NSANJA YA OLONDA May 2015 | Kodi Mapeto Ali Pafupidi?

Mukamva kuti “mapeto ali pafupi,” kodi mumaganiza chiyani? Kodi zimene mumaganizazo zimakuchititsani mantha?

NKHANI YAPACHIKUTO

Kodi N’chiyani Chidzachitike pa Nthawi ya “Mapeto”?

Kodi mukudziwa kuti zomwe Baibulo limanena zokhudza mapeto ndi nkhani yabwino osati yoopsa?

NKHANI YAPACHIKUTO

Kodi Mapeto Ali Pafupidi?

Werengani nkhaniyi kuti mudziwe zizindikiro 4 zimene Baibulo limanena zosonyeza kuti mapeto ali pafupi.

NKHANI YAPACHIKUTO

Inunso Mukhoza Kudzapulumuka Oipa Akamadzawonongedwa

Koma mungatani? Kodi muyenera kusunga katundu wambiri woti adzakuthandizeni kupulumuka pa nthawi ya mapeto?

Kodi Mukudziwa?

Kodi zimene akatswiri ofukula zinthu zakale anapeza zimagwirizana ndi zimene Baibulo limanena? Kodi mikango inasiya liti kupezeka m’madera otchulidwa m’Baibulo?

BAIBULO LIMASINTHA ANTHU

Ndinaphunzira Kuti Yehova Ndi Wachifundo Komanso Amakhululuka

Normand Pelletier ankakonda kubera anthu mwachinyengo moti ankalephera kusiya. Koma tsiku lina analira kwambiri atawerenga vesi lina la m’Baibulo.

TSANZIRANI CHIKHULUPIRIRO CHAWO

“Kodi Ine Ndatenga Malo a Mulungu?”

Ngati abale anu amakuchitirani nsanje, kukudani kapena kuchita zinthu zina zosakhulupirika, nkhani ya Yosefe ingakuthandizeni.

Kuyankha Mafunso a M’Baibulo

N’chifukwa chiyani Tsiku la Chiweruzo lidzakhale la zaka 1,000?

Zina zimene zili pawebusaiti

Kodi Ufumu wa Mulungu Udzachita Chiyani?

Werengani nkhaniyi kuti mudziwe zimene zidzachitike boma la Mulungu likadzayamba kulamulira dziko lapansili.