Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Yehova Adzakuthandizani Pamene Mukudwala

Yehova Adzakuthandizani Pamene Mukudwala

“Yehova adzachirikiza wonyozekayo pamene akudwala pabedi lake.”—SAL. 41:3.

NYIMBO: 23, 138

1, 2. Kodi kale Mulungu anathandiza bwanji anthu ena? (b) Kodi masiku ano anthu ena amaganiza zotani akadwala?

PA NTHAWI ina mutadwala kwambiri, mwina munadzifunsapo kuti: ‘Koma ndichiradi?’ Kapena munadzifunsapo funso ngati limeneli wachibale kapena mnzanu wina atadwala. Anthufe timada nkhawa anzathu kapena ifeyo tikadwala. Zoterezi zinachitikiranso Ahaziya ndi Beni-hadadi, omwe anali mafumu m’nthawi ya mneneri Eliya ndi Elisa. Ahaziya anali mwana wa Ahabu ndi Yezebeli ndipo atavulala kwambiri ankafuna kudziwa ngati angachire. Pa nthawi ina Beni-hadadi, yemwe anali mfumu ya ku Siriya, anadwalanso kwambiri ndipo anafunsa kuti: “Kodi ndichira matenda angawa?”—2 Maf. 1:2; 8:7, 8.

2 Baibulo limanena kuti kale, Yehova ankachiritsa anthu ena mozizwitsa. Anagwiritsanso ntchito aneneri ake kuti aukitse anthu ena amene amwalira. (1 Maf. 17:17-24; 2 Maf. 4:17-20, 32-35) Chifukwa cha zimenezi, anthu ena akadwala amafuna kudziwa ngati Mulungu angawachiritse.

3-5. Kodi Mulungu ndi Yesu ali ndi mphamvu zotani, nanga m’nkhaniyi tikambirana mafunso ati?

 3 Baibulo limasonyeza kuti Mulungu angathe kupangitsa kuti munthu adwale kapena kuchira. Mwachitsanzo m’nthawi ya Abulahamu, analanga Farao ndi matenda komanso pa nthawi ina anachititsa kuti Miriamu, mchemwali wake wa Mose, adwale khate. (Gen. 12:17; Num. 12:9, 10; 2 Sam. 24:15) Anachenjezanso Aisiraeli kuti akakhala osakhulupirika, adzawagwetsera “nthenda iliyonse ndi mliri.” (Deut. 28:58-61) Koma pa nthawi zina Yehova ankateteza anthu ake kuti asadwale. (Eks. 23:25; Deut. 7:15) Ankathanso kuwachiritsa. Mwachitsanzo, Yobu atadwala kwambiri mpaka kulakalaka atangofa, Mulungu anamuchiritsa.—Yobu 2:7; 3:11-13; 42:10, 16.

4 Choncho n’zosakayikitsa kuti Mulungu ali ndi mphamvu zoti angachiritse munthu amene akudwala. N’chimodzimodzinso ndi Mwana wake, Yesu. Baibulo limati Yesu ankachiritsa anthu osaona, ofa ziwalo, odwala khate komanso odwala khunyu. (Werengani Mateyu 4:23, 24; Yoh. 9:1-7) N’zolimbikitsa kwambiri kudziwa kuti zimene Yesu anachitazi zimasonyeza zimene adzachite padziko lonse m’tsogolo. Pa nthawiyo, palibe munthu “amene adzanene kuti: ‘Ndikudwala.’”—Yes. 33:24.

5 Koma kodi panopa tingayembekezere kuti Mulungu kapena Yesu atichiritse tikadwala? Nanga ndi zinthu ziti zimene tiyenera kuganizira tikamasankha mankhwala? M’nkhaniyi tikambirana mafunso amenewa.

ZIMENE YEHOVA ANGACHITE POTITHANDIZA TIKADWALA

6. Kodi Baibulo limati chiyani pa nkhani ya “mphatso za kuchiritsa”?

6 Baibulo limanena kuti kale, Mulungu anapatsa Akhristu ena odzozedwa mphamvu zoti azichita zozizwitsa. (Mac. 3:2-7; 9:36-42) Mwachitsanzo, ena anapatsidwa “mphatso za kuchiritsa,” ena kulankhula malilime komanso ena kunenera. (1 Akor. 12:4-11) Koma mphatso zimenezi zinali zoti zidzatha. (1 Akor. 13:8) Choncho palibe amene ali ndi mphatsozi masiku ano. Chifukwa cha zimenezi, sitingayembekezere kuti Mulungu atichiritsa kapena kuchiritsa achibale athu mozizwitsa.

