Kalata Yaciwili kwa Timoteyo 2:1-26
2 Conco iwe mwana wanga, pitiliza kupeza mphamvu mu cisomo cimene cili mwa Khristu Yesu.
2 Mau amene unamva kwa ine, omwenso mboni zambili zinatsimikizila, uwaphunzitse kwa anthu okhulupilika, ndipo naonso adzakhala oyenelela kuphunzitsako ena.
3 Monga msilikali wabwino wa Khristu Yesu, khala wokonzeka kukumana ndi mabvuto.
4 Palibe msilikali amene amacita nao* zamalonda* zimene anthu ena amacita, cifukwa amafuna kukondweletsa amene anamulemba usilikali.
5 Cimodzi-modzinso munthu amene ali pa masewela a mpikisano, sangalandile mphoto* akapanda kutsatila malamulo a mpikisanowo.
6 Mlimi wogwila nchito molimbika, ndiye ayenela kukhala woyamba kudya zipatso za mbeu zake.
7 Uziganizila zimene ndikukuuzazi nthawi zonse, ndipo Ambuye adzakuthandiza kumvetsa zinthu zonse.
8 Kumbukila kuti Yesu Khristu anaukitsidwa kwa akufa, ndipo anali mbadwa* ya Davide. Izi n’zogwilizana ndi uthenga wabwino umene ndikuulalikila.
9 Cifukwa ca uthengawu ndikubvutika, ndipo ndatsekeledwa m’ndende ngati cigawenga. Koma mau a Mulungu sangathe kumangidwa.
10 Pa cifukwa cimeneci, ndikupililabe zinthu zonse cifukwa ca osankhidwa, kuti naonso akalandile cipulumutso ndi ulemelelo wamuyaya mwa Khristu Yesu.
11 Mau awa ndi odalilika: Ngati tinafadi naye limodzi, tidzakhalanso ndi moyo limodzi naye.
12 Tikapitilizabe kupilila, tidzalamulilanso naye monga mafumu. Koma tikamukana, iyenso adzatikana.
13 Ndipo tikakhala osakhulupilika, iye adzakhalabe wokhulupilika, cifukwa sangadzikane.
14 Nthawi zonse uziwakumbutsa zimenezi, ndipo uziwalangiza* pamaso pa Mulungu kuti asamakangane pa mau. Cifukwa kucita zimenezi kulibe phindu m’pang’ono pomwe, koma kumangoononga* cikhulupililo ca omvetsela.
15 Cita ciliconse cotheka kuti uonetse kuti ndiwe wobvomelezeka pamaso pa Mulungu, wanchito wopanda cifukwa cocitila manyazi, ndiponso wophunzitsa ndi kufotokoza bwino mau a coonadi.
16 Koma uzipewa nkhani zopanda pake zimene zimaipitsa zinthu zoyela, cifukwa zimalimbikitsa anthu ambili kuti asamaope Mulungu.
17 Ndipo mau ao amafalikila ngati cilonda conyeka.* Ena a iwo ndi Hemenayo ndi Fileto.
18 Iwo asocela n’kupatuka pa coonadi ponena kuti kuuka kwa akufa kunacitika kale, ndipo akuononga cikhulupililo ca ena.
19 Ngakhale n’conco, maziko olimba a Mulungu akalipobe, ndipo ali ndi cidindo ca mau akuti: “Yehova* amadziwa anthu ake,” ndiponso akuti: “Aliyense woitana pa dzina la Yehova* aleke kucita zosalungama.”
20 M’nyumba yaikulu simukhala ziwiya zagolide ndi zasiliva zokha ai, mumakhalanso zamitengo ndi zadothi. Zina zimakhala za nchito yolemekezeka, koma zina zimakhala za nchito yonyozeka.
21 Cotelo, ngati munthu amapewa ziwiya za nchito yonyozeka, adzakhala ciwiya ca nchito yolemekezeka, coyela, cofunika kwa mwiniwake, ndi cokonzeka kugwila nchito iliyonse yabwino.
22 Conco thawa zilakolako za unyamata. Koma pamodzi ndi anthu oitana pa Ambuye ndi mtima woyela, tsatila cilungamo, cikhulupililo, cikondi, ndi mtendele.
23 Ndiponso uzipewa kutsutsana pa zinthu zopusa ndi zopanda nzelu, podziwa kuti zimabutsa ndeu.
24 Paja kapolo wa Ambuye sayenela kucita ndeu. Koma azikhala wodekha kwa onse, woyenelela kuphunzitsa, komanso wougwila mtima ena akamulakwila.
25 Akhalenso wofatsa polangiza anthu otsutsa kuti mwina Mulungu angawalole kulapa* ndi kukhala ndi cidziwitso colondola ca coonadi,
26 komanso kuti mwina nzelu zao zingawabwelele n’kupulumuka mumsampha wa Mdyelekezi, popeza waagwila amoyo kuti azicita cifunilo cake.
Mau a m'Munsi
^ Kapena kuti, “amene amasokonezedwa ndi.”
^ Ma Baibo ena amati, “nao zocita za tsiku ndi tsiku.”
^ Kapena kuti, “sangalandile nkhata yoonetsa kuti wapambana.”
^ Kucokela ku Cigiriki, “mbeu.”
^ Kucokela ku Cigiriki, “ndipo uzicitila umboni mokwanila.”
^ Kapena kuti, “kumabvulaza; kumatembenuza.”
^ Ici ndi cilonda cimene cimafalikila mwa kudya mnofu.
^ Onani Zakumapeto A5.
^ Onani Zakumapeto A5.
^ Kapena kuti, “angawalole kusintha maganizo.”

