NSANJA YA OLONDA (YOPHUNZIRA) December 2015

M’magaziniyi muli nkhani zophunzira kuyambira pa February 1 mpaka 28, 2016.

Kodi Mukukumbukira?

Onani zimene mukukumbukira m’magazini a Nsanja ya Olonda amene anatuluka m’mwezi wa July mpaka December mu 2015.

Yehova Amalankhula Nafe

Timaphunzira mfundo ina yofunika kwambiri tikaganizira kuti Mulungu wakhala akulankhula ndi anthu m’zilankhulo zosiyanasiyana.

Baibulo Lomveka Bwino Kwambiri

Mfundo zitatu zomwe Komiti Yomasulira Baibulo la Dziko Latsopano inatsatira pomasulira Baibuloli.

Baibulo la Dziko Latsopano Lokonzedwanso Lomwe Linatuluka mu 2013

Kodi ndi zinthu zikuluzikulu ziti zimene anasintha m’Baibuloli?

Muzigwiritsa Ntchito Bwino Lilime Lanu

Kodi chitsanzo cha Yesu chingatithandize bwanji kudziwa nthawi yoyenera kulankhula, zimene tiyenera kulankhula ndiponso mmene tiyenera kulankhulira?

Yehova Adzakuthandizani Pamene Mukudwala

Kodi tiyenera kuona bwanji zinthu tikadwala ndipo tiyenera kuchita chiyani?

MBIRI YA MOYO WANGA

Tsopano Ndili pa Mtendere ndi Mulungu Komanso Amayi Anga

Pamene Michiyo Kumagai anasiya kulambira makolo akale, amayi ake anasiya kugwirizana naye. Kodi Michiyo anachita zotani kuti ayambenso kugwirizana nawo?

Mlozera Nkhani wa Magazini a Nsanja ya Olonda a 2015

Mndandanda wa nkhani za mu Nsanja ya Olonda yophunzira ndiponso yogawira.