Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 MBIRI YA MOYO WANGA

Makolo Anga Anandithandiza Kuti Ndizitumikira Yehova

Makolo Anga Anandithandiza Kuti Ndizitumikira Yehova

NTHAWI zina tinkayenera kuwoloka mtsinje wa Niger, womwe madzi ake ankathamanga kwambiri ndipo unali wautali makilomita 1.6 m’mbali. Pa nthawiyo ku Nigeria kunali nkhondo yapachiweniweni choncho kuwoloka mtsinjewo kunali koopsa kwambiri. Kodi n’chifukwa chiyani ndinkachita nawo zimenezi? Choyamba, ndikufotokozereni zimene zinachitika ndisanabadwe.

Mu 1913, bambo anga dzina lawo a John Mills anabatizidwa mumzinda wa New York ali ndi zaka 25. M’bale Russell ndi amene anakamba nkhani ya ubatizo. Pasanapite nthawi yaitali, bambo anapita ku Trinidad ndipo kenako anakwatira Constance Farmer, yemwe anali Wophunzira Baibulo wakhama. Bambo ndi mayi anali odzozedwa. Bambo ankathandiza anzawo dzina lawo a William R. Brown kuonetsa filimu yakuti “Sewero la Pakanema la Chilengedwe.” Ankachita zimenezi mpaka nthawi imene banja la a Brown linatumizidwa ku West Africa mu 1923. Bambo ndi mayi anapitiriza kutumikira ku Trinidad.

MAKOLO ATHU ANKATIKONDA

M’banja mwathu munali ana 9 ndipo makolo anapatsa mwana woyamba dzina lakuti Rutherford, lomwe linali dzina la pulezidenti wa Watch Tower Bible and Tract Society. Ine ndinabadwa pa 30 December 1922 ndipo anandipatsa dzina lakuti Woodworth potengera dzina la Clayton J. Woodworth, yemwe ankayang’anira ntchito yokonza magazini ya Galamukani (pa nthawiyo inkadziwika kuti The Golden Age). Makolo athu anatithandiza kuti tiphunzire sukulu, koma ankatilimbikitsa kwambiri kuti tikhale ndi zolinga zauzimu. Amayi anali ndi luso lotiphunzitsa mogwira mtima pogwiritsa ntchito Malemba. Bambo ankakonda kutifotokozera nkhani za m’Baibulo ndipo ankayendetsa thupi lonse pofuna kutithandiza kuona nkhanizo m’maganizo mwathu.

Zimene ankachitazi zinatithandiza kwambiri. N’zosangalatsa kwambiri kuti anyamata atatu mwa anyamata 5, tinalowa Sukulu ya Giliyadi. Azichemwali athu atatu anachita upainiya kwa zaka zambiri ku Trinidad ndi ku Tobago. Makolo athu ankatiphunzitsa mwaluso komanso kutipatsa chitsanzo chabwino. Zimenezi zinathandiza anafe kuti tikhazikike “m’nyumba ya Yehova.” Iwo anapitiriza kutilimbikitsa kuti tikhalebe m’nyumbayi komanso ‘tizikula mosangalala m’mabwalo a Mulungu wathu.’​—Sal. 92:13.

Anthu ankakonda kukumana kwathu pokonzekera kukalalikira. Apainiya ankabwera kunyumba ndipo  nthawi zambiri ankakamba za M’bale George Young, yemwe anali mmishonale wa ku Canada amene anabwera ku Trinidad. Makolo anga ankakonda kukamba za banja la M’bale Brown, lomwe pa nthawiyo linali ku West Africa. Zinthu zonsezi zinandilimbikitsa kuti ndiyambe kulalikira ndili ndi zaka 10.

