Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YOPHUNZIRA 15

Zimene Tingaphunzire pa Mawu Omaliza a Yesu

Zimene Tingaphunzire pa Mawu Omaliza a Yesu

“Uyu ndiye Mwana wanga wokondedwa, amene ndikukondwera naye, muzimumvera.”​—MAT. 17:5.

NYIMBO NA. 17 “Ndikufuna”

ZIMENE TIPHUNZIRE *

1-2. Kodi zinthu zinali bwanji pamene Yesu analankhula mawu ake omaliza?

NDI MASANA pa Nisani 14, mu 33 C.E. Pambuyo poti wanamiziridwa komanso kuweruzidwa pamlandu womwe sanapalamule, Yesu akunyozedwa, kuzunzidwa kwambiri ndipo kenako akukhomereredwa pamtengo wozunzikirapo. Amukhomerera ndi misomali imene yaboola manja ndi mapazi ake. Kuti alankhule, ngakhale kupuma kumene akumva ululu kwambiri. Komabe ayenera kulankhula, chifukwa pali zinthu zofunika kwambiri zoti anene.

2 Tsopano tiyeni tikambirane mawu amene Yesu analankhula atatsala pang’ono kufa pamtengo wozunzikirapo komanso zimene tingaphunzirepo pa mawu amenewa. M’mawu ena, tiyeni ‘timumvere.’​—Mat. 17:5.

“ATATE, AKHULULUKIRENI”

3. Kodi Yesu ankanena za ndani pamene ananena kuti: “Atate, akhululukireni”?

3 Kodi Yesu ananena kuti chiyani? Atamukhomerera pamtengo wozunzikirapo, Yesu anapemphera kuti: “Atate, akhululukireni.” Kodi pamenepa iye ankafuna kuti Atate ake akhululukire ndani? Tikupeza yankho pa mawu otsatira amene analankhula akuti: “Sakudziwa chimene akuchita.” (Luka 23:33, 34) Pamenepa Yesu ayenera kuti ankanena za asilikali a Chiroma omwe anakhomerera manja ndi mapazi ake ndi misomali. Iwo sankadziwa kuti iye anali ndani kwenikweni. Mwina iye ankanenanso anthu ena m’khamu la anthulo omwe ankafuula nawo kuti iye apachikidwe, koma pambuyo pake iwo anadzayamba kumukhulupirira. (Mac. 2:36-38) Yesu sanalole kuti zinthu zopanda chilungamo zomwe zinamuchitikira zimuchititse kukhala wokwiya komanso kulephera kukhululukira ena. (1 Pet. 2:23) M’malomwake iye anapempha Yehova kuti akhululukire anthu amene anamupha.

4. Kodi tikuphunzira chiyani pa zimene Yesu anachita pokhala wofunitsitsa kukhululukira anthu amene ankamutsutsa?

4 Kodi tingaphunzire chiyani pa mawu a Yesu? Mofanana ndi Yesu, tiyenera kukhala okonzeka kukhululukira ena. (Akol. 3:13) Anthu ena kuphatikizapo achibale athu, angamatitsutse chifukwa samvetsa zimene timakhulupirira komanso mmene timachitira zinthu. Iwo akhoza kutinenera zabodza, kutichititsa manyazi pamaso pa anthu ena, kutiwonongera mabuku ngakhalenso kutiopseza kuti atichitira zinthu zankhanza. M’malo mosunga chakukhosi tingam’pemphe Yehova kuti awathandize kuti tsiku lina nawonso adzaphunzire choonadi. (Mat. 5:44, 45) Nthawi zina zingativute kukhululuka makamaka ngati anthu ena anatichitira zinthu zoipa kwambiri. Koma ngati sitingakhululuke n’kumangokhalabe okwiya, tingakhale tikudzivulaza tokha. Mlongo wina anafotokoza kuti: “Ndinazindikira kuti kukhululuka si kutanthauza kuti zimene ena anakuchitira n’zoyenera kapenanso umangofuna kuti anthu ena azikuchitira zoipa. Koma kumangotanthauza kuti wasankha kuti usasunge chakukhosi.” (Sal. 37:8) Tikasankha kukhululuka, zimasonyeza kuti sitikufuna kumangopitirizabe kukhala okwiya chifukwa cha zinthu zoipa zimene ena anatichitira.​—Aef. 4:31, 32.

