Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Zimene Achinyamata Amadzifunsa

Kodi Ndiziyembekezera Chiyani M’banja?—Gawo 1

Kodi Ndiziyembekezera Chiyani M’banja?—Gawo 1

“Ndikamacheza naye, kumtimaku kumangoti myaa. Ndikungoona ngati tsiku la ukwati wathu likuchedwa.”

“Palibiretu chimene timagwirizana. Palibenso za banja moti timangokhala ngati anthu ongokhala nyumba imodzi basi.”

MWINA mutawerenga ziganizo zili pamwambapa, mungaganize kuti zinanenedwa ndi anthu awiri osiyana. Koma choti mudziwe n’chakuti mawu onse amene ali muziganizo ziwirizi ananenedwa ndi munthu mmodzi. Mawu a muchiganizo choyamba anawanena ali pachibwenzi ndipo mawu amuchiganizo chachiwiri anawanena atalowa m’banja.

Koma kodi chinalakwika ndi chiyani? Ngati mukukonzekera kuti tsiku lina mudzalowa m’banja, kodi mungatani kuti mudzakhale osangalala m’banja ngati mmene munkafunira muli pa chibwenzi?

Dziwani izi: Kuti munthu akhale wosangalala m’banja zimangodalira zimene amayembekezera m’banjamo.

Nkhani ino komanso nkhani ya “Zimene Achinyamata Amadzifunsa,” yomwe idzatuluke mu Galamukani! ya mwezi wamawa, idzakuthandizani kuti musamayembekezere zinthu zomwe sizingachitike m’banja.

Kodi ndi zinthu ziti zimene munthu angayembekezere kuti zizidzachitika akadzalowa m’banja? Zina mwa zinthu zimenezi ndi izi:

  1. Zinthu zabwino

  2. Mavuto

  3. Zinthu zosayembekezereka

Tiyeni tikambirane zinthu zimenezi chimodzi ndi chimodzi.

ZINTHU ZABWINO

Baibulo limasonyeza kuti banja ndi chinthu chabwino. (Miyambo 18:22) Taonani zina mwa zinthu zabwino zimene mungayembekezere m’banja.

Mumapeza mnzanu weniweni. Baibulo limanena kuti patapita kanthawi Adamu atalengedwa, Mulungu ananena kuti: “Si bwino kuti munthu akhale yekha.” Kenako analenga Hava kuti akhale mnzake womuyenerera. (Genesis 2:18) Mulungu analenga Adamu ndi Hava monga anthu awiri osiyana koma anali oyenererana. N’chifukwa chake mwamuna ndi mkazi okwatirana amakhala ogwirizana kwambiri.—Miyambo 5:18.

Mumapeza wothandizana naye. Baibulo limanena kuti: “Awiri amaposa mmodzi, . . . ngati mmodzi wa iwo atagwa, winayo akhoza kum’dzutsa mnzakeyo.” (Mlaliki 4:9, 10) Mfundo imeneyi imagwiranso ntchito kwambiri m’banja. Mwachitsanzo, mtsikana wina yemwe wangokwatiwa kumene, dzina lake Brenda, * anati: “Ndikuona kuti banja limayenda bwino ngati mumachitira zinthu limodzi. Nthawi zina umafunika kudzichepetsa komanso kungololera zinthu zina.”

Kugonana. Baibulo limati: “Mwamuna azipereka kwa mkazi wake mangawa ake, mkazinso achite chimodzimodzi kwa mwamuna wake.” (1 Akorinto 7:3) Anthu amene ali m’banja amakhala omasuka kugonana popanda kudziimba mlandu kapena kudera nkhawa za mavuto amene anthu omwe amagonana asanalowe m’banja amakumana nawo.—Miyambo 7:22, 23; 1 Akorinto 7:8, 9.

Mfundo yoti muziikumbukira: Ukwati ndi mphatso yochokera kwa Mulungu. (Yakobo 1:17) Mukamadzatsatira malangizo ake, ndiye kuti muzidzakhala osangalala m’banja mwanu.

