Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Kodi Gogi wa kudziko la Magogi wotchulidwa m’buku la Ezekieli ndi ndani?

Kwa zaka zambiri, mabuku athu akhala akufotokoza kuti Gogi wa kudziko la Magogi ndi dzina limene Satana anapatsidwa kuchokera pamene anathamangitsidwa kumwamba. Zinali choncho chifukwa choti buku la Chivumbulutso limanena kuti Satana Mdyerekezi ndi amene adzatsogolere poukira anthu a Mulungu. (Chiv. 12:1-17) Choncho zinkaonekadi kuti dzina lakuti Gogi ndi la Satanayo.

Koma mafotokozedwe amenewa akubweretsa mafunso angapo. Mwachitsanzo, pofotokoza za nthawi imene Gogi adzawonongedwe, Yehova analosera kuti adzapereka Gogiyo ‘kwa mbalame zodya nyama, mbalame zamitundumitundu ndi zilombo zakutchire kuti akhale chakudya chawo.’ (Ezek. 39:4) Kenako Yehova ananena kuti: “Pa tsiku limenelo Gogi ndidzam’patsa malo kuti akhale manda ake mu Isiraeli. . . . Kumeneko iwo adzaika m’manda Gogi pamodzi ndi khamu lake lonse.” (Ezek. 39:11) Ndiye zingatheke bwanji kuti “mbalame zamitundumitundu ndi zilombo zakutchire” zidye Satana yemwe ndi mzimu? Nanga zingatheke bwanji kuti aikidwe m’manda padzikoli? Baibulo limanena kuti Satana adzatsekeredwa m’phompho kwa zaka 1,000 osati adzadyedwa kapena kuikidwa m’manda.—Chiv. 20:1, 2.

Ndiyeno Baibulo limanena kuti zikadzatha zaka 1,000, Satanayo adzamasulidwa ndipo “adzatuluka kukasocheretsa mitundu ya anthu kumakona onse anayi a dziko lapansi. Mitunduyo ndiyo Gogi ndi Magogi, ndipo adzaisonkhanitsa pamodzi kunkhondo.” (Chiv. 20:8) Ndiyeno ngati Gogi ndi Satana, kodi angadzisocheretse yekha? Izi zikutichititsa kuzindikira kuti “Gogi” wotchulidwa m’buku la Ezekieli komanso la Chivumbulutso si Satana ayi.

Ndiyeno kodi Gogi ndi ndani? Kuti tiyankhe funsoli tiyenera kuona bwinobwino zimene Malemba amanena pa nkhani ya amene adzaukire anthu a Mulungu. Paja Baibulo limanena kuti anthu a Mulungu adzaukiridwa ndi “Gogi wa kudziko la Magogi,” “mfumu ya kumpoto” ndiponso “mafumu a dziko lapansi.” (Ezek. 38:2, 10-13; Dan. 11:40, 44, 45; Chiv. 17:14; 19:19) Kodi zimenezi zidzachitika pa nthawi zitatu zosiyana? N’kutheka kuti ayi. Zikuoneka kuti Baibulo limangogwiritsa ntchito mayina osiyanasiyana pofotokoza nkhani imodzi. Tikutero chifukwa chakuti Malemba amasonyeza kuti mitundu yonse ya anthu idzasonkhanitsidwa kuti iukire komaliza anthu a Mulungu ndipo izi n’zimene zidzayambitse nkhondo ya Aramagedo.—Chiv. 16:14, 16.

Choncho malinga ndi zimene Malemba amanena pa nkhani ya kuukiridwa komaliza kwa anthu a Mulungu, titha kuona kuti dzina loti Gogi wa kudziko la Magogi si la Satana koma ndi la mgwirizano wa mitundu ya anthu. Ndiyeno kodi “mfumu ya kumpoto” ndi imene idzatsogolere poukirapo? Apo ndiye sitinganeneretu. Koma mwina zikhoza kukhaladi choncho chifukwa ponena za Gogi, Yehova anati: “Udzabwera kuchokera kumalo ako, kumadera akutali a kumpoto. Udzabwera ndi mitundu yambiri ya anthu. Anthuwo adzakhala khamu lalikulu, adzakhala chigulu chachikulu chankhondo. Onsewo adzabwera atakwera pamahatchi.”—Ezek. 38:6, 15.

Nayenso Danieli amene anali mneneri pa nthawi imodzi ndi Ezekieli ananenanso za mfumu ya kumpoto. Anati: “Koma kotulukira dzuwa ndi kumpoto kudzachokera mauthenga amene adzaisokoneza. Pamenepo iyo idzapita ndi ukali waukulu kuti ikafafanize ndi kuwononga ambiri. Ndipo idzamanga mahema okhala ngati nyumba yachifumu pakati pa nyanja yaikulu ndi phiri lopatulika la Dziko Lokongola. Ndiyeno iyo idzafika kumapeto a moyo wake ndipo sipadzapezeka woithandiza.” (Dan. 11:44, 45) Izi zikufanana ndi zimene Ezekieli ananena kuti Gogi adzachita.—Ezek. 38:8-12, 16.

Kodi chidzachitike n’chiyani anthu a Mulungu akadzaukiridwa komaliza? Danieli anati: “Pa nthawi imeneyo Mikayeli [Yesu Khristu], kalonga wamkulu amene waimirira [kuyambira mu 1914] kuti athandize anthu a mtundu wako, adzaimirira [pa Aramagedo]. Ndiyeno padzafika nthawi ya masautso imene sinakhalepo kuyambira pamene mtundu woyambirira wa anthu unakhalapo kufikira nthawi imeneyo. Pa nthawi imeneyo, aliyense mwa anthu a mtundu wako amene dzina lake lidzakhala litalembedwa m’buku adzapulumuka.” (Dan. 12:1) Zimene Yesu adzachitezi zafotokozedwanso pa Chivumbulutso 19:11-21.

Nanga kodi “Gogi ndi Magogi” otchulidwa pa Chivumbulutso 20:8 ndi ndani? Zaka 1,000 zikadzatha, anthu amene adzasiye kutumikira Yehova adzakhalanso ndi mtima wachiwembu ngati wa “Gogi wa kudziko la Magogi.” Ndiye paja tanena kale kuti Gogi wa kudziko la Magogi ndi mitundu ya anthu imene idzaukire anthu a Mulungu chakumapeto kwa chisautso chachikulu. Ndiyeno zimene zidzachitikire “Gogi wa kudziko la Magogi” zidzafanana ndi zimene zidzachitikire “Gogi ndi Magogi.” Onse adzawonongedwa ndipo sadzakhalakonso. (Chiv. 19:20, 21; 20:9) Malinga ndi zimene tanenazi, “Gogi ndi Magogi” akuimira anthu onse amene adzasiye kutumikira Mulungu pambuyo pa zaka 1,000.

Akhristufe timachita chidwi ndi Malemba ndipo tiyeni tizingodikira chifukwa posachedwapa “mfumu ya kumpoto” idzadziwika. Koma kaya amene adzatsogolere poukira komaliza anthu a Mulungu ndi ndani, pali zinthu ziwiri zimene sitikukayikira. (1)  Gogi wa kudziko la Magogi ndi khamu lake adzawonongedwa ndiponso (2) Mfumu yathu Yesu Khristu idzapulumutsa anthu a Mulungu kuti alowe m’dziko latsopano la mtendere komanso lotetezeka.—Chiv. 7:14-17.