Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Tisalole Chilichonse Kutisokoneza Potumikira Yehova

Tisalole Chilichonse Kutisokoneza Potumikira Yehova

‘Mariya ankamvetsera mawu a Yesu koma Marita anatanganidwa ndi ntchito zochuluka.’—LUKA 10:39, 40.

NYIMBO: 94, 134

1, 2. Kodi n’chifukwa chiyani Yesu ankakonda Marita, nanga n’chiyani chikusonyeza kuti Maritayo sanali wangwiro?

KODI n’chiyani chimabwera m’maganizo mwanu mukamva za Marita? Baibulo limanena kuti Yesu ankakonda Marita. Koma sikuti ndi mayi yekhayu amene Yesu ankagwirizana naye. Iye ankakonda ndiponso kulemekeza azimayi ena monga amayi ake komanso Mariya yemwe anali mchemwali wake wa Marita. (Yoh. 11:5; 19:25-27) Koma kodi n’chifukwa chiyani Yesu ankakonda Marita?

2 Iye ankamukonda kwambiri chifukwa chakuti ankalandira bwino alendo, anali wakhama komanso ankakonda kwambiri Mulungu. Marita ankakhulupirira kwambiri zimene Yesu ankaphunzitsa ndipo sankakayikira kuti Yesu ndi Mesiya wolonjezedwa. (Yoh. 11:21-27) Koma Marita sanali wangwiro ndipo ankalakwitsa zinthu zina. Tsiku lina Yesu atapita kunyumba kwawo, Marita anakhumudwa ndi zimene Mariya anachita ndipo anauza  Yesu kuti: “Ambuye, kodi sizikukukhudzani kuti m’bale wangayu wandilekerera ndekha ntchito? Tamuuzani kuti andithandize.” (Werengani Luka 10:38-42.) Kodi tingaphunzire chiyani pa zimene zinachitikazi?

MARITA ANATANGANIDWA

3, 4. (a) N’chifukwa chiyani Yesu ananena kuti Mariya anasankha “chinthu chabwino”? (Onani chithunzi patsamba 18.) (b) Kodi Yesu anathandiza bwanji Marita?

3 Yesu anayamikira kwambiri kuti Marita ndi Mariya anamulandira bwino ndipo anayamba kuwaphunzitsa zinthu zokhudza Mulungu. Mariya “anakhala pansi pafupi ndi Ambuye n’kumamvetsera mawu awo.” Yesu ayenera kuti akanayamikira Marita ngati akanakhalaponso n’kumamumvetsera.

4 Koma m’malomwake, Marita anatanganidwa ndi kukonza chakudya ndiponso kuchita zinthu zina n’cholinga choti Yesu asangalale. Ndiyeno ataona kuti Mariya sakumuthandiza anayamba kudandaula. Yesu anaona kuti Marita akukonza zinthu zambiri ndipo anamuuza mokoma mtima kuti: “Marita, Marita, ukuda nkhawa ndiponso kutanganidwa ndi zinthu zambiri.” Kenako anamuuza kuti akhoza kungokonza zinthu zochepa kuti adye. Atatero, anayamikira Mariya ponena kuti: “Mariya wasankha chinthu chabwino kwambiri, ndipo sadzalandidwa chinthu chimenechi.” N’kutheka kuti Mariya akanaiwala mwamsanga zimene anadya tsikulo koma sakanaiwala mpaka kalekale zimene Yesu ananena pomuyamikira komanso zimene anamuphunzitsa. Zikuonekanso kuti Marita anamvera malangizo a Yesu ndipo ankayesetsa kutumikira Yehova mokhulupirika pa moyo wake wonse. Tikutero chifukwa chakuti patapita zaka zoposa 60, mtumwi Yohane ananena kuti: “Yesu anali kukonda onsewa, Marita ndi m’bale wake.”—Yoh. 11:5.

5. (a) N’chifukwa chiyani tiyenera kusamala kwambiri masiku ano kuti tisasokonezedwe? (b) Kodi tikambirana funso liti?

5 Kodi nanga masiku ano palinso zinthu zimene zingatisokoneze? Nsanja ya Olonda ya September 15, 1958 inalimbikitsa Akhristu kuti asalole kuti azisokonezedwa ndi zinthu zamakono akamatumikira Yehova. Pa nthawiyo, zinthu zatsopano zinkatuluka tsiku lililonse ngati mmenenso zilili masiku ano. Kunali zinthu zambiri monga magazini, mawailesi, mafilimu ndi ma TV. Nsanja ya Olonda imeneyo inanenanso kuti mapeto akamayandikira “zinthu zimene zingatisokoneze zizichulukirachulukira.” Zimenezi ndi zoonadi chifukwa masiku ano pali zinthu zambiri zimene zingatisokoneze. Ndiyeno funso n’kumati: Kodi tingatani kuti tikhale ngati Mariya n’kumapewa kusokonezedwa potumikira Yehova?

