Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Yehova Amalankhula Nafe

Yehova Amalankhula Nafe

“Tamvera, ndikufuna ndikulankhule.”—YOBU 42:4.

NYIMBO: 113, 114

1-3. a) N’chifukwa chiyani tinganene kuti Mulungu ndi wapamwamba kwambiri kuposa anthu? (b) Kodi tikambirana chiyani m’nkhaniyi?

MULUNGU analenga angelo ndiponso anthu ndipo ankafuna kuti azilankhula nawo komanso kukhala nawo pa ubwenzi. (Sal. 36:9; 1 Tim. 1:11) Mtumwi Yohane ananena za Yesu kuti ndi “Mawu” komanso “woyamba wa chilengedwe cha Mulungu.” (Yoh. 1:1; Chiv. 3:14) Yehova ankamuuza Yesu maganizo ake ndiponso mmene ankamvera mumtima mwake. (Yoh. 1:14, 17; Akol. 1:15) Komanso nthawi ina mtumwi Paulo ananena za ‘malilime a angelo.’ Pamenepa, ankanena za chilankhulo cha angelo chomwe ndi chapamwamba kuposa cha anthu.—1 Akor. 13:1.

2 Angelo ndiponso anthu, alipo ambirimbiri koma Yehova amawadziwa bwino onsewa. Nthawi iliyonse anthu ambiri amapemphera kwa Yehova m’zilankhulo zosiyanasiyana. Komabe Yehova amatha kumvetsera mapemphero onsewo kwinaku akulankhulanso ndi angelo ake. Mulungu ndi wapamwamba kwambiri kuposa anthu, n’chifukwa chake amakwanitsa kuchita zimenezi. (Werengani Yesaya 55:8, 9.) N’zoona kuti Yehova akhoza kulankhula m’njira yapamwamba kwambiri. Koma akamalankhula ndi anthu amanena zinthu m’njira yosavuta kumva, n’cholinga choti anthuwo amve zimene akufuna.

3 M’nkhaniyi tikambirana zimene Mulungu wakhala akuchita kuti azilankhula ndi anthu m’njira yosavuta kumva. Tikambirananso  kuti nthawi zina amasintha njira yolankhulira ndi anthu kuti zigwirizane ndi mmene zinthu zilili pa nthawiyo.

MULUNGU ANATIPATSA MAWU AKE

4. a) Kodi Yehova anagwiritsa ntchito chilankhulo chiti polankhula ndi Mose, Samueli komanso Davide? (b) Kodi ndi nkhani ziti zimene anthuwa analemba m’Baibulo?

4 M’munda wa Edeni, Yehova ankalankhulana ndi Adamu pogwiritsa ntchito chilankhulo chimene Adamuyo akanatha kumva. N’kutheka kuti Mulungu ankalankhula naye m’Chiheberi chakale. Kenako Mulungu anauza anthu monga Mose, Samueli komanso Davide kuti alembe mawu ake. Anthuwa analemba mawuwa m’Chiheberi, chomwe chinali chilankhulo chawo, ndipo aliyense analemba mogwirizana ndi luso lake. Anthuwa analemba zinthu zimene Mulungu ankawauza komanso zimene ankachita ndi anthu ake. Analembanso zimene anthu ena anachita posonyeza kuti ankakhulupirira Mulungu ndiponso kumukonda. Zina zomwe analemba zimasonyeza zimene anthuwo analakwitsa chifukwa chosowa chikhulupiriro. Nkhani zonsezi zinalembedwa m’Baibulo kuti zitithandize masiku ano.—Aroma 15:4.

5. Kodi tikudziwa bwanji kuti Mulungu sankangolankhula ndi anthu ake m’Chiheberi chokha?

5 Patapita nthawi, Yehova anayamba kulankhula ndi anthu m’zilankhulo zinanso. Anthu a Mulungu atachoka ku ukapolo wa ku Babulo, ena ankalankhula Chiaramu. Mwina n’chifukwa chake Mulungu anachititsa kuti Danieli, Yeremiya komanso Ezara alembe mbali zina za m’mabuku awo m’Chiaramu. *

6. Kodi zinatheka bwanji kuti Malemba Achiheberi ayambenso kupezeka m’Chigiriki?

6 Alekizanda Wamkulu atayamba kulamulira m’madera ambiri, anthu a m’maderawo anayamba kulankhula Chigiriki. Ayuda ambiri anayambanso kulankhula chilankhulochi ndipo izi zinachititsa kuti Malemba Achiheberi amasuliridwe m’Chigiriki. Baibulo limene linamasuliridwa m’Chigirikili (Septuagint) linali loyamba kumasuliridwa kuchokera m’Malemba oyambirira. * Pomasulira Baibuloli, ena ankamasulira liwu ndi liwu pomwe ena ankangomasulira mfundo za m’malembawo. Ayuda komanso Akhristu amene ankalankhula Chigiriki ankalemekeza Baibuloli ndipo ankaliona kuti ndi Mawu a Mulungu.

