Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YA PACHIKUTO

Kodi Mapeto Ali Pafupidi?

Kodi Mapeto Ali Pafupidi?

Kodi Mulungu alola kuti anthu apitirizebe kupondereza anzawo komanso kuchita zinthu zomwe zingadzabweretse mavuto aakulu m’tsogolo? Ayi. Monga taonera kale, Mulungu, yemwe ndi Mlengi wathu komanso wa dzikoli, adzathetsa mavuto onse omwe anthufe tikukumana nawo. Ndipotu Mulungu akufuna kuti tidziwe zoti nthawi yoti achite zimenezi yayandikira. Koma kodi Mulungu amatithandiza bwanji kudziwa zimenezi?

Taganizirani chitsanzo ichi. Tiyerekeze kuti mukufuna kupita kwinakwake komwe simunayambe mwapitako. Mwina mungapemphe munthu wina kuti akuuzeni mapu a kumene mukupitako. Munthuyo angakuuzeni mapuwo komanso zinthu zina zomwe mungaone mumsewu. Ndiye mukayamba kuona zinthu zomwe munthu uja ananena, mumadziwa kuti mwatsala pang’ono kufika. Mofanana ndi zimenezi, Mulungu watipatsa Mawu ake, amene amatchula zinthu zomwe zingatithandize kudziwa kuti mapeto ali pafupi. Tikamaona zimenezi zikuchitika, timadziwa kuti mapeto ayandikira.

Baibulo linaneneratu kuti zinthu zidzaipa kwambiri mapeto akadzayandikira. Ngakhale kuti zoipa zakhala zikuchitika, Baibulo linaneneratu kuti mapeto akadzayandikira, zinthu padziko lonse zidzaipa kwambiri. Tiyeni tikambirane zinthu zina zomwe Baibulo linaneneratu kuti zidzakhala zizindikiro zosonyeza kuti mapeto ayandikira.

1. KUCHULUKA KWA MAVUTO Ulosi womwe umapezeka m’chaputala 24 cha Mateyu, unatchula zinthu zomwe zizidzachitika m’masiku otsiriza. Baibulo linaneneratu kuti zinthu zimenezi zidzakhala zizindikiro zosonyeza kuti “mapeto” ali pafupi ndipo kenako “mapeto adzafika.” (Vesi 3 ndi 14) Zinthu zimenezi ndi monga nkhondo zikuluzikulu, njala, zivomerezi, kupanda chikondi komanso kuchuluka kwa anthu osamvera malamulo. Baibulo linaneneratunso kuti m’masiku otsiriza, atsogoleri a zipembedzo azidzasocheretsa anthu. (Vesi 6 mpaka 26) N’zoona kuti zimenezi zakhala zikuchitika kuyambira kale. Komabe, ulosi wa m’Baibulo unasonyeza kuti mapeto akadzayandikira, zinthuzi zizidzachitika kwambiri komanso padziko lonse.

2. ANTHU AMBIRI ADZAKHALA NDI MAKHALIDWE OIPA Baibulo linaneneratu kuti m’masiku otsiriza anthu ambiri adzakhala a makhalidwe oipa. Limati: “Anthu adzakhala odzikonda, okonda ndalama, odzimva, odzikweza, onyoza, osamvera makolo, osayamika, osakhulupirika, osakonda achibale awo, osafuna kugwirizana ndi anzawo, onenera anzawo zoipa, osadziletsa, oopsa, osakonda zabwino, achiwembu, osamva za ena, odzitukumula ndiponso onyada, okonda zosangalatsa, m’malo mokonda Mulungu.” (2 Timoteyo 3:1-4) N’zoona kuti kuyambira kale, anthu akhala akuchita makhalidwe amenewa. Koma Baibulo linanena kuti m’masiku otsiriza, anthu ambiri azidzachita makhalidwe oipa kwambiri moti imeneyi idzakhala “nthawi yapadera komanso yovuta.” Kodi si zoona kuti zimenezi zikuchitika kwambiri masiku ano?

3. DZIKO LAIPA KOMANSO ANTHU AKUWONONGA ZACHILENGEDWE Baibulo limanena kuti Mulungu ‘adzawononga amene akuwononga dziko lapansi.’ (Chivumbulutso 11:18) Koma kodi anthu akuwononga bwanji dzikoli? Baibulo limafotokoza kuti anthu akuchita zimenezi mofanana ndi mmene anthu a m’nthawi ya Nowa ankachitira. Limati: “Dziko lapansi linali litaipa pamaso pa Mulungu woona, ndipo linadzaza ndi chiwawa. Chotero, Mulungu poyang’ana dziko lapansi anaona kuti laipa.” (Genesis 6:11-13) Choncho, Mulungu ananena kuti awononga anthu achiwawawo. Kodi nanunso mukuona kuti anthu padziko lonse akuchita zachiwawa kuposa kale? Panopa anthu ali ndi zida zoopsa kwambiri zomwe zingathe kupha anthu onse padzikoli. Komanso, anthu akuwononga zinthu zimene zimathandiza kuti padzikoli pakhalebe zamoyo. Zimenezi ndi zinthu monga mpweya, nyama, nyanja komanso zomera.

