Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 NKHANI YOPHUNZIRA 6

Pitirizani Kukhala ndi Mtima Wosagawanika

Pitirizani Kukhala ndi Mtima Wosagawanika

“Mpaka ine kumwalira, sindidzasiya kukhala ndi mtima wosagawanika.”​YOBU 27:5.

NYIMBO NA. 34 Kuyenda ndi Mtima Wosagawanika

ZIMENE TIPHUNZIRE *

1. Kodi a Mboni atatu amene tawafotokoza mundimeyi asonyeza bwanji kuti ndi okhulupirika kwa Yehova?

TAGANIZIRANI za nkhani zitatu zoyerekezera izi. (1) Mlongo wachitsikana ali kusukulu ndipo mphunzitsi wake wapempha ana onse m’kalasimo kuti achite zinthu zina zokhudza holide inayake. Mlongoyo akudziwa kuti holide imeneyi sisangalatsa Mulungu ndipo akukana mwaulemu. (2) M’bale wachinyamata, yemwe ndi wamanyazi, akulalikira kunyumba ndi nyumba. Iye wazindikira kuti mnzake wakusukulu, yemwe amanyoza a Mboni za Yehova, amakhala kunyumba yotsatira. Koma mnyamatayo akupitabe kunyumbayo. (3) M’bale wina akugwira ntchito mwakhama kuti apezere banja lake zofunika pa moyo ndipo tsiku lina abwana ake amupempha kuti achite zinthu zina zachinyengo. Ngakhale kuti akhoza kuchotsedwa ntchito, m’baleyo akufotokozera abwana akewo kuti ayenera kuchita zinthu moona mtima ndiponso kumvera malamulo a boma chifukwa ndi zimene Mulungu amafuna.​—Aroma 13:1-4; Aheb. 13:18.

2. Kodi tikambirana mafunso atatu ati, nanga n’chifukwa chiyani?

2 Kodi anthu atatuwa asonyeza khalidwe liti? Mwina mwaona kuti asonyeza makhalidwe angapo monga kulimba mtima komanso kuona mtima. Koma pali khalidwe lina lofunika kwambiri limene asonyeza lomwe ndi kukhala ndi mtima wosagawanika. Aliyense wasonyeza kuti ndi wokhulupirika kwa Yehova. Tikutero chifukwa chakuti wakana kuchita zinthu zosemphana ndi mfundo za Mulungu. Iwo akwanitsa kukana chifukwa chokhala ndi mtima wosagawanika. Yehova akhoza kusangalala kwambiri ndi zimene aliyense wa anthuwa anachita. Nafenso timafuna kusangalatsa Atate wathu wakumwamba. Choncho tiyeni tikambirane mafunso atatu awa: Kodi mawu oti mtima wosagawanika amatanthauza chiyani? N’chifukwa chiyani tiyenera kukhala ndi  mtima umenewu? Nanga tingatani kuti tipitirize kukhala ndi mtimawu m’masiku ovutawa?

KODI MAWU OTI MTIMA WOSAGAWANIKA AMATANTHAUZA CHIYANI?

3. (a) Kodi tingasonyeze bwanji kuti tili ndi mtima wosagawanika? (b) N’chiyani chimasonyeza kuti tonsefe timakonda zinthu zathunthu zopanda vuto lililonse?

3 Kodi atumiki a Mulungufe timasonyeza bwanji kuti tili ndi mtima wosagawanika? Timasonyeza zimenezi tikamakonda Mulungu ndi mtima wathu wonse komanso tikamaika zofuna zake pamalo oyamba posankha zochita nthawi zonse. Mawu amene anamasuliridwa m’Baibulo kuti “mtima wosagawanika” angatanthauze chinthu chathunthu kapena chopanda vuto lililonse. Mwachitsanzo, Aisiraeli ankapereka nyama kwa Yehova ndipo Chilamulo chinkanena kuti nyamazi ziyenera kukhala zopanda chilema chilichonse. * (Lev. 22:21, 22) Sankayenera kupereka nyama yopanda mwendo, khutu kapena diso. Komanso nyamayo inkayenera kukhala yopanda matenda. Yehova ankafuna kuti nyamayo ikhale yabwinobwino, yathunthu komanso yopanda vuto lililonse. (Mal. 1:6-9) Zimenezi ndi zomveka. Paja anthufe tikamagula chinthu, kaya chikhale chipatso, buku kapena chida chinachake, timafuna kuti chikhale ndi mbali zake zonse komanso chisakhale ndi vuto lililonse. Timafuna kuti chikhale chabwinobwino komanso chathunthu. Izi n’zimene Yehova amafunanso pa nkhani ya mtima wathu. Iye amafuna kuti tizimukonda ndi mtima wathunthu kapena kuti wosagawanika.

