Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 NKHANI YOPHUNZIRA 8

Tizisonyeza Kuti Ndife Oyamikira

Tizisonyeza Kuti Ndife Oyamikira

“Sonyezani kuti ndinu oyamikira.”​AKOL. 3:15.

NYIMBO NA. 46 Timakuyamikirani Yehova

ZIMENE TIPHUNZIRE *

1. Kodi munthu wa ku Samariya amene Yesu anamuchiritsa anasonyeza bwanji kuyamikira?

TSIKU lina anthu 10 amene ankadwala khate anaona Yesu akubwera. Anthuwa analibe mtengo wogwira koma anali atamva kuti Yesu amachiritsa anthu odwala matenda osiyanasiyana ndipo ankakhulupirira kuti awathandiza. Choncho anafuula kuti: “Yesu, Mlangizi, tichitireni chifundo!” Yesu anachiritsadi anthuwa. N’zosachita kufunsa kuti onsewa anayamikira * zimene Yesu anawachitira. Koma mmodzi wa iwo, yemwe anali wochokera ku Samariya sanangoyamikira mumtima. Iye anapita kwa Yesu kukathokoza. Munthuyo anakhudzidwa mumtima moti anatamanda Mulungu “mokweza mawu.”​—Luka 17:12-19.

2-3. (a) N’chiyani chingatilepheretse kusonyeza kuyamikira?(b) Kodi tikambirana chiyani munkhaniyi?

2 Ifenso tiyenera kuthokoza munthu aliyense amene watichitira zinthu mokoma mtima. Koma nthawi zina tingaiwale kulankhula kapena kuchita zinthu zosonyeza kuyamikira.

3 Munkhaniyi tikambirana chifukwa chake tiyenera kulankhula kapena kuchita zinthu zosonyeza kuti tikuyamikira. Tikambirananso zitsanzo za anthu otchulidwa m’Baibulo amene anali oyamikira komanso amene anali osayamikira. Kenako tiona njira zina zimene tingasonyezere kuyamikira.

N’CHIFUKWA CHIYANI TIYENERA KUYAMIKIRA ENA?

4-5. N’chifukwa chiyani tiyenera kuyamikira ena?

4 Yehova ndi chitsanzo chabwino kwambiri pa nkhani yoyamikira. Njira ina imene amachitira zimenezi ndi kupereka  mphoto kwa anthu amene amachita zinthu zomusangalatsa. (2 Sam. 22:21; Sal. 13:6; Mat. 10:40, 41) Malemba amatilimbikitsa kuti ‘tizitsanzira Mulungu monga ana ake okondedwa.’ (Aef. 5:1) Choncho chifukwa chachikulu chotichititsa kuyamikira n’chakuti timafuna kutsanzira Yehova.

5 Kodi chifukwa china chotichititsa kuyamikira n’chiyani? Kuyamikira kuli ngati chakudya chabwino chimene chimasangalatsa ukamadya ndi anzako. Munthu akatiyamikira timamva bwino mumtima ndipo ifeyo tikayamikira munthu timamuthandiza kuti nayenso amve bwino. Munthu amene tamuyamikira amazindikira kuti zimene anatichitira zinali zothandiza. Zimenezi zimachititsa kuti tizigwirizana kwambiri ndi munthuyo.

6. Kodi mawu oyamikira amafanana bwanji ndi maapozi agolide?

6 Mawu athu oyamikira amakhala amtengo wapatali. Paja Baibulo limati: “Mawu olankhulidwa pa nthawi yoyenera ali ngati zipatso za maapozi agolide m’mbale zasiliva.” (Miy. 25:11) Tangoganizani mmene maapozi agolide angakongolere ataikidwa m’mbale zasiliva. Nanga mungawagule ndalama zingati? Ndiye inuyo mungamve bwanji munthu atakupatsani? Mawu amene munganene poyamikira munthu amakhalanso amtengo wapatali choncho. Mfundo ina yoyenera kuikumbukira ndi yakuti maapozi agolide sangawonongeke. N’chimodzimodzi ndi mawu athu oyamikira. N’kutheka kuti munthu amene tamuyamikirayo sangaiwale kwa moyo wake wonse.

