Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mumadziwa Yehova Ngati Mmene Nowa, Danieli ndi Yobu Ankamudziwira?

Kodi Mumadziwa Yehova Ngati Mmene Nowa, Danieli ndi Yobu Ankamudziwira?

“Anthu okonda kuchita zoipa sangamvetse chilungamo, koma amene akufunafuna Yehova amamvetsa chilichonse.”​—MIY. 28:5.

NYIMBO: 126, 150

1-3. (a) Kodi n’chiyani chingatithandize kukhalabe okhulupirika kwa Mulungu m’masiku otsirizawa? (b) Kodi tikambirana chiyani munkhaniyi?

PAMENE mapeto akuyandikira, anthu oipa ‘akuphuka ngati msipu.’ (Sal. 92:7) Choncho n’zosadabwitsa kuti anthu ambiri alibe makhalidwe abwino. Ndiyeno kodi ifeyo tingatani kuti tikhale “tiana pa zoipa” koma ‘aakulu msinkhu pa luntha la kuzindikira’?​—1 Akor. 14:20.

2 Yankho la funsoli tingalipeze mulemba lotsogolera lomwe likuti: “Amene akufunafuna Yehova amamvetsa chilichonse.” (Miy. 28:5) Palembali, mawu akuti “chilichonse” akutanthauza chilichonse chofunika kuti tizisangalatsa Mulungu. Mfundo yofanana ndi imeneyi ikupezekanso pa Miyambo 2:7, 9 pamene pamanena kuti Yehova ‘amasungira anthu owongoka mtima nzeru zopindulitsa.’ Izi zimawathandiza kuti azimvetsa “zinthu zolondola, zolungama, zowongoka, ndiponso njira yonse ya zinthu zabwino.”

3 Nowa, Danieli ndi Yobu anapeza nzeru zimenezi. (Ezek. 14:14) N’chimodzimodzinso ndi anthu a Mulungu masiku ano. Koma bwanji za inuyo panokha? Kodi ‘mumamvetsa chilichonse’ chofunika kuti musangalatse Yehova? Kuti muthe kuchita zimenezi, muyenera kumudziwa bwino Yehova. Choncho tiyeni tikambirane (1) zimene zinathandiza Nowa, Danieli ndi Yobu kuti adziwe Mulungu, (2) mmene kudziwa Mulungu kunawathandizira komanso (3) zimene tingachite potsanzira chikhulupiriro chawo.

NOWA ANAYENDA NDI MULUNGU M’DZIKO LOIPA

4. Kodi Nowa anadziwa bwanji Yehova ndipo zimenezi zinamuthandiza bwanji?

4 Kodi n’chiyani chinathandiza Nowa kudziwa Yehova? Kuyambira kalekale, anthu okhulupirika akhala akuphunzira za Mulungu m’njira zitatu izi: poona zinthu zimene Mulungu analenga, kumva kwa atumiki ena okhulupirika komanso poona madalitso amene amapeza akamatsatira mfundo zachilungamo za Mulungu. (Yes. 48:18) Nowa akayang’ana zimene Mulungu analenga ayenera kuti ankaona umboni wakuti Mulungu aliko komanso kuzindikira makhalidwe ake monga “mphamvu zake zosatha ndiponso Umulungu.” (Aroma 1:20) Chifukwa cha zimenezi, Nowa sanangovomereza kuti kuli Mulungu koma anayamba kumukhulupirira ndi mtima wonse.

5. Kodi Nowa anaphunzira bwanji za cholinga cha Mulungu chokhudza anthu?

5 Baibulo limanena kuti “munthu amakhala ndi chikhulupiriro chifukwa cha zimene wamva.” (Aroma 10:17) Kodi Nowa anamva bwanji za Yehova? Ayenera kuti anamva kuchokera kwa achibale ake. Achibalewo anali anthu monga Lameki, yemwe anali munthu wokhulupirika ndipo anakhala ndi moyo Adamu asanamwalire. (Onani chithunzi choyambirira.) Panalinso agogo a Nowa dzina lawo Metusela ndiponso agogo a agogo ake dzina lawo Yaledi, omwe anakhala ndi moyo zaka zina 366 Nowa atabadwa. * (Luka 3:36, 37) N’kutheka kuti anthuwa limodzi ndi akazi awo ankauza Nowa za kulengedwa kwa anthu, cholinga cha Mulungu chakuti anthu olungama adzaze dziko ndiponso mavuto amene anayambira mu Edeni, omwe Nowa ankatha kuwaona yekha. (Gen. 1:28; 3:16-19, 24) Mulimonse mmene zinalili, zimene Nowa anaphunzira zinamufika pamtima ndipo anayamba kutumikira Mulungu.​—Gen. 6:9.

