Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mukukumbukira?

Kodi Mukukumbukira?

Kodi mwawerenga mosamala magazini aposachedwapa a Nsanja ya Olonda? Tayesani kuyankha mafunso otsatirawa:

Kodi n’zoyenera kuti Akhristu azitentha mtembo?

Mkhristu aliyense ayenera kusankha yekha pa nkhaniyi. Ngakhale kuti Baibulo silifotokoza mwachindunji nkhani imeneyi, tiyenera kukumbukira kuti mtembo wa Mfumu Sauli komanso wa mwana wake Yonatani unatenthedwa kenako n’kuikidwa m’manda. (1 Sam. 31:2, 8-136/15, tsamba 7.

Kodi tikudziwa bwanji kuti Mulungu si amene amachititsa mavuto?

Njira zonse za Mulungu ndi zolungama ndipo iye ndi wokhulupirika komanso wowongoka. Iye ndi wachikondi ndi wachifundo. (Deut. 32:4; Sal. 145:17; Yak. 5:11)7/1, tsamba 4.

Kodi anthu amene amapita kukatumikira m’mayiko ena angakumane ndi mavuto ati?

Pali mavuto atatu awa: (1) Amavutika kuzolowera moyo watsopano, (2) amasowa achibale awo komanso (3) zinthu monga kaganizidwe ndi chilankhulo zimakhala zachilendo. Anthu amene amapirira n’kuthana ndi mavutowa amadalitsidwa kwambiri.7/15, tsamba 4-5.

N’chifukwa chiyani Yosefe ankadedwa ndi azichimwene ake?

Chifukwa china n’chakuti Yakobo ankakonda kwambiri Yosefe moti anamugulira mkanjo wapadera. Azichimwene ake ankamuchitira nsanje ndipo anamugulitsa n’kukakhala kapolo.8/1, tsamba 11-13.

N’chifukwa chiyani tinganene kuti timapepala tatsopano n’tabwino komanso tosavuta kugwiritsa ntchito?

Timapepalati anatipanga mofanana. Kalikonse kali ndi funso limene tingafunse. Kaya munthuyo ayankha bwanji, pali lemba limene tingamuwerengere. Kenako tikhoza kumusonyeza funso limene tingadzakambirane naye ulendo wotsatira.8/15, tsamba 13-14.

Kodi Baibulo lotchedwa Peshitta ndi liti?

Chisiriya chinali chinenero chimene chinkalankhulidwa kwambiri cha m’ma 100 kapena 200 C.E. ndipo ankachilemba m’zilembo za Chiaramu. Zikuoneka kuti mabuku ena a Malemba Achigiriki anayamba kumasuliridwa m’chilankhulochi ndipo Baibulo la Chisiriya linkatchedwa Peshitta.9/1, tsamba 13-14.

Kodi makolo achikhristu angasamalire bwanji ana awo?

Ayenera kuwamvetsera akamalankhula n’cholinga choti awadziwe bwino. Ayenera kuwadyetsa bwino pogwiritsa ntchito Mawu a Mulungu. Ayeneranso kuwatsogolera bwino. Mwachitsanzo, angawathandize kuti asamakayikire zinthu zimene akuphunzira.9/15, tsamba 18-21.

Kodi Ufumu wa Mulungu udzachotsa mavuto ati?

Udzachotsa matenda, imfa, kusowa ntchito, nkhondo, njala ndiponso umphawi.10/1, tsamba 6-7.

Kodi ndi pangano liti m’Baibulo limene linavomereza kuti anthu ena alamulire ndi Khristu?

Yesu atadya Pasika womaliza, anachita pangano ndi atumwi ake okhulupirika lomwe limatchedwa kuti pangano la Ufumu. (Luka 22:28-30) Panganoli linawatsimikizira kuti adzakalamulira ndi Yesu kumwamba.10/15, tsamba 16-17.

Perekani zitsanzo ziwiri za m’Baibulo zosonyeza kuti Satana alipodi.

Malemba amanena kuti Satana analankhula ndi Yesu pomuyesa. Pa nthawi ya Yobu, Satana analankhulanso ndi Mulungu. Zitsanzo ziwirizi zikusonyeza kuti Satana alipodi.11/1, tsamba 4-5.

Kodi “anthu odziwika ndi dzina lake” omwe Yakobo anatchula pa Machitidwe 15:14 ndi ndani?

Iwo ndi Ayuda komanso anthu a mitundu ina amene Mulungu anawasankha kuti ‘kuti alengeze makhalidwe abwino kwambiri a amene anawaitana.’ (1 Pet. 2:9, 10)11/15, tsamba 24-25.

Kodi mzinda wa Timgad unali kuti ndipo anthu ena a mumzindawu ankakhulupirira chiyani?

Mzindawu unali kumpoto kwa Africa (komwe panopa ndi ku Algeria). Unali waukulu ndipo unali m’manja mwa Aroma. Pamwala wina womwe anaufukula pamalo amene panali mzindawu pali mawu osonyeza zimene anthu ena ankakhulupirira. Mawu ake ndi akuti: “Kusaka, kusamba, kusewera ndiponso kuseka n’kumene kumachititsa kuti munthu akhale wosangalala.” Lemba la 1 Akorinto 15:32 limafotokoza maganizo ofanana ndi amenewa.12/1, tsamba 8-10.