Komabe sindinkakhala wosangalala. Ndinkakumana ndi mavuto ambiri ndipo ndinkaona kuti anthu akundidyera masuku pamutu. Ndinkadziwa kuti zimene ndinkachitazo zinali zoipa. Ndinayamba kumadzifunsa kuti, ‘Kodi padzikoli pangakhaledi anthu abwino?’

Ndinaganizira za mchemwali wanga yemwe anayamba kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova ndipo kenako anabatizidwa. Nthawi zambiri mchemwali wangayu ankandiuza zimene anali kuphunzira, kungoti ndinalibe nazo chidwi kwenikweni. Ngakhale zinali choncho, ndinkasirira khalidwe lake komanso ndinkaona kuti iye ndi mwamuna wake ankakhala mosangalala. Ndinkaonanso kuti iwo ankakondana kwambiri, ankalemekezana komanso ankachitirana zinthu mwachifundo. Patapita nthawi munthu wina wa Mboni anayamba kundiphunzitsa Baibulo. Poyamba ndinkangophunzira basi, opanda chidwi kwenikweni. Koma kenako zinthu zinasintha.

MMENE BAIBULO LINASINTHIRA MOYO WANGA: A Mboni anandiitanira ku misonkhano yawo ndipo zimene ndinaona kumeneko zinali zachilendo. Iwo sanandinyoze ngati mmene anthu ena ankandinyozera. Anandipatsa moni mwansangala ndipo anandilandira mwaulemu kwambiri. Zimenezi zinandikhudza kwambiri.

Ndinayamba kukonda kwambiri Mboni za Yehova nthawi imene ndinapita nawo ku msonkhano wawo waukulu. Ndinaona kuti ngakhale pa misonkhano ikuluikulu, khalidwe la anthu amenewa linali lofanana ndi la mchemwali wanga uja. Anali oona mtima ndipo sankachita zinthu mwachiphamaso. Zimenezi zinandichititsa kuganiza kuti limeneli ndi gulu la anthu abwino komanso aphindu amene ndakhala ndikulakalaka nditakumana nawo. Chikondi chawo komanso mgwirizano wawo zinandigometsa kwambiri. Komanso ndinachita chidwi kwambiri ndi mmene ankagwiritsira ntchito Baibulo poyankha funso lililonse. Ndinazindikira kuti Baibulo ndi limene lachititsa kuti anthu amenewa akhale ndi makhalidwe abwino. Komanso ndinaona kuti ngati ndikufuna kukhala ngati anthu amenewa, ndinayenera kusintha zinthu zambiri pa moyo wanga.

Kunena zoona ndinafunikadi kusintha kwambiri chifukwa ndinkachita zinthu ngati mkazi. Ndinafunikanso kusintha kalankhulidwe, khalidwe, kavalidwe, kapesedwe komanso anthu ocheza nawo. Nditayamba kusintha, anzanga anayamba kundinyoza ndipo ankandifunsa kuti: “N’chifukwa chiyani ukuchita zimenezi? Zinali bwino mmene unalili muja. Usamaphunzire  Baibulo chifukwa palibe chimene ukusowa pa moyo wako.” Koma khalidwe langa lachiwerewere lija ndi limene linandivuta kusiya.

Komabe ndinkadziwa kuti n’zotheka kusintha ndipo mawu a m’Baibulo a pa 1 Akorinto 6:9-11 anandifika pamtima. Lembali limati: “Kodi zoonadi inu simukudziwa kuti anthu osalungama sadzalowa mu ufumu wa Mulungu? Musasocheretsedwe. Adama, opembedza mafano, achigololo, amuna amene amagonedwa ndi amuna anzawo, amuna ogona amuna anzawo . . . sadzalowa mu ufumu wa Mulungu. Ndipo ena mwa inu munali otero. Koma mwasambitsidwa kukhala oyera.” Ndinkadziwa kuti Yehova anathandiza anthu amenewa kusintha ndipo ndinkakhulupirira kuti andithandizanso ineyo. Zinanditengera zaka zambiri kuti ndisinthe ndipo malangizo a Mboni za Yehova ndiponso chikondi chawo zinandithandiza kwambiri.

PHINDU LIMENE NDAPEZA: Panopo ndine munthu wabwinobwino. Ndinakwatira ndipo ine ndi mkazi wanga tikuphunzitsa mwana wathu kuti azitsatira malangizo a m’Baibulo pa moyo wake. Ndinasiyiratu khalidwe langa lija ndipo ndikusangalala kwambiri ndi madalitso auzimu. Ndikutumikira mumpingo wathu monga mkulu ndipo ndathandiza anthu ena kuphunzira choonadi cha m’Mawu a Mulungu. Mayi anga anasangalala kwambiri kuona kuti ndasintha khalidwe langa, choncho nawonso anayamba kuphunzira Baibulo moti ndikunena pano ndi Mkhristu wobatizidwa. Komanso mchemwali wanga wina amene anali ndi khalidwe lachiwerewere anasintha n’kukhala wa Mboni za Yehova.

