Kalata Yoyamba ya Petulo 2:1-25

  • Muzilakalaka Mau a Mulungu (1-3)

  • Miyala yamoyo yomangidwa m’nyumba yauzimu (4-10)

  • Muzikhala ngati alendo m’dzikoli (11, 12)

  • Kugonjela koyenela (13-25)

    • Khristu ndi citsanzo cathu (21)

2  Conco siyani zoipa zonse, zacinyengo zonse, zaciphamaso, kaduka, komanso mtundu ulionse wa misece. 2  Koma monga makanda obadwa kumene, muzilakalaka mkaka wosasukuluka wa m’mau a Mulungu, kuti kudzela mu mkakawo mukule n’kukhala oyenela cipulumutso, 3  malinga ngati mwalawa n’kuona kuti Ambuye ndi wokoma mtima. 4  Mukabwela kwa iye, amene ndi mwala wamoyo umene anthu anaukana, koma wosankhidwa ndi Mulungu, umenenso ndi wamtengo wapatali kwa iye, 5  ndiye kuti inu miyala yamoyo mukumangidwa n’kukhala nyumba yauzimu kuti mukakhale ansembe oyela, n’colinga cakuti muzikapeleka nsembe zauzimu zobvomelezeka kwa Mulungu, kudzela mwa Yesu Khristu. 6  Pakuti Lemba limati: “Taonani, ndikuyala mwala wosankhidwa mu Ziyoni, mwala wa maziko wapakona wamtengo wapatali. Ndipo aliyense wokhulupilila mwalawo sadzakhumudwa.”* 7  Conco iye ndi wamtengo wapatali kwa inu cifukwa mumamukhulupilila. Koma kwa amene samukhulupilila, “mwala umene omanga anaukana, wakhala mwala wapakona* wofunika kwambili,” 8  komanso “mwala wopunthwitsa ndiponso thanthwe lokhumudwitsa.” Anthu amenewa amapunthwa cifukwa samvela mau. Izi n’zimene ziyenela kuwacitikila. 9  Koma inu, ndinu “anthu osankhidwa, ansembe acifumu, mtundu woyela, komanso cuma cake capadela, kuti mulengeze makhalidwe abwino kwambili” a Mulungu amene anakuitanani, kuti mucoke mumdima ndi kulowa m’kuwala kwake kodabwitsa. 10  Kale simunali anthu a Mulungu, koma tsopano ndinu anthu ake. Kale Mulungu sanakucitileni cifundo, koma tsopano wakucitilani cifundo. 11  Okondedwa, popeza ndinu alendo komanso anthu osakhalitsa m’dzikoli, ndikukudandaulilani kuti muzipewa zilakolako za thupi, zimene zili pankhondo yolimbana ndi inu. 12  Khalani ndi khalidwe labwino pakati pa anthu a m’dzikoli, kuti pamene akukunenezani monga anthu ocita zoipa, pamapeto pake, iwo pokhala mboni zimene zikuona ndi maso nchito zanu zabwino, akatamande Mulungu pa tsiku lake loyendela. 13  Cifukwa ca Ambuye, muzigonjela ulamulilo ulionse umene anthu anakhazikitsa, kaya ndi mfumu cifukwa ili ndi udindo waukulu, 14  kapenanso nduna cifukwa zimatumidwa ndi mfumuyo kuti zilange anthu amene acita zoipa, komanso kuyamikila amene acita zabwino. 15  Pakuti cifunilo ca Mulungu n’cakuti muzicita zabwino kuti muwatseke pakamwa anthu amene amalankhula zopanda nzelu cifukwa ca umbuli. 16  Muzikhala ngati mfulu, koma ufulu wanuwo musamaugwilitse nchito monga pobisalila pocita zoipa. Koma muziugwilitsa nchito ngati akapolo a Mulungu. 17  Muzilemekeza anthu, kaya ndi amtundu wotani. Muzikonda gulu lonse la abale. Muziopa Mulungu komanso muzilemekeza mfumu. 18  Anchito azigonjela ambuye ao ndi mantha oyenela. Azicita zimenezi osati kwa ambuye abwino ndi ololela okha, komanso ngakhale kwa ao obvuta kuwakondweletsa. 19  Pakuti zili bwino ngati munthu akupilila zowawa, komanso ngati akukumana ndi mabvuto* cifukwa cofuna kukhala ndi cikumbumtima coyela kwa Mulungu. 20  Kodi kupilila pamene akukumenyani cifukwa cakuti mwacimwa, kuli ndi phindu lanji? Koma ngati mukupilila mabvuto cifukwa ca kucita zabwino, Mulungu amakondwela. 21  Si paja Mulungu anakuitanani kuti muyende m’njila imeneyi. Pakuti ngakhale Khristu nayenso anabvutika cifukwa ca inu, ndipo anakusiilani citsanzo kuti mutsatile mapazi ake mosamala kwambili. 22  Iye sanacitepo chimo, ndipo sanalankhulepo mau acinyengo. 23  Pamene anthu anali kumucita zacipongwe, sanabwezele cipongwe. Pamene anali kumuzunza, sanawaopsyeze. Koma anasiya zonse m’manja mwa Woweluza wacilungamo. 24  Iye ananyamula macimo athu m’thupi lake pamtengo, kuti tife ku macimo n’kukhala amoyo m’cilungamo. Ndipo “munacilitsidwa ndi zilonda zake.” 25  Pakuti munali monga nkhosa zosocela, koma tsopano mwabwelela kwa m’busa wanu ndi woyang’anila miyoyo yanu.

Mau a m'Munsi

^ Kucokela ku Cigiriki, “mwalawo sadzacititsidwa manyazi.”
^ Kucokela ku Cigiriki, “wakhala mutu wakona.” Mwala umenewu anali kuuika pa kona ya nyumba, pomwe zipupa ziwili zimakumana.
^ Kapena kuti, “ngati akumva cisoni; kumva kupweteka.”