Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Khalani Maso Satana Akufuna Kukumezani

Khalani Maso Satana Akufuna Kukumezani

“Khalani maso. Mdani wanu Mdyerekezi akuyendayenda uku ndi uku ngati mkango wobangula, wofunitsitsa kuti umeze winawake.”—1 PET. 5:8.

1. Kodi zinatheka bwanji kuti mngelo wabwino akhale Satana?

POYAMBA, Satana anali mngelo wabwino ndipo anali pa ubwenzi ndi Yehova. Koma kenako ankafuna kuti anthu azimulambira. Maganizo amenewa anamukulira mpaka anachimwa. (Yak. 1:14, 15) Satana “sanakhazikike m’choonadi.” Iye anayamba kudana ndi ulamuliro wa Yehova ndipo anakhala “tate wake wa bodza.”—Yoh. 8:44.

2, 3. Kodi mayina akuti “Satana,” “Mdyerekezi,” “njoka yakale ija” ndiponso “chinjoka” amatanthauza chiyani?

2 Kuchokera pa nthawi imene Satana anachimwa, iye wakhala mdani wamkulu wa Yehova ndi anthu. Mayina omwe amadziwika nawo amasonyeza kuti iye ndi woipa kwambiri. Mwachitsanzo, dzina lakuti Satana limatanthauza “Wotsutsa” ndipo zimenezi zikusonyeza kuti iye amalimbana kwambiri ndi ulamuliro wa Yehova. Iye amafunitsitsa ulamulirowu utatha.

3 Pa Chivumbulutso 12:9, Satana amatchulidwa ndi mayina akuti “Mdyerekezi,” “njoka yakale ija” ndiponso “chinjoka.” Dzina lakuti Mdyerekezi limatanthauza “Woneneza” ndipo limasonyeza kuti Satana wakhala akuneneza Yehova kuti ndi wabodza. Koma dzina lakuti “njoka yakale ija,” limatikumbutsa nthawi yomwe anagwiritsa ntchito njoka popusitsa Hava m’munda wa Edeni. Ndiyeno dzina lakuti “chinjoka,” likusonyeza kuti iye ali ngati chilombo choopsa chimene chikulimbana ndi zolinga za Yehova ndipo chimafuna kuwononga atumiki a Mulungu.

4. Kodi tikambirana chiyani m’nkhaniyi?

4 Tikaganizira mayinawa, titha kuona kuti tiyenera kusamala kuti Satana asatilepheretse kutumikira Yehova. M’pake kuti Baibulo limatichenjeza kuti: “Khalanibe oganiza bwino ndipo khalani maso. Mdani wanu Mdyerekezi akuyendayenda uku ndi uku ngati mkango wobangula, wofunitsitsa kuti umeze winawake.” (1 Pet. 5:8) Choncho m’nkhaniyi tikambirana makhalidwe atatu a Satana omwe akusonyeza kuti tiyenera kusamala naye kwambiri.

SATANA NDI WAMPHAMVU

5, 6. (a) Perekani zitsanzo zosonyeza kuti angelo ndi amphamvu. (b) N’chifukwa chiyani tinganene kuti Satana “ali ndi njira yobweretsera imfa”?

5 Baibulo limanena kuti angelo ndi “amphamvu.” (Sal. 103:20) Iwo ali ndi mphamvu komanso nzeru kuposa anthufe. Angelo okhulupirika amagwiritsa ntchito bwino mphamvu zawo. Mwachitsanzo, mngelo mmodzi yekha anawononga asilikali 185,000 a Asuri. N’zosatheka kuti munthu mmodzi achite zimenezi ndipo ngakhale litakhala gulu la asilikali likhoza kuvutika kupha asilikali onsewo. (2 Maf. 19:35) Pa nthawi ina, mngelo wina anamasula atumwi a Yesu m’ndende m’njira yodabwitsa. Mngeloyo anatsegula zitseko, kutulutsa atumwi kenako n’kutsekanso. Anachita zonsezi asilikali ali pomwepo.—Mac. 5:18-23.

