Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mukukumbukira?

Kodi Mukukumbukira?

Kodi mwawerenga mosamala magazini aposachedwapa a Nsanja ya Olonda? Tayesani kuyankha mafunso otsatirawa:

Kodi ndi zinthu zina ziti zimene zidzachitike pa nthawi ya mapeto?

Anthu oipa komanso maboma a anthu adzawonongedwa. Zipembedzo zabodza nazonso zidzawonongedwa chifukwa zalephera kukwaniritsa zofuna za Mulungu ndi anthu. Komanso nkhondo ndi zinthu zopanda chilungamo zidzatha.—5/1, tsa. 3-5.

Kodi Gogi wa kudziko la Magogi wotchulidwa m’buku la Ezekieli ndi ndani?

Zikuoneka kuti Gogi wa kudziko la Magogi si Satana, koma ndi mitundu ya anthu imene mogwirizana idzaukire anthu a Mulungu chisautso chachikulu chikadzayamba.—5/15, tsa. 29-30.

Kodi ndi zinthu 6 ziti zimene zingakuthandizeni kuti muzisangalalabe ngakhale kuti ndinu wokalamba?

M’Baibulo muli malangizo akuti (1) muzidziwa kuti pali zina zomwe simungakwanitse kuchita, (2) muzivala bwino, (3) musamangoganizira zimene simungathe kuchita, (4) muzikhala wowolowa manja, (5) muzikhala ochezeka ndipo (6) muziyamikira zomwe ena akuchitirani. Mukamayesetsa kuchita zimenezi, zingakuthandizeni kuti muzisangalalabe.—6/1, tsa. 8-10.

Kodi zozizwitsa zimene Yesu anachita zinasonyeza bwanji kuti anali ndi mtima wopatsa?

Ku ukwati wa ku Kana, Yesu anasandutsa madzi okwana malita 380 kukhala vinyo. Pa nthawi inanso anadyetsa mozizwitsa anthu 5,000. (Mat. 14:14-21; Yoh. 2:6-11) Yesu anachita zozizwitsa ziwiri zonsezi potsanzira mtima wopatsa wa Atate wake.—6/15, tsa. 4-5.

Kodi anthu opanda ungwirofe tingasangalatse bwanji Mulungu?

Anthu ngati Yobu, Loti ndi Davide ankalakwitsanso zinthu. Komabe, ankayesetsa kutumikira Mulungu ndiponso ankavomereza zolakwa zawo n’kusintha. Mulungu ankawakonda ndipo inunso mukamachita zimenezi, angamakukondeni.—7/1, tsa. 12-14.

Kodi Babulo Wamkulu akamadzawonongedwa anthu ake onse adzaphedwa?

Zikuoneka kuti ayi. Lemba la Zekariya 13:4-6 limasonyeza kuti atsogoleri ena adzasiya zipembedzo zawo n’kunena kuti sanali m’zipembedzozo.—7/15, tsa. 15-16.

N’chifukwa chiyani Baraki ananena kuti apita kukamenya nkhondo pokhapokha Debora akapita nawo?

Baraki ankakhulupirira kwambiri Mulungu. M’malo mopempha kuti Yehova amupatse zida zambiri, iye anapempha kuti apite ndi Debora, yemwe anali mneneri wa Mulungu. Ankafuna kuti Debora azikamulimbikitsa komanso azikalimbikitsa anthu omwe anali nawo. (Ower. 4:6-8; 5:7)—8/1, tsa. 13.

Ndi zinthu zina ziti zimene Mkhristu ayenera kuziganizira kwambiri?

Ayenera kuganizira zinthu monga Mawu a Mulungu amtengo wapatali, zimene analenga, mwayi wathu wopemphera ndiponso dipo limene anapereka chifukwa chotikonda.—8/15, tsa. 10-13.

Kodi mfundo yakuti tisamagwirizane ndi anthu oipa ingatithandize bwanji tikafuna kupeza chibwenzi?

N’zoona kuti tiyenera kuchita zinthu mwaulemu ndi anthu amene satumikira Yehova. Komabe kuchita chibwenzi ndi munthu amene sanadzipereke kwa Mulungu ndiponso samumvera kungasonyeze kuti sitikutsatira malangizo a Yehova. (1 Akor. 15:33)—8/15, tsa. 25.

N’chifukwa chiyani Petulo anachita mantha koma n’chiyani chinamuthandiza kukhalanso ndi chikhulupiriro?

Petulo anali ndi chikhulupiriro ndipo anayenda pamadzi n’kupita kumene kunali Yesu. (Mat. 14:24-32) Koma atayang’ana mphepo yamkuntho anayamba kuchita mantha. Kenako anayang’anitsitsa Yesu n’kulola kuti amuthandize.—9/15, tsa. 16-17.

Lemba la Machitidwe 28:4 limanena kuti anthu a ku Melita ankaganiza kuti Paulo ndi chigawenga. N’chifukwa chiyani ankaganiza zimenezi?

Njoka italuma Paulo anthuwo anaganiza kuti Dike, yemwe anali mulungu wamkazi wachilungamo, ndi amene anaitumiza pofuna kumulanga.—10/1, tsa. 9.

Kodi tikuphunzira chiyani pa zimene Marita anachita?

Nthawi ina Marita anatanganidwa kwambiri ndi kukonza chakudya. Koma Yesu ananena kuti mchemwali wake ndi amene anasankha chinthu chabwino chifukwa ankamvetsera zimene iye ankaphunzitsa. Ifenso tiyenera kusamala kuti zinthu zosafunika zisamatisokoneze potumikira Yehova.—10/15, tsa. 18-20.