Zaka 100 zapitazo, anthu analibe zida zoti angathe kuwonongera anthu onse padziko lapansi. Koma panopa angathe kuwononga anthu padziko lonse chifukwa apanga zida zoopsa kwambiri. Akuwononganso kwambiri zinthu zachilengedwe moti zitati zipitirire chonchi, zamoyo zikhoza kudzatheratu padzikoli. Anthu akupanganso zinthu zamakono zomwe zimawononga zachilengedwe, koma akulephera kupeza njira yothetsera vutoli. Komabe, ubwino wake ndi woti tsogolo la dziko lapansili silili m’manja mwa anthu. Zinthu zisanafike poipa kwambiri, Mulungu adzalowererapo ndipo adzawononga anthu onse amene akuwononga dziko. Baibulo limanena kuti Mulungu analonjeza kuti adzachita zimenezi.

4. NTCHITO YOLALIKIRA IKUCHITIKA PADZIKO LONSE Chinanso chomwe chimatithandiza kudziwa kuti tikukhala m’masiku otsiriza, ndi ntchito yolalikira yomwe ikuchitika padziko lonse. Baibulo linaneneratu kuti: “Uthenga wabwino uwu wa ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi kumene kuli anthu, kuti ukhale umboni ku mitundu yonse, kenako mapeto adzafika.” (Mateyu 24:14) Ntchito yolalikira imeneyi ndi yosiyana kwambiri ndi imene anthu azipembedzo akhala akuchita. Baibulo linaneneratu za uthenga womwe uzidzalalikidwa m’masiku otsiriza kuti udzakhala, ‘uthenga wabwino wa Ufumu.’ Kodi mukudziwa chipembedzo chilichonse chomwe chimakonda kulalikira uthenga umenewu? Komanso ngati pali ena omwe amaoneka kuti amalalikira uthenga umenewu, kodi amalalikira “padziko lonse lapansi kumene kuli anthu, kuti ukhale umboni ku mitundu yonse”?

Ufumu wa Mulungu ukulalikidwa padziko lonse m’zinenero zambiri

Palinso webusaiti ya www.jw.org yomwe cholinga chake chachikulu n’kulengeza ‘uthenga wabwino wa Ufumu.’ Pa webusaitiyi pamapezeka mabuku, magazini, timabuku komanso timapepala m’zinenero zoposa 700. Cholinga cha zonsezi n’kuthandiza anthu kudziwa za Ufumu wa Mulungu. Kodi mukudziwanso webusaiti ina yomwe cholinga chake chachikulu n’kuthandiza anthu padziko lonse lapansi kumva za Ufumu wa Mulungu? M’mbuyomu kulibe Intaneti, a Mboni za Yehova ankadziwikabe ndi ntchito yawo yolalikira. Ankagwiritsa ntchito njira zosiyanasiyana kuti alalikire uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu. Ndipotu kuyambira mu 1939, pachikuto cha magazini yathu ya Nsanja ya Olonda pamakhala mawu akuti, “Yolengeza Ufumu wa Yehova.” Buku lina lofotokoza nkhani za chipembedzo linanena kuti, ntchito yolalikira yomwe a Mboni za Yehova amagwira “ndi yosiyana kwambiri ndi zimene a zipembedzo zina amachita, chifukwa ndi yaikulu kwambiri komanso imachitika padziko lonse lapansi.” A Mboni za Yehova amalalikira uthenga wabwino woti, posachedwapa “mapeto adzafika.” Amalalikiranso kuti Ufumu wa Mulungu ndi womwe udzabweretse mapetowo.

MAPETO ALI PAFUPI

Kodi mwaona kuti maulosi onse 4, omwe takambirana m’nkhaniyi, akukwaniritsidwa masiku ano? Kwa zaka zoposa 100 tsopano, magazini ya Nsanja ya Olonda yakhala ikuthandiza anthu kudziwa kuti zomwe zikuchitika padzikoli zikusonyeza kuti tili m’masiku otsiriza. Komabe anthu ena amatsutsa zimenezi. Amanena kuti anthu amangokokomeza zimene zikuchitika kuti zigwirizane ndi mfundo zawo. Amanenanso kuti popeza anthu masiku ano akutha kudziwa zomwe zikuchitika padziko lonse mosavuta, zikupangitsa kuti anthu aziganiza kuti zinthu zaipa kwambiri poyerekeza ndi kale. Ngakhale zili choncho, anthu ambiri amazindikira kuti zomwe zikuchitika padzikoli ndi umboni woti mapeto ali pafupi.

Akatswiri ena amaona kuti pali umboni wosonyeza kuti zinthu padzikoli zikusintha kwambiri. Mwachitsanzo mu 2014, magazini ina inachenjeza nthambi ya bungwe la United Nations yoona zachitetezo kuti anthu onse akhoza kuphedwa padzikoli. Magaziniyi inati: “Malinga ndi kafukufuku yemwe tachita, tikuona kuti anthu akhoza kugwiritsa ntchito zida zoopsa zomwe apanga n’kupha anthu onse padzikoli.” Zinthu ngati zimenezi, zikupangitsa anthu ambiri kuona kuti mapeto ali pafupi. A Mboni za Yehova komanso anthu ambiri amene amawerenga magazini a Nsanja ya Olonda sakayikira kuti tili m’masiku otsiriza ndiponso kuti mapeto ali pafupi. Koma simuyenera kuchita mantha ndi zomwe zidzachitike m’tsogolo. Tikutero chifukwa mukhoza kudzapulumuka pa nthawi yamapeto.