7. Kodi Yesu ayenera kuti ankaphunzitsa m’chilankhulo chiti?

7 Yesu atabwera padziko lapansi, ayenera kuti ankalankhula komanso kuphunzitsa anthu m’Chiheberi. (Yoh. 19:20; 20:16; Mac. 26:14) Popeza Chiheberi cha m’nthawi ya atumwi chinalinso ndi mawu ena achiaramu, n’kutheka kuti Yesu ankagwiritsanso ntchito mawu achiaramu. Komabe ankadziwanso Chiheberi choyambirira chomwe Mose ndi aneneri ena anagwiritsa ntchito polemba mabuku awo, omwe ankawerengedwa m’masunagoge mlungu uliwonse. (Luka 4:17-19; 24:44, 45; Mac. 15:21) Anthu ena a ku Isiraeli ankalankhulanso Chigiriki ndi Chilatini. Komabe Malemba sanena ngati Yesu ankalankhulanso zilankhulo zimenezi.

8, 9. a) Chikhristu chitafalikira, kodi anthu a Mulungu ambiri ankalankhula chilankhulo chiti? (b) Kodi zimenezi zikusonyeza kuti Mulungu ndi wotani?

8 Otsatira a Yesu oyambirira ankalankhula Chiheberi, koma Yesu atamwalira Akhristu anayamba kugwiritsa ntchito zilankhulo zina. (Werengani Machitidwe 6:1.) Chikhristu  chitafalikira, anthu a Mulungu ambiri ankalankhula Chigiriki osati Chiheberi. Tikutero chifukwa chakuti mabuku a Maliko, Luka komanso Yohane, omwe amafotokoza zimene Yesu anaphunzitsa ndiponso kuchita, analembedwa ndiponso kufalitsidwa m’Chigiriki. * Makalata a mtumwi Paulo ndiponso mabuku ena analembedwanso m’Chigiriki.

9 Anthu amene analemba Malemba Achigiriki akafuna kugwira mawu Malemba Achiheberi, nthawi zambiri ankatenga mawuwo m’Baibulo limene linamasuliridwa m’Chigiriki lija. Mawu amenewa amapezekabe m’Baibulo ngakhale kuti amasiyana pang’ono ndi mawu a m’Malemba Achiheberi oyambirira. Choncho Yehova analola kuti mawu ena a anthu amene anamasulira Baibulo lachigiriki lija apezeke m’Mawu ake. Izi zikusonyeza kuti Mulungu sakondera chilankhulo kapena chikhalidwe chinachake.—Werengani Machitidwe 10:34.

10. Kodi taona kuti Yehova amalankhula bwanji ndi anthu?

10 Pofika apa, taona kuti Yehova amalankhula ndi anthu mogwirizana ndi zimene zikufunika pa nthawiyo. Iye satikakamiza kuphunzira chilankhulo chinachake kuti timudziwe ndiponso kumvetsa zimene amafuna. (Werengani Zekariya 8:23; Chivumbulutso 7:9, 10.) N’zoona kuti Yehova anatsogolera kuti Baibulo lilembedwe. Komabe analola kuti anthu asankhe okha mawu amene angagwiritse ntchito polemba Baibulolo.

MULUNGU AMATETEZA MAWU AKE

11. Kodi Mulungu walephera kulankhula ndi anthu chifukwa choti anthuwo amalankhula zilankhulo zosiyanasiyana?

11 Kodi Mulungu walephera kulankhula ndi anthu chifukwa choti anthuwo amalankhula zilankhulo zosiyanasiyana? Ayi. N’zoona kuti m’Baibulo muli mawu ochepa a chilankhulo chimene Yesu ankalankhula akamaphunzitsa anthu. (Mat. 27:46; Maliko 5:41; 7:34; 14:36) Komabe Yehova anaonetsetsa kuti zimene Yesu anaphunzitsa zimasuliridwe m’Chigiriki ndiponso m’zilankhulo zina. Ayuda ndiponso Akhristu ankakopera Malemba ndipo izi zinathandiza kuti Malembawo asungike. Ndiyeno zimene anakoperazo zinamasuliridwa m’zilankhulo zina. Pafupifupi zaka 400 kuchokera pamene Yesu anaphedwa, mtsogoleri wina wachipembedzo ananena kuti zimene Yesu anaphunzitsa zinali zitamasuliridwa m’zilankhulo zambiri. Mwachitsanzo, zinali zitamasuliridwa m’chilankhulo cha ku Siriya, Iguputo, Indiya, Perisiya komanso ku Itiyopiya.

