Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Khristu Ndiye Mphamvu ya Mulungu

Khristu Ndiye Mphamvu ya Mulungu

“Khristu ndiye mphamvu ya Mulungu.”—1 AKOR. 1:24.

1. N’chifukwa chiyani Paulo ananena kuti “Khristu ndiye mphamvu ya Mulungu”?

ZINTHU zodabwitsa zimene Yesu ankachita zinkasonyeza mphamvu za Yehova. Mabuku 4 a Uthenga Wabwino amafotokoza zinthu ngati zimenezi ndipo kuziwerenga kungalimbitse chikhulupiriro chathu. Koma n’kutheka kuti Yesu anachita zozizwitsa zina zambiri zimene sizinalembedwe. (Mat. 9:35; Luka 9:11) M’pomveka kuti mtumwi Paulo ananena kuti: “Khristu ndiye mphamvu ya Mulungu.” (1 Akor. 1:24) Koma funso n’kumati, kodi tikuphunzira chiyani pa zinthu zodabwitsa zimene Yesu ankachita?

2. Kodi zodabwitsa zimene Yesu ankachita zimasonyeza chiyani?

2 Mtumwi Petulo ananenanso kuti Yesu ankachita “zodabwitsa.” (Mac. 2:22) Zomwe Yesu ankachita zimasonyeza zinthu zosangalatsa zimene adzachite padziko lonse akamadzalamulira. Zimatithandizanso kudziwa bwino makhalidwe ake ndiponso a Atate wake. Tiyeni  tikambirane zozizwitsa zina zimene Yesu anachita ndipo tione zimene tikuphunzirapo.

YESU ANASONYEZA MTIMA WOPATSA

3. (a) Kodi chinachitika n’chiyani kuti Yesu achite chozizwitsa choyamba? (b) Kodi zimenezi zinasonyeza bwanji kuti ali ndi mtima wopatsa?

3 Yesu anachita chozizwitsa choyamba pa phwando la ukwati ku Kana m’dera la Galileya. Pa phwandoli, vinyo anatha mwina chifukwa chakuti kunabwera alendo ambiri kuposa amene ankayembekezera. Mayi ake a Yesu analiponso. Iwo ankadziwa kuti Yesu ndi “Mwana wa Wam’mwambamwamba” ndipo ayenera kuti kwa zaka zambiri ankaganizira maulosi onena za Yesuyo. (Luka 1:30-32; 2:52) Sitikudziwa ngati ankakhulupirira kuti Yesu ali ndi mphamvu zapadera zothandizira banjalo. Koma chomwe tikudziwa n’chakuti pa phwandolo, Mariya ndi Yesu anamvera chisoni banja latsopanolo ndipo ankafuna kulithandiza kuti lisachite manyazi. Yesu ankadziwanso kuti kulandira bwino alendo n’kofunika kwambiri. Choncho anasandutsa madzi okwana malita 380 kukhala “vinyo wabwino.” (Werengani Yohane 2:3, 6-11.) Sikuti Yesu ndi amene anali ndi udindo wopezera anthuwo vinyo. Koma ankaganizira kwambiri anthu ndipo ankatsanzira mtima wopatsa wa Atate wake.

4, 5. (a) Kodi tikuphunzira chiyani pa chozizwitsa choyamba cha Yesu? (b) Kodi zimenezi zikusonyeza kuti zinthu zidzakhala bwanji m’tsogolo?

4 Yesu anasandutsa madzi kukhala vinyo wokwanira anthu ambiri. Kodi tikuphunzira chiyani pa zimene anachitazi? Nkhaniyi ikusonyeza kuti iye ndiponso Atate wake amaganizira kwambiri mmene anthu akumvera mumtima mwawo. Zikusonyezanso kuti Yehova ndi Yesu ali ndi mtima wopatsa kwambiri. Ndiyeno kodi mukuganiza kuti Yehova adzachita zotani m’dziko latsopano pofuna kukonzera “anthu a mitundu yonse” phwando la zakudya zabwino?—Werengani Yesaya 25:6.

5 Posachedwapa munthu aliyense adzakhala ndi zinthu zonse zofunika kwambiri monga chakudya chokwanira ndiponso nyumba zabwino. Timasangalala kwambiri poganizira zinthu zabwino zambirimbiri zimene Yehova adzatipatse m’Paradaiso.

