Kodi Mukudziwa?
Kodi Mukudziwa?
Kodi Baraba anapalamula milandu yotani?
▪ Mauthenga Abwino onse anayi amatchula Baraba, amene bwanamkubwa wachiroma Pontiyo Pilato anamumasula n’kusiya Yesu. Baibulo limasonyeza kuti Baraba anali “mkaidi wowopsa” komanso munthu “wachifwamba.” (Mateyu 27:16; Yohane 18:40) Iye anali m’ndende ya Aroma ku Yerusalemu ‘limodzi ndi oukira boma amene anapha munthu pa kuukira kwawoko.’—Maliko 15:7.
Ngakhale kuti palibe mabuku ofotokoza milandu imene Baraba anapalamula, akatswiri ena amaganiza kuti Baraba anali m’gulu la zigawenga zimene zinali ku Isiraeli m’nthawi ya atumwi. Iwo amaganiza choncho chifukwa Baraba akutchulidwa pamodzi ndi anthu oukira boma. Mwachitsanzo katswiri wina wolemba mbiri yakale dzina lake Flavius Josephus analemba kuti, pa nthawi imeneyo kunali magulu a zigawenga amene ankachita zachiwawa. Zigawengazo zinkanena kuti cholinga chawo pochita zimenezi chinali kumenyera ufulu wa Ayuda osauka. Pofika zaka za m’ma 50 C.E., chiwawa chinali ponseponse chifukwa cha magulu oukira boma amenewa. Kenako mu 66 C.E., Ayuda anathamangitsa Aroma ku Yudeya ndipo ambiri mwa Ayuda amenewa anali zigawenga zimenezi.
Dikishonale ina yomasulira mawu a m’Baibulo imanena kuti: “Baraba ayenera kuti anali m’gulu la zigawenga za m’madera akumidzi. Zigawengazi zinkakondedwa kwambiri ndi anthu wamba chifukwa chakuti zinkabera anthu olemera ku Isiraeli ndipo zinkasowetsa mtendere boma la Aroma.”—The Anchor Bible Dictionary.
Kodi mu ulamuliro wa Aroma munthu ankapatsidwa chilango chophedwa ngati chimene Yesu analandira akapalamula mlandu wotani?
▪ Chilango chimene Aroma ankapereka kwa anthu oukira boma, zigawenga ndi anthu ena osagwirizana ndi ulamuliro wa boma, chinali kuwapachika pa mtengo wozunzirapo anthu n’kuwasiya kuti afere pompo. Munthu amene walandira chilango chimenechi ankaonedwa kuti wafa imfa yowawa kwambiri.
Buku lina linanena kuti: “Munthu ankamupachika pamalo oti aliyense aone ndipo imfa imeneyi inali yochititsa manyazi komanso yowawa kwambiri. Ankachita zimenezi n’cholinga chofuna kuopseza aliyense amene angaganize zoukira boma.” (Palestine in the Time of Jesus) Ponena za mmene anthu oswa malamulo ankawaphera, munthu wina wolemba mabuku wa ku Roma ananena kuti: “Ankasankha msewu womwe munkadutsa anthu ambiri ndi cholinga choti anthu azichita mantha kuukira boma akaona anthu opachikidwayo.”
Malinga ndi zimene Josephus ananena, mkaidi wina amene anagwidwa ndi asilikali a Tito pa nthawi imene asilikaliwo ankafuna kulanda mzinda wa Yerusalemu mu 70 C.E., anaphedwa m’njira imeneyi pafupi ndi mpanda wa mzindawu. Iwo anachita zimenezi pofuna kuopseza anthu a mumzindawo kuti alengeze kuti agonja. Kenako mzinda wonsewu utagonjetsedwa, anthu ambiri anaphedwanso mwa njira imeneyi.
Chiwerengero chachikulu kwambiri cha anthu amene anaphedwa nthawi imodzi mwa njira imeneyi, malinga ndi zimene zinalembedwa m’mabuku akale, ndi anthu okwana 6,000. Anthu amenewa anali akapolo ndi anthu ochita masewera omenyana ndi nyama, amene motsogoleredwa ndi Spartacus anaukira boma la Roma mu 73 mpaka mu 71 B.C.E. Oukirawa anagonja pa nkhondoyi ndipo anaphedwera m’mbali mwa msewu wochokera ku Capua kupita ku Roma.
[Chithunzi patsamba 10]
“Timasulireni Baraba” Chithunzi Chojambulidwa ndi Charles Muller, 1878