ZIMENE ZINKACHITIKA PA NTCHITO YOLALIKIRA

Pa nthawiyo, magazini athu ankafotokoza mosapita m’mbali zinthu zoipa zimene zinkachitika m’chipembedzo chonyenga komanso zimene amalonda ndi andale ankachita. Choncho mu 1936, atsogoleri achipembedzo analimbikitsa akuluakulu a boma la Trinidad kuti aletse mabuku onse a Watch Tower. Tinkabisa mabuku athu koma tinkawagwiritsabe ntchito mpaka mabuku onse atatha. Tinkayenda m’chigulu n’kumalalikira pogwiritsa ntchito timapepala ndi zikwangwani. Nthawi zina tinkachita zimenezi titakwera njinga. Tinkakalalikira kumadera akutali kwambiri limodzi ndi gulu lakutauni ya Tunapuna lomwe linali ndi galimoto yokhala ndi zokuzira mawu. Ntchitoyi inali yosangalatsa kwambiri. Kugwira nawo ntchito imeneyi kunandithandiza kuti ndibatizidwe ndili ndi zaka 16.

A Gulu la ku Tunapuna limene linkagwiritsa ntchito galimoto yokhala ndi zokuzira mawu

Zimene makolo anga anachita komanso kugwira nawo ntchitoyi zinandithandiza kuti ndizifuna kwambiri kukhala mmishonale. Ndinapitiriza kukhala ndi mtima umenewu mpaka pamene ndinapita kuchilumba cha Aruba mu 1944 kukatumikira limodzi ndi M’bale Edmund W. Cummings. Tinasangalala kwambiri kuti mu 1945 anthu 10 amene tinawaitanira ku Chikumbutso anabwera. Chaka chotsatira, mpingo woyamba unakhazikitsidwa pachilumbachi.

Ndinkasangalala kwambiri nditakwatira Oris

Kenako ndinalalikira mtsikana wina wakuntchito dzina lake Oris Williams. Iye ankaikira kumbuyo kwambiri zimene ankakhulupirira. Koma atayamba kuphunzira Baibulo anazindikira mfundo zoona za m’Mawu a Mulungu ndipo anabatizidwa pa 5 January 1947. Patapita nthawi, tinayamba kukondana ndipo kenako tinakwatirana. Iye anayamba upainiya mu November 1950. Ndinayamba kusangalala kwambiri kutumikira limodzi ndi Oris.

TINKASANGALALA KUTUMIKIRA KU NIGERIA

Mu 1955, tinaitanidwa kupita ku Sukulu ya Giliyadi. Pokonzekera sukuluyi, ine ndi Oris tinasiya ntchito n’kugulitsa nyumba ndi katundu wathu. Kenako tinachoka ku Aruba. Tinalowa kalasi ya nambala 27 ndipo tinamaliza maphunziro athu pa 29 July 1956. Titamaliza anatitumiza ku Nigeria.

Mu 1957, ndili ndi banja la Beteli ku Lagos m’dziko la Nigeria

Oris ataganizira zimene takwanitsa kuchita ananena kuti: “Mzimu wa Yehova ungathandize munthu kupirira bwinobwino mavuto amene amakumana nawo pochita umishonale. Mosiyana ndi mwamuna wanga, ine sindinkafuna kukhala mmishonale. Ndinkafuna kungokhala kunyumba n’kumalera ana. Ndinasintha maganizo amenewa nditazindikira kuti uthenga wabwino uyenera kulalikidwa mwamsanga. Pamene tinkamaliza maphunziro a Giliyadi ndinali wokonzeka kukagwira ntchito yolalikira. M’bale Worth Thornton, yemwe ankagwira ntchito mu ofesi ya M’bale Knorr, anatiperekeza pamene tinkapita kukakwera sitima yotchedwa Queen Mary. Iye anatiuza kuti tizikatumikira ku Beteli ndipo ndinadandaula kwambiri. Koma ndinasintha maganizo n’kuyamba kukonda utumiki wosiyanasiyana umene ndinkachita ku Beteli. Ndinkasangalala kwambiri kugwira ntchito pamalo olandirira alendo. Ine ndimakonda kwambiri anthu ndipo ntchito imeneyi inkachititsa kuti ndizikumana ndi abale komanso alongo ambiri a ku Nigeria. Ambiri ankafika atatuwa, atatopa, ali ndi ludzu komanso njala. Ndinkasangalala kuwapatsa zonse zofunikira. Kuchita zonsezi kunkandisangalatsa chifukwa ndinkaona kuti ndi utumiki wopatulika kwa Yehova.” Kunena zoona, munthu akhoza kusangalala ndi utumiki uliwonse.