“IWE UDZAKHALA NDI INE M’PARADAISO”

5. Kodi Yesu analonjeza chiyani wachifwamba amene anapachikidwa naye limodzi, ndipo n’chifukwa chiyani anamulonjeza zimenezi?

5 Kodi Yesu ananena kuti chiyani? Pamene ankaphedwa, Yesu anapachikidwa limodzi ndi achifwamba ena awiri. Poyamba, iwo ankamunyoza nawo. (Mat. 27:44) Koma kenako mmodzi wa awiriwa anasintha maganizo. Iye anazindikira kuti Yesu “sanalakwe chilichonse.” (Luka 23:40, 41) Koma chofunika kwambiri n’chakuti, iye anasonyeza kuti ankakhulupirira kuti Yesu adzaukitsidwa komanso kuti adzalamulira monga mfumu tsiku lina. Iye anamuuza Yesu kuti: “Yesu, mukandikumbukire mukakalowa mu ufumu wanu.” (Luka 23:42) Apatu munthuyu anasonyeza kuti anali ndi chikhulupiriro champhamvu. Poyankha Yesu anamuuza kuti: “Ndithu ndikukuuza lero, iwe udzakhala ndi ine [osati mu Ufumu, koma] m’Paradaiso.” (Luka 23:43) Pogwiritsa ntchito mawu akuti, “iwe” komanso “ine” Yesu anasonyeza kuti ankamuganizira kwambiri munthuyu. Yesu analankhula mawu opatsa chiyembekezo kwa wachifwambayo chifukwa ankadziwa kuti Atate wake ndi wachifundo.​—Sal. 103:8.

6. Kodi tikuphunzira chiyani pa mawu amene Yesu anauza wachifwamba wina?

6 Kodi tikuphunzira chiyani pa mawu a Yesu? Yesu ndi wofanana kwambiri ndi Atate wake. (Aheb. 1:3) Yehova ndi wokonzeka kutikhululukira komanso kutisonyeza chifundo ngati tikudzimvera chisoni chifukwa cha zinthu zoipa zimene tinachita m’mbuyo komanso ngati timakhulupirira kuti iye angatikhululukire machimo athu kudzera m’magazi a Mwana wake Yesu Khristu. (1 Yoh. 1:7) Anthu ena zimawavuta kukhulupirira kuti Yehova angawakhululukire machimo amene anachita m’mbuyo. Ngati inunso mumamva choncho nthawi zina, taganizirani izi: Yesu atatsala pang’ono kuphedwa, anasonyeza chifundo kwa wachifwamba yemwe anali atangoyamba kumene kumukhulupirira. Choncho Yehova amachitira chifundo atumiki ake okhulupirika omwe amayesetsa kumvera malamulo ake.​—Sal. 51:1; 1 Yoh. 2:1, 2.

“UYU AKHALA MWANA WANU. . . . AWA AKHALA MAYI AKO”

7. Mogwirizana ndi Yohane 19:26, 27, kodi Yesu anauza chiyani Mariya ndi Yohane, nanga n’chifukwa chiyani anawauza zimenezi?

7 Kodi Yesu ananena kuti chiyani? (Werengani Yohane 19:26, 27.) Yesu ankadera nkhawa mayi ake omwe ayenera kuti pa nthawiyi anali amasiye. Abale ake akanatha kuwapezera mayi akewo zinthu zofunika pa moyo. Koma kodi ndani akanawathandiza kuti akhalebe okhulupirika kwa Yehova? Palibe umboni wosonyeza kuti pa nthawiyi abale akewa anali atayamba kumukhulupirira. Komabe Yohane anali mtumwi wokhulupirika komanso mnzake wapamtima wa Yesu. Yesu ankaona anthu amene ankalambira nawo Yehova ngati anthu a m’banja lake. (Mat. 12:46-50) Choncho chifukwa chakuti iye ankakonda kwambiri mayi ake, anapereka udindo wowasamalira kwa Yohane chifukwa ankadziwa kuti iye angawathandize kupitirizabe kutumikira Yehova. Yesu anauza mayi ake kuti: “Uyu akhala mwana wanu.” Ndipo anauza Yohane kuti: “Awa akhala mayi ako.” Kuyambira tsiku limenelo, Yohane anakhala ngati mwana wa Mariya ndipo iye ankawasamalira ngati mayi ake enieni. Yesu anasonyeza chikondi chachikulu kwa mayi ake okondedwawa, omwe anamusamalira kuchokera pa nthawi imene anabadwa ndiponso amene anaima chapafupi pa nthawi imene ankaphedwa.