7. Kodi lemba la Salimo 41:3 limatilimbikitsa bwanji?

7 Komabe tikadwala, Mulungu angatilimbikitse, kutipatsa nzeru komanso kutithandiza ngati mmene anachitira ndi atumiki ake akale. Mfumu Davide analemba kuti: “Wodala ndi munthu amene amachita zinthu moganizira munthu wonyozeka. Pa tsiku la tsoka, Yehova adzamupulumutsa. Yehova adzamuteteza ndi kumusunga ali wamoyo.” (Sal. 41:1,2) Davide sankatanthauza kuti anthu amene amachita zinthu moganizira ovutika, sangafe. M’malomwake, ankangotanthauza kuti Mulungu amawathandiza anthu oterewa. Koma kodi amawathandiza bwanji? Davide anati, ‘Yehova adzawachirikiza pamene akudwala ndi kuwasamalira bwino kwambiri.’ (Sal. 41:3) Munthu amene amachita zinthu moganizira ovutika ayenera kudziwa kuti Mulungu amaona zabwino zimene amachitazo ndiponso kukhulupirika kwake. Komanso Mulungu amatithandiza chifukwa ndi amene anapanga thupi lathu m’njira yoti lizitha kuchira.

8. Mogwirizana ndi lemba la Salimo 41:4, kodi Davide anapempha chiyani kwa Yehova?

8 Davide analemba kuti: “Ine ndinati: ‘Inu Yehova, ndikomereni mtima. Ndichiritseni, pakuti ndakuchimwirani.’” (Sal. 41:4) N’kutheka kuti apa Davide ankanena za zimene anapempha Yehova pamene Abisalomu ankafuna kulanda ufumu wake. Pa nthawiyo, n’kuti akudwala kwambiri moti sakanatha kulimbana ndi mwana wakeyo. Ankadziwa kuti akukumana ndi mavuto amenewa chifukwa cha tchimo limene  anachita ndi Bati-seba. (2 Sam. 12:7-14) Koma Davide ankadziwanso kuti Mulungu anamukhululukira ndipo ankakhulupirira kuti amuthandiza pamene akudwala. Komabe kodi iye ankapempha Mulungu kuti amuchiritse mozizwitsa kapena kumupatsa moyo wautali?

9. (a) Kodi Yehova anathandiza bwanji Mfumu Hezekiya? (b) Kodi Davide ankafuna kuti Yehova amuthandize bwanji?

9 Pa nthawi ina, Mulungu anachiritsa Mfumu Hezekiya pamene “anadwala mpaka kutsala pang’ono kufa.” Si nthawi zonse pamene Mulungu ankachita zimenezi. Komabe pa nthawiyi anasankha kuchiritsa Hezekiya ndipo iye anakhala ndi moyo zaka zinanso 15. (2 Maf. 20:1-6) Koma sikuti Davide ankapempha Mulungu kuti amuchiritse mozizwitsa. Nkhani ya mu Salimo 41 imasonyeza kuti ankangopempha Mulungu kuti amuthandize ngati mmene Mulunguyo akanathandizira anthu amene amaganizira onyozeka. Popeza Davide anali pa ubwenzi wolimba ndi Yehova, anamupempha kuti amulimbikitse, kumusamalira komanso kumuthandiza kuti thupi lake lizigwira ntchito bwino kuti achire. (Sal. 103:3) Ifenso tikadwala tingapemphe Yehova kuti atichitire zimenezi.

10. Kodi tikuphunzira chiyani pa zimene zinachitikira Terofimo ndi Epafurodito?

10 Kale mtumwi Paulo ndiponso anthu ena anapatsidwa mphamvu zochiritsa, koma si Akhristu onse amene ankachiritsidwa mozizwitsa. (Werengani Machitidwe 14:8-10.) Mwachitsanzo, Paulo anachiritsa ‘bambo ake a Papuliyo amene anali chigonere, akuvutika ndi malungo komanso kamwazi.’ Powachiritsa, ‘anapemphera ndiponso kuwasanjika manja.’ (Mac. 28:8) Koma Paulo sanachiritse Terofimo yemwe anayenda naye pa ulendo wina waumishonale. (Mac. 20:3-5, 22; 21:29) Terofimo atadwala moti sakanatha kupitiriza ulendowu, Paulo anamusiya ku Mileto kuti achire. (2 Tim. 4:20) Nayenso Epafurodito, ‘atadwala mpaka kutsala pang’ono kufa,’ Paulo sanamuchiritse ngakhale kuti anali mnzake wapamtima.—Afil. 2:25-27, 30.