Ena mwa anthu amene akudziwa mmene moyo wanga unalili kale azindikira kuti panopo khalidwe langa ndi labwino kwambiri. Ineyo ndikudziwa chimene chandithandiza kuti ndisinthe chonchi. Kale ndinkapempha madokotala ndi alangizi kuti andithandize kusintha khalidwe langa koma malangizo amene ankandipatsa anali osathandiza. Koma Yehova wandithandiza kwambiri. Ngakhale kuti ndinkaona kuti ndine munthu wachabechabe, Yehova anandisonyeza chikondi kwambiri ndipo anandilezera mtima. Ndaona kuti Mulungu wodabwitsa, wanzeru komanso wachikondi. Iye anali nane chidwi komanso anali wofunitsitsa kundithandiza. Kudziwa zimenezi n’kumene kwandithandiza kwambiri kuti ndisinthe moyo wanga.

“Sindinkakhala wosangalala komanso ndinkaona kuti ndine wachabechabe.”​—KAZUHIRO KUNIMOCHI

CHAKA CHOBADWA: 1951

DZIKO: JAPAN

POYAMBA: NDINKAKONDA KUCHITA MPIKISANO WOPALASA NJINGA

KALE LANGA: Ndinakulira ku Japan m’tauni inayake imene ili mphepete mwa nyanja m’dera la Shizuoka. M’banja mwathu tinalipo ana 8 ndipo tinkakhala m’nyumba yaing’ono. Bambo anga anali ndi shopu yogulitsira komanso kukonzeramo njinga. Kuyambira ndili mwana, bambo ankakonda kupita nane ku mpikisano wopalasa njinga ndi cholinga choti ndizikonda masewerawo. Kenako iwo anayamba kukonza zoti ndidzakhale katswiri wa mpikisano wopalasa njinga. Ndili ku sukulu ya pulayimale bambo anayamba kundiphunzitsa kupalasa njinga. Ndipo ndili ku sekondale ndinawina katatu mpikisano womwe unkachitika chaka chilichonse. Anandisankha kuti ndipite ku yunivesite koma ndinaganiza zokayamba sukulu yophunzitsa kupalasa njinga. Ndili ndi zaka 19 ndinakhala katswiri pa masewerawa.

Nthawi imeneyo cholinga changa chinali choti ndidzakhale katswiri m’dziko lonse la Japan pa masewera opalasa njinga. Ndinkafuna kuti ndizidzapeza ndalama zambiri n’cholinga choti banja langa lizidzasangalala. Choncho ndinayamba kulimbikira kwambiri maphunziro anga. Nthawi zonse ndikakumana ndi vuto  pa masewerawa ndinkadziuza kuti ndinabadwa kuti ndizidzapalasa njinga choncho ndiyenera kupitirizabe. Ndikatero ndinkapitirizadi. Kenako chifukwa cha khama langali ndinayamba kupeza ndalama zambiri. M’chaka changa choyamba kuchita nawo mpikisano, ndinakhala nambala wani pa akatswiri onse atsopano opalasa njinga. M’chaka chotsatira ndinasankhidwa kuti ndikachite nawo mpikisano umene munthu akawina amakhala katswiri m’dziko lonse la Japan. Koma kwa zaka 6 ndinkakhala nambala 2 pa mpikisanowu.

Nthawi zonse ndinkakhala m’gulu la anthu amene asankhidwa kuti alandire mphoto chifukwa chopambana mpikisano. Anthu anandipatsa dzina lakuti ‘samvamtunda wa ku Tokai.’ Sindinkafuna kuti munthu aliyense andipose. Kenako anthu anayamba kundiopa chifukwa sindinkachitira chifundo aliyense amene ndikupikisana naye. Ndinalemera kwambiri ndipo ndinkaona kuti ndingathe kugula chilichonse chimene ndikufuna. Ndinagula nyumba yomwenso inali ndi chipinda chochitira masewera olimbitsa thupi. Chipinda chimenechi chinali ndi zipangizo zapamwamba kwambiri. Ndinagulanso galimoto yodula kwambiri imene mtengo wake unali pafupifupi mtengo wa nyumba ija. Poganizira zam’tsogolo, ndinayamba bizinezi yogula ndi kugulitsa nyumba komanso kugula masheya a m’makampani.