6 Koma Satana amagwiritsa ntchito mphamvu zake kuti achite zinthu zoipa. Iye ndi wamphamvu kwambiri ndipo wapotoza kale anthu ambirimbiri. Paja Baibulo limati iye ndi “wolamulira wa dzikoli” komanso “mulungu wa nthawi ino.” (Yoh. 12:31; 2 Akor. 4:4) Limanenanso kuti Satana Mdyerekezi “ali ndi njira yobweretsera imfa.” (Aheb. 2:14) Izi sizikutanthauza kuti iye ndi amene amapha munthu aliyense. Koma mtima wake wofuna kupha anthu wafala kwambiri m’dzikoli. Komanso kungoyambira pamene Hava anakhulupirira bodza la Satana ndipo Adamu sanamvere Mulungu, uchimo ndi imfa zafalikira kwa anthu onse. (Aroma 5:12) Choncho tinganenedi kuti Satana “ali ndi njira yobweretsera imfa.” M’pake kuti Yesu ananena kuti iye ndi “wopha anthu.” (Yoh. 8:44) Apatu mutha kuona kuti Satana ndi mdani wamphamvu kwambiri.

7. N’chiyani chikusonyeza kuti ziwanda ndi zamphamvu?

7 Tikamatsutsa Satana timakhala pa udani ndi Satanayo komanso aliyense amene ali kumbali yake potsutsa ulamuliro wa Yehova. Kumbali yakeyo kulinso ziwanda. (Chiv. 12:3, 4) Ziwandazi ndi zamphamvunso ndipo zakhala zikuzunza anthu kwa nthawi yaitali. (Mat. 8:28-32; Maliko 5:1-5) Popeza ziwanda komanso wolamulira ziwandazo amadana nafe, tiyenera kusamala kwambiri. (Mat. 9:34) Popanda thandizo la Yehova sitingalimbane ndi Satana.

SATANA NDI WOLUSA

8. (a) Kodi cholinga cha Satana ndi chotani? (Onani chithunzi patsamba 9.) (b) Kodi inuyo mwaona zinthu ziti zimene zakutsimikizirani kuti Satana ndi wolusa?

8 Mtumwi Petulo anayerekezera Satana ndi “mkango wobangula.” Buku lina linanena kuti mawu achigiriki omwe anamasuliridwa kuti “wobangula,” amatanthauza “kulira kwa nyama yolusa yomwe ili ndi njala.” Izitu zikugwirizana ndi zochita za Satana. Ngakhale kuti dziko lonse lili m’manja mwake, iye akulusirabe anthu ambiri. (1 Yoh. 5:19) Satana ali ngati chilombo cholusa chomwe sichikhuta dzikoli koma chimaona kuti chingakhute ngati chitadya Akhristu odzozedwa kapena a “nkhosa zina.” (Yoh. 10:16; Chiv. 12:17) Satana wakhala akufunitsitsa kumeza atumiki a Yehova kuyambira m’nthawi ya atumwi mpaka masiku ano.

9, 10. (a) Kodi Satana ankachitira zotani mtundu wa Aisiraeli pofuna kulepheretsa cholinga cha Yehova? (Perekani zitsanzo.) (b) N’chifukwa chiyani Satana ankalusira kwambiri mtundu wa Aisiraeli? (c) Kodi Satana amamva bwanji mtumiki wa Yehova akamachita machimo aakulu?

9 Mkango wolusa sumvera chisoni nyama ndipo ukapha sudandaula kapena kudziimba mlandu. Choncho Satana sachita chisoni ndi anthu omwe akufuna kuwameza. Mwachitsanzo, Satana sankadandaula pamene Aisiraeli ankachita chiwerewere ndiponso dyera. Kodi mukuganiza kuti Satana anamva bwanji ataona zimene zinachitikira Zimiri chifukwa chochita chiwerewere kapena Gehazi chifukwa cha dyera? Iye ayenera kuti anasangalala kwambiri.—Num. 25:6-8, 14, 15; 2 Maf. 5:20-27.   

Satana amasangalala mtumiki wa Yehova akachita tchimo (Onani ndime 10)

10 N’chifukwa chiyani Satana ankalusira Aisiraeli? Iye ankadziwa kuti Mesiya adzabadwa mumtundu umenewu. Ankadziwanso kuti Mesiyayo ndi amene adzaphwanye mutu wake ndiponso kusonyeza kuti Yehova ndi woyenera kulamulira. (Gen. 3:15) M’pake kuti sankafunira zabwino Aisiraeliwo ndipo ankayesetsa kuti iwo achimwire Yehova. Satana sanamve chisoni pamene Mose analephera kukalowa m’Dziko Lolonjezedwa ndiponso pamene Davide anachimwa. Masiku anonso, Satana amasangalala akaona mtumiki wa Yehova akuchita machimo aakulu. N’kutheka kuti zinthu ngati zimenezi zikachitika, Satana amatonza Yehova.—Miy. 27:11.

