Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

N’zotheka Kugonjetsa Satana

N’zotheka Kugonjetsa Satana

“Khalani olimba m’chikhulupiriro ndipo mulimbane naye [Satana].”—1 PET. 5:9.

1. (a) N’chifukwa chiyani tiyenera kusamala kwambiri ndi Satana panopa? (b) Kodi tikudziwa bwanji kuti tikhoza kugonjetsa Satana?

SATANA akulimbana kwambiri ndi odzozedwa amene ali padzikoli ndiponso a “nkhosa zina.” (Yoh. 10:16) Popeza wangotsala ndi kanthawi kochepa, Mdyerekezi akufuna kumeza atumiki ambiri a Yehova. (Werengani Chivumbulutso 12:9, 12.) Koma n’zotheka kugonjetsa Satana. Tikutero chifukwa Baibulo limati: “Tsutsani Mdyerekezi ndipo adzakuthawani.”—Yak. 4:7.

2, 3. (a) Kodi maganizo akuti Satana kulibe amathandiza bwanji kukwaniritsa zolinga zake? (b) Kodi inuyo mumadziwa bwanji kuti Satana alikodi?

2 Anthu ambiri amanena kuti Satana kulibeko. Iwo amaganiza kuti Satana ndiponso ziwanda angokhala zinthu zotchulidwa m’mabuku, m’mafilimu ndiponso m’masewera a pakompyuta. Ndipo amanenanso kuti munthu wanzeru sangamakhulupirire zoti kuli ziwanda. Kodi mukuganiza kuti Satana amadandaula ndi zimene anthu amanenazi? Ayi ndithu. Ndipo zimenezi zimamuthandiza kuti azipusitsa anthuwo mosavuta. (2 Akor. 4:4) Satana amapusitsa anthu ndi maganizo akuti iyeyo kulibeko ndiponso m’njira zina zosiyanasiyana.

3 Atumiki a Yehova amadziwa kuti Satana alikodi ndipo ndi amene ananyenga Hava pogwiritsa ntchito njoka. (Gen. 3:1-5) Iye ananyozanso Yehova pa nthawi ya Yobu. (Yobu 1:9-12) Satana ndi amenenso anayesa Yesu. (Mat. 4:1-10) Ndiyeno Ufumu utakhazikitsidwa mu 1914, iye anayamba ‘kuchita nkhondo’ ndi odzozedwa amene ali padziko lapansi. (Chiv. 12:17) Nkhondoyi sinathe ndipo Satana akufunitsitsabe kusokoneza odzozedwa ndi a nkhosa zina. Kuti tigonjetse Satana, tiyenera kulimbana naye ndiponso kulimbitsa chikhulupiriro chathu. M’nkhaniyi tikambirana zinthu zitatu zimene zingatithandize kugonjetsa Satana.

PEWANI KUNYADA

4. Kodi Satana wasonyeza bwanji kuti ndi wonyada kwambiri?

4 Satana ndi wonyada kwambiri. Ngati anafika pokula mtima n’kumaderera ulamuliro wa Yehova ndiye kuti kunyada kwake ndiponso kudzikuza kwake zinafika poipa kwambiri. Choncho kuti tigonjetse Satana tiyenera kupeweratu mtima wonyada n’kumayesetsa kwambiri kukhala odzichepetsa. (Werengani 1 Petulo 5:5.) Koma kodi kunyada kumasiyana bwanji ndi kunyadira zinthu zina?

5, 6. (a) N’chifukwa chiyani tinganene kuti kunyadira zinthu zina si kulakwa? (b) Perekani zitsanzo za m’Baibulo zosonyeza kuti kunyada n’koopsa.

5 Kodi n’kulakwa ngati munthu akusangalala kuti iyeyo kapena anthu ena achita zabwino? Ayi. Paja mtumwi Paulo anauza Atesalonika kuti: “Ifeyo timakunyadirani ku mipingo ya Mulungu chifukwa cha kupirira kwanu ndi chikhulupiriro chanu pokumana ndi mazunzo ndi masautso onse amene mukulimbana nawo.” (2 Ates. 1:4) Choncho kusangalala ndi zinthu zabwino zimene ena achita kapena zimene ifeyo tachita si kulakwa. Sitichitanso manyazi chifukwa cha zinthu monga banja lathu, chikhalidwe chathu kapena dera limene tinakulira.—Mac. 21:39.

