NYIMBO 124
Tizikhulupirika Nthawi Zonse
-
1. Tizikhulupirikadi
Kwa M’lungu ndi kum’konda.
Tiyesetse kuphunzira
Malamulo akewo.
Tikamamvera Mulungu
Timamusangalatsa.
Tizikondabe Yehova
Ndipo tisamusiye.
-
2. Tizikhulupirikanso
Kwa akulu mumpingo.
Nthawi zonse pamavuto
Amatisamalira.
Tiziwapatsa ulemu
Kuchokera mumtima.
Tiwamvere nthawi zonse.
Titumikire nawo.
-
3. Tizikhulupirikabe
Tikamalangizidwa
Ndi akulu amumpingo.
Inde tiziwamvera
Ndipo Yehova Mulungu
Adzatidalitsadi.
Tikamakhulupirika,
Iye azitikonda.
(Onaninso Sal. 149:1; 1 Tim. 2:8; Aheb. 13:17.)