11. Kodi Satana anali ndi zolinga zotani pamene ankalusira Sara?

11 Satana ankalusiranso kwambiri anthu amene anali mu mzera wobadwira wa Mesiya. Mwachitsanzo, taganizirani zimene zinachitikira Abulahamu atangouzidwa kuti adzakhala “mtundu waukulu.” (Gen. 12:1-3) Abulahamu ndi Sara atapita ku Iguputo, Farao anatenga Sara kuti akhale mkazi wake. Koma Yehova anapulumutsa Sara. (Werengani Genesis 12:14-20.) Ndiyeno Isake atatsala pang’ono kubadwa, zinthu ngati zimenezi zinachitikanso ku Gerari. (Gen. 20:1-7) Kodi Satana ndi amene ankachititsa zinthu zonsezi? Kodi iye ankaganiza kuti Sara angakopeke ndi chuma cha Farao ndi Abimeleki? Paja Sara anali atachoka mumzinda wotukuka wa Uri n’kumakhala m’mahema. Kodi mwina Satanayo ankaganiza kuti Sara asiya kumvera mwamuna wake ndiponso Yehova n’kuchita chigololo? Baibulo silinena chilichonse. Koma sitikukayikira kuti Satana ankafuna kulepheretsa Sara kudzabereka mbewu yolonjezedwa. Satana sakanadziimba mlandu chifukwa chosokoneza banja la Sara ndiponso ubwenzi wake ndi Yehova. Zimenezi zikusonyezeratu kuti Satana ndi wolusa kwambiri.

12, 13. (a) Kodi Satana anachita zotani Yesu atangobadwa? (b) Kodi Satana amamva bwanji akamaona ana amene akutumikira Yehova mwakhama masiku ano?

12 Patadutsa zaka mahandiredi ambiri, Yesu anabadwa. Kodi Satana anasangalala kuti kwabadwa mwana wofunika kwambiri komanso wokongola? Ayi. Tikutero chifukwa chakuti iye ankadziwa kuti mwanayu adzakhala Mesiya. Yesu anali mbewu imene inalonjezedwa kwa Abulahamu kuti ‘adzawononge ntchito za Mdyerekezi.’ (1 Yoh. 3:8) Kodi Satana akanaganiza kuti kupha mwanayo ikanakhala nkhanza? Ayi. Iye sadandaula akachita zoipa moti mwamsanga anayamba mapulani ofuna kupha mwanayo. Tiyeni tione zimene zinachitika.

13 Mfumu Herode anakwiya koopsa pamene okhulupirira nyenyezi anamuuza kuti akufuna kuona “mfumu ya Ayuda imene yabadwa.” (Mat. 2:1-3, 13) Iye anakonza zoti aphe ana onse aamuna osapitirira zaka ziwiri ku Betelehemu ndi madera ena. (Werengani Mateyu 2:13-18.) Yesu anapulumuka chiwembuchi. Kodi zimenezi zikusonyeza kuti Satana ndi wotani? N’zoonekeratu kuti Satana salemekeza moyo wa munthu ndipo samvera chisoni ana. Iye ndi “mkango wobangula” ndipo tiyenera kusamala naye.

SATANA NDI WACHINYENGO

14, 15. Kodi Satana wachititsa bwanji “khungu maganizo a anthu osakhulupirira”?

14 Satana amadziwa kuti Yehova ndi wachikondi, choncho amachita zinthu mwachinyengo pofuna kuti anthu asiye kumvera Mulungu. (1 Yoh. 4:8) Amapusitsa anthu kuti asamazindikire “zosowa zawo zauzimu.” (Mat. 5:3) Iye “wachititsa khungu maganizo a anthu osakhulupirira, kuti asaone kuwala kwa uthenga wabwino waulemerero wonena za Khristu, yemwe ali chifaniziro cha Mulungu.”—2 Akor. 4:4.