Tsiku lina tikucheza ndi achibale ku Trinidad mu 1961, M’bale Brown anafotokoza zinthu zina zosangalatsa zimene zinachitika akutumikira ku Africa. Kenako nane ndinafotokoza zimene zinkachitika ku Nigeria. Ndiyeno M’bale Brown anandikumbatira uku akuuza bambo anga kuti: “Johnny, iwe sunapitepo ku Africa koma mwana wakoyu anapita.” Poyankha, bambo angawo anati: “Pitiriza utumiki mwana wanga, usasiye.” Zimene akuluakuluwa anachita zinandilimbikitsa kuti ndizichita utumiki wanga mwakhama kwambiri.

William “Bible” Brown ndi mkazi wake Antonia anatilimbikitsa kwambiri

Mu 1962, ndinali ndi mwayi wolowanso kalasi ya nambala 37 ya Giliyadi ndipo inali ya miyezi 10. M’bale Wilfred Gooch, yemwe anali woyang’anira nthambi ku Nigeria analowa kalasi ya nambala 38 ndipo anatumizidwa ku England. Zitatero ineyo ndi  amene ndinali woyang’anira nthambi ya ku Nigeria. Ndinkayesetsa kutsanzira M’bale Brown moti ndinkayenda m’madera osiyanasiyana kuti ndiwadziwe bwino abale a ku Nigeria. N’zoona kuti ambiri analibe zinthu zimene anthu a m’mayiko olemera ali nazo. Koma ankakhala osangalala ndipo izi zinasonyeza kuti ndalama ndi chuma si zimene zimathandiza munthu kukhala wosangalala. Ngakhale kuti anali ndi mavuto osiyanasiyana, ndinkasangalala kuwaona pamisonkhano ali aukhondo komanso akuoneka bwino. Popita kumisonkhano yachigawo, ambiri ankakwera malole kapena mabasi osatseka m’mbali otchedwa bolekajas. * Nthawi zambiri mabasiwa ankalembedwa mawu ena ochititsa chidwi. Mwachitsanzo, ina inalembedwa kuti: “Madontho ang’onoang’ono a madzi amadzaza nyanja yaikulu.”

Mawu amenewatu ndi oona. Chilichonse chimene munthu amachita, kaya chichepe bwanji, chimathandiza kuti ntchito iziyenda bwino. Nafenso tinachita zimene tikanatha. Pofika mu 1974, dziko la Nigeria linali lachiwiri kukhala ndi ofalitsa okwana 100,000. Dziko la United States ndi limene linali loyamba kukhala ndi ofalitsa ochuluka chonchi. Apa tingati ntchito inkayenda bwino.

Pamene zinthu zinkayenda bwino chonchi, nkhondo yapachiweniweni inayamba mu 1967 mpaka kufika mu 1970. Kwa miyezi yambiri, abale akutsidya lina la mtsinje wa Niger ku Biafran sankalumikizananso ndi abale a ku ofesi ya nthambi. Tinkayenera kuwapititsira chakudya chauzimu. Monga ndanenera kumayambiriro kuja, tinakwanitsa kuwoloka mtsinjewo maulendo angapo. Izi zinatheka chifukwa chakuti tinkapemphera komanso kudalira Yehova.

