Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Tizisankha Mwanzeru Anthu Ocheza Nawo M’masiku Otsiriza Ano

Tizisankha Mwanzeru Anthu Ocheza Nawo M’masiku Otsiriza Ano

“Kugwirizana ndi anthu oipa kumawononga makhalidwe abwino.” 1 AKOR. 15:33.

NYIMBO: 73, 119

1. Kodi tikukhala m’nthawi yotani?

TIKUKHALA m’masiku ovuta kusiyana ndi kale lonse. Zinthu zinayamba kuvuta kwambiri mu 1914 ndipo Baibulo limanena kuti amenewa ndi “masiku otsiriza.” (2 Tim. 3:1-5) Zinthu zipitirira kuipa chifukwa Baibulo linalosera kuti “anthu oipa ndi onyenga adzaipiraipirabe.”—2 Tim. 3:13.

2. Kodi anthu akukonda zosangalatsa zotani masiku ano? (Onani chithunzi pamwambapa.)

2 Anthu ambiri m’dzikoli amasangalala ndi zinthu zimene Baibulo limaletsa. Mwachitsanzo, amakonda zosangalatsa zokhudza chiwawa, chiwerewere ndiponso matsenga. Zosangalatsa zoipazi zimapezeka pa Intaneti, pa TV, m’mafilimu, m’mabuku ndiponso m’magazini. Masiku ano, makhalidwe omwe kale ankaoneka kuti ndi oipa akuvomerezedwa m’mayiko ena. Koma Yehova sasintha n’kuyamba kuvomereza makhalidwewa.—Werengani Aroma 1:28-32.

3. Kodi anthu a m’dzikoli amaona bwanji atumiki a Mulungu?

 3 Akhristu oyambirira ankakana kuchita zosangalatsa zoipa ndipo khalidwe lawo labwino linkachititsa kuti azizunzidwa. M’pake kuti mtumwi Petulo anati: “Chifukwa chakuti simukupitiriza kuthamanga nawo limodzi m’chithaphwi cha makhalidwe oipa, anthu a m’dzikoli sakumvetsa, choncho amakunyozani.” (1 Pet. 4:4) Masiku anonso anthu amaona kuti ife timasiyana nawo kwambiri ndipo amatinyoza. Paja Baibulo limati: “Onse ofuna kukhala ndi moyo wodzipereka kwa Mulungu mwa Khristu Yesu, nawonso adzazunzidwa.”—2 Tim. 3:12.

“KUGWIRIZANA NDI ANTHU OIPA KUMAWONONGA MAKHALIDWE ABWINO”

4. Kodi Baibulo limatipatsa malangizo ati okhudza dzikoli?

4 Anthu amene akufuna kusangalatsa Mulungu sayenera kukonda dziko kapena zinthu za m’dziko. (Werengani 1 Yohane 2:15, 16.) Baibulo limanena kuti Satana Mdyerekezi ndi “mulungu wa nthawi ino” ndipo ndi amene akulamulira dzikoli. Iye amasocheretsa anthu pogwiritsa ntchito zipembedzo, ndale ndiponso malonda. (2 Akor. 4:4; 1 Yoh. 5:19) Choncho Akhristu ayenera kusankha bwino anthu ocheza nawo. Paja Baibulo limanena mosapita m’mbali kuti: “Musasocheretsedwe. Kugwirizana ndi anthu oipa kumawononga makhalidwe abwino.”—1 Akor. 15:33.

5, 6. Kodi tiyenera kupewa kucheza ndi anthu ati? Perekani chifukwa.

5 Tiyenera kupewa kucheza ndi anthu oipa n’cholinga choti makhalidwe athu abwino asawonongeke. Apa tikutanthauza anthu omwe salambira Mulungu ndiponso anthu amene tili nawo mumpingo koma amachitanso zoipa. Si bwino kuchezanso ndi anthu amene amati ndi Akhristu koma amachita machimo akuluakulu ndipo salapa.—Aroma 16:17, 18.

6 Vuto locheza ndi anthu osamvera malamulo a Mulungu ndi lakuti nafenso timayamba khalidwe lawo loipa n’cholinga choti tikakhala nawo tisamanyozeke. Mwachitsanzo, kuzolowerana ndi anthu achiwerewere kungachititse kuti nafenso tiyambe chiwerewerecho. Akhristu ena zawachitikirapo ndipo anachotsedwa mumpingo chifukwa sanalape. (1 Akor. 5:11-13) Ngati Mkhristu wachita tchimo lalikulu koma osalapa amafanana ndi anthu amene Petulo anawatchula pa 2 Petulo 2:20-22.—Werengani.