TISAMASOKONEZEDWE NDI ZINTHU ZA M’DZIKOLI

6. N’chiyani chikusonyeza kuti anthu a Yehova amagwiritsa ntchito bwino zinthu zamakono polalikira?

6 Anthu a Yehova amayesetsa kugwiritsa ntchito zinthu zamakono polalikira uthenga wabwino. Mwachitsanzo, nkhondo yoyamba ya padziko lonse isanayambe komanso ili mkati, ankaonetsa filimu yotchedwa “Sewero la Pakanema la Chilengedwe.” Anthu ambiri analimbikitsidwa ndi filimuyi chifukwa chakuti kumapeto kwake inkasonyeza kuti mu Ulamuliro wa Zaka 1,000 wa Yesu mudzakhala mtendere wochuluka. Kenako uthenga wa Ufumu unayamba kulalikidwa pa wailesi ndipo anthu ambiri padzikoli ankaumva. Masiku anonso, anthu a Yehova amagwiritsa ntchito makompyuta ndi Intaneti kuti uthenga wabwino ufike paliponse ngakhale m’madera akutali kwambiri.

Tisamalole kuti zinthu zosafunika zisokoneze utumiki wathu (Onani ndime 7)

7. (a) Kodi chingachitike n’chiyani ngati timagwiritsa ntchito kwambiri zinthu za m’dzikoli? (b) Kodi tiyenera kusamala kwambiri ndi chiyani? (Onani mawu am’munsi.)

 7 Baibulo limatichenjeza kuti sitiyenera kugwiritsa ntchito kwambiri zinthu za m’dzikoli. (Werengani 1 Akorinto 7:29-31.) Pali zinthu zina zomwe si zolakwika koma zikhoza kuchititsa Mkhristu kutaya nthawi yambiri. Mwachitsanzo, ena amakonda kuchita zinthu zosangalatsa monga kuwerenga mabuku, kuonera TV, kupita koyenda, kuyendayenda m’mashopu ndiponso kusakasaka zipangizo zamakono. Ena amangokhalira kucheza pa Intaneti kapena kutumizirana mauthenga, pomwe ena amatanganidwa kufufuza nkhani zatsopano kapena zotsatira za masewera enaake. * (Mlal. 3:1, 6) Kupanda kusamala, zinthu zosafunika kwenikweni zikhoza kutilepheretsa kuchita zinthu zofunika kwambiri zokhudza kulambira Mulungu.—Werengani Aefeso 5:15-17.

8. N’chifukwa chiyani sitiyenera kukonda kwambiri zinthu za m’dzikoli?

8 Satana amagwiritsa ntchito zinthu za m’dzikoli pofuna kutikopa ndiponso kutisokoneza. Zimenezi zinkachitika m’nthawi ya atumwi koma zikuchitika kwambiri masiku ano. (2 Tim. 4:10) Choncho tiyenera kutsatira malangizo akuti: “Musamakonde . . . zinthu za m’dziko.” Tikamayesetsa nthawi zonse kutsatira malangizo amenewa, sitingasokonezedwe ndipo tizikonda kwambiri Mulungu. Izi zidzatithandiza kuchita chifuniro cha Mulungu n’kupitiriza kukhala naye pa ubwenzi wolimba.—1 Yoh. 2:15-17.

DISO LANU LIZILUNJIKA PA CHINTHU CHIMODZI

9. Kodi Yesu anauza ophunzira ake kuti azichita chiyani ndipo iye anapereka chitsanzo chotani pa nkhaniyi?

9 Malangizo achikondi amene Yesu anauza Marita anali ogwirizana kwambiri ndi zimene iye ankachita komanso kuphunzitsa. Mwachitsanzo, iye anauza ophunzira ake kuti diso lawo lizilunjika pa chinthu chimodzi n’cholinga choti azitumikira Yehova popanda kusokonezedwa. (Werengani Mateyu 6:22, 33.) Yesu sankatanganidwa ndi zinthu zambiri. Paja iye analibe nyumba kapena malo.—Luka 9:58; 19:33-35.