8. Kodi tingaphunzire chiyani pa mawu amene Yesu anauza Mariya ndi Yohane?

8 Kodi tikuphunzira chiyani pa mawu a Yesu? Ubwenzi wathu ndi Akhristu anzathu ungathe kukhala wolimba kwambiri kuposa ubwenzi umene tingakhale nawo ndi achibale athu. Achibale athu angamatitsutse kapena kutikana koma Yesu analonjeza kuti tikapitiriza kukhala pa ubwenzi ndi Yehova komanso kukhalabe m’gulu lake tidzapeza zochuluka “kuwirikiza maulendo 100” kuposa zimene tingataye. Tingapeze ambiri omwe angakhale ngati ana athu, mayi athu komanso bambo athu. (Maliko 10:29, 30) Kodi mumamva bwanji chifukwa chokhala m’banja la Yehova limene anthu ake amagwirizana chifukwa choti amakhulupirira komanso amakonda Yehova ndi anthu anzawo?​—Akol. 3:14; 1 Pet. 2:17.

“MULUNGU WANGA, MWANDISIYIRANJI INE?”

9. Kodi tikuphunzira chiyani pa mawu a Yesu a pa Mateyu 27:46?

9 Kodi Yesu ananena kuti chiyani? Atatsala pang’ono kufa, Yesu ananena kuti: “Mulungu wanga, Mulungu wanga, mwandisiyiranji ine?” (Mat. 27:46) Baibulo silifotokoza chifukwa chake Yesu ananena zimenezi. Koma tiyeni tione zimene tingaphunzire pa mawu amenewa. Ponena mawuwa Yesu anakwaniritsa ulosi wopezeka pa Salimo 22:1. * Komanso mawuwa akusonyeza kuti Yehova ‘sanam’tchinge’ kapena kum’teteza Mwana wakeyu. (Yobu 1:10) Yesu ankadziwa kuti Atate ake analola kuti adani ake amuyese mokwanira mpaka imfa yake, ndipo palibe munthu amene anakumana ndi mayesero amene iye anakumana nawo. Kuonjezera pamenepo, mawuwa akusonyeza kuti Yesu sanapalamule mlandu uliwonse woti mpaka ankafunika kuphedwa.

10. Kodi tingaphunzire chiyani pa mawu amene Yesu anauza Atate wake?

10 Kodi tikuphunzira chiyani pa mawu a Yesu? Chinthu chimodzi chimene tikuphunzirapo ndi chakuti sitimayembekezera kuti Yehova azititeteza kuti tisakumane ndi mavuto amene angayese chikhulupiriro chathu. Mofanana ndi Yesu, yemwe anayesedwa mokwanira ifenso tizikhala okonzeka kukhalabe okhulupirika ngakhale pamene anthu akufuna kutipha. (Mat. 16:24, 25) Komabe tiyenera kukhala otsimikiza kuti Mulungu sadzatisiya kuti tiyesedwe mpaka kufika poti sitingathenso kupirira. (1 Akor. 10:13) Chinthu china chimene tikuphunzirapo ndi chakuti mofanana ndi Yesu, ifenso tingachitiridwe zinthu zopanda chilungamo. (1 Pet. 2:19, 20) Anthu amene amatitsutsa angatichitire zinthu zopanda chilungamo osati chifukwa choti talakwitsa zinazake koma chifukwa chakuti sitili mbali ya dzikoli komanso timachitira umboni choonadi. (Yoh. 17:14; 1 Pet. 4:15, 16) Yesu ankamvetsa chifukwa chake Yehova analola kuti akumane ndi mavuto. Koma mosiyana ndi Yesu, atumiki ena okhulupirika a Yehova amadabwa kuti n’chifukwa chiyani iye amalola kuti iwo akumane ndi zinthu zina. (Hab. 1:3) Koma Mulungu wathu yemwe ndi wachifundo komanso woleza mtima amamvetsa ndipo saona kuti atumiki akewo alibe chikhulupiriro, koma amangofunika kuwalimbikitsa.​—2 Akor. 1:3, 4.

