Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Anthufe Tingasangalatsedi Mulungu?

Kodi Anthufe Tingasangalatsedi Mulungu?

Kodi munayamba mwawerengapo nkhani zokhudza anthu amene amatchulidwa m’Baibulo kuti anali abwino n’kunena kuti, ‘Ine sindingafike pamenepa?’ Mwina munganene choncho chifukwa mumaona kuti inuyo si munthu wopanda cholakwa kapena wolungama ndipo nthawi zambiri mumalakwitsa zinthu.

Yobu ‘anali munthu wopanda cholakwa ndi wowongoka mtima.’—Yobu 1:1

Baibulo limanena kuti Yobu ‘anali munthu wopanda cholakwa ndi wowongoka mtima.’ (Yobu 1:1) Limanenanso kuti Loti anali “munthu wolungama.” (2 Petulo 2:8) Nayenso Davide amatchulidwa kuti ankachita “zinthu zoyenera zokhazokha” m’maso mwa Mulungu. (1 Mafumu 14:8) Komano tiyeni tione bwinobwino za moyo wa anthu amenewa. Tiona kuti (1) analakwitsapo zinthu zina, (2) tingaphunzire zambiri kwa iwo, ndipo (3) n’zotheka kuti anthu opanda ungwiro asangalatse Mulungu.

NAWONSO ANALAKWITSAPO ZINTHU

“[Mulungu] anapulumutsa Loti, munthu wolungama amene anavutika mtima kwambiri ndi kulowerera kwa anthu ophwanya malamulo mu khalidwe lawo lotayirira.”—2 Petulo 2:7

Yobu anakumana ndi mavuto ambiri motsatizana ndipo mavutowa ankaoneka kuti samayenera kukumana nawo. Izi zinamuchititsa kuti aganize molakwika n’kumaona kuti Mulungu analibe nazo ntchito zakuti iyeyo ndi munthu wokhulupirika. (Yobu 9:20-22) Yobu ankadziona kuti anali munthu wolungama kwambiri moti anthu ena ankaganiza kuti Yobuyo akunena kuti ndi wolungama kuposa Mulungu.—Yobu 32:1, 2; 35:1, 2.

Loti ankazengereza kuthawa mumzinda wa Sodomu. Pa nthawiyo, iye anali atatopa ndi makhalidwe onyansa amene ankachitika m’mizinda ya Sodomu ndi Gomora moti ankavutika mumtima chifukwa cha zimenezi. (2 Petulo 2:8) Mulungu anali ataneneratu kuti akufuna kuwononga mizinda yoipayo ndipo anakonza zoti Loti ndi banja lake apulumutsidwe. Mwina mungaganize kuti munthu woyambirira kuthawa anayenera kukhala Loti chifukwa anali atatopa ndi makhalidwe a anthu a mumzindawo. Koma zinthu zitafika povuta choncho, m’pamene ankazengereza. Moti angelo amene anatumidwa kuti adzapulumutse Loti ndi banja lake, anachita kuwagwira manja n’kuwatulutsa mumzindawo.—Genesis 19:15, 16.

Davide ‘anatsatira [Mulungu] ndi mtima wake wonse mwa kuchita zinthu zoyenera zokhazokha m’maso mwanga [mwa Mulungu].’—1 Mafumu 14:8

Davide analephera kudziletsa ndipo anachita chigololo ndi mkazi wa mwiniwake. Pofuna kubisa zomwe anachitazi, iye anapangitsa kuti mwamuna wa mkaziyo aphedwe. (2 Samueli chaputala 11) Pa nkhaniyi, Baibulo limanena kuti “zimene Davide anachitazi zinamuipira kwambiri Yehova.”—2 Samueli 11:27.

Taona kuti Yobu ndi Loti analakwitsapo zinthu zina ndipo Davide anachita machimo aakulu. Koma m’nkhaniyi, tionanso kuti onsewa ankatumikira Mulungu modzipereka ndiponso anali ndi mtima wofuna kumusangalatsa. Iwo anavomereza zolakwa zawo ndipo anasintha. Zimenezi n’zimene zinachititsa kuti Mulungu azisangalala nawo ndipo n’chifukwa chake nthawi zambiri Baibulo limawatchula kuti anali anthu okhulupirika.