6, 7. Kodi kuyembekezera zinthu zabwino kunalimbitsa bwanji chikhulupiriro cha Nowa?

6 Chikhulupiriro cha munthu chimalimba ngati akuyembekezera zinthu zabwino. Choncho Nowa ayenera kuti analimbikitsidwa atadziwa kuti dzina lake, lomwe mwina linkatanthauza “Mpumulo kapena Chitonthozo,” linkasonyeza kuti pali chiyembekezo. (Gen. 5:29) Lameki ananeneratu kuti: “Uyu [Nowa] ndi amene adzatibweretsere mpumulo ku ntchito yathu yopweteketsa manja, chifukwa cholima nthaka imene Yehova anaitemberera.” Nowa ankayembekezera kuti Mulungu adzakonza zinthu. Mofanana ndi Abele ndi Inoki, iye ankakhulupirira za “mbewu” imene idzaphwanye mutu wa njoka.​—Gen. 3:15.

7 Nowa sankamvetsa zinthu zonse zokhudza ulosi wa pa Genesis 3:15, koma ayenera kuti ankadziwa kuti ukunena za kupulumuka kwa anthu. Ulosiwu unkagwirizananso ndi zimene Inoki ananeneratu zoti Mulungu adzawononga anthu oipa. (Yuda 14, 15) Uthenga wa Inokiwu, womwe udzakwaniritsidwa komaliza pa Aramagedo, uyenera kuti unalimbitsa chikhulupiriro cha Nowa.

8. Kodi kudziwa bwino Mulungu kunateteza bwanji Nowa?

8 Kodi kudziwa bwino Mulungu kunathandiza bwanji Nowa? Kunamuthandiza kukhala ndi chikhulupiriro cholimba komanso nzeru yochokera kwa Mulungu. Zimenezi zinamuthandizanso kuti asamachite chilichonse chimene chingasokoneze ubwenzi wake ndi Yehova. Mwachitsanzo, popeza Nowa ‘ankayenda ndi Mulungu woona,’ sankayenda kapena kucheza ndi anthu oipa. Anthu opanda chikhulupiriro ankagometsedwa ndi mphamvu za ziwanda zimene zinabwera padzikoli ngati anthu ndipo mwina anafika pomalambira ziwandazo. Koma Nowa sanapusitsidwe ndi ziwandazi. (Gen. 6:1-4, 9) Nowa ankadziwa kuti anthu ndi amene anauzidwa kuti aberekane n’kudzaza dziko lapansi. (Gen. 1:27, 28) Choncho ayenera kuti ankadziwa kuti kugonana pakati pa akazi ndi angelo oipa ndi kosayenera. Mfundo imeneyi inaonekeratu pamene kunabadwa ana amene anali aakulu komanso amphamvu mwachilendo. Patapita nthawi, Mulungu anachenjeza Nowa kuti adzabweretsa chigumula padziko lapansi. Nowa ankakhulupirira kwambiri Mulungu ndipo anamanga chingalawa chomwe iye ndi banja lake anapulumukiramo.​—Aheb. 11:7.

9, 10. Kodi tingatsanzire bwanji chikhulupiriro cha Nowa?

9 Kodi tingatsanzire bwanji chikhulupiriro cha Nowa? Chimene chingatithandize ndi kuphunzira kwambiri Mawu a Mulungu, kuganizira zimene timaphunzirazo komanso kuzitsatira pa moyo wathu. (1 Pet. 1:13-15) Tikamachita zimenezi chikhulupiriro ndiponso nzeru yochokera kwa Mulungu zidzatithandiza kupewa ziwembu za Satana komanso mzimu woipa wa m’dzikoli. (2 Akor. 2:11) Mzimuwu umalimbikitsa anthu kukonda chiwawa ndiponso chiwerewere. Umawalimbikitsanso kuganizira kwambiri zimene amalakalaka. (1 Yoh. 2:15, 16) Ukhozanso kuchititsa anthu amene afooka mwauzimu kuti azinyalanyaza umboni wakuti tsiku lalikulu la Mulungu layandikira. Kumbukirani kuti pamene Yesu anayerekezera masiku a Nowa ndi masiku ano ananena kwambiri za kusakhala tcheru mwauzimu osati za chiwawa ndi chiwerewere.​—Werengani Mateyu 24:36-39.