Tikamagwiritsa ntchito nthawi yathu pothandiza anthu ena, timatsanzira mtima wopatsa wa Yesu (Onani ndime 6)

6. (a) Kodi Yesu ankagwiritsa ntchito bwanji mphamvu zake zodabwitsa? (b) Kodi tingatsanzire bwanji Yesu?

6 Chochititsa chidwi n’chakuti Mdyerekezi atauza Yesu kuti asandutse miyala kukhala mkate iye anakana. Sanafune kugwiritsa ntchito mphamvu zake zodabwitsa kuti apeze zimene ankalakalaka. (Mat. 4:2-4) Koma ankagwiritsa ntchito mphamvuzo pofuna kuthandiza anthu ena. Kodi tingatsanzire bwanji Yesu pa nkhaniyi? Kumbukirani kuti iye analimbikitsa atumiki a Yehova onse kuti ‘akhale opatsa.’ (Luka 6:38) Mwina tingaitane anzathu kuti adzadye nafe chakudya ndiponso kuti tilimbikitsane. Tikapita ku misonkhano tingagawe nthawi yathu kuti tithandize ena. Mwachitsanzo, pambuyo pa misonkhano ena angafune  kuti timvetsere pamene akuyesezera nkhani yawo. Tikakhalanso mu utumiki tiyenera kuona zimene tingachite kuti tithandize anthu ena. Tikamapatsa anthu zinthu komanso kuwalimbikitsa ndi mfundo za m’Malemba timasonyeza kuti tikutsanzira mtima wopatsa wa Yesu.

“ONSE ANADYA N’KUKHUTA”

7. Kodi ndi vuto liti limene silingathe m’dziko loipali?

7 Kuyambira kalekale, anthu akhala akuvutika ndi umphawi. Paja Yehova anauza Aisiraeli kuti padzakhala osauka m’dziko lawo nthawi zonse. (Deut. 15:11) Patapita zaka zambiri, Yesu ananenanso kuti: “Osaukawo muli nawo nthawi zonse.” (Mat. 26:11) Kodi Yesu anatanthauza kuti padzakhala osauka padzikoli mpaka kalekale? Ayi. Koma anatanthauza kuti vuto la umphawi silingathe m’dziko loipali. Choncho timalimbikitsidwa tikaganizira kuti zozizwitsa za Yesu zimasonyeza kuti anthu onse adzakhala ndi chakudya chokwanira pa nthawi imene Ufumu wa Mulungu uzidzalamulira dzikoli.

8, 9. (a) Kodi chinachitika n’chiyani kuti Yesu adyetse anthu ambirimbiri? (b) Kodi mumalimbikitsidwa bwanji mukaganizira zimene anachitazi?

8 Wamasalimo ananena za Yehova kuti: “Mumatambasula dzanja lanu ndi kukhutiritsa zokhumba za chamoyo chilichonse.” (Sal. 145:16) Potsanzira Atate wake, Khristu ankathandiza anthu kupeza zinthu zimene ankafuna. Sankachita zimenezi pongofuna kusonyeza kuti ali ndi mphamvu. Koma ankafunitsitsa kuthandiza anthu. Chitsanzo pa nkhaniyi tingachipeze pa Mateyu 14:14-21. (Werengani.) Ophunzira a Yesu anamufunsa zimene angachite kuti apeze chakudya. Mwina iwowo anali ndi njala komanso ankadera nkhawa anthu ochokera kutali amene anayenda wapansi kuti atsatire Yesu. Anthuwo anali atatopa ndipo anali ndi njala. (Mat. 14:13) Kodi Yesu anachita chiyani?

9 Yesu anadyetsa amuna 5,000 komanso akazi ndi ana ambiri pongogwiritsa ntchito mitanda 5 ya mkate ndi nsomba ziwiri. Timalimbikitsidwa kwambiri tikaganizira kuti Yesu anagwiritsa ntchito mphamvu zake pothandiza mabanja komanso ana ang’onoang’ono. Anthu onsewo “anadya n’kukhuta” ndipo chakudya chimene chinatsala chinadzaza madengu 12. Izi zikusonyeza kuti panali chakudya chambiri. Yesu anawapatsa chakudya chokwanira kuti asavutike ndi njala pa ulendo wawo wautali wobwerera kunyumba zawo.—Luka 9:10-17.

