Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Chimafunika N’chiyani Kuti Phwando Likhale Losangalatsa?

Kodi Chimafunika N’chiyani Kuti Phwando Likhale Losangalatsa?

 Zimene Achinyamata Amadzifunsa

Kodi Chimafunika N’chiyani Kuti Phwando Likhale Losangalatsa?

Chongani chonchi ✔ chinthu chimene mumaona kuti chiyenera kukhalapo basi pa phwando.

○ chakudya

○ kuvina

○ kuchita masewera enaake

○ kupeza anzanu atsopano

○ kukumananso ndi anzanu akale

○ zina ․․․․․

ACHINYAMATA ambiri amakonda kupita kuphwando. Zimenezi si zolakwika ndipo ngakhale Baibulo sililetsa phwando.

Kodi mukudziwa?

● Ana a Yobu ankachita phwando.—Yobu 1:4.

● Pa nthawi ina, Yesu anapita ku phwando la ukwati.—Yohane 2:1-11.

● Akhristu akale ankakumana pamodzi n’kumasangalala.—Machitidwe 2:46, 47.

Kunena zoona, kupatula nthawi yocheza ndi anzathu n’kosangalatsa. Koma n’zomvetsa chisoni kuti pa maphwando ena pamachitika zinthu zokhumudwitsa.

NKHANI IMENE INACHITIKADI “Ndinaitanidwa ku phwando linalake kunyumba kwa mnyamata wina kumene anaitana aliyense amene akufuna. Pa nthawi ya phwandoyo, makolo a mnyamatayo kunalibe. Ineyo sindinapiteko ndipo ndimaona kuti ndinachita bwino kwambiri. Tsiku lotsatira ndinamva kuti kuphwandoko kunali mowa wochita kusamba ndipo ena analedzereratu. Akuti anyamata atatu anafika pokomoka ndi mowa. Komanso kunali ndewu moti mpaka kunafika apolisi.”—Anatero Janelle.

PHUNZIRO Musamachite zinthu popanda kuganizira zotsatirapo zake. Kaya mukukonza zokhala ndi phwando kapena mwaitanidwa ku phwando, tsimikizirani kuti mukudziwa mayankho a mafunso amene ali pamasamba otsatira. Zimenezi zingakuthandizeni kuti pambuyo pake musanong’oneze bondo kuti munapitiranji kuphwandoko.

ZITSANZO ZABWINO

“Mnzanga wina atakonza phwando, mayi ake ankaonetsetsa chilichonse chimene tonse tikuchita. Ngakhale pamene ndimapita kukatenga jekete langa m’galimoto anandifunsa kuti ndikupita kuti. Kodi iwowo anaonjeza? Mwina ena angatero. Koma ineyo sindinakhumudwe chifukwa ndimaona kuti ndi bwino kutetezedwa kusiyana ndi kulekereredwa n’kukumana ndi mavuto.”—Anatero Kim.

“Maphwando abwino amene ndapitapo ndi amene panali anthu amisinkhu yosiyanasiyana. Komanso amene anaitana anthu ku phwandolo anakonzeratu zochitika zosiyanasiyana kuti anthu adzasangalale nazo, zimene zinachititsa kuti pasapezeke aliyense wochoka pagulupo n’kumakachita zinthu payekha.”—Anatero Andrea.

Nkhani zina zakuti “Zimene Achinyamata Amafunsa,“ mungazipeze pa adiresi yathu ya pa Intaneti ya www.jw.org.

 [Bokosi/Zithunzi pamasamba 26, 27]

“Anthu ena ndi abwino ndipo ena zimavuta kuwadziwa kuti ndi otani. Choncho munthu ukamaitana anthu oti abwere kuphwando lako, ndi bwino kusamala.’’

  “Ndapitako kumaphwando amene ndimaona kuti anakonzedwa bwino kwambiri. Chifukwa chakuti panali malamulo oti azitsatiridwa, panalibe zosokoneza ndipo anthu anasangalala kwambiri.”

[Zithunzi]

Nicole

Andrew

[Bokosi/Chithunzi patsamba 26]

● Mudzaitana ndani ndipo kudzakhala anthu ochuluka bwanji?

“Ndikuganiza kuti ndi bwino kuitana anthu okhawo amene mukuwadziwa bwino komanso kuwauza anthuwo kuti adzabwere okha.”—Anatero Renee.