4. N’chifukwa chiyani tikhoza kukhala ndi mtima wosagawanika ngakhale kuti si ife angwiro? (b) Mogwirizana ndi Salimo 103:12-14, kodi Yehova amayembekezera kuti tizitani?

4 Popeza kuti si ife angwiro, kodi tiziganiza kuti sitingakhale ndi mtima wosagawanika? Mwina tingaganize choncho chifukwa choona kuti tili ndi mavuto ambiri ndipo timalakwitsa zinthu zina. Koma tiyeni tikambirane zifukwa ziwiri zosonyeza kuti tikhoza kukhala ndi mtima wosagawanika pamaso pa Mulungu. Choyamba, Yehova saganizira kwambiri zinthu zimene timalakwitsa. Paja Mawu ake amanena kuti: “Mukanakhala kuti mumayang’anitsitsa zolakwa, ndani akanaima pamaso panu, inu Yehova?” (Sal. 130:3) Iye amadziwa kuti si ife angwiro ndipo amatikhululukira ndi mtima wonse. (Sal. 86:5) Chachiwiri, Yehova amadziwa zimene sitingakwanitse kuchita ndipo amayembekezera kuti tizingochita zimene tingakwanitse. (Werengani Salimo 103:12-14.) Ndiye kodi tingatani kuti tikhale athunthu komanso opanda vuto lililonse pamaso pa Mulungu?

5. Kodi kukonda Mulungu kumatithandiza bwanji kukhala ndi mtima wosagawanika?

5 Kukonda Mulungu n’kumene kungatithandize kuti tikhale ndi mtima wosagawanika. Tiyenera kukonda Mulungu ndiponso kukhala odzipereka kwa iye ndi mtima wathu wonse. Tikamatero ngakhale titakumana ndi mayesero, tidzakhala ndi mtima wosagawanika komanso tidzakhala okhulupirika kwa Yehova. (1 Mbiri 28:9; Mat. 22:37) Taganiziraninso za anthu amene tawatchula kumayambiriro aja. N’chifukwa chiyani anachita zimene zija? Kodi mtsikana uja ankadana ndi kuchita zinthu zosangalatsa kusukulu? Kapena kodi mnyamata uja ankafuna kuti mnzake amuseke mu utumiki? Nanga bambo uja ankafuna kuti achotsedwe ntchito? Ayi. Koma onse amadziwa mfundo za Yehova ndipo amafuna kuchita zimene zimamusangalatsa. Chifukwa chomukonda amaika zofuna zake pamalo oyamba posankha zochita. Ndipo pochita zimenezi amasonyeza kuti ali ndi mtima wosagawanika.

 N’CHIFUKWA CHIYANI TIYENERA KUKHALA NDI MTIMA WOSAGAWANIKA?

6. (a) N’chifukwa chiyani tiyenera kukhala ndi mtima wosagawanika? (b) Kodi Adamu ndi Hava anasonyeza bwanji kuti analibe mtima wosagawanika?

6 Tonsefe tiyenera kukhala ndi mtima wosagawanika chifukwa chakuti Satana amatsutsa Yehova komanso ifeyo. Mngelo woipa ameneyu anadzipangitsa yekha kukhala Satana, kapena kuti “Wotsutsa.” M’munda wa Edeni, iye anayesetsa kuipitsa mbiri yabwino ya Yehova ponena zinthu zosonyeza kuti Mulungu ndi woipa, wodzikonda komanso wabodza. N’zomvetsa chisoni kuti Adamu ndi Hava anasankha kumvera Satana osati Yehova. (Gen. 3:1-6) Mu Edeni anali ndi zinthu zambiri zimene zikanawathandiza kukonda kwambiri Yehova. Koma pamene Satana anawayesa, anasonyeza kuti sankakonda Yehova ndi mtima wathunthu kapena kuti ndi mtima wonse. Patapita nthawi, Satana anatsutsanso zoti anthu angakhalebe okhulupirika kwa Yehova Mulungu chifukwa chomukonda. Tingati anakayikira zoti anthu angapitirize kukhala ndi mtima wosagawanika. Satana anayambitsa nkhani imeneyi munthawi ya Yobu.

