Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

 Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Kodi mu likasa lachipangano munkakhala magome awiri okha aja, kapena munkakhalanso zinthu zina?

Panthawi yopatulira kachisi wa Solomo mu 1026 B.C.E., “munalibe kanthu kena m’likasa, koma magome awiri Mose anawaika mmwemo ku Horebu, muja Yehova anachita chipangano ndi ana a Israyeli potuluka iwo m’Aigupto.” (2 Mbiri 5:10) Komatu si kuti nthawi zonse munkangokhala magome awiri okhawo.

“Mwezi wachitatu atatuluka ana a Israyeli m’dziko la Aigupto,” analowa m’chipululu cha Sinai. (Eksodo 19:1, 2) Kenaka, Mose anapita ku phiri la Sinai n’kukalandira magome awiri a Chilamulo. Iye anati: “Ndipo ndinatembenuka ndi kutsika m’phiri, ndi kuika magome m’likasa ndinalipanga, ali mmenemo monga Yehova anandilamulira ine.” (Deuteronomo 10:5) Ili linali likasa kapena kuti chotengera cha kanthawi chabe, chimene Yehova ananena kuti Mose apange kuti muzikhala magome a Chilamulo awiri aja. (Deuteronomo 10:1) Likasa lachipangano sanalipange mpaka cha kumapeto kwa chaka cha 1513 B.C.E.

Patatha nthawi yochepa chabe atalanditsidwa ku Aigupto, Aisrayeli anayamba kung’ung’udza pankhani ya chakudya. Motero Yehova anawapatsa mana. (Eksodo 12:17, 18; 16:1-5) Panthawiyi, Mose analangiza Aroni kuti: “Tenga mphika, nuthiremo mana odzala omeri, nuuike pamaso pa Yehova, usungikire mibadwo yanu.” Nkhaniyo imati: “Monga Yehova anauza Mose, momwemo Aroni anauika patsogolo pa Mboni [kapena kuti mosungira zolembedwa zofunika], usungikeko.” (Eksodo 16:33, 34) N’zosakayikitsa kuti panthawiyi Aroni anatola mana n’kuuika m’mbiya inayake, koma sanauike patsogolo pa Mboni chifukwa anafunika kudikira kaye kuti Mose apange Likasa n’kuikamo magome aja.

Monga tanena kale, likasa lachipangano analipanga chakumapeto kwa chaka cha 1513 B.C.E. Ndodo ya Aroni anadzaiika mu Likasalo patatha nthawi yaitali kwambiri, pomwe Kora ndi anzake ena anagalukira. Lemba la Numeri 17:10 limati: “Ndipo Yehova anati kwa Mose, Bweza ndodo ya Aroni kuiika chakuno cha Mboni, isungike ikhale chizindikiro cha pa ana opikisana; kuti unditsirizire madandaulo awo, kuti angafe.” Zitachitika zimenezi, likasa lachipangano linayamba kukhala ndi zinthu zonse zimene mtumwi Paulo anatchula. Zinthu zake ndizo “mbiya yagolidi yosungamo mana, ndi ndodo ya Aroni idaphukayo, ndi magome a chipangano.”​—Ahebri 9:4.

Mana chinali chakudya chimene Mulungu anawapatsa Aisrayeli paulendo wawo wa zaka 40 m’chipululu. Anasiya kuwapatsa pamene anayamba kudya “zipatso za dziko” lolonjezedwa. (Yoswa 5:11, 12) Ndodo ya Aroni anaiika mu likasa lachipangano ndi cholinga choti ikhale chizindikiro kapena mboni kwa mbadwo wogalukirawo. Zimenezi zikusonyeza kuti ndodoyi inakhala mmenemo pa ulendo wonse m’chipululumo. Motero, n’zomveka kunena kuti patapita nthawi Aisrayeli atalowa m’Dziko Lolonjezedwa, ndiponso asanapatulire kachisi wa Solomo, ndodo ya Aroni ndiponso mbiya yagolidi yosungiramo mana zinachotsedwa mu likasa lachipangano.