7. Kodi tiyenera kugwirizana ndi anthu ati?

7 N’zoona kuti timafuna kukomera mtima anthu ngakhale amene satsatira malamulo a Mulungu koma tiyenera kupewa kugwirizana nawo kwambiri. Choncho n’kulakwa kuti m’bale kapena mlongo akhale pa chibwenzi ndi munthu amene sanadzipereke kwa Mulungu ndipo satsatira mfundo zake. Tiyenera kugwirizana ndi anthu amene amachita zofuna za Mulungu. Paja Yesu anati: “Aliyense wochita chifuniro cha Mulungu, ameneyo ndiye m’bale wanga, mlongo wanga ndi mayi anga.”—Maliko 3:35.

8. N’chiyani chinachitikira Aisiraeli chifukwa chogwirizana ndi anthu oipa?

8 Kugwirizana ndi anthu oipa kumabweretsa mavuto aakulu. Umboni wake ndi zimene zinachitikira Aisiraeli. Yehova anawapulumutsa ku Iguputo n’kuwatsogolera popita ku Dziko Lolonjezedwa. Ndiyeno anawauza zoyenera kuchita akafika m’dzikolo. Anati: ‘Musaweramire milungu yawo kapena kuitumikira, ndipo musapange chilichonse chofanana ndi zifaniziro zawo, koma muzigwetse ndithu ndi kuphwanya zipilala  zawo zopatulika. Muzitumikira Yehova Mulungu wanu.’ (Eks. 23:24, 25) Koma Aisiraeli ambiri sanamvere malangizo a Mulungu. (Sal. 106:35-39) Iwo sanakhulupirike kwa Mulungu ndipo pa nthawi ina Yesu anawauza kuti: “Tsopano tamverani! Mulungu wachoka n’kukusiyirani nyumba yanuyi.” (Mat. 23:38) Yehova anakana Aisiraeli n’kuyamba kudalitsa mpingo wachikhristu.—Mac. 2:1-4.

TIZISANKHA MWANZERU ZIMENE TIMAWERENGA NDI KUONERA

9. N’chifukwa chiyani tiyenera kusamala posankha zimene timawerenga ndi kuonera?

9 Zinthu zambiri m’dzikoli zimene anthu angawerenge kapena kuonera ndi zoipa. Siziwathandiza kukhulupirira Yehova ndiponso malonjezo ake. Koma zimawalimbikitsa kukhala ndi maganizo ndiponso zolinga zogwirizana ndi dziko loipali. Choncho tiyenera kusamala kwambiri kuti tisamawerenge kapena kuonera zinthu zolimbikitsa “zilakolako za dziko.”—Tito 2:12.

10. Kodi n’chiyani chidzachitikire zinthu zoipa zimene anthu amawerenga ndiponso kuonera?

10 Posachedwapa dziko la Satanali lidzawonongedwa ndipo zinthu zoipa sizidzapezekanso. Paja Malemba amati: “Dziko likupita limodzi ndi chilakolako chake, koma wochita chifuniro cha Mulungu adzakhala kosatha.” (1 Yoh. 2:17) Amanenanso kuti: “Pakuti ochita zoipa adzaphedwa. Koma oyembekezera Yehova ndi amene adzalandire dziko lapansi. Koma anthu ofatsa adzalandira dziko lapansi, ndipo adzasangalala ndi mtendere wochuluka.” Ndiyeno kodi adzasangalala kwa nthawi yaitali bwanji? Baibulo limati: “Olungama adzalandira dziko lapansi, ndipo adzakhala mmenemo kwamuyaya.”—Sal. 37:9, 11, 29.

