Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Tsanzirani Amene Wakulonjezani Moyo Wosatha

Tsanzirani Amene Wakulonjezani Moyo Wosatha

“Muzitsanzira Mulungu, monga ana ake okondedwa.”—AEF. 5:1.

1. Kodi ndi luso liti limene lingatithandize kutsanzira makhalidwe a Mulungu?

ANTHUFE tinalengedwa ndi luso lotha kumvetsa mmene anthu ena akumvera ngakhale kuti sitinakumanepo ndi zimene zikuwachitikira. (Werengani Aefeso 5:1, 2.) Kodi tingagwiritse ntchito bwanji lusoli mwanzeru? Nanga tingatani kuti tisaligwiritse ntchito molakwika?

2. Kodi Yehova amamva bwanji tikamakumana ndi mavuto?

2 Timasangalala tikaganizira zimene Mulungu walonjeza. Mwachitsanzo, odzozedwa okhulupirika adzalandira moyo wosafa kumwamba ndipo a nkhosa zina adzalandira moyo wosatha padziko lapansi. (Yoh. 10:16; 17:3; 1 Akor. 15:53) Kaya tili ndi chiyembekezo chopita kumwamba kapena chodzakhala ndi moyo wosatha padziko lapansi, mavuto amene tikukumana nawowa adzatha. Yehova amadziwa bwino mavuto amene tikukumana nawo ngati mmene ankadziwira mavuto a Aisiraeli ku Iguputo. Paja Baibulo limati: “Pamene iwo anali kuvutika m’masautso awo onse, iyenso anali kuvutika.” (Yes. 63:9) Patapita zaka mahandiredi angapo, adani a Aisiraeli sankafuna kuti Aisiraeliwo amangenso kachisi. Koma Yehova anauza Aisiraeli kuti: “Amene akukukhudzani, akukhudza mwana wa diso langa.” (Zek. 2:8) Yehova amachitira chifundo anthu ake ngati mmene mayi amachitira ndi mwana wake. (Yes. 49:15) Choncho Yehova amamvetsa zomwe tikukumana nazo ndipo tikhoza kumutsanzira.—Sal. 103:13, 14.

YESU ANKASONYEZA CHIKONDI CHA MULUNGU

3. N’chiyani chikusonyeza kuti Yesu ankamvera anthu chifundo?

3 Yesu ankamvetsa mavuto a anthu ngakhale kuti mavuto a anthu ena anali oti iyeyo sanakumanepo nawo. Mwachitsanzo, anthu wamba ankaopa atsogoleri achipembedzo amene ankawanamiza komanso kuwapanikiza ndi malamulo ambirimbiri. (Mat. 23:4; Maliko 7:1-5; Yoh. 7:13) Yesu ankamvetsa mavuto a anthu wambawo ngakhale kuti iye sankaopa atsogoleriwo ndipo iwo sanamunamizepo. Yesu ataona chikhamu cha anthu, “anawamvera chisoni, chifukwa anali onyukanyuka ndi otayika ngati nkhosa zopanda m’busa.” (Mat. 9:36) Yesu anatengera Atate wake ndipo ankakonda anthu komanso kuwachitira chifundo.—Sal. 103:8.

4. Kodi Yesu ankachita chiyani akaona anthu akuvutika?

4 Yesu akaona anthu ovutika ankawasonyeza chikondi powathandiza. Apa tingati ankatsanzira Atate wake. Pa nthawi ina, Yesu ndi ophunzira ake anapita kutali kwambiri kukalalikira. Ndiyeno anafuna kupeza malo oti apumule. Koma athu ambirimbiri atafika, iye anawamvera chifundo n’kuyamba “kuwaphunzitsa zinthu zambiri.”—Maliko 6:30, 31, 34.

KODI TINGASONYEZE BWANJI CHIKONDI CHA YEHOVA?

5, 6. Kodi tingasonyeze bwanji chikondi cha Yehova kwa anzathu? Perekani chitsanzo. (Onani chithunzi patsamba 24.)

5 Tiyenera kusonyeza chikondi cha Yehova pochita zinthu ndi anzathu. Tiyerekeze kuti pali mnyamata wina dzina lake Alani. Iye akuganizira za m’bale wina amene amavutika kuwerenga chifukwa cha ukalamba. M’baleyo amavutikanso kuyenda kuti akalalikire. Kenako Alani akukumbukira mawu a Yesu akuti: “Zimene mukufuna kuti anthu akuchitireni, inuyo muwachitire zomwezo.” (Luka 6:31) Ndiyeno Alani akudzifunsa kuti, ‘Kodi ndimafuna kuti anthu ena azindichitira zotani?’ Kenako akudziyankha kuti, ‘Ndimafuna kuti azisewera nane mpira.’ Koma Alani akudziwa kuti m’bale wachikulire uja sangasewere mpira. Choncho funso limene Alani ayenera kudzifunsa ndi lakuti, ‘Kodi ndikanakhala m’baleyu ndikanafuna kuti anthu ena andichitire zotani?’