6 Koma kunyada n’kumene kumasokoneza ubwenzi wathu ndi anthu komanso ndi Yehova. Munthu wonyada amakhala wodzikuza ndipo safuna kuuzidwa zochita kapena kulangizidwa. (Sal. 141:5) Munthu wotereyu amadziganizira kwambiri n’kumaona kuti ndi wapamwamba kuposa ena. Yehova amadana kwambiri ndi anthu oterewa. (Ezek. 33:28; Amosi 6:8) Koma Satana amasangalala akamaona anthu akunyada podziwa kuti akutengera khalidwe lake. Satana ayenera kuti anasangalala kwambiri poona anthu monga Nimurodi, Farao ndi Abisalomu akusonyeza mtima wonyada. (Gen. 10:8, 9; Eks. 5:1, 2; 2 Sam. 15:4-6) Kunyada n’kumenenso kunachimwitsa Kaini. Mulungu anamupatsa malangizo koma iye anakula mtima ndipo sanatsatire. Makani ake anachititsa kuti aphe m’bale wake.—Gen. 4:6-8.

7, 8. (a) Kodi kunyada kumagwirizananso ndi khalidwe liti? (b) Kodi munthu watsankho amatani? (c) Kodi kunyada kungasokoneze bwanji mtendere mumpingo?

7 Masiku ano anthu amasonyeza mtima wonyada m’njira zosiyanasiyana. Anthu ena onyada amakhala atsankho. Buku lina limanena kuti munthu watsankho amadana ndi anthu amitundu ina. Linati munthu wotereyu amakhulupirira kuti mtundu wake ndi wabwino komanso waluso kuposa mitundu ina. Maganizo amenewa ndi amene achititsa kuti m’dzikoli muchitike zipolowe, nkhondo ndiponso kuphana kosaneneka.

8 Zinthu ngati zimenezi siziyenera kuchitika mumpingo. Koma nthawi zina zinthu zazing’ono zikhoza kukula n’kufika pochititsa Akhristu kuyambana koopsa chifukwa choti ali ndi kamtima konyada. N’kutheka kuti vuto limeneli ndi limene linali ndi Akhristu ena m’nthawi ya atumwi. Yakobo anafika powafunsa kuti: “Kodi nkhondo zimene zikuchitika pakati panu zikuchokera kuti? Nanga kukangana pakati panu kukuchokera kuti?” (Yak. 4:1) Munthu amene ali ndi mtima wodana ndi anthu ena komanso maganizo oti mtundu wake ndi wapamwamba kuposa wa ena, angalankhule kapena kuchita zinthu zimene zingapweteke kwambiri anzake. (Miy. 12:18) Apa n’zoonekeratu kuti kunyada kumasokoneza kwambiri mtendere mumpingo.

9. Kodi Baibulo limatithandiza bwanji kupewa tsankho komanso kunyada? (Onani chithunzi patsamba 14.)

9 Aliyense ayenera kudzifunsa kuti, ‘Kodi ineyo ndimadziona kuti ndine wapamwamba kuposa ena?’ Ngati yankho ndi loti inde, ndi bwino kukumbukira kuti “Yehova amanyansidwa ndi munthu aliyense wa mtima wonyada.” (Miy. 16:5) Kodi mumtima mwathu timamva bwanji tikaona anthu amene tikusiyana nawo mtundu, dziko kapena chikhalidwe? Kodi timaona kuti ndife apamwamba kuposa iwowo? Tisaiwale kuti “kuchokera mwa munthu mmodzi [Mulungu] anapanga mtundu wonse wa anthu.” (Mac. 17:26) Malinga ndi lembali, anthufe ndi amtundu umodzi basi chifukwa tonsefe ndife ana a Adamu. Ndi anthu opanda nzeru okha amene amaganiza kuti mtundu wina ndi wapamwamba kuposa unzake. Satana amasangalala akaona anthu akukhala ndi maganizo amenewa podziwa kuti akhoza kuchititsa kuti Akhristu asamakondane komanso asamagwirizane. (Yoh. 13:35) Choncho kuti tigonjetse Satana, tiyenera kupeweratu mtima wonyada.—Miy. 16:18.

PEWANI KUKONDA CHUMA NDIPONSO ZINTHU ZA M’DZIKOLI

10, 11. (a) N’chifukwa chiyani n’zosavuta kuyamba kukonda zinthu za m’dzikoli? (b) Kodi n’chiyani chinachitikira Dema chifukwa chokonda zinthu za m’dzikoli?