10 Muyenera kudzifunsa kuti, ‘Kodi zimene ndimachita pa moyo zimasonyeza kuti ndimamudziwa bwino Yehova? Nanga kodi chikhulupiriro changa chimandilimbikitsa kutsatira mfundo zachilungamo za Mulungu komanso kuziphunzitsa kwa anthu ena?’ Mayankho anu pa mafunsowa angakuthandizeni kudziwa ngati ‘mukuyendadi ndi Mulungu woona’ kapena ayi.

DANIELI ANASONYEZA NZERU YOCHOKERA KWA MULUNGU MUMZINDA WOIPA WA BABULO

11. (a) Kodi tingaphunzire chiyani zokhudza makolo a Danieli tikaganizira mmene iye ankakondera Mulungu? (b) Kodi inuyo mungakonde kutsanzira makhalidwe ati a Danieli?

11 Kodi n’chiyani chinathandiza Danieli kudziwa Yehova? Danieli ayenera kuti anaphunzitsidwa bwino ndi makolo ake kuti azikonda Yehova komanso Mawu ake ndipo sanasinthe kwa moyo wake wonse. Iye ankakonda kuphunzira Malemba ngakhale atakalamba. (Dan. 9:1, 2) Pemphero la Danieli lochokera pansi pa mtima limene lili pa Danieli 9:3-19 limasonyeza kuti ankadziwa bwino Yehova komanso mmene ankachitira zinthu ndi Aisiraeli. Mungachite bwino kupeza mpata wowerenga pempheroli n’kuliganizira mofatsa kuti mudziwe zambiri zokhudza Danieli.

12-14. (a) Kodi Danieli anasonyeza bwanji kuti anali ndi nzeru yochokera kwa Mulungu? (b) Kodi Danieli anadalitsidwa bwanji chifukwa cholimba mtima komanso kukhala wokhulupirika kwa Mulungu?

12 Kodi kudziwa bwino Mulungu kunathandiza bwanji Danieli? Moyo wa ku Babulo unali wovuta kwambiri kwa Ayuda okhulupirika. Mwachitsanzo, Yehova anauza Ayuda kuti: “Mzinda umene ndakuchititsani kukhalamo monga akapolo, muziufunira mtendere.” (Yer. 29:7) Koma pa nthawi imodzimodziyo Yehova ankafuna kuti Ayudawo azilambira iye yekha. (Eks. 34:14) Ndiye kodi n’chiyani chinathandiza Danieli kuti azichita zonsezi bwinobwino? Nzeru yochokera kwa Mulungu inamuthandiza kuti azilemekeza olamulira koma mosapitirira malire. Patapita zaka zambiri, Yesu anaphunzitsanso anthu mfundo yomweyi.​—Luka 20:25.

13 Taganizirani zimene Danieli anachita pataikidwa lamulo loletsa anthu kupemphera kwa mulungu kapena munthu wina aliyense kupatulapo mfumu kwa masiku 30. (Werengani Danieli 6:7-10.) Danieli akanatha kupeza zifukwa zodzikhululukira. Mwachitsanzo, akanati: ‘Masiku 30 si nthawi yaitali kwenikweni.’ Koma iye sanalole kuti lamuloli limulepheretse kulambira Mulungu. N’zoona kuti akanapemphera mobisa kuti anthu asamamuone. Koma iye ankadziwa kuti chizolowezi chake chopemphera chinali chodziwika kwambiri. Choncho Danieli analolera kuika moyo wake pa ngozi n’kupitiriza kupemphera poyera chifukwa sankafuna kuti anthu aganize zoti wasiya kutumikira Yehova.

14 Yehova anadalitsa Danieli chifukwa choti analimba mtima ndipo anamupulumutsa modabwitsa kuti asaphedwe ndi mikango. Ndipotu zimenezi zinachititsa kuti anthu a mu ufumu wonse wa Amedi ndi Aperisiya adziwe za Yehova.​—Dan. 6:25-27.