“NDIKUMVA LUDZU”

11. N’chifukwa chiyani Yesu analankhula mawu a pa Yohane 19:28?

11 Kodi Yesu ananena kuti chiyani? (Werengani Yohane 19:28.) Kodi n’chifukwa chiyani Yesu ananena kuti: “Ndikumva ludzu”? Iye ananena zimenezi “pofuna kuti Malemba akwaniritsidwe.” Zimene ananenazi ndi ulosi wopezeka pa Salimo 22:15, pomwe pamati: “Mphamvu yanga yauma gwaa ngati phale. Lilime langa lamamatira ku nkhama zanga.” Pambuyo poti Yesu wakumana ndi mavuto osiyanasiyana kuphatikizaponso kumva ululu pamtengo wozunzikirapo, iye ayenera kuti analidi ndi ludzu choncho ankafunika munthu wina kuti amuthandize kuti athetse ludzu lakelo.

12. Kodi tikuphunzira chiyani pa mawu a Yesu akuti: “Ndikumva ludzu”?

12 Kodi tikuphunzira chiyani pa mawu a Yesu? Yesu sankaona kuti aoneka wofooka akafotokoza mmene ankamvera. Ifenso sitiyenera kuona choncho. N’kutheka kuti nthawi zambiri sitimakonda kuuza anthu ena zimene tikufunikira. Koma ngati pa nthawi ina titadzaona kuti tikufunika thandizo, tisadzanyalanyaze kupempha ena kuti atithandize. Mwachitsanzo, ngati ndife wachikulire kapena tikudwala, tingapemphe mnzathu kuti atiperekeze kukagula zinthu kapena kukaonana ndi adokotala. Ngati takhumudwa kapena kufooka ndi zinazake, tizifotokozera mkulu kapena Mkhristu wolimba mwauzimu n’cholinga choti atimvetsere komanso kutilimbikitsa ndi “mawu abwino.” (Miy. 12:25) Tizikumbukira kuti abale ndi alongo athu amatikonda ndipo amafuna kutithandiza tikakumana ndi mavuto. (Miy. 17:17) Koma si kuti iwo amadziwa zimene zili m’maganizo mwathu. Iwo sangadziwiretu ngati tikufunika kuti munthu winawake atithandize pokhapokha ngati tawafotokozera.

“NDAKWANIRITSA CHIFUNIRO CHANU!”

13. Kodi Yesu anakwaniritsa zinthu ziti chifukwa chokhalabe wokhulupirika mpaka imfa yake?

13 Kodi Yesu ananena kuti chiyani? Cha m’ma 3 koloko masana pa Nisani 14, Yesu anafuula kuti: “Ndakwaniritsa chifuniro chanu!” (Yoh. 19:30) Mawu amenewa akusonyeza kuti kutangotsala kanthawi kochepa kuti afe, Yesu anaona kuti wakwaniritsa zonse zimene Yehova ankafuna kuti achite. Chifukwa choti anakhalabe wokhulupirika mpaka imfa yake, Yesu anakwaniritsa zinthu zingapo. Choyamba, iye anasonyeza kuti Satana ndi wabodza. Yesu anasonyeza kuti munthu wangwiro akhoza kukhalabe wokhulupirika ngakhale Satana atamuyesa chotani. Chachiwiri, Yesu anapereka moyo wake monga dipo. Chifukwa chakuti iye anapereka moyo wake, zinakhala zotheka kuti anthu omwe si angwiro akhale pa ubwenzi ndi Mulungu komanso kukhala ndi chiyembekezo chodzapeza moyo wosatha. Chachitatu, Yesu anasonyeza kuti Yehova ndiye woyenera kulamulira ndipo zimenezi zinathandiza kuti dzina la Atate wake lilemekezedwe.

14. Kodi tiyenera kuyesetsa kuchita chiyani tsiku lililonse? Fotokozani.

14 Kodi tikuphunzira chiyani pa mawu a Yesu? Tiyenera kuyesetsa kuti tizikhala okhulupirika tsiku lililonse. Taganizirani zimene ananena M’bale Maxwell Friend, yemwe anali mlangizi wa Sukulu ya Giliyadi Yophunzitsa Baibulo. Pofotokoza za kukhala wokhulupirika, pamene ankakamba nkhani pamsonkhano wina, iye anati: “Musamazengereze kuti mudzachita mawa zinthu zimene muyenera kuchita kapena kulankhula lero. Kodi mukudziwa kuti mukhala ndi moyo mpaka mawa? Tsiku lililonse muziliona kuti ndi mwayi wanu womaliza kuti musonyeze kuti ndinu wokhulupirika komanso woyenera kudzalandira moyo wosatha.” Choncho tiyeni tiziona tsiku lililonse ngati mwayi wathu womaliza wosonyeza kuti ndife okhulupirika. Ndiye ngati titatsala pang’ono kufa, tingathe kunena kuti, “Yehova, ndayesetsa kuchita zomwe ndingathe kuti ndikhale wokhulupirika kwa inu, kuti ndisonyeze kuti Satana ndi wabodza komanso kuyeretsa dzina lanu ndi kusonyeza kuti ndinu woyenera kulamulira.”

