Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 Zimene Achinyamata Amadzifunsa

Kodi Mwamuna Weniweni Amakhala Wotani?

Kodi Mwamuna Weniweni Amakhala Wotani?

“Bambo anga anamwalira ndili ndi zaka zitatu moti nthawi zina ndimasirira anyamata amene ali ndi bambo awo. Amaoneka kuti amachita zinthu mosadzikayikira kusiyana ndi mmene ndimachitira.”—Anatero Alex. *

“Sindicheza kwambiri ndi bambo anga moti ndimachita kuphunzira ndekha zinthu zimene mwamuna ayenera kuchita.”—Anatero Jonathan.

KODI inuyo munayamba mwamvapo ngati mmene anyamata awiri omwe atchulidwa pamwambawa amamvera? Kodi mumakayikira zoti mungakwanitse kuchita zimene mwamuna weniweni amayenera kuchita? Ngati zili choncho, musadandaule.

Tiyeni tione zimene mungachite kuti muthane ndi mavuto awiri amene anyamata ambiri amakumana nawo.

VUTO LOYAMBA: Kukhala ndi maganizo olakwika pa nkhani ya mwamuna weniweni

Zimene ena amanena:

  • Mwamuna salira.

  • Mwamuna weniweni sauzidwa zochita.

  • Mwamuna weniweni sachita zinthu ngati mkazi.

Zoona zake: Sizoona kuti mwamuna amakhala ndi nzeru kuposa mkazi, koma zoona zake n’zakuti mwamuna weniweni sachita zinthu mwachibwana. Munthu amakhala mwamuna weniweni akayamba kuchita zinthu ngati munthu wamkulu. Mtumwi Paulo analemba kuti: “Pamene ndinali kamwana, ndinali kulankhula ngati kamwana, kuganiza ngati kamwana, ndiponso kuona zinthu ngati kamwana. Koma tsopano pamene ndakula, ndasiya zachibwana.” (1 Akorinto 13:11) Mawu amenewa akusonyeza kuti munthu akasiya kuganiza, kulankhula komanso kuchita zinthu ngati mwana ndiye kuti ndi mwamuna weniweni. *

 Yesani izi: Lembani papepala mayankho a mafunso awa:

  1. Kodi ndi zinthu ziti zomwe zikusonyeza kuti ndasiya “zachibwana”?

  2. Kodi ndi zinthu ziti zomwe ndikufunikabe kusintha?

Mavesi amene mungawerenge: Luka 7:36-50. Pamene mukuwerenga mavesiwa yesani kuona zimene Yesu anachita zosonyeza kuti anali mwamuna weniweni (1) poyesetsa kuchita zinthu mwachilungamo komanso (2) kulemekeza ena kuphatikizapo azimayi.

“Ndili ndi mnzanga, dzina lake Ken, ndipo ndimamusirira chifukwa ndi wamphamvu, wolimba mtima, wokonda kutsatira mfundo za m’Baibulo komanso ndi wachifundo. Zimene amachita zandithandiza kuona kuti mwamuna weniweni saona kuti anthu ena ndi otsika.”—Anatero Jonathan.

VUTO LACHIWIRI: Kukula popanda kuthandizidwa ndi bambo

Zimene ena amanena:

  • Ngati mnyamata alibe bambo ake sangadziwe zimene mwamuna weniweni ayenera kuchita.

  • Ngati mnyamata ali ndi bambo omwe sasonyeza chitsanzo chabwino, akakula amachita zimene bambo ake ankachita.

Zoona zake: Ngakhale kuti munakula opanda bambo kapena bambo anu sankasonyeza chitsanzo chabwino, sizikutanthauza kuti mulibe tsogolo labwino. Pali zimene mungachite kuti zinthu zikuyendereni bwino. (2 Akorinto 10:4) Mukhoza kutsatira malangizo amene Mfumu Davide anapereka kwa mwana wake Solomo kuti: “Uchite zinthu mwamphamvu ndipo ukhale wolimba mtima.”—1 Mafumu 2:2.

N’zoona kuti ndi zovuta kukula popanda bambo kapena kukhala ndi bambo amene sasamala ana. Alex amene tamutchula koyambirira uja ananena kuti:  “Zimakhala zovuta kwambiri ukakhala kuti suwadziwa bambo ako bwinobwino. Panopa ndili ndi zaka 25, koma ndimaona kuti zimene ndikuphunzira panopa ndimayenera kuziphunzira kalekale.” Kodi mungatani ngati muli ndi mavuto ngati a Alex?

Yesani izi: Pezani munthu amene mukuona kuti ndi chitsanzo chabwino pa zimene mwamuna ayenera kuchita. * Mufunseni kuti ndi makhalidwe ati amene akuona kuti mwamuna weniweni ayenera kukhala nawo. Kenako akuuzeni zimene inuyo mungachite kuti mukhale ndi makhalidwewo.​—Miyambo 1:5.

Mavesi amene mungawerenge: Miyambo chaputala 1 mpaka 9. Pamene mukuwerenga machaputalawa, yesani kupeza malangizo omwe angathandize mnyamata kuti akhale wanzeru komanso kuti azikonda kutsatira mfundo za m’Baibulo.

“Ndikusangalala kuti panopa ndili ndi makhalidwe amene mwamuna weniweni amafunika kukhala nawo. N’zoona kuti zikanakhala bwino kwambiri ndikanakula ndi bambo anga koma sindiganizira kwambiri zam’mbuyo ndipo ndimaona kuti ndili ndi tsogolo labwino.”—Anatero Jonathan.

 

^ ndime 3 Tasintha mayina ena m’nkhani ino.

^ ndime 24 Mungapemphe akulu mumpingo wachikhristu kuti akuthandizeni.

FUNSANI MAKOLO ANU

Kodi inuyo mumaganiza kuti mwamuna weniweni ndi wotani? Kodi mukuona kuti ineyo ndimachitabe zachibwana?