15 Yehova amafuna kuti anthu ‘azidzipereka kwa iye yekha.’ (Eks. 20:5) Ndiyeno Satana amagwiritsa ntchito chipembedzo chonyenga pofuna kupusitsa anthu. Iye amasangalala akaona anthu akulambira zinthu zina monga makolo akale kapena zinthu za m’chilengedwe. Anthu ena amene amaona kuti akulambira bwinobwino Mulungu amapusitsidwa n’kumakhulupirira zinthu zabodza komanso miyambo yachabechabe. Anthu oterewa ndi omvetsa chisoni chifukwa akufanana ndi amene Yehova anawauza kuti: “N’chifukwa chiyani anthu inu mukuwononga ndalama polipirira zinthu zimene si chakudya, ndipo n’chifukwa chiyani mukuvutika kugwirira ntchito zinthu zimene sizikhutitsa? Tcherani khutu kwa ine kuti mudye zabwino, ndiponso kuti moyo wanu usangalale kwambiri ndi zakudya zamafuta.”—Yes. 55:2.

16, 17. (a) N’chifukwa chiyani Yesu anauza Petulo kuti: “Pita kumbuyo kwanga Satana”? (b) Kodi Satana angatipusitse bwanji masiku ano?

16 Satana amatha kupusitsanso atumiki a Yehova akhama. Taganizirani zimene zinachitika Yesu atauza ophunzira ake kuti watsala pang’ono kuphedwa. Petulo anamumvera chisoni n’kumutengera pambali ndipo anamuuza kuti: “Dzikomereni mtima Ambuye. Musalole kuti zimenezi zikuchitikireni ngakhale pang’ono.” Koma Yesu anamuyankha mosanyengerera kuti: “Pita kumbuyo kwanga, Satana!” (Mat. 16:22, 23) N’chifukwa chiyani Yesu ananena Petulo kuti “Satana”? Yesu ankadziwa kuti watsala pang’ono kufa kuti apereke nsembe ya dipo ndiponso kusonyeza kuti Mdyerekezi ndi wabodza. Ndiyeno imeneyo sinali nthawi ‘yodzikomera mtima.’ Satana ankafuna kuti Yesu apuse pa nthawi yovutayo.

17 Ifenso tili kumapeto kwenikweni kwa masiku otsiriza ndipo zinthu zikuvutiravutirabe. Ndiyeno Satana akufuna kuti tipuse, tiyambe ‘kudzikomera mtima’ ndiponso tiiwale zoti tili m’masiku otsiriza. Choncho “khalanibe maso” ndipo musalole kuti zimenezi zikuchitikireni. (Mat. 24:42) Tisayerekeze ngakhale pang’ono kukhulupirira mabodza a Satana oti mapeto ali kutali kapena safika.

18, 19. (a) Kodi njira ina imene Satana amagwiritsa ntchito ndi iti? (b) Kodi Yehova amatithandiza bwanji kuti tikhale maso komanso oganiza bwino?

18 Pali njira inanso imene Satana amagwiritsa ntchito pofuna kutipusitsa. Iye amafuna kuti tiziganiza kuti Mulungu satikonda ndipo sangatikhululukire machimo athu. Koma limeneli ndi bodza lankunkhuniza. Satanayo ndi amene sangakondedwe kapena kukhululukiridwa ndi Yehova. Koma Baibulo limanena kuti: “Mulungu si wosalungama woti angaiwale ntchito yanu ndi chikondi chimene munachisonyeza pa dzina lake.” (Aheb. 6:10) Yehova amasangalala tikamayesetsa kumutumikira ndipo sadzaiwala zimene tikuchita. (Werengani 1 Akorinto 15:58.) Tiyeni tisalole kuti Satana atipusitse.

19 M’nkhaniyi taona kuti Satana ndi wamphamvu, wolusa komanso wachinyengo. Ndiyeno kodi tingatani kuti asatigonjetse? Yehova sanangotisiyasiya kuti tizilimbana ndi Satana patokha. Iye watifotokozera m’Baibulo njira zimene Satana amagwiritsa ntchito ndipo “tikudziwa bwino ziwembu zake.” (2 Akor. 2:11) Tikadziwa njira zimene iye amagwiritsa ntchito timakhala maso ndiponso oganiza bwino. Koma kungodziwa ziwembuzi si kokwanira. Baibulo limati: “Tsutsani Mdyerekezi ndipo adzakuthawani.” (Yak. 4:7) Nkhani yotsatira ikufotokoza zimene tingachite kuti tisakodwe m’misampha itatu ya Satana.