10 Satana ndi “wolamulira wa dzikoli” ndipo dziko lonse lili m’manja mwake. (Yoh. 12:31; 1 Yoh. 5:19) Choncho amachititsa kuti dzikoli lizilimbikitsa zinthu zambiri zosemphana ndi mfundo za m’Baibulo. Apa sitikutanthauza kuti zinthu zonse za m’dzikoli ndi zoipa. Koma tiyenera kukumbukira kuti Satana angakonde kuti titengeke ndi zinthu zimene timalakalaka n’kufika pochimwa kapena kusiya kutumikira Yehova.—Werengani 1 Yohane 2:15, 16.

11 Baibulo limasonyeza kuti m’nthawi ya atumwi Akhristu ena anayamba kukonda zinthu za m’dzikoli. Mwachitsanzo, mtumwi Paulo analemba kuti: “Dema wandisiya chifukwa chokonda zinthu za m’nthawi ino.” (2 Tim. 4:10) Komabe Baibulo silitchula zinthu za m’dzikoli zimene Dema anayamba kuzikonda kuti asiye kuyenda ndi mtumwi Paulo. Mwina iye anayamba kukonda kwambiri chuma ndipo anasiya kutumikira Yehova. Ngati ndi choncho, ndiye kuti anataya mwayi wamtengo wapatali. Apatu sanaganize bwino chifukwa dzikoli silikanamupatsa zinthu zabwino kuposa madalitso amene Yehova akanamupatsa chifukwa choyenda ndi Paulo.—Miy. 10:22.

12. Kodi “chinyengo champhamvu cha chuma” chingatisokoneze bwanji?

12 Zimene zinachitikira Dema zikhoza kutichitikiranso. Akhristu ali ndi udindo wosamalira mabanja awo. (1 Tim. 5:8) Komanso Yehova amafuna kuti tizikhala ndi moyo wabwino. Umboni wake ndi munda wokongola umene anapatsa Adamu ndi Hava. (Gen. 2:9) Koma Satana angasokoneze maganizo athu ndi “chinyengo champhamvu cha chuma.” (Mat. 13:22) Anthu ambiri amaganiza kuti chuma chambiri chingawachititse kukhala osangalala. Maganizo amenewa ndi bodza lenileni ndipo angasokoneze ubwenzi wathu ndi Yehova. Yesu anachenjeza otsatira ake kuti: “Kapolo sangatumikire ambuye awiri, pakuti adzadana ndi mmodzi ndi kukonda winayo, kapena adzakhulupirika kwa mmodzi ndi kunyoza winayo. Simungathe kutumikira Mulungu ndi Chuma nthawi imodzi.” (Mat. 6:24) Satana amafuna kuti tizichita khama kusakasaka chuma n’cholinga choti tisiye kutumikira Yehova. Choncho tisalole kuti chuma chisokoneze ubwenzi wathu ndi Yehova. Kuti tigonjetse Satana tiyenera kupewa kukonda zinthu za m’dzikoli.—Werengani 1 Timoteyo 6:6-10.

PEWANI CHIWEREWERE

13. Perekani umboni wotsimikizira kuti anthu ali ndi maganizo opotoka pa nkhani ya ukwati.

13 Chiwerewere ndi msampha wina umene Satana amagwiritsa ntchito. Anthu ambiri masiku ano amaona kuti ukwati ndi wopanikiza ndipo kukhala wokhulupirika m’banja ndi nkhani yachikale. Mtsikana wina wotchuka kwambiri anati: “N’zosatheka kuti mwamuna akhale ndi mkazi mmodzi kapena kuti mkazi akhale ndi mwamuna mmodzi. Sindinaonepo munthu wokhulupirika m’banja ndipo palibe amene amafuna kukhala wopanda chibwenzi.” Ananenanso kuti: “Ndikukhulupirira kuti mwachibadwa anthufe sitingakhale ndi mwamuna kapena mkazi mmodzi kwa moyo wathu wonse.” Satana ayenera kuti amasangalala kwambiri akamaona anthu otchuka akulimbikitsa maganizo opotokawa pa nkhani ya ukwati. Iye safuna kuti anthu azimangitsa bwinobwino mabanja kapena kuti azikhalabe m’banjamo. Choncho kuti tigonjetse Satana, tiyenera kuona ukwati mmene Mulungu amauonera.

14, 15. Kodi tingapewe bwanji chiwerewere?