Maulendowa anali oopsa kwambiri. Tikanatha kufa chifukwa chowomberedwa ndi asilikali, kudwala kapena kukumana ndi zinthu zina zoopsa. N’zoona kuti kudutsa m’dera limene munali asilikali mbali imene tinkakhalayo kunali kovuta. Koma oopsa kwambiri anali asilikali amene ankakhala tsidya lina la mtsinjewu, choncho zinali zovuta kudutsako. Tsiku lina ndinawoloka mtsinjewu usiku pa bwato kuchoka mumzinda wa Asaba kupita mumzinda wa Onitsha ndipo ndinakalimbikitsa akulu ku Enugu. Ulendo wina ndinapita kukalimbikitsa abale a ku Aba komwe pa nthawiyo anthu sankaloledwa kuyatsa magetsi usiku. Kumzinda wa Port Harcourt, msonkhano wathu unatha msangamsanga ndi pemphero chifukwa choti kunafika gulu la asilikali lolimbana ndi asilikali amene anali kumeneku.

Misonkhano imeneyi inali yofunika kwambiri chifukwa tinkalimbikitsa abale athu, kuwatsimikizira kuti Yehova amawakonda komanso kuwapatsa malangizo ofunika pa nkhani yopewa zandale. Abale athu a ku Nigeria anakhalabe okhulupirika pa nthawi yonse ya nkhondoyi. M’malo modana ndi anthu a mitundu ina, iwo ankasonyeza chikondi ndipo ankagwirizana ndi Akhristu anzawo. Ndinasangalala kwambiri kuwalimbikitsa pa nthawi yovutayi.

Mu 1969, M’bale Milton G. Henschel anali tcheyamani wa msonkhano wamayiko wakuti “Mtendere Padziko Lapansi” umene unachitikira ku Yankee Stadium ku New York. Ineyo ndinali womuthandizira ndipo ndinaphunzira zambiri. Izi zinachitika pa nthawi yabwino chifukwa mu 1970 tinali ndi msonkhano wamayiko ku Lagos m’dziko la Nigeria womwe unkanena za anthu amene Mulungu amakondwera nawo. Yehova anatidalitsa kwambiri moti msonkhanowu unayenda bwino ngakhale kuti m’dzikolo munali mutachitika nkhondo. Msonkhanowu unali m’zilankhulo 17 ndipo kunali anthu 121,128. M’bale Knorr ndi M’bale Henschel anafika pamsonkhanowu. Panalinso abale ndi alongo ena amene anafika kuchokera ku United States ndi ku England. Pamsonkhanowu, anthu 3,775 anabatizidwa ndipo umenewu unali umodzi mwa misonkhano pamene anthu ochuluka chonchi anabatizidwa chichitikireni ubatizo wa pa Pentekosite. Ndinatanganidwa kwambiri pokonzekera msonkhano umenewu. Anthu ankawonjezereka m’gulu kuposa mmene tinkayembekezera.

Pamsonkhano wamayiko umene unachitika m’zilankhulo 17 kuphatikizapo Chiibo, ndipo panali anthu 121,128

Ndinatumikira ku Nigeria zaka zoposa 30 ndipo nthawi zina ndinkatumikira ngati woyang’anira woyendayenda komanso woyendera nthambi za ku West Africa. Amishonale ankayamikira kwambiri akayenderedwa n’kulimbikitsidwa aliyense payekha. Ndinkasangalala kwambiri kuwatsimikizira kuti gulu la Yehova limawaganizira. Apa ndinaphunzira kuti kuchita zinthu moganizira anthu kumawathandiza kuti azisangalala, akhale ndi mphamvu komanso azichita zinthu mogwirizana ndi gulu la Yehova.

 Kunena zoona, Yehova ndi amene anatithandiza kuti tipirire mavuto okhudza nkhondo komanso matenda. Zinkachita kuonekeratu kuti Yehova akutidalitsa. Oris anati:

“Tonse tinadwala malungo nthawi zingapo. Ulendo wina, mwamuna wanga anafika kuchipatala chamumzinda wa Lagos atakomoka. Kuchipatalako anandiuza kuti mwina sachira, koma mwamwayi anachira. Atatsitsimuka, analalikira bambo wina dzina lake Nwambiwe, yemwe anali nesi womuyang’anira. Tsiku lina tinapita kuchipatalako kukaona nesiyo n’cholinga choti timuthandize kuti ayambe kuphunzira Baibulo. Iye anayambadi kuphunzira ndipo anadzakhala mkulu mumpingo wamumzinda wa Aba. Inenso ndinathandiza anthu ambiri, ndipo ena anali Asilamu apaphata, omwe anayamba kutumikira Yehova mwakhama. Koma chimene chinkatisangalatsa kwambiri chinali chakuti tinayamba kukonda anthu a ku Nigeria, chikhalidwe chawo komanso chilankhulo chawo.”

