Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mukudziwa?

Kodi Mukudziwa?

Kodi zimene akatswiri ofukula zinthu zakale anapeza zimagwirizana ndi zimene Baibulo limanena?

Chithunzi cha Mfumu Sarigoni Wachiwiri yemwe amatchulidwa pa Yesaya 20:1

Nkhani yomwe inalembedwa m’magazini ina inanena kuti akatswiri ofukula zinthu zakale anapeza mayina a “anthu 50” otchulidwa m’Chipangano Chakale. (Biblical Archaeology Review) Ena a anthuwa ndi mafumu 14 a Yuda ndi Isiraeli. Mafumuwa ndi monga Davide ndi Hezekiya komanso ena omwe sadziwika kwenikweni monga Menahemu ndi Peka. Enanso ndi mafumu 5 a ku Iguputo, 19 a ku Babulo, ku Mowabu, ku Perisiya, ku Siriya ndi Asuri. Komatu si mafumu okha omwe akatswiri ofukula zakalewa anapeza. Anapezanso mayina a ansembe, alembi komanso akuluakulu ena a boma.

Nkhani ija inanenanso kuti, “akatswiri ambiri ofukula zinthu zakale amavomereza” kuti mayina omwe anawapezawa ndi a anthu omwe amatchulidwadi m’Baibulo. Akatswiri ofukula zinthu zakale anapezanso umboni wosonyeza kuti anthu otchulidwa m’Chipangano Chatsopano analipodi. Anthu ake ndi monga Herode, Pontiyo Pilato, Tiberiyo, Kayafa ndi Serigio Paulo.

Kodi mikango inasiya liti kupezeka m’madera otchulidwa m’Baibulo?

Khoma lakale la ku Babulo lokongoletsedwa ndi chithunzi cha mkango

Ngakhale kuti m’madera omwe amatchulidwa m’Baibulo kulibe mikango masiku ano, m’Baibulo muli mavesi pafupifupi 150 amene amatchula za mikango. Izi zikusonyeza mkango unali nyama yodziwika bwino kwa anthu amene analemba Baibulo. Ena a mavesi amenewa amatchula mkango pophiphiritsira zinthu zina. Komabe mavesi ena amanena za mikango yeniyeni. Mwachitsanzo Baibulo limanena kuti Samisoni, Davide ndi Benaya anapha mikango. (Oweruza 14:5, 6; 1 Samueli 17:34, 35; 2 Samueli 23:20) Baibulo limanenanso za anthu ena omwe anaphedwa ndi mikango.1 Mafumu 13:24; 2 Mafumu 17:25.

Kale panali mtundu winawake wa mikango yomwe inkapezeka ku Asia Minor, Girisi, Palesitina, Siriya, Mesopotamiya komanso kumpoto chakumadzulo kwa India. Anthu a m’maderawa ankakonda kukongoletsa zinthu zawo ndi zithunzi za mikango chifukwa ankaiona kuti ndi nyama yoopsa komanso yapadera. Mwachitsanzo, khoma la m’mbali mwa msewu womwe unadutsa pageti yaikulu ya mpanda umene Nebukadinezara anamanga, analikongoletsa ndi zithunzi za mikango.

Komanso anthu amanena kuti asilikali omwe ankamenya nkhondo pofuna kukakamiza anthu kulowa Chikhristu, cha m’ma 1100 C.E., ankasaka ndi kupha mikango. Zikuoneka kuti mikango inayamba kusowa m’madera otchulidwa m’Baibulo chitadutsa chaka cha 1300 C.E. Mikangoyi inkapezekabe ku Mesopotamiya ndi ku Siriya mpaka m’zaka za m’ma 1800. Inkapezekanso ku Iran ndi ku Iraq mpaka chitatsala pang’ono kufika chaka cha 1950