14 Kaya tili pa banja kapena ayi, tiyenera kupeweratu khalidwe lachiwerewere. N’zoona kuti kuchita zimenezi si kophweka. Mwina ngati muli pa sukulu, mumamva anzanu akunyadira zoti agonana ndi winawake kapena amatumizirana mauthenga a zachiwerewere. Mwina ena amatumizirananso zithunzi zolaula. Koma Baibulo limati: “Amene amachita dama amachimwira thupi lake.” (1 Akor. 6:18) Panopa pali anthu ambiri amene akudwala kapena amene amwalira chifukwa cha matenda opatsirana pogonana. Achinyamata ambiri amene amayamba kugonana amanena kuti amanong’oneza bondo. Mafilimu amasonyeza kuti chiwerewere n’chosangalatsa. Koma zoona zake n’zakuti pamakhala mavuto ambiri munthu akaphwanya malamulo a Mulungu pa nkhani imeneyi. Anthu amene amakhulupirira za m’mafilimuzi amapusitsidwa ndi “chinyengo champhamvu cha uchimo.”—Aheb. 3:13.

15 Kodi mungatani ngati mukuyesedwa kuti muchite chiwerewere? Choyamba, muyenera kuvomereza kuti panokha simungalimbe. (Aroma 7:22, 23) Ndiyeno muyenera kupempha Yehova kuti akupatseni mphamvu. (Afil. 4:6, 7, 13) Muyeneranso kupewa zinthu zimene zingakugwetsereni mumsampha wa chiwerewere. (Miy. 22:3) Ndiyeno mayeserowo akafika muyenera kukanitsitsa nthawi yomweyo.—Gen. 39:12.

16. (a) Kodi Yesu anatani pamene ankayesedwa ndi Satana? (b) Nanga ife tikuphunzirapo chiyani?

16 Yesu anapereka chitsanzo chabwino pa nkhani yopewa mayesero. Iye sanapusitsidwe ndi zimene Satana anamulonjeza ndipo sanataye nthawi n’kumaganizaganiza kuti, ‘Kodi ndichite, ndisachite?’ M’malomwake ankayankha nthawi yomweyo kuti: “Kwalembedwa.” (Werengani Mateyu 4:4-10.) Yesu ankadziwa bwino Mawu a Mulungu ndipo izi zinamuthandiza kuti pamene ankayesedwa asachedwechedwe kukana ndipo ankatchula malemba oyenerera. Choncho kuti tigonjetse Satana, tiyenera kupewa chilichonse chimene chingatigwetsere mumsampha wa chiwerewere.—1 Akor. 6:9, 10.

PIRIRANI NDIPO MUDZAGONJETSA SATANA

17, 18. (a) Kodi Satana amagwiritsa ntchito njira zina ziti? (b) N’chifukwa chiyani zimenezi n’zosadabwitsa?

17 Satana amasokoneza anthu pogwiritsa ntchito kunyada, kukonda chuma ndiponso chiwerewere. Komatu pali zina zimene amagwiritsanso ntchito. Mwachitsanzo, Akhristu ena amatsutsidwa ndi achibale awo kapena anzawo kusukulu ndipo ena amatsutsidwa ndi boma. Zimenezi n’zosadabwitsa. Paja Yesu anati: “Anthu onse adzadana nanu chifukwa cha dzina langa, koma yekhayo amene adzapirire mpaka pa mapeto ndi amene adzapulumuke.”—Mat. 10:22.

Satana adzawonongedwa (Onani ndime 18)

18 Kodi tingagonjetse bwanji Satana? Yesu anauza ophunzira ake kuti: “Ngati inu mudzapirire, mudzapeza moyo.” (Luka 21:19) Kaya anthu atichitire zotani, tsogolo lathu likhoza kukhalabe lowala. Palibe amene angatilande ubwenzi wathu ndi Yehova pokhapokha ngati titalolera tokha. (Aroma 8:38, 39) Kodi atumiki a Yehova akamwalira ndiye kuti Satana wapambana? Ayi ndithu. Pajatu Yehova adzawaukitsa. (Yoh. 5:28, 29) Tiyeneranso kudziwa kuti Satana ndi amene alibe tsogolo labwino. Dziko loipali likadzawonongedwa, iye adzaponyedwa m’phompho kwa zaka 1,000. (Chiv. 20:1-3) Kumapeto kwa Ulamuliro wa Zaka 1,000 wa Yesu, Satana adzamasulidwa kwa kanthawi kuti ayese anthu angwiro komaliza kenako adzaphedwa. (Chiv. 20:7-10) Inuyo muli ndi tsogolo labwino koma Satana alibiretu tsogolo. Yesetsani kulimbana naye ndiponso kulimbitsa chikhulupiriro chanu. N’zotheka kugonjetsa Satana.