Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Mmene Angelo Amatikhudzira

Mmene Angelo Amatikhudzira

 Mmene Angelo Amatikhudzira

POLONGOSOLA za masomphenya okhudza gulu la angelo a Mulungu, mneneri Danieli analemba kuti: “Zikwizikwi [za angelo] anam’tumikira [Mulungu], ndi unyinji wosawerengeka unaima pamaso pake.” (Danieli 7:10) Vesili likusonyeza za chifuniro cha Mulungu polenga angelo. Iwo amatumikira Mulungu ndiponso amakhala okonzeka kutsatira malangizo ake.

Nthawi zina Mulungu amagwiritsa ntchito angelo kuchita zinthu zina zokhudza anthu. Tikambirana za njira zimene Mulungu amagwiritsira ntchito angelo polimbikitsa ndi kuteteza anthu ake, popereka uthenga kwa anthu, ndiponso popereka chilango kwa anthu oipa.

Angelo Amalimbikitsa ndi Kuteteza

Chiyambire pamene zolengedwa zauzimu zinaona dziko lapansi ndiponso anthu oyambirira akulengedwa, zolengedwa zauzimu zimenezi zinaonetsa chidwi chachikulu pa anthu. Yesu Kristu asanakhale munthu, analankhula ngati kuti ndi nzeru imene ikulankhula, ndipo anati: ‘Ndinali kusekerera ndi ana a anthu.’ (Miyambo 8:31) Ndiponso Baibulo limatiuza kuti “angelo alakalaka kusuzumiramo” m’zinthu zonena za Kristu ndiponso za m’tsogolo, zimene aneneri a Mulungu anaziulula.​—1 Petro 1:11, 12.

Patapita nthawi, angelo anaona kuti anthu ambiri sanali kutumikira Mlengi wawo wachikondi. Zimenezi zinakhumudwitsa kwambiri angelo okhulupirika amenewa. Komabe, munthu wochimwa mmodzi akalapa n’kubwerera kwa Yehova, angelo amasangalala kwambiri. (Luka 15:10) Angelo amada nkhawa kwambiri ndi moyo wa anthu amene amatumikira Mulungu, ndipo Yehova wagwiritsa ntchito angelo mobwerezabwereza kulimbikitsa ndi kuteteza atumiki ake okhulupirika padziko lapansi. (Ahebri 1:14) Tiyeni tione zina mwa zitsanzo zake.

Angelo awiri anathandiza Loti wolungama ndi ana ake aakazi awiri kupulumuka chiwonongeko cha mizinda iwiri yoipa ya Sodomu ndi Gomora, powatulutsa mu mzindawo. * (Genesis 19:1, 15-26) Patapita zaka zambiri, mneneri Danieli anaponyedwa m’dzenje la mikango, koma sanavulazidwe. N’chifukwa chiyani? Danieli anati: “Mulungu wanga  watuma mthenga wake, natseka pakamwa pa mikango.” (Danieli 6:22) Angelo anathandiza Yesu pa nthawi imene amayamba utumiki wake padziko lapansi. (Marko 1:13) Ndiponso Yesu atatsala pang’ono kufa, mngelo anamuonekera “nam’limbitsa iye.” (Luka 22:43) Chithandizo cha angelo chimenechi mosakayikira chinalimbikitsa Yesu pa nthawi zimenezi zomwe ankafunikira kulimbikitsidwa kwambiri. Mngelo anatulutsanso mtumwi Petro kundende.​—Machitidwe 12:6-11.

Kodi angelo amatiteteza masiku ano? Ngati timalambira Yehova mogwirizana ndi Mawu ake, tisakayike kuti angelo a Mulungu amphamvu ndiponso osaonekawo, amatiteteza. Baibulo limalonjeza kuti: “Mngelo wa Yehova azinga kuwatchinjiriza iwo akuopa iye, nawalanditsa iwo.”​—Salmo 34:7.