15. Kodi tingatsanzire bwanji chikhulupiriro cha Danieli?

15 Kodi tingatsanzire bwanji chikhulupiriro cha Danieli? Kuti tikhale ndi chikhulupiriro cholimba, chofunika si kungowerenga Mawu a Mulungu koma “kuzindikira tanthauzo lake.” (Mat. 13:23) Tiyenera kumvetsa bwino mfundo za m’Baibulo kuti tizidziwa bwino maganizo a Yehova. Kuti zimenezi zitheke, tiyenera kuganizira kwambiri zimene timawerenga m’Baibulo. Tiyeneranso kupemphera kuchokera pansi pa mtima, makamaka tikamakumana ndi mayesero kapena mavuto. Tikamapempha Mulungu mwachikhulupiriro kuti atipatse nzeru ndiponso mphamvu, adzatipatsadi mowolowa manja.​—Yak. 1:5.

YOBU ANKATSATIRA MFUNDO ZA MULUNGU PA NTHAWI YAMTENDERE KOMANSO YOVUTA

16, 17. Kodi Yobu anadziwa bwanji Yehova?

16 Kodi n’chiyani chinathandiza Yobu kudziwa Yehova? Yobu sanali wa mtundu wa Isiraeli koma anali wachibale wa Abulahamu, Isaki ndi Yakobo. Yehova anadziulula kwa anthu atatuwa ndiponso anawafotokozera cholinga chake chokhudza anthu. Nayenso Yobu anaphunzira zambiri zokhudza Yehova m’njira inayake. (Yobu 23:12) Paja iye anauza Yehova kuti: “Ndinkangomva za inu.” (Yobu 42:5) Komanso Yehova ananena kuti Yobu analankhula zoona zokhudza iyeyo.​—Yobu 42:7, 8.

Chikhulupiriro chathu chimalimba tikamaona makhalidwe a Mulungu osaoneka m’zinthu zimene analenga (Onani ndime 17)

17 Yobu anazindikiranso makhalidwe ambiri a Mulungu poona zimene analenga. (Yobu 12:7-9, 13) Pa nthawi ina, Elihu komanso Yehova anagwiritsa ntchito zimene Yehovayo analenga pofuna kukumbutsa Yobu kuti anthu ndi aang’ono kwambiri poyerekezera ndi Mulungu. (Yobu 37:14; 38:1-4) Mawu a Yehova anafika Yobu pamtima ndipo modzichepetsa anauza Mulungu kuti: “Ndadziwa kuti inu mumatha kuchita zinthu zonse, ndipo palibe zimene simungakwanitse. . . . Ndikulapa m’fumbi ndi m’phulusa.”​—Yobu 42:2, 6.

18, 19. Kodi Yobu anasonyeza bwanji kuti ankadziwa bwino Yehova?

18 Kodi kudziwa bwino Mulungu kunathandiza bwanji Yobu? Yobu anamvetsa bwino mfundo za Mulungu. Iye ankadziwa kwambiri Yehova ndipo zimene ankadziwazo zinamuthandiza. Mwachitsanzo, Yobu ankadziwa kuti sanganene kuti amakonda Mulungu koma pa nthawi imodzimodziyo n’kumachitira nkhanza anzake. (Yobu 6:14) Iye sankadziona kuti ndi wapamwamba koma ankakonda ndiponso kuganizira anthu onse, kaya akhale olemera kapena osauka. Iye anati: “Kodi amene anandipanga m’mimba si amene anapanganso [iwowo]?” (Yobu 31:13-22) Apa zikuonekeratu kuti udindo komanso chuma zimene Yobu anali nazo sizinamuchititse kuti azidziona kuti ndi woposa anthu ena. Zimenezi ndi zosiyana kwambiri ndi zimene anthu ambiri a udindo komanso olemera amachita m’dzikoli.

