Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 Zimene Baibulo Limanena

Kodi Mumaona Kuti Chipembedzo N’chofunika?

Kodi Mumaona Kuti Chipembedzo N’chofunika?

NGATI munakhumudwapo ndi zimene zipembedzo zimachita kapena mumaona kuti zipembedzo ndi zosafunika, dziwani kuti si inu nokha. Chiwerengero cha anthu amene sakufuna kukhala m’chipembedzo chilichonse chikuwonjezereka.

Anthu ena asiya zipembedzo zawo chifukwa amaona kuti zimachita zinthu zachinyengo komanso zimalimbikitsa kuti anthu asamagwirizane. Ena amaona kuti n’zovuta kutsatira miyambo yonse ya m’zipembedzo zawo. Ndipo ena amaona kuti chipembedzo ndi chosafunika chifukwa munthu akhoza kulambira popanda kukhala m’chipembedzo chinachake. Komano kodi Baibulo limaphunzitsa chiyani pa nkhani yokhala ndi mpingo?

Anthu Akale Omwe Anali Mabwenzi a Mulungu

Baibulo limafotokoza bwino za mmene anthu akale monga Abulahamu, Isaki ndi Yakobo ankalambirira Mulungu. Mwachitsanzo, nthawi ina Mulungu ananena kuti: “Ndapalana ubwenzi ndi Abulahamu kuti aphunzitse ana ake ndi mbadwa zake kuyenda m’njira ya Yehova ndi kuchita chilungamo.” (Genesis 18:19) Abulahamu ankachedwa bwenzi la Mulungu chifukwa iyeyo payekha anali pa ubwenzi weniweni ndi Mlengi. Komabe iye ankalambiranso Mulungu limodzi ndi banja lake. N’chimodzimodzinso ndi anthu ena omwe anali pa ubwenzi ndi Mulungu. Iwo ankalambira Mulungu limodzi ndi anthu a m’dera lawo, mabanja awo, achibale awo ndiponso antchito awo.

Patapita nthawi, Mulungu anafuna kuti Aisiraeli komanso Akhristu a m’nthawi ya atumwi azikumana pamodzi kuti azimulambira. (Levitiko 23:2, 4; Aheberi 10:24, 25) Iye ankafuna kuti anthuwa akakumana aziimba nyimbo, kuwerenga Malemba komanso kupemphera. (Nehemiya 8:1-8; Akolose 3:16) Malemba amasonyezanso kuti masiku ano payenera kukhala gulu la anthu amene azitsogolera mpingo polambira.—1 Timoteyo 3:1-10.

Ubwino Wolambira Mulungu Limodzi ndi Mpingo

Mogwirizana ndi zimene taonazi, masiku anonso Mulungu amafuna kuti anthu amene ndi mabwenzi ake azimulambira limodzi ndi mpingo. Ndipotu anthu amene amalambira Mulungu limodzi ndi mpingo amapindula kwambiri.

Mwachitsanzo, Malemba amayerekezera munthu amene amalambira Mulungu moona ndi munthu amene akuyenda mumsewu wopanikiza. Amamuyerekezeranso ndi munthu amene ali pa mpikisano wothamanga. (Mateyu 7:14; 1 Akorinto 9:24-27) Munthu amene akuthamanga ulendo wautali komanso mumsewu wazitunda angasiye kuthamanga chifukwa chotopa. Komabe ngati anthu ena akumuchemerera, akhoza kulimbikira mpaka kumaliza mpikisanowo. Mofanana ndi zimenezi, munthu amene akufuna kulambira Mulungu movomerezeka, akhoza kupitirizabe kukhala bwenzi la Mulungu ngakhale atakumana ndi mavuto, ngati anthu amene akulambira naye limodzi akumulimbikitsa.

Zimenezi zikugwirizana ndi mawu amene amapezeka pa Aheberi 10:24, 25. Lembali limati: “Tiyeni tiganizirane kuti tilimbikitsane pa  chikondi ndi ntchito zabwino. Tisaleke kusonkhana pamodzi.” Komanso Malemba amasonyeza kuti anthu amene amalambira Mulungu movomerezeka, amalambira limodzi monga abale ndi alongo, ndipo amachita zimenezi mogwirizana ngati mmene thupi limagwirira ntchito.

Baibulo limafotokoza kuti mpingo uli ngati thupi ndipo umachita zinthu mwachikondi komanso mwamtendere. Mwachitsanzo, lemba la Aefeso 4:2, 3 limalimbikitsa atumiki a Mulungu kuti azichita zinthu “modzichepetsa nthawi zonse, mofatsa, moleza mtima, ndiponso mololerana m’chikondi.” Limapitirizanso kuti: “Muziyesetsa ndi mtima wonse kusunga umodzi [wanu] mwa mzimuwo, ndi mwamtendere monga chomangira,” chogwirizanitsa Akhristu. Ndiyeno kodi mungatsatire bwanji malangizo amenewa ngati simulambira Mulungu limodzi ndi anthu ena?

Mulungu amafuna kuti atumiki ake azimulambira monga gulu m’malo moti aliyense azimulambira kwayekha. Baibulo limalimbikitsa atumiki a Mulungu kuti azilankhula mogwirizana, apewe magawano, akhale “ogwirizana pokhala ndi mtima umodzi ndi maganizo amodzi.” (1 Akorinto 1:10) Zikanakhala kuti Mulungu amafuna kuti aliyense azimulambira payekhapayekha, mawu amenewa akanakhala opanda tanthauzo.

Pamenepa taona kuti Baibulo limasonyeza kuti Mulungu amafuna kuti anthu azimulambira limodzi ndi anthu ena. Chipembedzo chimene Malemba amafotokoza komanso chimene Mulungu amachivomereza chingakuthandizeni kuti muzimulambira moyenerera.—Mateyu 5:3.

N’zoona kuti zipembedzo zambiri masiku ano zimalimbikitsa chinyengo komanso nkhanza. Koma zimenezi sizikutanthauza kuti zipembedzo zonse ndi zoipa. Payenera kuti pali chipembedzo chimodzi chimene chimalimbikitsa kuti anthu azikondana komanso chimene chimalimbikitsa anthu kukhala ndi makhalidwe amene Mulungu amafuna. Chipembedzo chimenechi chingakuthandizeni kuti mukhale ndi chikhulupiriro chenicheni. Baibulo limafotokoza mmene mungadziwire chipembedzo chimene chimalambira Mulungu movomerezeka.