10. Kodi posachedwapa zinthu zidzasintha bwanji padzikoli?

10 Masiku ano, anthu mamiliyoni ambiri amalephera kupeza zinthu zofunika pa moyo chifukwa cha ulamuliro wopanda chilungamo. Ngakhale abale ena amavutika kupeza chakudya chokwanira. Komabe posachedwapa anthu omvera Mulungu adzasangalala m’dziko lopanda chinyengo ndi umphawi. Kodi inuyo mukanakhala ndi mphamvu zambiri mukanapereka zinthu zofunika pa moyo kwa anthu onse? Yehova ndi wamphamvuyonse ndipo ndi wofunitsitsa kuchita zimenezi. Choncho sitingakayikire kuti posachedwapa anthu onse adzakhaladi ndi zinthu zonse zofunika.—Werengani Salimo 72:16.

11. (a) N’chiyani chikukuthandizani kudziwa kuti Yesu adzagwiritsa ntchito mphamvu zake pothandiza anthu padziko lonse? (b) Kodi inuyo muyenera kuchita chiyani?

11 Yesu ali padzikoli, anagwira ntchito yothandiza anthu m’madera ochepa ndiponso kwa zaka zitatu ndi hafu basi. (Mat. 15:24) Koma panopa iye ndi Mfumu kumwamba ndipo posachedwapa adzathandiza anthu padziko lonse. (Sal. 72:8) Zinthu zodabwitsa zimene  Yesu ankachita zimasonyeza kuti ali ndi mphamvu ndiponso ndi wofunitsitsa kutithandiza. Ngakhale kuti ifeyo sitingachite zozizwitsa, tingathandize anthu kudziwa maulosi osonyeza zinthu zabwino zimene tikuyembekezera. Mboni za Yehovafe, tikudziwa zinthu zabwino zimene Mulungu watilonjeza. Choncho tili ndi udindo wothandiza anthu ena kudziwa zinthuzi. (Aroma 1:14, 15) Kuganizira zimenezi kungatilimbikitse kuti tizilalikira mwakhama za Ufumu wa Mulungu.—Sal. 45:1; 49:3.

AMATHA KULAMULIRA MPHAMVU ZA M’CHILENGEDWE

12. N’chifukwa chiyani sitiyenera kukayikira zoti Yesu amadziwa zinthu zonse zokhudza dziko lapansi?

12 Yesu anagwira ntchito ndi Mulungu polenga dziko ndiponso zinthu zonse zapadzikoli. Baibulo limanena kuti iye anali “mmisiri waluso.” (Miy. 8:22, 30, 31; Akol. 1:15-17) Choncho Yesu amadziwa bwinobwino zinthu zonse zokhudza dziko lapansi. Iye amadziwa zimene angachite kuti alamulire bwinobwino zinthu za m’chilengedwe.

N’chiyani chimakuchititsani chidwi ndi mmene Yesu ankagwiritsira ntchito mphamvu zake? (Onani ndime 13 ndi 14)

13, 14. Perekani chitsanzo chosonyeza kuti Khristu amatha kulamulira mphamvu za m’chilengedwe.

13 Yesu ali padziko lapansi, anasonyezadi kuti ali ndi “mphamvu ya Mulungu” chifukwa ankalamulira mphamvu za m’chilengedwe. Mwachitsanzo, analamulira chimphepo champhamvu chomwe chikanapha ophunzira ake. (Werengani Maliko 4:37-39.) Katswiri wina wa Baibulo anati: ‘Mawu achigiriki amene anawamasulira kuti “chimphepo champhamvu chamkuntho” pa Maliko 4:37, amanena za mvula yamkuntho kapena namondwe. Sikuti amangonena za chimphepo wamba koma chimphepo limodzi ndi mvula yamkuntho imene imawononga zinthu.’

14 Taganizirani zimene zinachitika. Khristu anali atatoperatu chifukwa chogwira ntchito yolalikira. Mafunde ankamenya kwambiri ngalawa yawo ndipo madzi ankalowa mkati. Koma ngakhale kuti chimphepocho chinkasokosera komanso ngalawayo inkagwedezeka, Yesu ankagonabe chifukwa chotopa kwambiri. Ophunzira ake anachita mantha kwambiri ndipo anamudzutsa pofuula kuti: “Tikufa!” (Mat. 8:25) Yesu anadzuka n’kulamula mphepo ndi nyanja kuti: “Leka! Khala bata!” Nthawi yomweyo, chimphepocho chinasiya. (Maliko 4:39) Ndiyeno “panachita bata lalikulu.” Iye anasonyezadi kuti ali ndi mphamvu zambiri.