10. Kodi Yesu anapereka chitsanzo chotani?

 10 Yesu sankalola chilichonse kumusokoneza pa ntchito yolalikira. Mwachitsanzo, atangoyamba ntchito yake anaphunzitsa anthu ambiri komanso kuchita zozizwitsa ku Kaperenao. Ndiyeno anthu a mumzindawo anamuuza kuti asachoke. Koma iye anayankha kuti: “Ndiyenera kukalengeza uthenga wabwino wa ufumu wa Mulungu kumizinda inanso, chifukwa ndi zimene anandituma kudzachita.” (Luka 4:42-44) Yesu ankayenda mitunda italiitali kukalalikira ndi kuphunzitsa uthenga wabwino kwa anthu ambiri ku Palesitina. Ngakhale kuti anali wangwiro, nthawi zina ankatopa ndipo ankafuna kupuma chifukwa chogwira kwambiri ntchito yolalikira.—Luka 8:23; Yoh. 4:6.

11. (a) Kodi Yesu anayankha bwanji munthu amene anadandaula za m’bale wake? (b) Kodi Yesu anachenjeza anthu kuti apewe chiyani?

11 Tsiku lina Yesu akuphunzitsa zimene ophunzira ake angachite akamatsutsidwa, munthu wina anamudula mawu n’kunena kuti: “Mphunzitsi, mundiuzireko m’bale wanga kuti andigawireko cholowa.” Koma Yesu sanalole kuti nkhani yawoyi imusokoneze ndipo anamuyankha kuti: “Munthu iwe, ndani anandiika ine kukhala woweruza kapena wogawa chuma chanu?” Atatero, Yesu anapitiriza kuphunzitsa anthuwo ndipo anawachenjeza kuti sayenera kulola mtima wofuna zinthu zambiri kuwasokoneza potumikira Mulungu.—Luka 12:13-15.

12, 13. (a) N’chifukwa chiyani Agiriki ena ankafuna kukumana ndi Yesu? (b) Kodi Yesu anachita chiyani kuti asasokonezedwe?

12 Kutangotsala masiku ochepa kuti aphedwe, Yesu anali ndi nkhawa. (Mat. 26:38; Yoh. 12:27) Iye ankayembekezera kuzengedwa mlandu wochititsa manyazi komanso kuphedwa mwankhanza. Koma ankadziwanso kuti anali ndi ntchito yambiri yoti agwire asanaphedwe. Chitsanzo ndi zimene zinachitika Lamlungu pa Nisani 9 mu 33 C.E. Mogwirizana ndi ulosi, Yesu analowa mumzinda wa Yerusalemu atakwera bulu ndipo khamu la anthu linayamba kumutamanda kuti iye wabwera “monga Mfumu m’dzina la Yehova.” (Luka 19:38) Tsiku lotsatira, Yesu analowa m’kachisi n’kuthamangitsa anthu amene ankachita malonda n’kumadyera masuku pamutu Ayuda anzawo.—Luka 19:45, 46.

13 Anthu ena amene anabwera kudzachita nawo Pasika ku Yerusalemu anali Agiriki ndipo anachita chidwi ndi zimene Yesu anachita. Iwo anapempha Filipo kuti akonze zoti adzakumane ndi Yesu. Koma Yesu sanalole zimenezo podziwa kuti pali zinthu zofunika kwambiri zimene ankayenera kuchita. Iye sankafuna kusangalatsa anthu n’cholinga choti adzamuteteze pa nthawi imene adani a Mulungu azidzafuna kumupha. Choncho Yesu anakumbutsa ophunzira ake kuti watsala pang’ono kuphedwa ndipo anati: “Aliyense wokonda moyo wake akuuwononga, koma wodana ndi moyo wake m’dziko lino akuusungira moyo wosatha.” M’malo mopita kukakumana ndi Agirikiwo, iye analimbikitsa ophunzira ake kuti azimutsanzira ndipo anati: “Aliyense wonditumikira ine, Atate adzamulemekeza.” Filipo ayenera kuti anakauza Agirikiwo mawu olimbikitsawa.—Yoh. 12:20-26.

14. Perekani zitsanzo zosonyeza kuti Yesu ankapezanso nthawi yochita zinthu zina.

14 N’zoona kuti Yesu sankafuna kusokonezedwa pa ntchito yolalikira koma ankapezanso nthawi yochita zinthu zina. Mwachitsanzo, iye anapita ku ukwati wina ndipo anasandutsa madzi kukhala vinyo n’cholinga choti anthu asangalale. (Yoh. 2:2, 6-10) Ankapitanso kukacheza ndiponso kukadya kunyumba kwa anzake komanso kwa anthu  ena amene ankafuna kuphunzira. (Luka 5:29; Yoh. 12:2) Koma chofunika kwambiri n’chakuti iye ankapeza nthawi yopemphera, kusinkhasinkha komanso kupuma.—Mat. 14:23; Maliko 1:35; 6:31, 32.