Komabe, tiyenera kudziwa kuti angelo ntchito yawo makamaka n’kutumikira Mulungu, osati anthu ayi. (Salmo 103:20, 21) Iwo amamvera malangizo a Mulungu, osati zopempha za anthu. Choncho, Yehova Mulungu ndiye woyenera kum’pempha thandizo, osati angelo ayi. (Mateyu 26:53) Koma popeza angelo sitiwaona, sitingadziwe mmene Mulungu amawagwiritsira ntchito pothandiza anthu m’zinthu zosiyanasiyana. Ndipo timadziwa kuti Yehova ‘amadzionetsera wamphamvu kwa iwo amene mtima wawo uli wangwiro ndi iye.’ (2 Mbiri 16:9; Salmo 91:11) Timatsimikizanso kuti “ngati tipempha kanthu monga mwa chifuniro chake, [Mulungu] atimvera.”​—1 Yohane 5:14.

Malemba amatiuzanso kuti tizipemphera ndi kulambira Mulungu yekha basi. (Eksodo 20:3-5; Salmo 5:1, 2; Mateyu 6:9) Angelo okhulupirika amatilimbikitsa kuchita zimenezo. Mwachitsanzo, pamene mtumwi Yohane anafuna kulambira mngelo, mngeloyo, anam’dzudzula kuti: “Tapenya, usatero; . . . Lambira Mulungu.”​—Chivumbulutso 19:10.

Angelo Amapereka Mauthenga a Mulungu

Liwu lakuti “mngelo” limatanthauza “mthenga,” ndipo imeneyo ndi njira ina imene angelo amatumikirira Mulungu, monga opereka mithenga kwa anthu. Mwachitsanzo, “mngelo Gabrieli anatumidwa ndi Mulungu kumka kumudzi wa ku Galileya dzina lake Nazarete.” Kukatani? Kukadziwitsa namwali yemwe dzina lake anali Mariya kuti ngakhale anali namwali, adzakhala ndi pakati ndipo adzabala mwana wamwamuna yemwe adzamutche dzina loti Yesu. (Luka 1:26-31) Mulungu anatumanso angelo kwa abusa omwe anali kuthengo kukawadziwitsa kuti “Kristu Ambuye” wabadwa. (Luka 2:8-11) Mofananamo, angelo anapereka mauthenga ochokera kwa Mulungu kwa Abrahamu, Mose,Yesu, ndi anthu enanso otchulidwa m’Baibulo.​—Genesis 18:1-5, 10; Eksodo 3:1, 2; Luka 22:39-43.

Kodi angelo amatumikira motani monga amithenga a Mulungu masiku ano? Taganizani za ntchito imene Yesu analosera kuti otsatira ake adzachita asanafike mapeto a dongosolo la zinthuli. Iye anati: “Uthenga uwu wabwino wa Ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi, ukhale mboni kwa anthu a mitundu yonse; ndipo pomwepo chidzafika chimaliziro.” (Mateyu 24:3, 14) Mboni za Yehova zimatha maola oposa biliyoni imodzi pachaka kulalikira uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu. Koma kodi mukudziwa kuti angelo nawonso amachita nawo ntchito imeneyi? Mtumwi Yohane ananena za masomphenya omwe anaona kuti: “Ndipo ndinaona  mngelo wina . . . , wakukhala nawo Uthenga Wabwino wosatha, aulalikire kwa iwo akukhala padziko, ndi kwa mtundu uliwonse ndi fuko ndi manenedwe ndi anthu.” (Chivumbulutso 14:6, 7) Lembali limatsimikiza za ntchito yofunika kwambiri imene angelo akuchita pothandiza anthu masiku ano.

Mboni za Yehova zimaona umboni wotsogoleredwa ndi angelo pamene zikugwira ntchito yawo yolalikira khomo ndi khomo. Nthawi zambiri zimakumana ndi anthu amene amapemphera kuti munthu wina awathandize kumvetsa zofuna za Mulungu. Chifukwa chotsogoleredwa ndi angelo ndiponso ntchito imene Mboni zimagwira, anthu masauzande ambiri amam’dziwa Yehova chaka chilichonse. Pindulani ndi ntchito yopulumutsa moyo imeneyi yomwe ikuchitika motsogoleredwa ndi angelo.