7. Malinga ndi Yobu 1:8-11, kodi Yehova ankamuona bwanji Yobu, nanga Satana ankafuna kuchita chiyani?

7 Yobu anakhala ndi moyo pa nthawi imene Aisiraeli anali ku Iguputo ndipo pa nthawiyo panalibe munthu wina wokhulupirika kwambiri ngati iyeyo. Iye sanali wangwiro ndipo ankalakwitsa zinthu zina ngati ifeyo. Koma Yehova ankamukonda kwambiri chifukwa anali ndi mtima wosagawanika. Zikuoneka kuti Satana anali atatsutsa kale zoti anthu angakhalebe okhulupirika kwa Yehova. Choncho Yehova anauza Satana kuti aone zimene Yobu ankachita. Zochita za Yobu zinasonyeza kuti Satana ndi wabodza. Ndiye Satana anafuna kuti ayese Yobu  kuti aone ngati angakhalebe wokhulupirika. Yehova ankakhulupirira Yobu ndipo analola kuti Satana amuyese.​—Werengani Yobu 1:8-11.

8. Kodi Satana anabweretsera Yobu mavuto otani?

8 Satana ndi wankhanza komanso wopha anthu. Iye anawononga chuma cha Yobu, kuipitsa mbiri yake komanso kupha atumiki ake. Satana anaphanso ana ake onse 10. Kenako anamudwalitsa pochititsa kuti atuluke zilonda thupi lonse. Mkazi wa Yobu anasokonezeka maganizo moti anamuuza kuti atukwane Mulungu kuti afe. Nayenso Yobu ankalakalaka atangofa koma anakhalabe wokhulupirika. Kenako Satana anapeza njira ina yomuyesera. Iye anagwiritsa ntchito anzake atatu a Yobu. Anthuwa anabwera kudzaona Yobu ndipo anakhala naye masiku angapo koma sanamulimbikitse. M’malomwake ankangolankhula mopanda chifundo ndiponso kumudzudzula. Iwo ananena kuti Mulungu ndi amene ankamubweretsera mavutowo ndipo kukhulupirika kwake analibe nako ntchito. Iwo anafika posonyeza kuti Yobu ndi munthu woipa moti m’pomveka kuti akukumana ndi mavutowo.​—Yobu 1:13-22; 2:7-11; 15:4, 5; 22:3-6; 25:4-6.

9. Kodi Yobu anachita chiyani atakumana ndi mayesero?

9 Kodi Yobu anatani atakumana ndi mayesero onsewa? N’zoona kuti analakwitsa zinthu zina chifukwa sanali wangwiro. Paja anapsa mtima n’kudzudzula anzakewo ndipo yekha anavomereza kuti analankhula zopanda pake. Komanso ankaikira kumbuyo kwambiri chilungamo chake osati cha Mulungu. (Yobu 6:3; 13:4, 5; 32:2; 34:5) Ngakhale zinali choncho, Yobu anapitirizabe kukhala wokhulupirika kwa Yehova Mulungu. Anakana kukhulupirira mabodza amene anzake achinyengowo ananena. Paja iye ananena kuti: “Inetu sindingayerekeze n’komwe kunena kuti amuna inu ndinu olungama. Mpaka ine kumwalira, sindidzasiya kukhala ndi mtima wosagawanika.” (Yobu 27:5) Apatu Yobu anasonyeza kuti anali wotsimikiza mtima kuti akhalebe wokhulupirika kwa Mulungu ndipo ifenso tingachite chimodzimodzi.

10. Kodi zimene Satana ananena potsutsa Yobu zimakukhudzani bwanji?

10 Satana amatsutsanso zoti aliyense wa ife angapitirize kukhala ndi mtima wosagawanika. Kodi zimenezi zimakukhudzani bwanji inuyo? Tingati Satana amanena kuti simukonda kwenikweni Yehova Mulungu, mudzasiya kumutumikira moyo wanu ukadzakhala pa ngozi komanso simungapitirize kukhala ndi mtima wosagawanika. (Yobu 2:4, 5; Chiv. 12:10) Kodi mumamva bwanji mukaganizira zimenezi? Muyenera kuti mumakhumudwa. Koma taganizirani mfundo iyi: Yehova amakukhulupirirani kwambiri moti amalola kuti Satana akuyeseni. Iye amadziwa kuti mukhoza kukhalabe ndi mtima wosagawanika ndipo mudzasonyeza kuti Satana ndi wabodza. Komanso Yehova walonjeza kuti adzakuthandizani kuchita zimenezi. (Aheb. 13:6) Kunena zoona, ndi mwayi waukulu kwambiri kuti Yehova amatikhulupirira chonchi. Kukhala ndi mtima wosagawanika n’kofunika kwambiri. Zili choncho chifukwa timasonyeza kuti Satana ndi wabodza, timalemekeza dzina labwino la Atate wathu komanso timasonyeza kuti tili kumbali ya ulamuliro wake. Koma kodi n’chiyani chingatithandize kukhala ndi mtima wosagawanika?