6 Ngakhale kuti Alani si wachikulire, iye akudziwa mavuto amene anthu ena amakumana nawo. Amachita chidwi ndi m’baleyo ndipo amayesetsa kumumvetsera akamafotokoza mavuto ake. Pang’ono ndi pang’ono Alani akumvetsa mavuto amene m’bale uja akukumana nawo. Chifukwa cha zimenezi, Alani akudziwa mmene angathandizire m’baleyo ndipo akufunitsitsa kuchita zimenezi. Nafenso tiyenera kuchita chimodzimodzi. Kuti tisonyeze chikondi cha Yehova, tiyenera kumvetsa mavuto amene abale athu akukumana nawo.—1 Akor. 12:26.

Tsanzirani chikondi cha Yehova (Onani ndime 7)

7. Kodi tingatani kuti timvetse mavuto amene abale athu akukumana nawo?

7 Kunena zoona, si zophweka kumvetsa mavuto a anthu ena chifukwa mavuto ena ndi oti sitinakumanepo nawo. Anthu ena akuvutika chifukwa chovulala, matenda kapena ukalamba. Enanso akuvutika maganizo chifukwa cha nkhawa kapena kuchitiridwa nkhanza. Ndiyenso pali ena amene ali m’banja ndi anthu osakhulupirira kapena akulera okha ana. Ndiye tingasonyeze bwanji chikondi cha Yehova kwa anthu amene akukumana ndi mavuto omwe sitinakumanepo nawo? Tiyenera kumawamvetsera mwachifundo akamafotokoza mavuto awo kuti tidziwe mmene akumvera mumtima mwawo n’kuona mmene tingawathandizire. Mwina tingawalimbikitse ndi mfundo za m’Baibulo kapena kuwathandiza m’njira ina. Tikamatero ndiye kuti tikutsanzira Yehova.—Werengani Aroma 12:15; 1 Petulo 3:8.

TSANZIRANI CHIFUNDO CHA YEHOVA

8. N’chiyani chinathandiza Yesu kutsanzira chifundo cha Yehova?

8 Yesu ananena kuti: “Wam’mwambamwamba . . . ndi wachifundo kwa osayamika ndi kwa oipa.” (Luka 6:35) Yesuyo ankatsanzira chifundo cha Yehova. Kodi n’chiyani chinamuthandiza pa nkhaniyi? Iye ankakomera anthu mtima ndipo ankaganizira mmene mawu ndi zochita zake zingawakhudzire. Mwachitsanzo, mayi wina yemwe ankadziwika kuti ndi wochimwa anabwera kwa Yesu n’kuyamba kulira ndipo misozi yake inanyowetsa mapazi a Yesu. Yesu anazindikira kuti mayiyo walapa ndipo zingamupweteke kwambiri ngati atamuthamangitsa mopanda chifundo. Choncho iye anayamikira mayiyo n’kumukhululukira. Mfarisi wina atasonyeza kuti sakugwirizana ndi zimenezi, Yesu anamuthandizanso mokoma mtima.—Luka 7:36-48.

9. Kodi tingatsanzire bwanji chifundo cha Yehova? Perekani chitsanzo.

9 Kodi ifeyo tingatsanzire bwanji chifundo cha Yehova? Mtumwi Paulo analemba kuti: “Kapolo wa Ambuye sayenera kukangana ndi anthu, koma ayenera kukhala wodekha [kapena kuti wosamala polankhula] kwa onse.” (2 Tim. 2:24) Munthu wodekha amasamala polankhula ndi anthu n’cholinga choti mawu ake asawapweteke. Kodi inuyo mungatani ngati oyang’anira kuntchito kwanu sagwira bwino ntchito yawo? Nanga munganene zotani ngati m’bale wina amene anasiya kusonkhana wafika ku Nyumba ya Ufumu? Kodi mungatani ngati munthu wina mu utumiki wakuuzani kuti alibe nthawi yokambirana nanu? Kodi mudzachita zinthu mwachifundo? Nanga mungayankhe bwanji ngati mkazi wanu wafunsa kuti, “Bwanji mwasankha zochita musanandifunse maganizo?” Choyamba tiyenera kuganizira mmene mnzathuyo akumvera mumtima mwake. Kenako tiyenera kuganizira mmene mawu athu angamukhudzire. Tikatero tidzatsanzira Yehova n’kumuyankha mnzathuyo mokoma mtima.—Werengani Miyambo 15:28.