Mfundo ina imene tinaiphunzira ndi yakuti: Kuti tizisangalala potumikira m’dziko lina, tinkafunika kukonda abale ndi alongo ngakhale kuti timasiyana nawo kwambiri.

UTUMIKI WATSOPANO

Titatumikira ku Beteli ya ku Nigeria, mu 1987 anatitumiza kuti tikachite umishonale kuchilumba cha St. Lucia ku Caribbean. Zinali zosangalatsa kwambiri koma tinakumana ndi mavuto ena. Mosiyana ndi ku Africa, komwe amuna ankakwatira mitala, ku St. Lucia anthu ankakonda kumangokhalira limodzi popanda kukwatirana mwalamulo. Koma Mawu a Mulungu omwe ndi amphamvu anathandiza anthu ambiri amene tinkaphunzira nawo kuti asinthe.

Ndinakhala m’banja ndi Oris kwa zaka 68 ndipo ndinkamukonda kwambiri

Titayamba kufooka chifukwa cha ukalamba, Bungwe Lolamulira linatiuza kuti tipite kulikulu lathu ku Brooklyn m’dziko la United States. Izi zinachitika mu 2005. Tsiku lililonse ndimathokoza Yehova chifukwa chondipatsa mkazi wabwino. N’zomvetsa chisoni kuti anamwalira mu 2015 ndipo zimandiwawa kwambiri. Anali mnzanga wapamtima komanso mkazi wachikondi ndipo ndinkamukonda kwambiri. Tinakhala m’banja zaka 68. Tinazindikira kuti munthu amakhala wosangalala m’banja kapena mumpingo ngati amalemekeza mutu wake, amakhululuka, amadzichepetsa komanso kusonyeza makhalidwe amene mzimu woyera umatulutsa.

Tikakhumudwa ndi zinazake tinkapempha Yehova kuti atithandize n’cholinga choti zonse zimene tachita zisalowe m’madzi. Pamene tinkayesetsa kusintha zinthu, tinkangoona kuti basi zayamba kuyenda bwino kwambiri ndipo tinkadziwa kuti zabwino zili m’tsogolo.​—Yes. 60:17; 2 Akor. 13:11.

Yehova anadalitsa ntchito imene makolo anga ndi anzawo anagwira ku Trinidad ndi ku Tobago. Malipoti apanopa akusonyeza kuti kuli ofalitsa 9,892. Ku Aruba, anthu ambiri anachita khama kuti alimbitse mpingo umene ndinkasonkhana. Panopa pachilumbapa pali mipingo 14. Nakonso ku Nigeria ofalitsa afika 381,398. Kuchilumba cha St. Lucia, anthu okwana 783 akulalikira za Ufumu wa Mulungu.

Panopa ndili ndi zaka za m’ma 90. Lemba la Salimo 92:14 limanena kuti anthu okhazikika m’nyumba ya Yehova “zinthu zidzapitiriza kuwayendera bwino ngakhale atachita imvi, adzakhalabe onenepa ndi athanzi.” Ndimasangalala kwambiri ndikaganizira zimene ndachita potumikira Yehova. Zimene makolo anga anachita zandithandiza kuti nditumikire Yehova ndi mtima wonse. Nayenso Yehova wandisonyeza chikondi pondilola kuti ‘ndikule mosangalala m’mabwalo a Mulungu wanga.’​—Sal. 92:13.

^ ndime 18 Onani Galamukani! yachingelezi ya March 8, 1972, tsamba 24-26.