“TIVULE CHOLEMERA CHILICHONSE”

15. Kodi Paulo anapereka malangizo otani ndipo iye anatsatira bwanji malangizowo?

15 Mtumwi Paulo anayerekezera Akhristu ndi anthu othamanga pa mpikisano ndipo analemba kuti: ‘Tiyeni tivule cholemera chilichonse.’ (Werengani Aheberi 12:1.) Paulo ankachita zinthu mogwirizana ndi zimene ananenazi. Mwachitsanzo, iye anali ndi mwayi wokhala mtsogoleri wachiyuda ndipo akanalemera komanso kutchuka. Koma anasiya zonsezi n’cholinga chakuti aike maganizo ake pa “zinthu zofunika kwambiri.” Ankalalikira mwakhama m’madera osiyanasiyana monga ku Siriya, Asia Minor, Makedoniya komanso ku Yudeya. Iye ankaganizira kwambiri mphoto imene adzalandire kumwamba, moti analemba kuti: “Ndikuiwala zinthu zakumbuyo ndipo ndikuyesetsa kuti ndikapeze zakutsogolo. Ndikuyesetsa kuchita zimenezi mpaka nditapeza mphoto.” (Afil. 1:10; 3:8, 13, 14) Paulo anali wosakwatira ndipo zimenezi zinamuthandiza kuti azitumikira “Ambuye nthawi zonse popanda chododometsa.”—1 Akor. 7:32-35.

16, 17. Kaya tili pa banja kapena ayi, kodi tingatsatire bwanji chitsanzo cha Paulo? Perekani chitsanzo.

16 Mofanana ndi Paulo, Akhristu ena amasankha kuti asakhale pa banja n’cholinga choti akhale ndi nthawi yambiri yotumikira Yehova. (Mat. 19:11, 12) Atumiki a Yehova amene ali pa banja amakhala ndi maudindo ambiri osamalira banjalo. Komabe kaya tili pa banja kapena ayi, tonsefe tikhoza ‘kuvula cholemera chilichonse’ chimene chingatisokoneze potumikira Yehova. Kuti zimenezi zitheke, tiyenera kupewa zinthu zimene zingatiwonongere nthawi n’cholinga choti tizichita zambiri mu utumiki.

17 Chitsanzo pa nkhaniyi ndi m’bale wina wa ku Wales dzina lake Mark ndi mkazi wake dzina lake Claire. Iwo anayamba upainiya atangomaliza sukulu ndipo atakwatirana anapitiriza upainiyawo. Mark ananena kuti: “Tinachoka m’nyumba yathu ya zipinda zitatu komanso tinasiya ntchito n’cholinga choti tikathandize pa ntchito ya zomangamanga kumayiko ena.” Pa zaka 20 zapitazi, iwo akhala akuthandiza pomanga Nyumba za Ufumu ku Africa. Ngakhale kuti iwo sapeza ndalama zambiri ngati mmene ankachitira kale, Yehova akuwasamalirabe. Claire anati: “Timakhala osangalala potumikira Yehova tsiku lililonse. Panopa tili ndi anzathu ambiri ndipo sitisowa chilichonse pa moyo wathu. Zimene tinasiya zija ndi zochepa tikaziyerekezera ndi moyo wosangalatsa umene tili nawo mu utumiki wa nthawi zonse.” Akhristu ambiri amene ali mu utumiki wa nthawi zonse angavomereze zimene mlongoyu ananena. *

18. Kodi tingachite bwino kudzifunsa mafunso ati?

18 Kodi nanunso mumaona kuti mukhoza kuwonjezera zimene mumachita mu utumiki? Kodi pali zinthu zina zimene muyenera kusintha kuti musamasokonezedwe potumikira Yehova? Kuchita khama powerenga Baibulo ndiponso kuliphunzira kungakuthandizeni kwambiri pa nkhaniyi. M’nkhani yotsatira tidzakambirana mmene tingachitire zimenezi.

^ ndime 7 Onani nkhani yakuti, “Munthu Wosadziwa Zinthu Amakhulupirira Mawu Alionse,” patsamba 30.

^ ndime 17 Onaninso mbiri ya moyo wa Hadyn ndi Melody Sanderson m’nkhani yakuti, “Kudziwa ndi Kuchita Chabwino” ya mu Nsanja ya Olonda ya March 1, 2006. Iwo anasiya bizinezi yawo ya ndalama zambiri ku Australia n’kuyamba utumiki wa nthawi zonse. Werengani zimene zinachitika ndalama zitawathera pamene ankachita umishonale ku India.