11. Kodi Yehova akuphunzitsa bwanji anthu ake kuti akhale naye pa ubwenzi?

11 Mosiyana ndi dzikoli, gulu la Yehova limatulutsa mabuku ndiponso mavidiyo amene angathandize anthu kuti adzapeze moyo wosatha. Yesu anapemphera kwa Yehova kuti: “Moyo wosatha adzaupeza akamaphunzira ndi kudziwa za inu, Mulungu yekhayo amene ali woona, ndi za Yesu Khristu, amene inu munamutuma.” (Yoh. 17:3) Yehova akugwiritsa ntchito gulu lake pothandiza anthu kuti akhale naye pa ubwenzi. Ifetu tili ndi mwayi waukulu wophunzira za Yehova pogwiritsa ntchito magazini, mabuku, mavidiyo ndiponso zinthu za pa webusaiti yathu. Gulu la Yehova limakonzanso misonkhano m’mipingo yoposa 110,000 padziko lonse. Pa misonkhano yampingo ndiponso ikuluikulu timaphunzira mfundo za m’Baibulo zomwe zimatithandiza kukhulupirira kwambiri Yehova ndiponso malonjezo ake.—Aheb. 10:24, 25.

TIYENERA KUKWATIRA NDIPONSO KUKWATIWA “MWA AMBUYE”

12. Kodi malangizo oti tiyenera kukwatira kapena kukwatiwa “mwa Ambuye” amatanthauza chiyani?

12 Anthu amene akufuna kukwatira kapena kukwatiwa ayeneranso kusankha bwino. Paja Mawu a Mulungu amanena mosapita m’mbali kuti: “Musamangidwe m’goli ndi osakhulupirira, chifukwa ndinu osiyana. Pali ubale wotani pakati pa chilungamo ndi kusamvera malamulo? Kapena pali kugwirizana kotani pakati pa kuwala ndi mdima?” (2 Akor. 6:14) Baibulo limalimbikitsa Akhristu amene akufuna kukwatira kapena kukwatiwa kuti azichita zimenezi “mwa Ambuye.” Izi zikutanthauza kuti ayenera kukwatirana ndi munthu wobatizidwa amene amatsatira mfundo  za m’Baibulo. (1 Akor. 7:39) Mkhristu akatsatira malangizo amenewa amasankha munthu amene angagwirizane naye ndiponso kuthandizana polambira Yehova mokhulupirika.

13. Kodi Yehova anapatsa Aisiraeli malangizo ati okhudza ukwati?

13 Yehova amadziwa zinthu zimene zingathandize kwambiri atumiki ake ndipo malangizo amene amapereka pa nkhani ya ukwati sasintha. Kumbukirani zimene analangiza Mose kuti auze Aisiraeli zokhudza anthu a mitundu ina amene sankamulambira. Iye anati: “Usadzachite nawo mgwirizano wa ukwati. Usadzapereke ana ako aakazi kwa ana awo aamuna ndipo usadzatenge ana awo aakazi ndi kuwapereka kwa ana ako aamuna. Pakuti adzapatutsa ana ako aamuna kuti asanditsatire ndipo adzatumikira ndithu milungu ina. Pamenepo mkwiyo wa Yehova udzakuyakirani ndipo adzakuwonongani ndithu mofulumira.”—Deut. 7:3, 4.

14, 15. Kodi chinachitika n’chiyani Solomo atanyalanyaza malangizo a Yehova?

14 Chitsanzo pa nkhaniyi ndi Mfumu Solomo. Iye ali wachinyamata anapempha Mulungu kuti amupatse nzeru ndipo anapatsidwadi nzeru zambiri. Anthu m’mayiko osiyanasiyana ankadziwa zoti Solomo ndi Mfumu yanzeru ya dziko lotukuka. Mfumukazi ya ku Sheba itafika kwa Solomo inati: “Sindinakhulupirire mawuwo mpaka pamene ndabwera n’kuona ndi maso anga, ndipo ndaona kuti ndinangouzidwa hafu chabe. Nzeru zanu ndi ulemerero wanu zaposa zinthu zimene ndinamva.” (1 Maf. 10:7) Koma kenako Solomo anasokoneza zinthu kwambiri pamene ananyalanyaza lamulo la Yehova loti asakwatire akazi a mitundu ina.—Mlal. 4:13.

15 Ngakhale kuti Yehova anamuchitira zambiri, iye anakwatira akazi ambiri a mitundu ina amene sankalambira Yehova. Baibulo limati iye anayamba kukonda akazi ambirimbiri achilendo moti anakwatira akazi 700 ndipo anali ndi akazi apambali okwana 300. Zotsatira zake zinali zoti atakalamba, “akazi ake anali atapotoza mtima wake moti iye anali kutsatira milungu ina. . . . Solomo anayamba kuchita zinthu zimene zinali zoipa m’maso mwa Yehova.” (1 Maf. 11:1-6) Akaziwo anachititsa Solomo kuti ayambe kuchita zinthu mopanda nzeru n’kusiya kutumikira Mulungu mokhulupirika. Choncho Akhristu amene akufuna kukwatirana ndi munthu wosalambira Yehova ayenera kuiganizira bwino nkhaniyi.