Mulungu Amapereka Chilango Pogwiritsa Ntchito Angelo

Ngakhale kuti sanapatsidwe mphamvu zoweruza anthu, angelo sangopenyerera chabe. (Yohane 5:22; Ahebri 12:22, 23) Nthawi zina kalelo, ankatumikira monga opereka chilango cha Mulungu. Mwachitsanzo, Mulungu anagwiritsa ntchito angelo pomenyana ndi Aiguputo akale, amene anagwira Aisrayeli ukapolo. (Salmo 78:49) Ndipo usiku umodzi wokha “mthenga wa Yehova” anakantha asilikali okwana 185,000 mu msasa wa adani a anthu a Mulungu.​—2 Mafumu 19:35.

Mulungu adzagwiritsanso ntchito angelo, kupereka chilango m’tsogolomu. Yesu adzabwera “pamodzi ndi angelo a mphamvu yake, m’lawi lamoto, ndi kubwezera chilango kwa iwo osam’dziwa Mulungu, ndi iwo osamvera Uthenga Wabwino.” (2 Atesalonika 1:7, 8) Anthu okha amene salabadira uthenga umene ukulalikidwa dziko lonse lapansi ndi chithandizo cha angelo ndi amene adzawonongedwe. Koma amene amafunafuna Mulungu ndi kutsatira ziphunzitso za m’Malemba, adzapulumutsidwa.​—Zefaniya 2:3.

Timayamikira kwambiri angelo okhulupirika, omwe amamvera malangizo a Mulungu nthawi zonse. Yehova amawagwiritsa ntchito kuthandiza ndi kuteteza atumiki ake okhulupirika padziko lapansi lino. Zimenezi n’zolimbikitsa kwambiri kwa ifeyo chifukwa pali zolengedwa zauzimu zoopsa zotchedwa ziwanda zimene zimafuna kutivulaza.

Nanga Ziwanda Ndani?

M’zaka 1,500 kuchokera pamene Satana ananyenga Hava m’munda wa Edene, angelo a Mulungu anaona kuti Satana Mdyerekezi anakwanitsa kupatutsa anthu kuchoka kwa Mulungu. Anapatutsa pafupifupi  anthu onse kupatulapo ochepa chabe okhulupirika, monga Abele, Enoke, ndi Nowa. (Genesis 3:1-7; Ahebri 11:4, 5, 7) Ena mwa angelowo anayambanso kutsatira Satana. Baibulo limawatchula kuti mizimu yosamvera “m’masiku a Nowa.” (1 Petro 3:19, 20) Kodi kusamvera kwawo kunaonekera motani?

M’nthawi ya Nowa, angelo ochuluka mosadziwika omwe anapandukira Mulungu anasiya malo amene Mulungu anawakonzera kumwamba, n’kubwera padziko lapansi, ndi kuvala matupi a anthu. N’chifukwa chiyani anatero? Iwo anali ndi chilakolako chofuna kugonana ndi akazi. Ndipo kenaka anabereka ana otchedwa Anefili, amene anakhala zimphona. Ndipo, “kuipa kwa anthu kunali kwakukulu padziko lapansi, ndiponso . . . ndingaliro zonse za maganizo a mitima yawo zinali zoipabe zokhazokha.” Komabe, Yehova Mulungu sanalole kuti anthu apitirirebe kuipa. Anabweretsa Chigumula padziko lapansi, chomwe chinawononga anthu onse oipa kuphatikizapo Anefiliwo. Ndipo anthu okha amene anapulumuka anali atumiki a Mulungu okhulupirika.​—Genesis 6:1-7, 17; 7:23.

