Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

‘Yehova Wakhala Chipulumutso Changa’

‘Yehova Wakhala Chipulumutso Changa’

 “Tiyenera Kumvera Mulungu Koposa Anthu”

‘Yehova Wakhala Chipulumutso Changa’

ANTHU a Yehova anafunika kusankha chochita. Kodi amvere zofuna za mfumu yoipa ya Aigupto wakale? Kapena amvere Yehova Mulungu, n’kuchoka m’dziko laukapolo, kupita ku Dziko Lolonjezedwa?

Chifukwa chakuti Farao wa ku Igupto, amene anali wamakani, sanafune kumasula anthu a Yehova, Mulungu anabweretsa Miliri Khumi m’dzikomo. Ndipo zimenezi zinasonyeza mphamvu za Mulungu. Milungu ya Aigupto sinathe kuchita kalikonse kuti iletse miliriyo.

Farao atauzidwa kuti amasule anthu a Mulungu, analankhula monyodola kuti: “Yehova ndani, kuti ndimvere mawu ake ndi kulola Israyeli apite? Sindim’dziwa Yehova, ndiponso sindidzalola Israyeli apite.” (Eksodo 5:2) Chifukwa cha zimenezi, Aigupto anakumana ndi miliri iyi: (1) madzi anasanduka magazi, (2) achule, (3) nsabwe, (4) mizaza, (5) mliri pa zoweta, (6) zilonda pa anthu ndi zoweta, (7) matalala, (8) dzombe, (9) mdima, ndiponso (10) imfa ya ana oyamba kubadwa a Aigupto, kuphatikizapo mwana wamwamuna wa Farao. Pomaliza, mfumuyi inamasula Ahebriwo. Ndipotu inachita kuwakakamiza kuti anyamuke.​—Eksodo 12:31, 32.

Anthu pafupifupi fili miliyoni, amuna, akazi ndi ana achiisrayeli komanso anthu a mitundu ina yosiyanasiyana ananyamuka mwachangu. (Eksodo 12:37, 38) Komabe, pasanapite nthawi, Farao anawalondola ndi gulu lake lankhondo lochititsa mantha. Aisrayeli anakhala ngati agwidwa mumsampha pakati pa Nyanja Yofiira, chipululu choopsa, ndi asilikali a Farao. Komabe, Mose anawauza kuti: “Musaope, chirimikani ndipo penyani chipulumutso cha Yehova.”​—Eksodo 14:8-14.

Ndipo Yehova anagawanitsa madzi a m’Nyanja Yofiira mozizwitsa kuti Aisrayeli awoloke. Koma pamene Aigupto analondola Aisrayeliwo m’nyanjamo, Mulungu anabwezeretsa madziwo m’malo mwake. ‘Magaleta a Farao ndi ankhondo ake [Yehova] anawaponya m’nyanja.’ (Eksodo 14:26-28; 15:4) Farao wodzikuzayo anakumana ndi zoopsa chifukwa chokana kulemekeza Yehova.

Pamenepa, Yehova anasonyeza kuti “ndiye wankhondo.” (Eksodo 15:3) Nkhani youziridwa imati: “Israyeli anaiona ntchito yaikulu imene Yehova anachitira Aigupto, ndipo anthuwo anaopa Yehova; nakhulupirira Yehova.” (Eksodo 14:31; Salmo 136:10-15) Aisrayeli anasonyeza kuyamikira Mulungu mochokera pansi pa mtima pomwe amuna anaimba limodzi ndi Mose nyimbo yosangalala kuti apambana ndipo mlongo wake wa Mose, Miriamu, anatsogolera akazi kuvina. *

Yehova Akupulumutsabe Anthu Ake

Atumiki a Yehova amakono angaphunzirepo zinthu zolimbikitsa chikhulupiriro pa nkhani yodabwitsayi ya mmene Mulungu anapulumutsira anthu ake. Chinthu choyamba n’chakuti Yehova ali ndi mphamvu yopanda malire ndiponso angathandize atumiki ake mokwanira. M’nyimbo yawo yosangalala kuti apambana, Mose ndi Aisrayeli anaimba kuti: “Dzanja lanu lamanja, Yehova, lalemekezedwa ndi mphamvu, dzanja lanu lamanja, Yehova, laphwanya mdani.”​—Eksodo 15:6.

Chinthu china chomwe tikuphunzirapo n’chakuti Mulungu Wamphamvuyonse amafunitsitsa kuteteza anthu ake. Aisrayeli anaimba kuti: “Yehova ndiye mphamvu yanga ndi nyimbo yanga, ndipo wakhala chipulumutso changa. Ameneyo ndiye Mulungu wanga, ndidzam’lemekeza.” Chinanso tingaphunzirepo n’chakuti palibe munthu amene angapambane potsutsa chifuniro cha  Yehova Mulungu. M’nyimbo yomwe anaimba posangalala kuti apambana ija, anthu amene Mulungu anawapulumutsa anati: “Afanana ndi inu ndani mwa milungu, Yehova? Afanana ndi inu ndani, wolemekezedwa woyera, woopsa pom’yamika, wakuchita zozizwa?”​—Eksodo 15:2, 11.

Mofanana ndi Farao wa ku Igupto wakale, olamulira dziko lerolino amazunza anthu a Yehova. Nthawi zina atsogoleri onyada ‘amanena mawu akutsutsana ndi Wam’mwambamwamba, naletsa opatulika a Wam’mwambamwamba.’ (Danieli 7:25; 11:36) Koma Yehova amatsimikizira anthu ake kuti: “Palibe chida chosulidwira iwe chidzapindula; ndipo lilime lonse limene lidzakangana nawe m’chiweruzo udzalitsutsa. Ichi ndi cholowa cha atumiki a Yehova.”​—Yesaya 54:17.

Amene amatsutsana ndi Yehova adzagonja ngati mmene anachitira Farao ndi gulu lake lankhondo. Ntchito za Yehova zopulumutsa anthu ake, monga anachitira populumutsa Aisrayeli paulendo wawo wochokera ku Aigupto, zimatsimikizira kuti n’koyeneradi kutsatira mfundo imene atumwi a Yesu ananena, yakuti: “Tiyenera kumvera Mulungu koposa anthu.”​—Machitidwe 5:29.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 8 Onani Kalendala ya 2006 ya Mboni za Yehova, mwezi wa January/​February.

[Bokosi/​Chithunzi patsamba 9]

KODI MUKUDZIWA?

• Yehova anachititsa kuti mphepo yamphamvu iombe usiku wonse kuti Aisrayeli awoloke pouma m’Nyanja Yofiira.​—Eksodo 14:21, 22.

• Kuti Aisrayeli awoloke Nyanja Yofiira panthawi yochepa chonchi ndiye kuti njira yake inali yotambalala kilomita imodzi ndi theka kapena kuposerapo.

[Zithunzi patsamba 9]

Milungu yonama ya Aigupto sinathe kuletsa Miliri Khumi yochokera kwa Yehova

[Mawu a Chithunzi]

All three figurines: Photograph taken by courtesy of the British Museum