12. Kodi anthu anachita zotani pofuna kulepheretsa kuti Baibulo lifalitsidwe?

12 Anthu ambiri ankafuna kuwononga Baibulo. Mwachitsanzo m’chaka cha 303, mfumu ina ya ku Roma dzina lake Diocletian inalamula kuti Mabaibulo onse awotchedwe. Koma zimenezi  sizinatheke chifukwa chakuti Baibulo linali litamasuliridwa kale m’zilankhulo zambiri. Olamulira ambiri ankawotcha Mabaibulo komanso kuzunza anthu amene ankamasulira ndiponso kufalitsa Baibulo. M’zaka za m’ma 1500, munthu wina dzina lake William Tyndale anayamba kumasulira Baibulo m’Chingelezi kuchokera m’Chiheberi ndi Chigiriki. Iye anauza munthu wina wophunzira kwambiri kuti: “Ngati Mulungu angandipulumutse, ndidzamasulira Baibulo limene lingathandize anthu wamba kudziwa Malemba kuposa munthu wophunzira ngati inuyo.” Tyndale anathawa ku England kuti akapitirize ntchito yomasulira ndiponso kusindikiza Baibulolo. Mabaibulo ambiri anapitiriza kufalitsidwa ngakhale kuti atsogoleri achipembedzo ankayesetsa kuti onse awotchedwe. Patapita nthawi, Tyndale anagwidwa ndipo anamumangirira pamtengo ndipo atafa anawotcha mtembo wake. Koma Baibulo lake linapitiriza kufalitsidwa ndipo linagwiritsidwa ntchito kwambiri pomasulira Baibulo lachingelezi la King James.Werengani 2 Timoteyo 2:9.

13. Kodi zimene akatswiri a Baibulo anapeza zimasonyeza chiyani?

13 N’zoona kuti m’Mabaibulo ena akalekale muli zinthu zina zolakwika. Komabe akatswiri ena a Baibulo atayerekezera zolemba zosiyanasiyana zakale za Baibulo, anapeza kuti zinthu zambiri ndi zofanana. Anaona kuti mfundo zake zazikulu n’zofanana ngakhale kuti mavesi ena amasiyana pang’ono. Zimenezi zimatitsimikizira kuti uthenga umene unali m’Mabaibulo oyambirira sunasinthe ndipo ndi umene uli m’Baibulo masiku ano.—Yes. 40:8. *

14. N’chifukwa chiyani tinganene kuti anthu ambiri akhoza kupeza Baibulo?

14 Ngakhale kuti anthu ambiri anayesetsa kuti Mabaibulo onse awotchedwe, Yehova waonetsetsa kuti Mawu akewo amasuliridwe m’zilankhulo zambiri kuposa buku lina lililonse. Panopa Baibulo lonse kapena mabuku ake ena amapezeka m’zilankhulo zoposa 2,800. Padziko lonse Baibulo limagulitsidwa kwambiri kuposa buku lililonse. Izi zili choncho ngakhale kuti masiku ano pali anthu ambiri amene sakhulupirira Mulungu. Kunena zoona, Baibulo ndi buku limene limapezeka mosavuta padziko lonse. Mabaibulo ena sanamasuliridwe bwinobwino komabe akhoza kuthandiza munthu kuti aphunzire ndi kumvetsa uthenga wake.

PANAFUNIKA BAIBULO LATSOPANO

15. a) Kodi zinthu zasintha bwanji kuchokera mu 1919? (b) N’chifukwa chiyani mabuku athu amayamba alembedwa kaye m’Chingelezi?

15 Gulu la “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” litangokhazikitsidwa mu 1919, linkalemba mabuku ndi zinthu zina m’Chingelezi, ndipo zambiri sizinkamasuliridwa m’zilankhulo zina. (Mat. 24:45) Koma panopa kapoloyu  akuyesetsa kuphunzitsa anthu m’zilankhulo zambiri ndipo mabuku athu akupezeka m’zilankhulo zoposa 700. Chingelezi chimagwiritsidwa ntchito kwambiri pa nkhani zamalonda komanso maphunziro, ngati mmene zinalili ndi Chigiriki m’nthawi ya atumwi. Choncho mabuku athu amalembedwa m’Chingelezi ndipo kenako amamasuliridwa m’zilankhulo zina.

16, 17. a) Kodi anthu a Mulungu ankafunika Baibulo lotani? (b) Kodi panakonzedwa zotani kuti Baibulo lotereli lipezeke? (c) Kodi M’bale Knorr ankafuna kuti Baibuloli lidzathandize bwanji anthu?