“Ngati mukungoitana anthu popanda kusamala, phwandolo likhoza kusokonekera. Chimene chimachitika n’chakuti umatha kuitana anthu 20, anthuwo n’kuitana anzawo 10, ndipo anzawo 10 aja n’kuitananso anzawo ena. . . . Ndaonapo zimenezi zikuchitika.”—Anatero Colette.

“Maphwando akuluakulu amavuta kuwayang’anira. Ndimaona kuti ndi bwino kuitana anthu ochepa.”—Anatero Alexis.

“Munthu woyenda ndi anthu anzeru adzakhala wanzeru, koma wochita zinthu ndi anthu opusa adzapeza mavuto.”—MIYAMBO 13:20.

[Bokosi/Chithunzi pamasamba  26, 27]

● Kodi kungakachitike zotani?

“Zikakhala kuti wakonza phwandolo ndi iweyo ndipo kwachitika zinazake zosokonekera, anthu amaona kuti wachititsa ndi iweyo.”—Anatero Bridget.

“Phwando likakonzedwa bwino, aliyense amasangalala. Pamangofunika kuoneratu zinthu patali.”—Anatero Seth.

NKHANI IMENE INACHITIKADI “Ndili ndi mnzanga wina amene anandiuza kuti sandiitana kuphwando chifukwa amaopa kuti makolo anga amufunsa mafunso ambirimbiri monga akuti, Kodi anthu ena amene aitanidwa ndi ndani? Phwandolo likatenga nthawi yaitali bwanji? Mnzangayu ananena kuti zimenezi sizimusangalatsa. Koma ineyo ndikuona kuti umenewu ndi umboni wakuti maphwando amene iye amakonza sakhala abwino. Ngati safuna kufunsidwa mafunso, ndiye kuti maphwando ake si oti ine ndingapiteko.”—Anatero Ellen.

“Kaya mukudya kapena kumwa kapena mukuchita china chilichonse, chitani zonse ku ulemerero wa Mulungu.”—1 AKORINTO 10:31.

[Bokosi/Chithunzi pamasamba 26, 27]

● Kodi mungatani ngati zinthu zayamba kusokonekera?

“Ndimaganiziratu zimene ndingachite ngati zinthu zitayamba kusokonekera. Ndikapita kuphwando ndimayimbira foni makolo anga n’kuwauza kuti ndibwera nthawi yakutiyakuti. Ndikatero iwo amandifunsa ngati zinthu zili bwino kuphwandoko. Ndikangoyankha kuti ayi, basi amayamba kundiuza ntchito zambirimbiri zomwe zikundidikira kunyumba. Ndikamaliza kulankhula nawo, ndimauza anzanga kuti ndikupita kunyumba chifukwa makolo anga akundifuna.”—Anatero Therese.

NKHANI IMENE INACHITIKADI “Kuphwando linalake kunabwera anyamata awiri omwe sanaitanidwe n’komwe ndipo mmodzi ankadziwika kuti amagwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo. Ndinkada nkhawa kuti nditani, koma kenako ndinayimbira foni bambo anga kuti adzanditenge.”—Anatero Mary.

“Wochenjera ndi amene amati akaona tsoka amabisala, koma anthu osadziwa zinthu amangopitabe ndipo amalangidwa”—MIYAMBO 22:3.

[Bokosi/Chithunzi patsamba 27]

● Ndani azikayang’anira zimene zikuchitika?

“Phwando limayenda bwino ngati pali anthu achikulire amene akuyang’anira zonse zimene zikuchitika.”—Anatero Mark.

“Kale sindinkamasuka makolo anga akakhala nawo paphwando. Koma pano ndimaona kuti amafunika n’cholinga choti pasachitike zosokonekera. Makolo sangalepheretse kusangalala.”—Anatero Laura.

“Khalani ndi chikumbumtima chabwino.”​—1 PETULO 3:16

[Bokosi patsamba 27]

FUNSANI MAKOLO ANU

Funsani makolo anu kuti akuuzeni maphwando amene ankakonda ali achinyamata. Afunseninso ngati ankasangalala ndi maphwandowo kapena ngati panali zinazake zokhumudwitsa zimene zinkachitika.

KUKONZEKERA PHWANDO

Ngati mukufuna kukonza phwando, kambiranani ndi makolo anu za nkhaniyo, ndipo ganizirani mofatsa zinthu zotsatirazi:

1. Kodi muitana ndani?

2. Muitana anthu angati?

3. Phwandolo likachitikira kuti?

4. Ndani adzayang’anire phwandolo?

5. Mukufuna kuti padzakhale zochitika zotani?

[Chithunzi patsamba 25]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

MUKUITANIDWA