Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YA PACHIKUTO | KODI MAPETO ALI PAFUPIDI?

Kodi N’chiyani Chidzachitike pa Nthawi ya “Mapeto”?

Kodi N’chiyani Chidzachitike pa Nthawi ya “Mapeto”?

Kodi mukamva mawu akuti, “mapeto” mumaganiza chiyani? Kodi mumaganiza kuti ndi nthawi yomwe Yesu adzabwere kudzatenga anthu abwino kupita nawo kumwamba koma anthu oipa n’kukawalanga kumoto? Kapena mumaganiza kuti Mulungu adzawotcha dzikoli ndi moto? Ena akaganizira zimenezi, amachita mantha kwambiri pomwe ena amaona kuti izi ndi nkhambakamwa chabe ndipo sizingachitike.

Komatu Baibulo limati: “Mapeto adzafika.” (Mateyu 24:14) Nthawi imeneyi imadziwikanso kuti, “tsiku lalikulu la Mulungu” komanso “Haramagedo.”(Chivumbulutso 16:14, 16) Anthu amakhulupirira zosiyanasiyana zokhudza zomwe zidzachitike pa nthawi yamapeto. Komatu Baibulo limafotokoza momveka bwino zomwe zidzachitike pa nthawiyi. Limatithandizanso kudziwa kuti mapeto ali pafupi. Limatiuzanso zomwe tingachite kuti tidzapulumuke pa nthawi yamapetoyo. Choyamba tiyeni tikambirane maganizo olakwika amene anthu amakhala nawo, okhudza zomwe zidzachitike pa nthawi yamapeto. Kenako tikambirananso zimene Baibulo limanena kuti n’zomwe zidzachitikedi pa nthawi imeneyo.

MAGANIZO OLAKWIKA OMWE ANTHU AMAKHALA NAWO ONENA ZA MAPETO

 1. DZIKO LONSE LIDZAWONONGEDWA NDI MOTO.

  Baibulo limati Mulungu ‘anakhazikitsa dziko lapansi pamaziko olimba. Silidzagwedezeka mpaka kalekale, mpaka muyaya.’ (Salimo 104:5) Vesili komanso mavesi ena ambiri amasonyeza kuti Mulungu sadzawononga dzikoli. Komanso sadzalola kuti anthu aliwononge n’kufika poti simungakhalenso chamoyo chilichonse.—Mlaliki 1:4; Yesaya 45:18.

 2. MAPETO ADZANGOFIKA OKHA.

  Baibulo limasonyeza kuti Mulungu anakhazikitsa nthawi yomwe mapeto adzafike. Limati: “Kunena za tsikulo kapena ola lake, palibe amene akudziwa, ngakhale angelo kumwamba kapenanso Mwana, koma Atate okha. Khalani maso, khalani tcheru, pakuti simukudziwa pamene nthawi yoikidwiratu idzafika.” (Maliko 13:32, 33) Izi zikusonyeza kuti pali “nthawi” yomwe Mulungu anakhazikitsa kuti mapeto adzafike.

 3. ANTHU KOMANSO MIYALA YOCHOKERA M’MLENGALENGA ZIDZACHITITSA KUTI MAPETO AFIKE.

  Kodi mapeto adzayamba bwanji? Lemba la Chivumbulutso 19:11 limati: “Nditayang’ana ndinaona kumwamba kutatseguka, kenako ndinaona hatchi yoyera. Wokwerapo wake dzina lake linali Wokhulupirika ndi Woona.” Ndipo vesi 19 limanena kuti: “Ndinaona chilombo, mafumu a dziko lapansi, ndi magulu awo ankhondo atasonkhana pamodzi kuti amenyane ndi wokwera pahatchi uja ndi gulu lake lankhondo.” (Chivumbulutso 19:11-21) Ngakhale kuti mawu ambiri a m’mavesi amenewa ndi ophiphiritsa, tikuphunzirapo mfundo yakuti, Mulungu adzatumiza angelo ake amphamvu kudzawononga adani ake.