ANTHU AMENE ANASONYEZA KUYAMIKIRA

7. Mogwirizana ndi Salimo 27:4, kodi Davide ndiponso anthu ena amene analemba masalimo anasonyeza bwanji kuyamikira?

7 Pali atumiki a Yehova akale ambiri amene anasonyeza kuyamikira. Mmodzi mwa anthu amenewa ndi Davide. (Werengani Salimo 27:4.) Iye ankayamikira kwambiri kulambira  koona ndipo anachita zinthu zosonyeza kuyamikirako. Davide anapereka chuma chambiri kuti chithandize pomanga kachisi. Nawonso ana a Asafu anasonyeza kuyamikira polemba masalimo kapena kuti nyimbo zotamanda Mulungu. Munyimbo ina anathokoza Yehova n’kusonyeza kuti ankachita chidwi kwambiri ndi ‘ntchito zake zodabwitsa.’ (Sal. 75:1) Apa zikuonekeratu kuti Davide komanso ana a Asafu ankafuna kusonyeza kuti ankayamikira madalitso onse amene Yehova anawapatsa. Kodi inuyo mungawatsanzire bwanji?

Kodi kalata ya Paulo yopita kwa Aroma imatiphunzitsa chiyani pa nkhani yoyamikira? (Onani ndime 8-9) *

8-9. Kodi Paulo anasonyeza bwanji kuti ankayamikira abale ndi alongo ake, nanga izi ziyenera kuti zinathandiza bwanji?

8 Mtumwi Paulo ankayamikira abale ndi alongo ake ndipo ananena mawu osonyeza kuyamikirako. Nthawi zonse ankayamikira Mulungu m’mapemphero ake chifukwa cha abale ndi alongowo. Iye ankasonyezanso kuti amawayamikira m’makalata ake. Mwachitsanzo, m’mavesi 15 oyambirira a Aroma chaputala 16, Paulo anatchula Akhristu anzake okwana 27. Iye ananena kuti Purisika ndi Akula ‘anaika miyoyo yawo pachiswe chifukwa cha moyo wake’ komanso Febe ‘anateteza iyeyo ndiponso abale ambirimbiri.’ Paulo anayamikira abale ndi alongo akhama amenewa.​—Aroma 16:1-15.

9 Paulo ankadziwa kuti abale ndi alongo akewo si angwiro. Koma m’mawu omaliza a kalata yake yopita kwa Aroma anangotchula makhalidwe awo abwino. Abale ndi alongowo ayenera kuti analimbikitsidwa kwambiri atamva zimene Paulo analembazo zikuwerengedwa mokweza mumpingo. Mosakayikira, izi zinathandiza kuti azigwirizana kwambiri ndi Paulo. Kodi inuyo mumalankhula kapena kuchita zinthu zosonyeza kuti mumayamikira zimene anthu mumpingo wanu amachita?

10. Kodi tikuphunzira chiyani pa zimene Yesu anachita poyamikira otsatira ake?

10 Yesu anayamikiranso zimene otsatira ake ankachita m’mipingo ya ku Asia Minor. Mwachitsanzo, anayamba uthenga wake wopita kumpingo wa ku Tiyatira ndi mawu akuti: “Ndikudziwa ntchito zako, chikondi chako, chikhulupiriro chako, utumiki wako, ndi kupirira kwako. Ndikudziwanso kuti ntchito zako zapanopa n’zambiri kuposa zoyamba zija.” (Chiv. 2:19) Yesu anayamikira ntchito zawo komanso makhalidwe amene anawachititsa kuti agwire ntchitozo. Ngakhale kuti iye ankafunika kuwapatsa malangizo, anayamba ndiponso kumaliza uthenga wake ndi mawu olimbikitsa. (Chiv. 2:25-28) Yesu ali ndi udindo waukulu chifukwa ndi mutu wa mipingo yonse. Choncho sikuti amafunika kutithokoza chifukwa cha ntchito imene timagwira. Ngakhale zili choncho, amayesetsa kutiyamikira. Kunena zoona, iye ndi chitsanzo chabwino kwambiri kwa akulu.