16. Kodi Mkhristu amene wayamba kutumikira Yehova atakwatirana kale ndi munthu wosalambira Yehova ayenera kutsatira malangizo ati?

16 Koma bwanji ngati munthu wayamba kutumikira Yehova atakwatirana kale ndi munthu wosalambira Yehova? Baibulo limati: “Inu akazi, muzigonjera amuna anu kuti ngati ali osamvera mawu akopeke, osati ndi mawu, koma ndi khalidwe lanu.” (1 Pet. 3:1) N’zoona kuti malangizowa ndi opita kwa akazi koma amathandizanso mwamuna amene wayamba kutumikira Yehova atakwatira mkazi wosalambira Yehova. Apa mfundo ndi yakuti tiziyesetsa kukhala mwamuna kapena mkazi wabwino n’kumatsatira malangizo a Mulungu onena za ukwati. Pali anthu ambiri amene ayamba kutumikira Yehova ataona kuti mwamuna kapena mkazi wawo wayamba kuchita bwino chifukwa chotsatira mfundo za m’Malemba.

TIZIGWIRIZANA NDI ANTHU AMENE AMAKONDA YEHOVA

17, 18. N’chifukwa chiyani Nowa ndiponso Akhristu oyambirira anapulumuka?

17 Kugwirizana ndi anthu oipa kumawononga makhalidwe abwino koma kugwirizana  ndi anthu abwino kumatithandiza. M’nthawi ya Nowa, anthu ambiri anali oipa ndipo iye sankafuna kugwirizana nawo. Pa nthawiyo, “Yehova anaona kuti kuipa kwa anthu kwachuluka padziko lapansi, ndipo malingaliro onse a m’mitima ya anthu anali oipa okhaokha nthawi zonse.” (Gen. 6:5) Choncho Mulungu anasankha kubweretsa chigumula kuti awononge anthu oipawo. Koma “Nowa anali munthu wolungama. Iye anali wopanda cholakwa pakati pa anthu a m’nthawi yake. Nowa anayenda ndi Mulungu woona.”—Gen. 6:7-9.

18 Nowa sankafuna kucheza ndi anthu osaopa Mulungu. Iye ndi banja lake lonse ankagwira ntchito zimene Mulungu anawapatsa monga kumanga chingalawa. Nowa analinso “mlaliki wa chilungamo.” (2 Pet. 2:5) Iye ankalalikira, kumanga chingalawa ndiponso kucheza ndi banja lake. Zonsezi zinkamuthandiza kuti azisangalatsa Mulungu. Chifukwa cha zimenezi, Nowa ndi banja lake anapulumuka. Tiyenera kuyamikira kwambiri zimene iwo anachita chifukwa pakanapanda iwowo sitikanabadwa. Nawonso Akhristu oyambirira amene ankamvera Mulungu sankagwirizana ndi anthu oipa ndipo anapulumuka pamene Yerusalemu anawonongedwa mu 70 C.E.—Luka 21:20-22.

Tikamacheza ndi Akhristu anzathu timakonzekera moyo wa m’dziko latsopano (Onani ndime 19)

19. Kodi tiyenera kuchita chiyani kuti tisangalatse Mulungu?

19 Ifenso tiyenera kutsanzira Nowa, banja lake ndiponso Akhristu oyambirira amene ankamvera Mulungu. Sitiyenera kugwirizana ndi anthu oipa m’dzikoli koma tiyenera kugwirizana ndi abale ndi alongo okhulupirika amene angatilimbikitse. Kugwirizana ndi anthu amene amatsogoleredwa ndi nzeru za Mulungu kudzatithandiza kukhala ndi chikhulupiriro cholimba m’masiku ovutawa. (1 Akor. 16:13; Miy. 13:20) Tikamasankha bwino anthu ocheza nawo m’masiku otsiriza ano tikhoza kukhala ndi mwayi waukulu wopulumuka n’kulowa m’dziko latsopano limene lili pafupi kwambiri.