TSANZIRANI NZERU ZA MULUNGU

10, 11. Kodi tingatsanzire bwanji nzeru za Mulungu? Perekani chitsanzo.

10 Popeza timatha kumvetsa zinthu zomwe sitinakumanepo nazo, tikhoza kutsanzira nzeru za Yehova n’kuoneratu zotsatira za zochita zathu. Limodzi mwa makhalidwe akuluakulu a Yehova ndi nzeru. Iye amagwiritsa ntchito khalidweli kuti adziwe bwinobwino zotsatira za zinazake. Ife tilibe nzeru ngati za Yehova, koma tikhoza kuoneratu zotsatira za zochita zathu. Koma n’zomvetsa chisoni kuti Aisiraeli analephera kuchita zimenezi. Iwo anaiwala zonse zimene Yehova anawachitira ndipo Mose ankadziwa kuti Aisiraeliwo apitirizabe kuchita zoipa. Mose ananena kuti Aisiraeliwo “ndi mtundu wopanda nzeru, ndipo ndi osazindikira. Akanakhala anzeru, akanaganizira mozama zimenezi. Akanalingalira kuti ziwathera bwanji.”—Deut. 31:29, 30; 32:28, 29.

11 Nafenso tingatsanzire Yehova poganizira kapena kuona m’maganizo mwathu zotsatira za zochita zathu. Mwachitsanzo, ngati tili pa chibwenzi tiyenera kukumbukira kuti n’zosavuta kuti tichite chiwerewere. Sitiyenera kuganizira kapena kuchita chilichonse chimene chingasokoneze ubwenzi wathu ndi Yehova. M’malomwake tiyenera kuchita zinthu mogwirizana ndi zimene Baibulo limanena. Paja limati: “Wochenjera ndi amene amati akaona tsoka amabisala, koma anthu osadziwa zinthu amangopitabe ndipo amalangidwa.”—Miy. 22:3.

PEWANI KUGANIZIRA ZOIPA

12. Kodi zimene timaganizira zingasokoneze bwanji ubwenzi wathu ndi Yehova?

12 Munthu wanzeru amadziwa kuti maganizo athu ali ngati moto. Moto umatithandiza kuti tiphike komanso kuchita zinthu zina. Koma ngati sitisamala, umatha kuwotcha nyumba n’kupha anthu. N’chimodzimodzi ndi maganizo. Zimene timaganiza zikhoza kutithandiza kutsanzira Yehova. Koma munthu amene amakonda kuganizira zinthu zoipa tsiku lina akhoza kuchitadi zinthuzo n’kusokoneza ubwenzi wake ndi Yehova.—Werengani Yakobo 1:14, 15.

13. Kodi Hava ankaganizira zinthu ziti zomwe zinamuchititsa kuti achimwe?

13 Chitsanzo pa nkhaniyi ndi Hava. Kodi iye anayamba bwanji kulakalaka “zipatso za mtengo wodziwitsa chabwino ndi choipa”? (Gen. 2:16, 17) Njoka inamuuza kuti: “Kufa simudzafa ayi. Mulungutu akudziwa kuti tsiku limene mudzadye chipatso cha mtengo umenewu, maso anu adzatseguka ndithu, ndipo mudzafanana ndi Mulungu. Mudzadziwa zabwino ndi zoipa.” Hava ayenera kuti anakopeka ndi mfundo imeneyi. Iye anayamba kuganiza kuti bola azisankha yekha zochita osati kumangouzidwa kuti ichi n’chabwino ichi n’choipa. Kuganizira kwambiri mfundoyi kunamugwetsera m’mavuto. Ndiyeno iye “anayamba kuona kuti zipatso za mtengowo n’zokoma kudya, zokhumbirika ndi zosiririka.” Kenako “anathyola chipatso cha mtengowo n’kudya. Pambuyo pake, anapatsako mwamuna wake pamene anali limodzi, ndipo nayenso anadya.” (Gen. 3:1-6) Izi zinachititsa kuti uchimo ulowe m’dziko n’kuyambitsa imfa.—Aroma 5:12.