KODI TIZITSATIRA MALANGIZO ATI?

11, 12. (a) N’chifukwa chiyani Luka ayenera kuti anathandiza kwambiri Paulo? (b) Kodi tikudziwa zotani zokhudza maphunziro a Luka?

11 Luka anali dokotala ndipo ankayendanso ndi Paulo. (Mac. 16:10-12; 20:5, 6; Akol. 4:14) Iye ayenera kuti ankathandiza Paulo ndiponso anthu ena amene ankayenda nawo, akadwala. (Agal. 4:13) Zimene ankachitazi n’zogwirizana ndi zimene Yesu ananena kuti: ‘Odwala amafuna dokotala.’—Luka 5:31.

12 Baibulo silinena kuti Luka anaphunzira kuti ntchito yaudokotala komanso anaphunzira liti. Koma limatiuza kuti Paulo anapereka moni wa Luka kwa Akhristu a ku Kolose. Choncho n’kutheka kuti Luka anaphunzira ntchito yakeyi kufupi ndi ku Kolose, kusukulu ina ya mumzinda wa Laodikaya. Kaya Luka anaphunziradi ntchito yake kumeneko kapena ayi, zimene tikudziwa n’zakuti sankangopereka malangizo okhudza mankhwala koma anali dokotala weniweni. Umboni wa zimenezi ndi mawu okhudza zachipatala amene anagwiritsa ntchito m’buku la Machitidwe ndiponso mu Uthenga Wabwino. Komanso anafotokoza kwambiri mmene Yesu anachiritsira anthu.

13. Kodi tiyenera kukumbukira chiyani tisanapereke kapena kutsatira malangizo okhudza mankhwala?

13 Masiku ano Akhristu alibe mphamvu zochiritsa. Koma abale ndi alongo ena amene akufuna kutithandiza akhoza kutipatsa malangizo okhudza mankhwala. N’zoona kuti malangizo ena angakhale othandiza. Mwachitsanzo, Paulo anapereka malangizo othandiza kwa Timoteyo pamene ankavutika m’mimba chifukwa choti madzi akuderalo sanali  abwino. * (Werengani 1 Timoteyo 5:23.) Koma izi n’zosiyana kwambiri ndi kukakamiza Akhristu anzathu kuti agwiritse ntchito mtundu winawake wa mankhwala, kudya zakudya zinazake kapena kupewa kudya zinthu zina. N’kutheka kuti zinthuzi sizingawathandize ndipo nthawi zina zikhoza kuwapweteka. Mwachitsanzo, Akhristu ena anganene kuti: ‘Mankhwala amenewa ndi othandiza kwambiri. Akutiakuti aja anali ndi vuto ngati lanuli ndipo anachira atamwa mankhwalawa.’ Koma tizikumbukira kuti ngakhale mankhwala odziwika bwino akhoza kukhala ndi mavuto ake.—Werengani Miyambo 27:12.

TIZISANKHA MWANZERU TIKADWALA

14, 15. (a) Kodi ndi anthu ati amene tiyenera kusamala nawo? (b) Kodi lemba la Miyambo 14:15 lingatithandize bwanji?

14 Akhristufe timafuna kukhala athanzi kuti tikhale osangalala ndiponso kuti tizitumikira Mulungu bwinobwino. Komabe timadwala chifukwa tinatengera uchimo kwa makolo athu oyambirira. Tikadwala, pali njira zosiyanasiyana zimene tingatsatire kuti tichire. Ndipo ndi udindo wa Mkhristu aliyense kusankha zochita pa nkhaniyi. Koma tikadwala, anthu ambiri m’dziko loipali amapezerapo mwayi wochita bizinezi. Ena amanena zabodza potsatsa mankhwala enaake. Ndipo anthu kapena makampani ena amalimbikitsa kwambiri anthu kugwiritsa ntchito mankhwala komanso zinthu zina zodula n’cholinga chongofuna kupeza ndalama zambiri. Munthu amene akuvutika kwambiri ndi matenda angatengeke mosavuta ndi zimenezi. Koma tisaiwale kuti Mawu a Mulungu amati: “Munthu amene sadziwa zinthu amakhulupirira mawu alionse. Koma wochenjera amaganizira za mmene akuyendera.”—Miy. 14:15.