Zimene Baibulo limanena zokhudza mapeto ndi nkhani yabwino osati yoopsa

ZOMWE ZIDZACHITIKEDI PA NTHAWI YA MAPETO

 1. MABOMA A ANTHU ADZAWONONGEDWA CHIFUKWA ALEPHERA KUTHETSA MAVUTO.

  Baibulo limati: “Mulungu wakumwamba adzakhazikitsa ufumu [kapena kuti boma] umene sudzawonongedwa ku nthawi zonse. Ufumuwo sudzaperekedwa kwa mtundu wina uliwonse wa anthu, koma udzaphwanya ndi kuthetsa maufumu ena onsewo, ndipo udzakhalapo mpaka kalekale.” (Danieli 2:44) Monga tafotokozera kale, ‘mafumu a dziko lapansi ndi magulu awo ankhondo adzasonkhana pamodzi kuti amenyane ndi wokwera pahatchi ndi gulu lake lankhondo.’ (Chivumbulutso 19:19) Koma Mulungu adzatumiza angelo ake amphamvu kuti awawononge.

 2. NKHONDO, CHIWAWA KOMANSO KUPANDA CHILUNGAMO ZIDZATHA.

  Baibulo limati: “[Mulungu] akuletsa nkhondo mpaka kumalekezero a dziko lapansi.” (Salimo 46:9) Limatinso: “Owongoka mtima ndi amene adzakhale m’dziko lapansi, ndipo opanda cholakwa ndi amene adzatsalemo. Koma oipa adzachotsedwa padziko lapansi ndipo achinyengo adzazulidwamo.” (Miyambo 2:21, 22) Komanso limanena kuti: “Taonani! Zinthu zonse zimene ndikupanga n’zatsopano.”—Chivumbulutso 21:4, 5.

 3. ZIPEMBEDZO ZABODZA ZIDZAWONONGEDWA CHIFUKWA ZALEPHERA KUKWANIRITSA ZOFUNA ZA MULUNGU NDI ANTHU.

  Lemba la Yeremiya 5:31 limati: “Aneneri akulosera monama, ndipo ansembe akupondereza anthu ndi mphamvu zawo. . . . kodi anthu inu mudzachita chiyani pamapeto pake?” Baibulo limanenanso kuti: “Ambiri adzati kwa ine pa tsiku limenelo, ‘Ambuye, Ambuye, kodi ife sitinalosere m’dzina lanu, ndi kutulutsa ziwanda m’dzina lanu, ndiponso kuchita ntchito zambiri zamphamvu m’dzina lanunso?’ Koma ine ndidzawauza momveka bwino kuti: ‘Sindikukudziwani ngakhale pang’ono! Chokani pamaso panga, anthu osamvera malamulo inu.’”—Mateyu 7:21-23.

 4. ANTHU ONSE OMWE AMALOWERERA ZA M’DZIKOLI ADZAWONONGEDWA.

  Yesu Khristu anati: “Tsopano maziko operekera chiweruzo ndi awa, kuwala kwafika m’dziko koma anthu akonda mdima m’malo mwa kuwala, pakuti ntchito zawo n’zoipa.” (Yohane 3:19) Baibulo limanena kuti Mulungu anawononga anthu onse oipa pa nthawi ya Nowa. Limati: “Dziko la pa nthawiyo linawonongedwa pamene linamizidwa ndi madzi. Ndipo mwa mawu amodzimodziwo, kumwamba kumene kulipo panopa limodzi ndi dziko lapansi, azisungira moto m’tsiku lachiweruzo ndi chiwonongeko cha anthu osaopa Mulungu.”—2 Petulo 3:5-7.

Onani kuti “tsiku lachiweruzo ndi chiwonongeko” lomwe likubwera, aliyerekezera ndi zomwe zinachitika m’nthawi ya Nowa. Kodi n’chiyani chinawonongedwa pa nthawiyo? Chomwe chinawonongedwa si dziko lapansili, koma ndi “anthu osaopa Mulungu” omwe tingati ndi adani ake. N’chimodzimodzinso ndi zomwe zidzachitike pa “tsiku lachiweruzo.” Anthu osaopa Mulungu ndi omwe adzawonongedwe. Koma anthu oopa Mulungu, omwe ndi mabwenzi ake, adzapulumuka ngati mmene zinalili ndi Nowa ndiponso banja lake.—Mateyu 24:37-42.

Mulungu akadzawononga anthu ochita zoipa, zinthu zidzasintha kwambiri padzikoli ndipo anthu opulumuka azidzasangalala. Choncho zimene Baibulo limanena zokhudza mapeto ndi nkhani yabwino, osati yoopsa. Komabe mwina mungafunse kuti, ‘Kodi Baibulo limatchula nthawi imene mapeto adzafike? Kodi mapeto ali pafupidi? Nanga ndingatani kuti ndidzapulumuke?’