Angelo opandukawo anathawa kuwonongedwa pa nthawi ya Chigumula. Iwo anavula matupi awo a anthu n’kubwerera ku malo amizimu monga zolengedwa zauzimu. Kuyambira nthawi imeneyo, iwo amatchedwa ziwanda. Ndipo anakhala ku mbali ya Satana Mdyerekezi, amene ali “mkulu wa ziwanda.” (Mateyu 12:24-27) Mofanana ndi mkulu wawoyo, ziwanda zimafuna kuti anthu azizilambira.

Ziwanda n’zoopsa, koma sitiyenera kuziopa. Chifukwa mphamvu zawo zili ndi malire. Pamene angelo osamvera aja anabwerera kumwamba, sanawalole kukhalanso ndi gulu la angelo okhulupirika a Mulungu. M’malo mwake, Mulungu sawaunikiranso mwauzimu, ndipo alibe chiyembekezo chilichonse. Zoonadi, anawaponya kundende. (2 Petro 2:4) Yehova anawatsekera “m’ndende zosatha pansi pa mdima” wauzimu. Kuwonjezera apo, Iwo sangathenso tsopano kuvala matupi a anthu.​—Yuda 6.

Kodi Muyenera Kutani?

Kodi ziwanda zimasokonezabe anthu? Inde, zimatero pogwiritsa ntchito “machenjerero” ofanana ndi amene mkulu wawo Satana Mdyerekezi amagwiritsa ntchito. (Aefeso 6:11, 12) Komabe pogwiritsa ntchito malangizo a Mawu a Mulungu, tingathe kukana ziwandazi molimba. Ndiponso, anthu amene amakonda Mulungu, amatetezedwa ndi angelo amphamvu.

N’chinthu chofunika kwambiri kuphunzira zofuna za Mulungu zomwe zimapezeka m’Malemba ndi kugwiritsa ntchito zimene mwaphunzirazo. Mungaphunzire zambiri zokhudza zimene Baibulo limaphunzitsa pokumana ndi Mboni za Yehova m’dera lanu kapena kulembera kalata kwa ofalitsa magaziniyi. Mboni za Yehova zingasangalale kuphunzira nanu Baibulo kwaulere ndiponso panthawi imene inuyo mungakonde.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 7 Baibulo limanena za angelo ngati amuna achikulire. Nthawi zonse ankaonekera kwa anthu monga amuna.

[Bokosi patsamba 6]

MAUDINDO A ANGELO

Yehova ali ndi angelo ambiri omwe anawaika m’maudindo otsatirawa:

Mngelo wamphamvu ndiponso waulamuliro waukulu kwambiri ndi Mikayeli mngelo wamkulu, kapena kuti Yesu Kristu. (1 Atesalonika 4:16; Yuda 9) Aserafi, akerubi, ndi angelo ena ali pansi pake.

Aserafi ali ndi udindo wapamwamba kwambiri pa maudindo amene Mulungu anakhazikitsawa. Iwo amatumikira ku mpando wachifumu wa Mulungu. Ntchito yawo ina ndiyo kulengeza za chiyero cha Mulungu ndi kuthandiza anthu a Mulungu kukhala oyera mwauzimu.​—Yesaya 6:1-3, 6, 7.

Akerubi amazinga mpando wachifumu wa Mulungu ndiponso amatamanda ulemerero wa Yehova.​—Salmo 80:1; 99:1; Ezekieli 10:1, 2.

Angelo enawo ndi nthumwi za Yehova, ndipo amachita chifuniro cha Mulungu.

[Chithunzi patsamba 4]

Angelo anathandiza kupulumutsa Loti ndi ana ake aakazi

[Chithunzi patsamba 5]

Pamene mtumwi Yohane anafuna kulambira mngelo, mngeloyo anamuuza kuti: “Usatero”

[Chithunzi patsamba 6]

Mulungu amapereka chilango pogwiritsa ntchito angelo

[Chithunzi patsamba 7]

Kodi mukupindula ndi ntchito yolalikira imene ikuchitika motsogoleredwa ndi angelo?