Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

KALE LATHU

Nkhani za Onse Zinathandiza Kufalitsa Uthenga Wabwino ku Ireland

Nkhani za Onse Zinathandiza Kufalitsa Uthenga Wabwino ku Ireland

MU MAY 1910, sitima yapamadzi inafika ku Belfast m’mawa ndipo anthu angapo amene anali pamwamba pa sitimayo anaona mapiri okongola kwambiri. Musitimayi munali Charles T. Russell ndipo umenewu unali ulendo wake wa nambala 5 wopita ku Ireland. Chapatsogolo pa sitimayi panali sitima ziwiri zikuluzikulu zomwe zinkapangidwa. Sitima zake zinali Titanic ndi Olympic. * Pamalowa panali ophunzira Baibulo angapo amene ankayembekezera M’bale Russell amene ankabwera.

Zaka 20 izi zisanachitike, M’bale Russell anaganiza zoti aziyenda m’mayiko ena n’kumakafalitsa uthenga wabwino. Iye anayambira ku Ireland mu July 1891. M’bale Russell anafika pasitima ku Queenstown madzulo ndipo ayenera kuti anakumbukira zimene makolo ake ankamuuza zokhudza kwawo. Pamene Russell ndi anzake ankadutsa m’madera okongola komanso m’matauni a m’dzikoli anazindikira kuti afika m’munda mmene “mwayera kale ndipo m’mofunika kukolola.”

M’bale Russell anapita ku Ireland maulendo 7. Anthu anachita chidwi kwambiri ndi zimene anakamba pa ulendo woyamba moti maulendo enawo anthu mahandiredi, nthawi zinanso masauzande, ankapita kukamvetsera nkhani zake. Pamene ankapita ulendo wachiwiri mu May 1903, nkhani za onse zinkalengezedwa munyuzipepala. M’bale Russell amakumbukira kuti “anthu ankamvetsera mwachidwi kwambiri” nkhani yakuti “Lonjezo Lochita Kulumbirira” imene inkafotokoza za chikhulupiriro cha Abulahamu komanso madalitso amene anthu adzapeze m’tsogolo.

Russell ataona kuti m’dzikoli muli anthu ambiri ofuna kuphunzira, anakonza zoti apitekonso ulendo wachitatu. Anapita ulendo wachitatuwu mu April 1908 ndipo atangotsika sitima ku Belfast, abale 5 anamulandira. Nkhani imene anakamba inali yakuti “Ulamuliro wa Satana Udzagonjetsedwa” ndipo inali italengezedwa moti anthu pafupifupi 300 anapezekapo. Munthu wina ankatsutsa zimene Russell ankanena koma anamuyankha mwaluso pogwiritsa ntchito Malemba. Atafika ku Dublin panali munthu wina wotsutsa kwambiri dzina lake O’Connor, yemwe anali mlembi wa bungwe linalake lachipembedzo. Munthu ameneyu ankafuna kuti anthu oposa 1,000 amene anasonkhana asiye kumvetsera zimene ophunzira Baibulo ankanena. Ndiye kodi chinachitika n’chiyani?

Tiyeni tsopano tiyese kuona m’maganizo mwathu zimene zikanachitika pa nthawiyo. Munthu wina wofuna kuphunzira Baibulo waganiza zokamvetsera nkhani imene inalengezedwa munyuzipepala ya The Irish Times. Atafika akupeza kuti mipando yonse yadzaza koma kenako n’kupeza pokhala. Akumvetsera mwachidwi pamene bambo waimvi komanso wandevu akukamba nkhani atavala jekete yakuda yaitali. Bamboyo akukamba nkhani uku akuyendayenda papulatifomu komanso akusonyeza kugwirizana pakati pa malemba ndipo izi zikuthandiza munthuyo kumvetsa choonadi. Palibe zokuzira mawu koma mawu a wokamba nkhaniyo akumveka muholo yonse moti anthu akumvetsera mwachidwi kwa ola limodzi ndi hafu. Ndiyeno ikufika nthawi ya mafunso ndipo O’Connor ndi anzake akutsutsa koma bamboyo akuwayankha pogwiritsa ntchito Baibulo. Izi zikuchititsa kuti anthu awombere m’manja. Zitatha zonse, munthuyo akufika kwa Ophunzira Baibulo n’kuwauza kuti akufuna kuphunzira zambiri. Umutu ndi mmene anthu ambiri a pa nthawiyo anayambira kuphunzira choonadi.

Pa ulendo wachinayi, M’bale Russell ananyamuka ku New York mu May 1909 ndipo anatenga M’bale Huntsinger kuti akamayenda panyanja azimuuza zoti alembe munkhani za mu Nsanja ya Olonda. Atafika ku Belfast, M’bale Russell anakamba nkhani ndipo panali anthu 450. Pa anthu amenewa, anthu 100 anangoima chifukwa chosowa malo okhala.

M’bale C. T. Russell ali musitima ya Lusitania

M’baleyu anapitanso ku Ireland ulendo wa nambala 5 umene tautchula kumayambiriro uja ndipo anakambanso nkhani. Atamaliza nkhaniyo ku Dublin anayankha mafunso a munthu wina wachipembedzo wotchuka amene anabwera ndi O’Connor ndipo anthu ataona zimenezi anasangalala kwambiri. Tsiku lotsatira, Ophunzira Baibulo anakwera sitima yopita kumzinda wa Liverpool kenako anakwera sitima yaikulu yotchedwa Lusitania n’kupita ku New York. *

Nkhani ya onse imene inalengezedwa mu nyuzipepala pa May 20, 1910

Nkhani zimene M’bale Russell anakamba pa ulendo wake wa nambala 6 ndi 7 mu 1911 zinkalengezedwanso. Mu April chaka chomwechi, Ophunzira Baibulo 20 limodzi ndi anthu ena 2,000 ku Belfast, anamvetsera nkhani yakuti “Moyo Umene Tidzakhale Nawo M’tsogolo.” Nakonso ku Dublin kunakambidwa nkhani koma kunafika O’Connor ndi munthu winanso wachipembedzo amene ankafunsa mafunso. M’bale Russell anayankhanso bwino pogwiritsa ntchito Malemba ndipo anthu ankaombera m’manja. Mu October ndi November chaka chomwechi, M’bale Russell ndi anzake anafikanso m’matauni ena ndipo anthu ambiri ankabwera kudzamvetsera nkhani. O’Connor ndi anzake 100 anafika ku Dublin kuti asokoneze msonkhano koma gulu lonse limene linkamvetsera linali kumbali ya wokamba nkhani.

Ngakhale kuti M’bale Russell ndi amene ankatsogolera pokamba nkhani, iye ankadziwa kuti “ntchito yathu sidalira munthu mmodzi” chifukwa “si ya munthu koma ya Mulungu.” Nkhani za onse zomwe zinkalengezedwa zinathandiza kwambiri kuti anthu ambiri amve mfundo za m’Baibulo. Zotsatira zake n’zakuti nkhanizi zinathandiza kuti uthenga wabwino ufalitsidwe ndipo mipingo inakhazikitsidwa m’mizinda yambiri ku Ireland.​—Nkhaniyi yachokera ku Britain.

^ ndime 3 Sitima ya Titanic inamira pasanathe zaka ziwiri.

^ ndime 9 Sitima ya Lusitania inaphulitsidwa mu May 1915 chakum’mwera kwa Ireland.