14. Kodi Baibulo limatithandiza bwanji kupewa chiwerewere?

14 N’zoona kuti tchimo la Hava silinali la chiwerewere. Koma kumbukirani chenjezo limene Yesu anapereka pa nkhani yoganizira zachiwerewere. Iye anati: “Aliyense woyang’anitsitsa mkazi mpaka kumulakalaka, wachita naye kale chigololo mumtima mwake.” (Mat. 5:28) Nayenso Paulo anapereka chenjezo lakuti: “Musamakonzekere kuchita zilakolako za thupi.”—Aroma 13:14.

15. Kodi chuma chimene tiyenera kuyesetsa kuti tikhale nacho ndi chiti? Perekani chifukwa.

15 Anthu ena amaganiza kuti akhoza kusangalala ngati atasiya kutumikira Yehova mwakhama n’kupeza chuma chambiri. Koma maganizo amenewa ndi oopsa. Paja Baibulo limati zinthu zamtengo wapatali za munthu wachuma “m’maganizo mwake zili ngati mpanda woteteza.” (Miy. 18:11) Yesu anapereka fanizo la ‘munthu amene anadziunjikira yekha chuma, koma amene sanali wolemera kwa Mulungu.’ (Luka 12:16-21) Zimene munthuyo anachita sizinamuthere bwino. Koma tikaunjika ‘chuma kumwamba’ n’kumachita zimene Yehova amafuna, iye amasangalala ndipo ifenso timakhala osangalala. (Mat. 6:20; Miy. 27:11) Ubwenzi wathu ndi Yehova uli ngati chuma choposa chuma chilichonse padzikoli.

MUSAMADE NKHAWA KWAMBIRI

16. Kodi tingatani kuti tichepetse nkhawa?

16 Taganizirani za nkhawa imene tingakhale nayo ngati tikufunitsitsa “kudziunjikira chuma padziko lapansi.” (Mat. 6:19) Yesu anapereka fanizo posonyeza kuti “nkhawa za moyo wa m’nthawi ino ndiponso chinyengo champhamvu cha chuma” zingatilepheretse kutumikira Mulungu. (Mat. 13:18, 19, 22) Kuwonjezera pa nkhawa zimene tanenazi, ena amakhalanso ndi nkhawa yoti zinthu zoipa zikhoza kuwachitikira nthawi iliyonse. Koma kupanda kusamala, kuda nkhawa kwambiri kukhoza kutidwalitsa kapena kusokoneza ubwenzi wathu ndi Yehova. Choncho tizidalira Yehova ndiponso kukumbukira kuti “nkhawa mumtima mwa munthu ndi imene imauweramitsa, koma mawu abwino ndi amene amausangalatsa.” (Miy. 12:25) Anthufe timasangalala tikamva mawu olimbikitsa kuchokera kwa anthu amene amatimvetsa. Choncho tikakhala ndi vuto tikhoza kuchepetsa nkhawa ngati tifotokozera makolo anthu, mkazi kapena mwamuna wathu kapena munthu wina amene angatithandize kudziwa maganizo a Yehova pa nkhaniyo.

17. Kodi Yehova angatithandize bwanji kuti tisamade nkhawa kwambiri?

17 Tiyenera kudziwa kuti Yehova ndi amene amamvetsa nkhawa zathu kuposa aliyense. Paja Baibulo limati: “Musamade nkhawa ndi kanthu kalikonse, koma pa chilichonse, mwa pemphero ndi pembedzero, pamodzi ndi chiyamiko, zopempha zanu zidziwike kwa Mulungu. Mukatero, mtendere wa Mulungu umene umaposa kuganiza mozama kulikonse, udzateteza mitima yanu ndi maganizo anu mwa Khristu Yesu.” (Afil. 4:6, 7) Tisamade nkhawa kwambiri chifuwa tingathandizidwe ndi Akhristu anzathu, akulu, kapolo wokhulupirika, angelo, Yesu ndiponso Yehova.

18. Kodi zimene timaganiza zingatithandize bwanji?

18 Taona kuti zimene timaganiza zingatithandize kutsanzira makhalidwe a Yehova monga chikondi. (1 Tim. 1:11; 1 Yoh. 4:8) Tidzakhala osangalala kwambiri ngati timakonda anzathu, kuganizira zotsatira za zochita zathu ndiponso kupewa kuda nkhawa kwambiri. Choncho tiyeni tizigwiritsa ntchito bwino luso loona zinthu m’maganizo mwathu. Tiziganizira madalitso amene Yehova watilonjeza, tizitsanzira chikondi chake, chifundo chake, nzeru zake ndiponso tisamade nkhawa kwambiri.—Aroma 12:12.