“NDIKUIKIZA MZIMU WANGA M’MANJA MWANU”

15. Mogwirizana ndi Luka 23:46, kodi Yesu sankakayikira chiyani?

15 Kodi Yesu ananena kuti chiyani? (Werengani Luka 23:46.) Yesu ananena motsimikiza kuti: “Atate, ndikuikiza mzimu wanga m’manja mwanu.” Yesu ankadziwa kuti Yehova ndi amene angatheketse kuti iye adzakhalenso ndi moyo ndipo sankakayikira kuti Atate wake adzamukumbukira.

16. Kodi tikuphunzira chiyani pa zimene zinachitikira wachinyamata wina wa Mboni?

16 Kodi tikuphunzira chiyani pa mawu a Yesu? Muzipitiriza kudalira Yehova ngakhale pamene zikuoneka kuti moyo wanu uli pangozi. Kuti muthe kuchita zimenezi, muyenera ‘kukhulupirira Yehova ndi mtima wanu wonse.’ (Miy. 3:5) Taganizirani chitsanzo cha wachinyamata wina wa Mboni, wazaka 15, dzina lake Joshua yemwe ankadwala matenda oopsa. Iye anakana kulandira thandizo lamankhwala lomwe linali losagwirizana ndi malamulo a Mulungu. Atatsala pang’ono kufa, iye anauza mayi ake kuti: “Amayi, Yehova andisamalira. . . . Sindikukayikira ngakhale pang’ono kuti Yehova adzandiukitsa. Akudziwa zimene zili mumtima mwanga komanso mmene ndikumvera ndipo ndimamukonda kwambiri.” Aliyense angachite bwino kudzifunsa kuti, ‘Kodi nditakumana ndi mayesero aakulu omwe mwina angachititse kuti ndife, ndidzadalira Yehova komanso kukhulupirira kuti adzandikumbukira?’

17-18. Kodi taphunzira chiyani? (Onaninso bokosi lakuti, “ Zimene Tingaphunzire pa Mawu Omaliza a Yesu.”)

17 Pali mfundo zofunika zambiri zimene tingaphunzire pa mawu omaliza a Yesu. Mwachitsanzo, taona kufunika koti tizikhululukira ena komanso kumakhulupirira kuti Yehova adzatikhululukira. Tilinso ndi abale ndi alongo mumpingo omwe ndi okonzeka kutithandiza. Koma pamene tikufunikira thandizo, tiyenera kupempha ena kuti atithandize. Tikudziwa kuti Yehova adzatithandiza kupirira mayesero alionse amene tingakumane nawo. Ndiponso taona kufunika koti tiziona tsiku lililonse ngati mwayi wathu womaliza wosonyeza kuti ndife okhulupirika kwa Yehova, n’kumakhulupirira kuti iye adzatiukitsa ngati tingamwalire.

18 Kunena zoona, mawu amene Yesu analankhula atatsala pang’ono kufa pamtengo wozunzikirapo angatiphunzitse zambiri. Tikamagwiritsa ntchito zimene taphunzirazi, ndiye kuti tikumvera zimene Yehova ananena zokhudza Mwana wake kuti: “Muzimumvera.”​—Mat. 17:5.

NYIMBO NA. 126 Khalani Maso, Limbani M’chikhulupiriro, Khalani Amphamvu

^ ndime 5 Mogwirizana ndi Mateyu 17:5, Yehova amafuna kuti tizimvera Mwana wake. Munkhaniyi tikambirana zimene tikuphunzirapo pa mawu omaliza amene Yesu analankhula atatsala pang’ono kufa pamtengo wozunzikirapo.

^ ndime 9 Kuti mudziwe zifukwa zina zimene zinachititsa Yesu kutchula mawu a mu ulosi wa pa Salimo 22:1, onani nkhani yakuti “Mafunso Ochokera kwa Owerenga,” yomwe ili m’magaziniyi.