KODI TIKUPHUNZIRAPO CHANI?

Anthufe sitingapeweretu kulakwitsa zinthu chifukwa ndife opanda ungwiro. (Aroma 3:23) Koma tikalakwitsa, timafunika kuvomereza zolakwa zathu ndi kuyesetsa kusintha kuti Yehova adzisangalala nafe.

Kodi n’chiyani chinathandiza Yobu, Loti ndi Davide kuti asinthe? Yobu anali munthu wa mtima wosagawanika. Ndipo Mulungu atamulangiza, Yobu anasintha maganizo ake n’kudzimvera chisoni chifukwa cha zimene ananenazo. (Yobu 42:6) Loti ankanyansidwa ndi khalidwe la chiwerewere limene anthu a m’mizinda ya Sodomu ndi Gomora ankachita ndipo maganizo akewa anali ogwirizana ndi malamulo a Mulungu. Koma atauzidwa kuti achoke mwansanga mumzindawo, Loti anazengereza ndipo pamenepa m’pamene panagona vuto lake. Pamapeto pake anatuluka m’mizinda imene Mulungu ankafuna kuiwonongayo ndipo anapulumuka. Iye anamvera chenjezo lakuti asayang’ane zinthu zakumbuyo. Davide, anachita tchimo lalikulu kwambiri, koma anasonyeza zimene zinali mumtima mwake chifukwa anavomereza kulakwa kwake ndi kupempha Mulungu kuti amukhululukire.—Salimo 51.

Zimene Mulungu anachita powakomera mtima anthuwa n’kuyambiranso kuwakonda, zikusonyeza mmene iye amaonera anthu opanda ungwiro. Baibulo limanena kuti “iye [Mulungu] akudziwa bwino mmene anatiumbira, amakumbukira kuti ndife fumbi.” (Salimo 103:14) Popeza Mulungu amadziwa bwino kuti anthufe timalakwitsa zinthu, kodi amafuna kuti tizitani kuti tizimusangalatsa?

Mulungu “akudziwa bwino mmene anatiumbira, amakumbukira kuti ndife fumbi.”—Salimo 103:14

KODI ANTHU OPANDA UNGWIROFE TINGASANGALATSE BWANJI MULUNGU?

Malangizo amene Davide anapatsa mwana wake Solomo angatithandize kudziwa zimene tingachite kuti tizisangalatsa Mulungu. Iye anati: “Iwe Solomo mwana wanga, dziwa Mulungu wa bambo wako, um’tumikire ndi mtima wathunthu.” (1 Mbiri 28:9) Kodi kukhala ndi mtima wathunthu kumatanthauza chiyani? Kumatanthauza kukonda Mulungu komanso kuyesetsa kumvera malamulo ake, osati kuchita chilichonse popanda kulakwitsa. Munthu wa mtima wathunthu amamvera Mulungu ndi kumutumikira mofunitsitsa komanso amavomereza akalakwitsa. Mulungu ankaona kuti Yobu anali “munthu wopanda cholakwa,” Loti anali “munthu wolungama,” ndipo Davide ankachita “zinthu zoyenera zokhazokha.” Anthu onsewa Mulungu ankawaona chonchi chifukwa ankamukonda komanso anali ndi mtima wofuna kumumvera. Choncho Mulungu ankasangalala nawo ngakhale kuti analakwitsapo zinthu zina.

Munthu wa mtima wathunthu amamvera Mulungu ndi kumutumikira mofunitsitsa

Ngati tikudziimba mlandu chifukwa chakuti taganiza, talankhula kapena kuchita zinthu zomwe pambuyo pake tazindikira kuti n’zolakwika, tiziganizira zimene zinachitikira anthu amene takambiranawa. Mulungu amadziwa kuti panopa sitingakwanitse kuchita chilichonse bwinobwino osalakwitsa ngakhale pang’ono chifukwa ndife opanda ungwiro. Komabe amafuna kuti tizimukonda komanso tiziyesetsa kumumvera. Tikamachita zimenezi timasonyeza kuti tili ndi mtima wathunthu ndipo tisamakayikire kuti Mulungu amasangalala nafe.