ANTHU AMENE ANALI OSAYAMIKIRA

11. Malinga ndi lemba la Aheberi 12:16, kodi Esau anasonyeza bwanji kuti sankayamikira zinthu zopatulika?

11 N’zomvetsa chisoni kuti anthu ena otchulidwa m’Baibulo anali osayamika. Chitsanzo pa nkhaniyi ndi Esau. Makolo ake ankakonda Yehova komanso kumulemekeza koma iye sankayamikira zinthu zopatulika. (Werengani Aheberi 12:16.) Kodi Esau anasonyeza bwanji kuti anali wosayamika? Iye anachita zinthu mopupuluma n’kugulitsa ukulu wake kwa Yakobo pousinthanitsa ndi mbale imodzi ya mphodza. (Gen. 25:30-34) Patapita nthawi, iye anadandaula kwambiri chifukwa cha zimene anachita. Koma popeza sanayamikire zimene anali nazo, panalibe chifukwa chomveka chodandaulira kuti walandidwa ukulu.

12-13. Kodi Aisiraeli anasonyeza bwanji kuti anali osayamika, nanga zotsatira zake zinali zotani?

 12 Aisiraeli nawonso anali ndi zifukwa zambiri zowachititsa kuyamikira Yehova. Paja Yehova anawapulumutsa ku ukapolo pobweretsa miliri 10 ku Iguputo. Kenako anawapulumutsanso powononga asilikali onse a ku Iguputo pa Nyanja Yofiira. Aisiraeliwo anayamikira kwambiri ndipo anaimba nyimbo yotamanda Yehova. Koma kodi mtima woyamikirawu unapitirira?

13 Aisiraeli atangokumana ndi mavuto ena anaiwaliratu zinthu zabwino zonse zimene Yehova anawachitira. Kenako anachita zinthu zosonyeza kuti analibe mtima woyamikira. (Sal. 106:7) Baibulo limanena kuti “khamu lonse la ana a Isiraeli linayamba kung’ung’udzira Mose ndi Aroni” koma zoona zake n’zakuti ankang’ung’udzira Yehova. (Eks. 16:2, 8) Yehova anakhumudwa kwambiri ndi mtima wosayamika umene Aisiraeliwa anasonyeza. Kenako ananena kuti m’badwo wonse wa Aisiraeliwo udzathera m’chipululu, kupatulapo Yoswa ndi Kalebe. (Num. 14:22-24; 26:65) Tiyeni tsopano tikambirane zimene tingachite kuti titsanzire anthu oyamikira n’kumapewa mtima wosayamika.

TIZISONYEZA KUYAMIKIRA

14-15. (a) Kodi mwamuna ndi mkazi wake angasonyeze bwanji kuti ali ndi mtima woyamikira? (b) Kodi makolo angaphunzitse bwanji ana awo kuti akhale oyamikira?

14 M’banja. Anthu m’banja akamayamikirana zinthu zimayenda bwino. Mwamuna ndi mkazi wake akamayamikirana kwambiri banja lawo limalimbanso kwambiri ndipo savutikanso kukhululukirana. Mwamuna amene amayamikira mkazi wake amaona zinthu zabwino zimene iye amachita ndipo “amaimirira n’kumuuza kuti ndi wodala.” (Miy. 31:10, 28) Nayenso mkazi wanzeru amayamikira zinthu zabwino zimene mwamuna wake amachita.

