Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mukudziwa?

Kodi Mukudziwa?

Kodi Herode anagwira ntchito yaikulu bwanji pokonza kachisi wa ku Yerusalemu?

Kachisi wa ku Yerusalemu anamangidwa koyamba ndi Solomo. Pa nthawiyo kachisiyu anamangidwa pamwamba pa phiri. Pofuna kuteteza kachisiyu, Solomo anamanga makoma mbali ya kum’mawa komanso ya kumadzulo kuti m’mbali mwa phirilo musagumuke. Herode ankafuna kuti kachisiyu akhale wokongola kwambiri kuposa mmene Solomo anamumangira. Choncho anaganiza zokulitsa kachisiyu komanso kumukonza mwina ndi mwina.

Akatswiri a zomangamanga omwe Herode anawalemba ntchito, anasalaza chigawo chakumpoto cha phiri lija ndi kumanganso makoma ena olimbitsa m’mbali mwa phirilo. Komanso anakulitsa bwalo la kachisiyu ndi mamita 32. Bwaloli linali mbali ya kum’mwera kwa kachisiyu. Pomanga makoma olimbitsa m’mbali mwa phirili, ankagwiritsa ntchito miyala ndipo malo ena, makomawa ankakhala aatali mpaka mamita 50.

Pa nthawi ya ntchitoyi, Herode sankafuna kukhumudwitsa Ayuda komanso sankafuna kuti ntchito za pakachisi ziime. Katswiri wina wofufuza mbiri ya Ayuda, dzina lake Josephus, ananena kuti Herode anafika mpaka pophunzitsa ansembe achiyuda ntchito yoswa miyala komanso ya ukalipentala. Anachita zimenezi chifukwa ankadziwa kuti ndi ansembe okha omwe ankafunika kulowa m’malo opatulika a m’kachisi. Choncho sakanagwiritsa ntchito anthu ena kumanga malowa.

Komabe Herode anamwalira ntchitoyi isanathe. Pofika mu 30 C.E., ntchitoyi inali idakali mkati ndipo panali patadutsa zaka 46. (Yohane 2:20) Ntchito yokonza kachisiyu inamalizidwa ndi Agiripa Wachiwiri yemwe anali chidzukulu cha mwana wa Herode, ndipo n’kutheka kuti inatha m’nthawi ya atumwi.

N’chifukwa chiyani anthu a pachilumba cha Melita ankaganiza kuti Paulo ndi chigawenga?

Mulungu wamkazi wachilungamo (kumanzere) akumenya mulungu wamkazi wopanda chilungamo

N’kutheka kuti anthu a pachilumba cha Melita ankakhulupirira komanso kutsatira miyambo inayake ya chipembedzo chachigiriki. Mwachitsanzo, taganizirani nkhani imene ili m’buku la Machitidwe yomwe imafotokoza zomwe zinachitika ngalawa imene Paulo anakwera itasweka. Nkhaniyi imanena kuti Paulo anatola kamtolo ka nkhuni n’kukaika pamoto womwe anthu a pachilumbachi anakolezera Paulo ndi anzake. Atangoika kamtoloko pamoto, njoka inamuluma n’kukanirira kudzanja lake. Anthuwo ataona zimenezi, ananena kuti: “Ndithu munthu uyu ndi wopha anthu, chifukwa ngakhale wapulumuka panyanja, chilungamo sichinamulole kuti akhalebe ndi moyo.”Machitidwe 28:4.

Mawu amene anawamasulira kuti “chilungamo” palembali, anachokera ku mawu achigiriki akuti “di’ke.” Nthano zina zachigiriki zimanena kuti Dike linali dzina la mulungu wamkazi wachilungamo. Anthu a pachilumbachi ankakhulupirira kuti mulunguyu, ankayang’anitsitsa zimene anthu amachita, ndipo akaona wina akuchita zopanda chilungamo mobisa, ankakaulula kwa mulungu wina, dzina lake Zeu. Akuti mulunguyu ankachita zimenezi n’cholinga choti munthuyo alangidwe. Buku lina linanena kuti n’kutheka kuti anthu a pachilumba cha Melita ankaganiza kuti: “Ngakhale kuti Paulo wapulumuka ngozi ya panyanja, mulungu wamkazi Dike, akudziwa kuti ndi munthu woipa, n’chifukwa chake wamutumizira njoka.” Koma anthu aja anasintha maganizo awo ataona kuti Paulo sanavulale.