KODI TINGATANI KUTI TIKHALEBE NDI MTIMA WOSAGAWANIKA?

11. Kodi tingaphunzire chiyani pa chitsanzo cha Yobu?

11 Satana akuyesetsa kwambiri kusokoneza anthu a Mulungu ‘m’masiku otsiriza’ ano. (2 Tim. 3:1) Ndiye kodi tingatani kuti tikhalebe ndi mtima wosagawanika m’nthawi yovutayi? Chitsanzo cha Yobu chingatithandizenso pa nkhaniyi. Ngakhale asanakumane ndi mayesero, Yobu anasonyeza kuti anali ndi mtima wosagawanika. Tiyeni tikambirane mfundo zitatu  zimene tingaphunzire kwa Yobu pa nkhani yokhala ndi mtima wosagawanika.

Kodi tingatani kuti tikhalebe ndi mtima wosagawanika? (Onani ndime 12) *

12. (a) Malinga ndi Yobu 26:7, 8, 14, n’chiyani chinathandiza Yobu kuti azilemekeza kwambiri Yehova? (b) Kodi tingatani kuti tizilemekeza kwambiri Mulungu?

12 Yobu ankalemekeza kwambiri Yehova ndipo izi zinamuthandiza kuti azikonda kwambiri Yehovayo. Iye ankaganizira kwambiri zinthu zodabwitsa zimene Yehova analenga. (Werengani Yobu 26:7, 8, 14.) Yobu ankagoma kwambiri akaganizira za dziko lapansi, mlengalenga, mitambo komanso mabingu. Koma ankazindikiranso kuti ankangodziwa zochepa zokha zokhudza zinthu zambiri zimene Mulungu analenga. Iye ankayamikiranso kwambiri mawu a Mulungu moti ananena kuti: “Ndasunga mosamala mawu a pakamwa pake.” (Yobu 23:12) Yobu ankalemekeza kwambiri Yehova. Iye ankakonda kwambiri Atate wake ndipo ankafunitsitsa kumusangalatsa. Zimenezi zinamuthandiza kukhala ndi mtima wosagawanika. Tiyenera kutengera chitsanzo chake. Ifeyo timadziwa zambiri zokhudza chilengedwe kuposa zimene anthu ankadziwa nthawi ya Yobu. Komanso tili ndi Baibulo lomwe limatithandiza kudziwa bwino Yehova. Zimene timaphunzira zokhudza Yehova zimatigometsa komanso zimatithandiza kuti tizimulemekeza kwambiri. Tikamachita zimenezi tidzamukonda kwambiri, tidzamumvera komanso tidzakhala ofunitsitsa kukhalabe ndi mtima wosagawanika.​—Yobu 28:28.

Tingakhalebe ndi mtima wosagawanika tikamakana kuona zolaula (Onani ndime 13) *

13-14. (a) Mogwirizana ndi Yobu 31:1, kodi Yobu anasonyeza bwanji kuti anali womvera? (b) Kodi tingatsanzire bwanji Yobu?

13 Kumvera Yehova kunathandiza Yobu kuti akhale ndi mtima wosagawanika. Yobu ankadziwa kuti munthu ayenera kukhala womvera kuti akhalebe ndi mtima wosagawanika. Nthawi iliyonse imene timamvera Yehova, mtima wofuna kukhala wokhulupirika umakula. Yobu ankachita khama kuti azimvera Mulungu tsiku lililonse. Mwachitsanzo, ankasamala pochita zinthu ndi atsikana kapena azimayi. (Werengani Yobu 31:1.) Popeza iye anali pa banja,  ankadziwa kuti sayenera kukopana ndi akazi ena. Masiku ano, anthu ambiri m’dzikoli amalimbikitsa chiwerewere. Mofanana ndi Yobu, kodi timakana kukopana ndi munthu amene sitili naye pa banja? Nanga kodi timapewa kuona zithunzi zilizonse zolaula? (Mat. 5:28) Tikamayesetsa kukhala odziletsa pa nkhaniyi tidzakwanitsa kukhalabe ndi mtima wosagawanika.