19 Yobu ankaika Yehova pamalo oyamba ndipo sankalola kuti chilichonse chimusokoneze. Iye ankadziwa kuti akayamba kulambira mafano kapena kukonda kwambiri chuma, ndiye kuti ‘akukana Mulungu woona wakumwamba.’ (Werengani Yobu 31:24-28.) Ankaonanso kuti mwamuna ndi mkazi akakwatirana amapanga mgwirizano wopatulika pamaso pa Mulungu. Choncho iye anachita pangano ndi maso ake kuti asamasirire atsikana. (Yobu 31:1) Komatu tisaiwale kuti nthawi imeneyi Mulungu ankalola amuna kukwatira mitala. Choncho Yobu akanafuna akanatha kutenga mkazi wachiwiri. * Koma zikuoneka kuti iye ankadziwa dongosolo limene Mulungu anakhazikitsa mu Edeni ndipo ankaona kuti limeneli ndi lamulo loti azilitsatira. (Gen. 2:18, 24) Patapita zaka 1,600, Yesu ananena mfundo yomweyi ndipo anasonyeza kuti ukwati komanso kugonana ziyenera kuchitika pakati pa mwamuna mmodzi ndi mkazi mmodzi.​—Mat. 5:28; 19:4, 5.

20. Kodi kudziwa bwino Yehova kungatithandize bwanji kusankha bwino anzathu komanso zosangalatsa?

20 Kodi tingatsanzire bwanji chikhulupiriro cha Yobu? Monga tanena kale, chofunika kwambiri ndi kudziwa bwino Yehova komanso kulola kuti zimene tikudziwazo zizititsogolera pa chilichonse. Mwachitsanzo, Davide analemba kuti “Mulungu amadana kwambiri ndi aliyense wokonda chiwawa.” Anasonyezanso kuti si bwino kugwirizana ndi “anthu achinyengo.” (Werengani Salimo 11:5; 26:4.) Kodi malemba amenewa amatithandiza bwanji kudziwa maganizo a Yehova? Nanga kudziwa zimenezi kungatithandize bwanji posankha zoyenera kuika pamalo oyamba, njira yabwino yogwiritsa ntchito Intaneti, anthu ocheza nawo komanso zosangalatsa? Mayankho anu pa mafunso amenewa angakuthandizeni kudziwa ngati mumadziwadi bwino Yehova. Kuti tikhalebe osalakwa m’dziko loipali tiyenera kuphunzitsa ‘mphamvu zathu za kuzindikira’ kuti tizitha “kusiyanitsa choyenera ndi chosayenera” komanso chanzeru ndi chopanda nzeru.​—Aheb. 5:14; Aef. 5:15.

21. N’chiyani chingatithandize kuti ‘timvetse chilichonse’ chofunika kuti tizisangalatsa Atate wathu wakumwamba?

21 Nowa, Danieli ndi Yobu ankayesetsa ndi mtima wonse kuti adziwe bwino Yehova ndipo Yehovayo anawathandiza. Iye anawathandiza ‘kumvetsa chilichonse’ chofunika kuti azimusangalatsa. Anthu amenewa anapereka chitsanzo chabwino kwambiri pa nkhani yochita zinthu mwachilungamo ndipo zinthu zinkawayendera bwino. (Sal. 1:1-3) Choncho ndi bwino kudzifunsa kuti, ‘Kodi ineyo ndimadziwa bwino Yehova ngati mmene ankachitira Nowa, Danieli ndi Yobu?’ Ndipotu masiku ano ifeyo tili ndi mwayi chifukwa tikhoza kudziwa zambiri zokhudza Yehova kuposa anthu atatuwa. (Miy. 4:18) Choncho muziyesetsa kuphunzira Mawu a Mulungu mozama ndipo muziganizira kwambiri zimene mukuphunzira. Muzipemphanso Mulungu kuti akupatseni mzimu woyera. Mukatero ubwenzi wanu ndi Atate wathu wakumwamba udzalimba kwambiri ndipo zidzakuthandizani kuti muzichita zinthu mwanzeru m’dziko loipali.​—Miy. 2:4-7.

^ ndime 5 Inoki, yemwe anali agogo a bambo a Nowa, ‘ankayendanso ndi Mulungu woona.’ Koma “Mulungu anam’tenga” kutatsala zaka 69 kuti Nowa abadwe.​—Gen. 5:23, 24.

^ ndime 19 Nowa anachitanso chimodzimodzi. Iye anali ndi mkazi mmodzi ngakhale kuti kukwatira mitala kunayamba pasanapite nthawi yaitali kuchokera pamene Adamu ndi Hava anachimwa.​—Gen. 4:19.