15 Ngati ndinu makolo, kodi mungatani kuti muziphunzitsa ana anu kuti akhale oyamikira? Muzikumbukira kuti ana anu amakonda kutengera zimene inuyo mumachita ndiponso kulankhula. Choncho muyenera kupereka chitsanzo chabwino ponena kuti zikomo ana anu akakuchitirani zinazake. Komanso muziphunzitsa ana anu kunena kuti zikomo anthu ena akawachitira zinthu zabwino. Muziwathandiza kudziwa kuti mawu oyamikira ayenera kuchokera mumtima komanso mawuwo akhoza kulimbikitsa kwambiri anthu. Mwachitsanzo, mlongo wina dzina lake Clary  anati: “Mayi anga ali ndi zaka 32 bambo anga anamangidwa ndipo mayiwo analera okha ana atatu. Ineyo nditakwanitsa zaka 32 ndinazindikira kuti sizinali zophweka kuti achite zimenezo pa msinkhu umenewu. Choncho ndinawauza kuti ndimayamikira kwambiri zonse zimene anachita pondilera limodzi ndi azichimwene anga. Posachedwapa, anandiuza kuti mawuwo anawafika pamtima kwambiri, amakonda kuwaganizira ndipo amawathandiza kukhala osangalala.”

Muziphunzitsa ana anu kuti aziyamikira ena (Onani ndime 15) *

16. Perekani chitsanzo chosonyeza kuti kuyamikira ena kumawalimbikitsa.

16 Mumpingo. Tikamayamikira abale ndi alongo athu timawalimbikitsa. Mwachitsanzo, Jorge yemwe ali ndi zaka 28 ndipo ndi mkulu, anayamba kudwala kwambiri moti sankatha kupita kumisonkhano kwa mwezi wathunthu. Ngakhale atayambiranso kusonkhana, sankatha kukamba nkhani iliyonse. Iye anati: “Ndinkadziona ngati wopanda pake chifukwa choti sindinkatha kuchita zinthu zina mumpingo. Koma pambuyo pa misonkhano ina, m’bale wina anandiuza kuti: ‘Zikomo kwambiri chifukwa mumapereka chitsanzo chabwino kwa anthu a m’banja langa. Kunena zoona, takhala tikusangalala kwambiri ndi nkhani zimene mwakamba pa zaka ziwiri zapitazi. Zatithandiza kulimbitsa ubwenzi wathu ndi Yehova.’ Mawuwa anandikhudza kwambiri moti ndinayamba kulira. Pa nthawiyo ndinkafunika kulimbikitsidwa ndipo n’zimene m’baleyo anachita.”

17. Mogwirizana ndi Akolose 3:15, kodi tingasonyeze bwanji kuti timayamikira Yehova chifukwa cha zimene amatipatsa?

17 Kwa Mulungu wathu wowolowa manja. Yehova watipatsa chakudya chauzimu chamwanaalirenji. Mwachitsanzo, timalandira malangizo kumisonkhano, m’magazini komanso pawebusaiti yathu. Kodi munayamba mwamvapo nkhani, kuwerenga nkhani kapena kuonera zinthu pa JW Broadcasting n’kuganiza kuti, ‘Nkhani imeneyi ndiye akonzera ineyotu’? Kodi tingasonyeze bwanji kuti timayamikira Yehova? (Werengani Akolose 3:15.) Njira imodzi ndi kumuthokoza nthawi zonse m’mapemphero athu chifukwa cha zinthu zabwino zimene amatipatsa.​—Yak. 1:17.