Tingakhalebe ndi mtima wosagawanika tikamapewa kukonda chuma (Onani ndime 14) *

14 Yobu ankamveranso Yehova pa nkhani ya chuma. Iye ankaona kuti akamadalira chuma chake, ndiye kuti akuchita cholakwa chofunika kupita nacho kwa oweruza. (Yobu 31:24, 25, 28) Anthu ambiri masiku ano ali ndi mtima wokonda chuma. Koma tikamatsatira mfundo za m’Baibulo zokhudza mmene tiyenera kuonera ndalama komanso chuma, tidzakhala ofunitsitsa kukhalabe ndi mtima wosagawanika.​—Miy. 30:8, 9; Mat. 6:19-21.

Tingakhalebe ndi mtima wosagawanika tikamaganizira chiyembekezo chathu (Onani ndime 15) *

15. (a) Kodi n’chiyani chinathandizanso Yobu kukhalabe ndi mtima wosagawanika? (b) N’chifukwa chiyani tinganene kuti kuganizira chiyembekezo chathu kungatithandize?

15 Yobu ankayembekezera kuti Mulungu adzamudalitsa ndipo izi zinamuthandiza kukhalabe ndi mtima wosagawanika. Iye ankadziwa kuti Mulungu ankayamikira kuti anali ndi mtima wosagawanika. (Yobu 31:6) Ngakhale kuti anakumana ndi mayesero, Yobu sankakayikira kuti Yehova adzamudalitsa. N’zosachita kufunsa kuti zimenezi zinamuthandiza kukhalabe wokhulupirika. Yehova anasangalala kwambiri kuti Yobu anali ndi mtima wosagawanika moti anamudalitsa. (Yobu 42:12-17; Yak. 5:11) Ndipo m’tsogolomu adzamudalitsanso kwambiri. Kodi inuyo muli ndi chikhulupiriro choti Yehova adzakudalitsani mukakhala okhulupirika? Tizikumbukira kuti Mulungu wathu sanasinthe. (Mal. 3:6) Choncho kudziwa kuti Mulungu amasangalala tikakhala ndi mtima wosagawanika, kungatithandize kuti tisamakayikire kuti adzatidalitsa m’tsogolomu.​—1 Ates. 5:8, 9.

16. Kodi tiyenera kukhala ofunitsitsa kuchita chiyani?

16 Tiyeni tiziyesetsa kukhalabe ndi mtima wosagawanika. Nthawi zina mungamve ngati ndinu nokha amene mukuyesetsa kuchita zimenezi. Koma simuli nokha. Pali anthu mamiliyoni ambiri amene akukhalabe okhulupirika kwa Mulungu. Mukhoza kukhalanso m’gulu la amuna ndi akazi akale amene anakhalabe ndi mtima wosagawanika ngakhale pamene moyo wawo unali pa ngozi. (Aheb. 11:36-38; 12:1) Tiyeni tonsefe tiziyesetsa kutsatira mawu a Yobu akuti: “Sindidzasiya kukhala ndi mtima wosagawanika.” Dziwani kuti kukhala ndi mtima umenewu kungachititse kuti Yehova alemekezeke mpaka kalekale.

NYIMBO NA. 124 Tizikhulupirika Nthawi Zonse

^ ndime 5 Kodi mawu oti mtima wosagawanika amatanthauza chiyani? N’chifukwa chiyani Yehova amafuna kuti tikhale nawo? Nanga n’chifukwa chiyani mtima wosagawanika ndi wofunika kwambiri? Nkhaniyi itithandiza kupeza mayankho a mafunsowa m’Baibulo. Itithandizanso kudziwa zimene tingachite kuti tizikhala ndi mtima wosagawanika nthawi zonse. Tikamachita zimenezi tidzapeza madalitso ambiri.

^ ndime 3 Mawu achiheberi amene anamasuliridwa kuti “yopanda chilema” amagwirizana ndi mawu amene anamasuliridwa kuti “mtima wosagawanika.”

^ ndime 50 MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: Yobu akuphunzitsa ana ake zinthu zodabwitsa zimene Yehova analenga.

^ ndime 52 MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: M’bale wina akukana kuona zithunzi zolaula zimene anzake akuntchito akuona

^ ndime 54 MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: M’bale wina akudziletsa kuti asagule TV yaikulu pa ngongole

^ ndime 56 MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: M’bale wina akuganizira kwambiri chiyembekezo chathu chodzakhala m’paradaiso.