Zoti muganizire: Kodi inuyo mumaona kuti banja silabwino chifukwa cha zimene mwaonapo zikuchitika m’mabanja ena, kapenanso m’banja lanu? Ngati ndi choncho, kodi ndi zitsanzo zabwino ziti zimene mungatengere?

MAVUTO

Baibulo silibisa kuti nthawi zina m’banja mumakhala mavuto. (1 Akorinto 7:28) Mavuto ena amene mungayembekezere ndi awa:

Kusemphana maganizo. N’zosatheka kuti mwamuna ndi mkazi azigwirizana pa chilichonse chifukwa tonse ndife opanda ungwiro. (Aroma 3:23) N’chifukwa chake nthawi zina mwamuna ndi mkazi wake akhoza kusiyana maganizo ngakhale kuti amakondana kwambiri. Nthawi zinanso angathe kulankhulirana mawu opweteka ndipo pambuyo pake akhoza kudandaula nazo. Baibulo limanena kuti: “Munthu amene sananenerepo mnzake mawu oipa . . . ndiye kuti ndi munthu wangwiro.” (Yakobo 3:2, Holy Bible—Easy-to-Read Version) N’zoona kuti anthu amene ali pabanja ayenera kuyesetsa kupewa mikangano, koma kuti banja lawo likhale losangalala, ayenera kumakambirana akasemphana maganizo.

Zimene mumayembekezera sizikuchitika. Mtsikana wina, dzina lake Karen, ananena kuti: “Timapusitsika ndi mafilimu komanso mapulogalamu a pa TV omwe amasonyeza mkazi atapeza mwamuna wopanda vuto lililonse, akukhala mosangalala kwa moyo wawo wonse.” Anthu amene ali m’banja akaona kuti zimene amaonera m’mafilimu sizikuchitika, amakhala okhumudwa. N’zoona kuti anthu akakwatirana amadzazindikira kuti mwamuna kapena mkaziyo ali ndi mavuto ena omwe samawadziwa poyamba. Ngati zimenezi zitachitika, mfundo yofunika kuikumbukira ndi yakuti chikondi chenicheni “chimapirira zinthu zonse.” Zimenezi zikuphatikizapo kukhumudwa chifukwa chakuti zimene mumayembekezera sizikuchitika.—1 Akorinto 13:4, 7.

Nkhawa. Baibulo limanenanso kuti anthu amene ali pa banja “amadera nkhawa zinthu za dziko.” (1 Akorinto 7:33, 34) Nthawi zina nkhawa imeneyi ndi yabwino. Mwachitsanzo, m’banja mungakhale vuto la ndalama. Mwina mwamuna ndi mkazi angafunike kumagwira ntchito kuti apeze chakudya, zovala ndi malo okhala. Komabe akamachita zinthu mogwirizana posamalira banja lawo, angamakhale osangalala.—1 Timoteyo 5:8.

Mfundo yoti muziikumbukira: Munthu akakhala pa chibwenzi amakhala ngati akuyendetsa galimoto ya mawaya. Koma akalowa m’banja amakhala ngati akuyendetsa galimoto yeniyeni. Choncho, kuti banja lanu lidzakhale losangalala mudzafunika kuchita zinthu mwaluso komanso mwakhama polimbana ndi mavuto amene mungakumane nawo.

Zoti muganizire: Kodi panopo mumatani mukakhala kuti simukugwirizana ndi makolo kapena abale anu? Kodi mumatha kuganiza bwinobwino mukakhumudwa? Kodi mumatani mukakhala ndi nkhawa?

NKHANI YOTSATIRA YA “ZIMENE ACHINYAMATA AMADZIFUNSA” IDZAFOTOKOZA . . . Mfundo za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni kuthana ndi zinthu zimene simumaziyembekezera.

 

^ ndime 17 Tasintha mayina ena m’nkhani ino.