15 Munthu “wochenjera” samangokhulupirira zilizonse zimene anthu osadziwa kwenikweni za mankhwala anganene. M’malomwake angadzifunse kuti: ‘Akuti mankhwalawa anathandizapo munthu wina, koma kodi pali umboni uliwonse woti zimenezi ndi zoona? Ngakhale zitakhala kuti ndi zoona, kodi mankhwala amenewa angandithandizenso ineyo? Nanga kodi pangafunike kuti ndifufuze kaye, mwinanso ndifunse dokotala kapena munthu wina wodziwa bwino za matenda angawa?’—Deut. 17:6.

16. Kodi tiyenera kudzifunsa mafunso ati posankha mankhwala?

16 Mawu a Mulungu amatiuza kuti tizikhala “amaganizo abwino.” (Tito 2:12) Tiyenera kuganiza bwino makamaka ngati taona kuti malangizo ena okhudza mankhwala enaake ndi okayikitsa. Tingadzifunse kuti: ‘Kodi amene akufuna kundipatsa mankhwalawa angafotokoze bwinobwino mmene amagwirira ntchito? Kodi zimene akufotokozazi ndi zomveka? Nanga madokotala amaona kuti mankhwalawa ndi othandizadi?’ (Miy. 22:29) Mwachitsanzo, munthu angatiuze kuti anthu a m’mayiko ena angotulukira kumene mankhwalawo ndipo madokotala ambiri sanawadziwe. Kodi zimenezi tiyenera kuzikhulupirira? Anthu ena sangafotokoze bwinobwino kumene mankhwala awo amachokera kapena amati pali mphamvu inayake imene imachititsa kuti mankhwalawo azigwira ntchito. Tiyenera kusamala kwambiri ndi zoterezi chifukwa Mawu a Mulungu amaletsa kugwiritsa ntchito “mphamvu zamatsenga.”—Yes. 1:13; Deut. 18:10-12.

“TIKUKUFUNIRANI ZABWINO ZONSE!”

17. Kodi tonsefe timafuna chiyani?

17 M’nthawi ya atumwi, bungwe lolamulira  linatumiza kalata yofunika kwambiri kumipingo. M’kalatayo, anafotokoza zinthu zimene Akhristu ayenera kupewa ndipo pomaliza anati: “Mukamapewa zinthu zimenezi mosamala kwambiri, zinthu zidzakuyenderani bwino. Tikukufunirani zabwino zonse!” (Mac. 15:29) M’zilankhulo zina, mawu omalizawa anawamasulira kuti “mukhale ndi moyo wathanzi” ndipo angatanthauzenso kuti “mukhale amphamvu.” Kunena zoona tonsefe timafuna kukhala athanzi kuti tizitha kutumikira bwino Mulungu.

Timafuna kukhala athanzi kuti tizitha kutumikira bwino Mulungu (Onani ndime 17)

18, 19. Kodi tikuyembekezera zotani m’dziko latsopano?

18 Lemba la Chivumbulutso 22:1, 2 limanena za nthawi imene sitidzadwalanso. Mtumwi Yohane anaona m’masomphenya “mtsinje wa madzi a moyo” ndiponso “mitengo ya moyo” yokhala ndi masamba “ochiritsira mitundu ya anthu.” Lembali silikunena za mankhwala azitsamba a masiku ano komanso silikutanthauza kuti tizidzapatsidwa mankhwala oterowo m’dziko latsopano. M’malomwake likunena za zinthu zonse zimene Yehova ndi Yesu adzachite kuti tidzakhale ndi moyo wosatha. Tidzasangalala kwambiri lembali likadzakwaniritsidwa.—Yes. 35:5, 6.

19 Koma panopa palibe zimene tingachite m’dziko loipali kuti tipeweretu matenda. Sitingayembekezerenso kuti tikadwala Mulungu atichiritsa mozizwitsa. Ngakhale zili choncho, timadziwa kuti Yehova amatikonda ndipo tikamadwala amamvetsa mmene tikumvera. Mofanana ndi Davide, timakhulupirira kuti tikadwala Mulungu amatithandiza. Choncho tikhoza kunenanso zimene Davide ananena kuti: “Ine mwandichirikiza chifukwa cha mtima wanga wosagawanika, ndipo mudzandiika pamaso panu mpaka kalekale.”—Sal. 41:12.

^ ndime 13 Buku lina lofotokoza za vinyo limati: “Asayansi apeza kuti tizilombo tina toyambitsa matenda timafa msanga akatiika m’vinyo.”