Tikamathandiza nawo kuyeretsa Nyumba ya Ufumu timasonyeza kuti tili ndi mtima woyamikira (Onani ndime 18)

18. Kodi tingasonyezenso bwanji kuti timayamikira Yehova?

18 Timasonyezanso kuti timayamikira Yehova tikamaonetsetsa kuti malo athu olambirira ndi aukhondo. Tiyenera kuyeretsa nawo komanso kukonza zinthu m’Nyumba ya Ufumu yathu. Komanso ngati tili ndi udindo wosamalira  zipangizo za mpingo monga zokuzira mawu kapena zoonetsera mavidiyo, tiyenera kuzisamalira bwino. Tikamasamalira bwino Nyumba za Ufumu zathu, zinthu sizingawonongeke msanga. Izi zimathandiza kuti pakhale ndalama zambiri zomangira kapena kukonzera Nyumba za Ufumu zina padziko lonse.

19. Kodi inuyo mukuphunzirapo chiyani pa chitsanzo cha woyang’anira dera wina ndi mkazi wake?

19 Kwa anthu amene amagwira ntchito mwakhama potithandiza. Munthu akamayamikiridwa akhoza kuyamba kuona moyenera mavuto amene akukumana nawo. Chitsanzo pa nkhaniyi ndi zimene zinachitikira woyang’anira dera wina ndi mkazi wake. Iwo anali mu utumiki tsiku lonse kunja kukuzizira kwambiri ndipo anaweruka atatoperatu. M’nyumba imene anafikira munkazizira kwambiri moti mlongoyo anagona atavala chijasi. Kutacha, iye anauza mwamuna wake kuti sangakwanitse kupitiriza utumiki wawo. Tsiku lomwelo analandira kalata yochokera ku ofesi ya nthambi ndipo inali ya mlongoyo. M’kalatayo anayamikira kwambiri mlongoyo chifukwa chotumikira Mulungu mwakhama komanso mopirira. Ananenanso kuti akuzindikira kuti si zophweka kusamuka mlungu uliwonse. Mwamuna wake anati: “Kalatayo inamulimbikitsa kwambiri moti sananenenso chilichonse chokhudza kusiya utumiki. Nthawi zingapo pamene ineyo ndinkamva kuti sindingapitirize utumikiwu iye ndi amene ankandilimbikitsa kuti ndisausiye.” Banjali linakhalabe mu utumiki woyendayenda kwa zaka pafupifupi 40.

20. Kodi tiyenera kuyesetsa kuchita chiyani tsiku lililonse?

20 Tiyeni tiziyesetsa kulankhula komanso kuchita zinthu zosonyeza kuyamikira. Mawu athu ochokera mumtima kapena zochita zathu zikhoza kuthandiza munthu kuti apitirize kupirira mavuto m’dzikoli lomwe anthu ambiri sayamika. Tikamayamikira anthu ena timayamba kugwirizana nawo kwambiri ndipo mgwirizanowu ukhoza kukhalapo mpaka kalekale. Koma chofunika kwambiri n’chakuti tikamayamikira ena timakhala tikutsanzira Atate wathu Yehova yemwe ndi wowolowa manja komanso wamtima woyamikira.

NYIMBO NA. 20 Munapereka Mwana Wanu Wobadwa Yekha

^ ndime 5 Kodi tingaphunzire chiyani kwa Yehova, Yesu komanso wakhate wina wa ku Samariya pa nkhani yoyamikira? Munkhaniyi tikambirana zitsanzo zimenezi komanso zina. Tikambirananso chifukwa chake tiyenera kusonyeza kuyamikira komanso mmene tingachitire zimenezi.

^ ndime 1 TANTHAUZO LA MAWU ENA: Kuyamikira munthu kapena chinthu kumatanthauza kuzindikira kuti munthuyo kapena chinthucho ndi chamtengo wapatali. Mawuwa anganene za kuthokoza kwambiri kuchokera mumtima.

^ ndime 55 MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: Kalata ya Paulo ikuwerengedwa mumpingo wa ku Roma; Akula, Purisika, Febe komanso anthu ena akusangalala kwambiri kumva mayina awo akutchulidwa.

^ ndime 57 MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: Mayi akuthandiza mwana wake kuti ayamikire mlongo wina wachikulire chifukwa cha chitsanzo chake chabwino.