15. Kodi Mulungu wasonyeza bwanji kuti amatha kulamulira mphamvu za m’chilengedwe?

15 Mphamvu za Khristu zimachokera kwa Yehova. Choncho tingakhulupirire kuti Yehovayo akhoza kulamulira mosavuta mphamvu za m’chilengedwe. Mwachitsanzo, chigumula chisanachitike, Yehova anati: “Kwangotsala masiku 7 okha kuti ndigwetse chimvula padziko lapansi kwa masiku 40, usana ndi usiku.” (Gen. 7:4) Komanso lemba la Ekisodo 14:21 limati: “Yehova anachititsa mphepo yamphamvu yakum’mawa kuyamba kugawa nyanjayo.” Lemba la Yona 1:4 limanenanso kuti: “Yehova anabweretsa chimphepo champhamvu panyanjapo, ndipo panachita mkuntho wamphamvu. Chotero chombocho chinatsala pang’ono kusweka.” Timalimbikitsidwa kudziwa kuti Yehova amatha kulamulira mphamvu za m’chilengedwe. Choncho sitiyenera kudera nkhawa za m’tsogolo.

16. N’chifukwa chiyani tingalimbikitsidwe podziwa kuti Mlengi wathu ndiponso Mwana wake amatha kulamulira mphamvu za m’chilengedwe?

16 Kuganizira mphamvu zazikulu zimene Mlengi wathu ndiponso ‘mmisiri wake waluso’ ali nazo kumatilimbikitsa kwambiri. Iwo akadzakonza zinthu padzikoli pa zaka 1,000, anthu onse adzakhaladi pa mtendere. Sitidzavutikanso ndi zinthu monga chimphepo kapena  mvula yamkuntho. M’dziko latsopano, sitidzaopanso zinthu ngati namondwe, chivomezi kapena kuphulika kwa mapiri. Tangoganizirani, pa nthawiyo ‘chihema cha Mulungu chidzakhala pakati pa anthu’ ndipo mphamvu za m’chilengedwe sizidzaphanso anthu kapena kuwavulaza. (Chiv. 21:3, 4) Sitiyenera kukayikira kuti Khristu ali ndi mphamvu zochokera kwa Mulungu ndipo adzatha kulamulira mphamvu za m’chilengedwe pa zaka zonse 1,000 za ulamuliro wake.

TIZITSANZIRA MULUNGU NDI KHRISTU

17. Kodi tingatsanzire bwanji Mulungu ndi Khristu?

17 Kunena zoona, tilibe mphamvu zolamulira zinthu za m’chilengedwe monga mmene Yehova ndi Yesu amachitira. Komabe tili ndi mphamvu zinazake. Tingazigwiritse ntchito pochita zimene zili pa Miyambo 3:27. (Werengani.) Tingathandize abale athu pamene ali pa mavuto powapatsa zinthu zofunika kapena kuwalimbikitsa. (Miy. 17:17) Mwachitsanzo, tingawathandize ngati pachitika ngozi. Mlongo wina wamasiye, nyumba yake inawonongeka kwambiri ndi mphepo yamkuntho ndipo atathandizidwa anati: “Ndimathokoza kwambiri kuti ndili m’gulu la Yehova chifukwa abale ndi alongo andithandiza kupeza zinthu zofunika komanso kundilimbikitsa ndi mfundo za m’Baibulo.” Mlongo winanso wosakwatiwa anadandaula kwambiri nyumba yake itawonongeka ndi mvula yamkuntho. Iye atathandizidwa anati: “Ndikusowa chonena . . . Ndikungothokoza Yehova.” Timasangalala kuti tili m’gulu la abale amene amakondanadi ndi kuthandizana. Koma timasangalala kwambiri chifukwa Yehova ndi Yesu amatikonda ndi kutisamalira.

18. N’chifukwa chiyani Yesu ankachita zozizwitsa?

18 Yesu ali padzikoli, ankasonyezadi kuti ali ndi “mphamvu ya Mulungu.” Koma iye sankagwiritsa ntchito mphamvuzo pofuna kugometsa anthu kapena kuchita zofuna zake. Anachita zozizwitsa chifukwa chokonda anthu. Tidzakambirana zimenezi m’nkhani yotsatira.