Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YA PACHIKUTO | KODI MAPETO ALI PAFUPIDI?

Inunso Mukhoza Kudzapulumuka Oipa Akamadzawonongedwa

Inunso Mukhoza Kudzapulumuka Oipa Akamadzawonongedwa

Pofotokoza zomwe zidzachitike pa nthawi ya mapeto, Baibulo limati: “Pa nthawiyo kudzakhala chisautso chachikulu chimene sichinachitikepo kuchokera pa chiyambi cha dziko mpaka tsopano . . . Kunena zoona, masikuwo akanapanda kufupikitsidwa, palibe amene akanapulumuka.” (Mateyu 24:21, 22) Koma Baibulo limasonyezanso kuti anthu ambiri adzapulumuka pa nthawiyi. Limati: “Dziko likupita . . . koma wochita chifuniro cha Mulungu adzakhala kosatha.”—1 Yohane 2:17.

Kodi mungatani kuti mudzapulumuke n’kukhala ndi moyo “kosatha”? Kodi muyenera kusunga katundu wambiri woti adzakuthandizeni kupulumuka pa nthawiyi? Ayi. Baibulo limasonyeza kuti katundu sadzapulumutsa munthu pa nthawi yamapeto. Limati: “Popeza zinthu zonsezi zidzasungunuka, ganizirani za mtundu wa munthu amene muyenera kukhala. Muyenera kukhala anthu akhalidwe loyera ndipo muzichita ntchito zosonyeza kuti ndinu odzipereka kwa Mulungu.” (2 Petulo 3:10-12) Baibulo limasonyeza kuti mawu akuti “zinthu zonsezi” akutanthauza olamulira a m’dzikoli komanso amene asankha ulamuliro wa anthu amenewa, m’malo mwa ulamuliro wa Mulungu. Choncho ngakhale titasunga katundu wochuluka bwanji, sangadzatipulumutse Mulungu akamadzawononga oipa.

Kuti mudzapulumuke pa nthawi ya mapeto, muyenera kukhala kumbali ya Yehova Mulungu. Muyeneranso kuphunzira Yehova n’kumachita zomwe zimamusangalatsa. (Zefaniya 2:3) M’malo motengera makhalidwe oipa a anthu ambiri a m’dzikoli, omwenso amanyalanyaza umboni woti tili m’masiku otsiriza, muyenera “kukumbukira nthawi zonse kukhalapo kwa tsiku la Yehova.” A Mboni za Yehova angakusonyezeni kuchokera m’Baibulo zimene mungachite kuti mudzapulumuke pa nthawi ya mapeto.