Koma ngakhale ndinali ndi zonsezi, sindinkakhala wosangalala komanso ndinkaona kuti ndine wachabechabe. Pa nthawiyi n’kuti nditakwatira komanso ndili ndi ana, koma sindinali bambo wabwino. Nthawi zambiri ndinkapsera mtima mkazi wanga komanso ana anga ndipo ndinkachita zimenezi ngakhale pa zinthu zazing’ono. Iwo anayamba kuchita nane mantha kwambiri moti nthawi zambiri ankandiyang’anitsitsa nkhope kuti adziwe ngati ndakwiya.

Patapita nthawi mkazi wanga anayamba kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova. Zimenezi zinachititsa kuti zinthu zisinthe m’banja mwathu. Mkazi wanga anandipempha kuti akufuna kuti azipita ku misonkhano ya a Mboni. Choncho ndinaganiza kuti tizipita tonse. Ndimakumbukirabe tsiku lina usiku pamene bambo wina wa Mboni amene anali mkulu mumpingo anabwera kunyumba kwathu kudzayamba kuphunzira nane Baibulo. Zimene ndinaphunzirazo zinandikhudza kwambiri.

MMENE BAIBULO LINASINTHIRA MOYO WANGA: Sindidzaiwala mmene ndinakhudzidwira nditawerenga Aefeso 5:5. Lembali limati: “Wadama kapena wodetsedwa kapena waumbombo, umene ndiwo kupembedza mafano, sadzalowa mu ufumu wa Khristu ndi wa Mulungu.” Ndinaona kuti mpikisano wopalasa njinga ndi wofanana ndi kutchova juga ndipo umachititsa munthu kukhala ndi mtima wofuna kuti zonse zikhale zako. Chikumbumtima changa chinayamba kundivutitsa kwambiri. Ndinazindikira kuti ngati ndikufuna kusangalatsa Yehova Mulungu ndiyenera kusiya kuchita mpikisano umenewu. Koma kusankha kuchita zimenezi kunali kovuta kwambiri.

Chaka chimenecho n’kuti zinthu zitandiyendera bwino kwambiri pa mpikisano wopalasa njinga moti ndinkafunitsitsa kuti zipitirize kundiyendera bwino. Koma ndinkaona kuti kuchita mpikisano sikunkandithandiza kuti ndizikhala ndi mtendere wamumtima, koma kuphunzira Baibulo n’kumene kunkandithandiza. Nditayamba kuphunzira Baibulo ndinachita nawo mpikisano katatu kokha ndipo mumtima mwanga sindinkafuna kusiya mpikisanowu. Komanso ndinkadera nkhawa kuti mwina ndizilephera kusamalira banja langa ndikasiya kuchita mpikisanowu. Ndinasowa chochita. Ndiponso achibale anga anayamba kundivutitsa chifukwa chophunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova. Nawonso bambo anga anakwiya kwambiri. Ndinathedwa nzeru moti nthawi zambiri ndinkakhala ndi nkhawa ndipo ndinayamba kudwala zilonda za m’mimba.

Komabe ndinapitiriza kuphunzira Baibulo komanso kusonkhana ndi Mboni za Yehova ndipo zimenezi ndi zimene zinandithandiza kwambiri. Pang’ono ndi pang’ono chikhulupiriro changa chinayamba kulimba. Ndinapemphera kwa Yehova kuti aziyankha mapemphero anga komanso kuti andithandize kukhala ndi chikhulupiriro choti ayankhadi. Nkhawa yanga inachepa kwambiri mkazi wanga atandiuza mawu olimbikitsa. Iye anandiuza kuti akhoza kukhala wosangalala ngakhale atamakhala m’nyumba yaing’ono. Pang’ono ndi pang’ono ubwenzi wanga ndi Mulungu unayamba kukula.

PHINDU LIMENE NDAPEZA: Ndaphunzira kuti mawu a Yesu opezeka pa Mateyu 6:33 ndi oonadi. Iye anati: “Pitirizani kufunafuna ufumu choyamba ndi chilungamo chake, ndipo zina zonsezi zidzawonjezedwa kwa inu.” Sitinasowepo “zina zonse” zimene Yesu anafotokoza palembali zomwe ndi zinthu zofunika kwambiri pa moyo. Panopa ndimapeza ndalama zochepa kwambiri poyerekeza ndi zimene ndinkapeza. Patha zaka 20 kuchokera pamene ndinasiya mpikisano koma pazaka zonsezi banja lathu silinasowepo kanthu.

Kuwonjezera pamenepa, ndikamagwira ntchito kapena kulambira ndi Akhristu anzanga, ndimakhala wosangalala kwambiri kuposa kale. Chifukwa chotanganidwa ndi zinthu zauzimu, ndimaona kuti nthawi ikufulumira kwambiri. Ndiponso zinthu m’banja langa zikuyenda bwino kwambiri. Panopa ana anga atatu onse, limodzi ndi akazi awo, akutumikira Yehova mokhulupirika.