16 Mfundo za m’mabuku athu zimachokera m’Baibulo. Poyamba anthu a Mulungu olankhula Chingelezi ankagwiritsa ntchito Baibulo la King James lomwe linatulutsidwa mu 1611. Komabe Chingelezi chake ndi chakale komanso chovuta. Vuto lina ndi lakuti m’Baibuloli dzina la Mulungu limangopezeka mwapatalipatali, pomwe m’Mabaibulo akalekale dzinali linkapezeka kambirimbiri. M’Baibuloli mulinso zinthu zina zolakwika komanso mavesi ena omwe sapezeka m’Mabaibulo akale. Mabaibulo ena achingelezi amene ankapezeka pa nthawiyo analinso ndi mavuto ambiri.

17 Choncho anthu a Mulungu ankafunika Baibulo lomasuliridwa molondola komanso losavuta kumva. Ndiyeno panakonzedwa komiti yoti imasulire Baibulo la Dziko Latsopano. Mbali yoyamba ya Baibuloli inatulutsidwa mu 1950, ndipo yomaliza inatulutsidwa mu 1960. Potulutsa mbali yoyamba ya Baibuloli pa msonkhano wa pa 2 August, 1950, M’bale Knorr anati: “Panopa tikuona kuti tikufunikira kwambiri Baibulo la m’chilankhulo chamakono lomasuliridwa mogwirizana ndi mfundo zoona za m’Baibulo. Komanso liyenera kukhala logwirizana ndi Baibulo loyambirira kuti lizitithandiza kuphunzira mfundo zina zoona. Liyeneranso kukhala losavuta kuwerenga ngati mmene zinalili ndi mabuku a m’Baibulo amene ophunzira a Khristu analemba. Mabukuwa anali osavuta kuwerenga ngakhale kwa anthu wamba.” M’bale Knorr ankafunitsitsa kuti Baibuloli lithandize anthu mamiliyoni ambiri kudziwa za Mulungu.

18. N’chiyani chathandiza kuti Baibulo limasuliridwe m’zilankhulo zambiri?

18 Zimene M’bale Knorr ankafuna zinayamba kuchitika mu 1963 pamene Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Achigiriki linatulutsidwa m’Chidatchi, Chifulenchi, Chijeremani, Chipwitikizi, Chisipanishi ndi m’Chitaliyana. Mu 1989, Bungwe Lolamulira linakhazikitsa dipatimenti kulikulu lathu yoti iziyang’anira ntchito yomasulira Baibulo. Kenako mu 2005, Bungwe Lolamulira linavomereza kuti Baibulo limasuliridwe m’zilankhulo zonse zomwe Nsanja ya Olonda imamasuliridwa. Chifukwa cha zimenezi, panopa Baibulo la Dziko Latsopano lonse kapena mabuku ake ena akupezeka m’zilankhulo zoposa 130.

19. a) N’chifukwa chiyani tinganene kuti chaka cha 2013 chinali chapadera? (b) Kodi tidzakambirana chiyani m’nkhani yotsatira?

19 Kuchokera nthawi imene Baibulo la Dziko Latsopano loyamba linatuluka, Chingelezi chasintha. Choncho Baibuloli linafunika kukonzedwanso. Ndiyeno pa msonkhano wapachaka wa nambala 129, womwe unachitika pa 5 ndi pa 6 October, 2013, Bungwe Lolamulira linatulutsa Baibulo la Dziko Latsopano lokonzedwanso m’Chingelezi. Anthu okwana 1,413,676 anamvetsera msonkhanowu m’mayiko 31. Ena mwa anthuwa anamvetsera msonkhanowu kudzera pa Intaneti. Anthu anasangalala kwambiri atalandira Baibuloli moti ena anagwetsa misozi. Pamene abale okamba nkhani pa msonkhanowu ankawerenga malemba m’Baibulo latsopanoli, anthu ambiri anaona kuti Chingelezi chake n’chomveka bwino kwambiri kuposa kale. M’nkhani yotsatira tidzakambirana zambiri zokhudza Baibuloli komanso zimene zikuchitika polimasulira m’zilankhulo zina.

^ ndime 6 Dzina la Baibuloli limatanthauza 70 ndipo ena amaganiza kuti linamasuliridwa ndi anthu 72. Zikuoneka kuti Baibuloli linayamba kumasuliridwa ku Iguputo pafupifupi zaka 300 Yesu asanabadwe ndipo n’kutheka kuti linamalizidwa patapita zaka 150. Baibulo limeneli ndi lofunikabe masiku ano chifukwa limathandiza akatswiri a Baibulo kumvetsa tanthauzo la mawu kapena mavesi ena a m’Malemba Achiheberi.

^ ndime 8 Anthu ena amaganiza kuti Mateyu analemba buku lake m’Chiheberi ndipo kenako iyeyo kapena anthu ena analimasulira m’Chigiriki.

^ ndime 13 Onani kabuku kakuti, Buku la Anthu Onse pamutu wakuti, “Kodi Bukulo Linapulumuka Bwanji?” kapena Baibulo la Dziko Latsopano lachingelezi limene linakonzedwanso, pa Zakumapeto A3.