Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Baibulo Ndi Buku la Maulosi Olondola, Gawo 5

Uthenga Wabwino kwa Anthu Amitundu Yonse

Baibulo Ndi Buku la Maulosi Olondola, Gawo 5

Nkhani zokwanira 8 zimene zikhale zikutuluka mu Galamukani!, zizifotokoza maulosi osiyanasiyana a m’Baibulo. Nkhanizi zikuthandizani kupeza mayankho a mafunso awa: Kodi maulosi a m’Baibulo analembedwa ndi anthu kapena pali umboni wakuti analembedwa ndi Mulungu? Kuwerenga nkhanizi kukuthandizani kudziwa zoona zenizeni.

BAIBULO lili ndi uthenga wabwino umene Mulungu akufuna kuti anthu onse aumve. N’chifukwa chake Yesu ali padziko lapansi ankalalikira “uthenga wabwino wa ufumu.” (Luka 4:43) Baibulo limasonyeza kuti Ufumu umenewu ndi boma la Mulungu ndipo lidzachotsa maulamuliro onse a anthu, omwe ndi opondereza. Limasonyezanso kuti boma limenelo lidzabweretsa mtendere padziko lonse ndipo lidzachotsa mavuto onse. (Danieli 2:44; Mateyu 6:9, 10) Umenewu ndi uthenga wabwinodi.

Uthenga wabwino umenewu unali woyenera kuti anthu onse aumve. Koma pamene Yesu ankaphedwa, panali otsatira ake ochepa okha omwe ankalalikira uthengawu. Kodi zikanatheka kuti uthengawu ulalikidwe kwa anthu onse? Baibulo linaneneratu zimene zidzachitike. Linalosera kuti: (1) Uthenga wabwino udzalalikidwa padziko lonse. (2) Anthu ena adzayesetsa kulepheretsa kuti uthenga wabwino usafalikire koma adzalephera. (3) Akhristu onyenga adzasocheretsa anthu ambiri. Tiyeni tione maulosi amenewa mwatsatanetsatane.

Uthenga Wabwino Udzalalikidwa Kwa Anthu Amitundu Yonse

Maulosi:

“M’mitundu yonse uthenga wabwino uyenera ulalikidwe choyamba.” (Maliko 13:10) “Mudzakhala mboni zanga mu Yerusalemu, ku Yudeya konse ndi ku Samariya, mpaka kumalekezero a dziko lapansi.”Machitidwe 1:8.

Kukwaniritsidwa kwake: Patangopita nthawi yochepa, Yesu ataphedwa mu 33 C.E., ophunzira ake anadzaza Yerusalemu yense ndi uthenga wa Ufumu. Analalikira mpaka ku Yudeya ndi ku Samariya ndipo patatha zaka 15, amishonale anali atatumizidwa kumadera ena mu Ufumu wa Roma. Pofika mu 61 C.E., uthenga wabwino unali utalalikidwa m’madera ambiri padziko lapansi.

 Zimene mbiri imasonyeza:

  • Mabuku ena ofotokoza mbiri yakale a m’zaka za m’ma 100 C.E., amasonyeza kuti pofika m’zaka zimenezi, Chikhristu chinali chitafalikira m’madera ambiri. Munthu wina wolemba mbiri yakale wa ku Roma, dzina lake Suetonius, ananena kuti chakumayambiriro kwa 49 C.E., ku Roma kunali Akhristu ambiri. Mwachitsanzo, mu 112 C.E., Pliny Wamng’ono, yemwe anali bwanamkubwa wa ku Bituniya (komwe masiku ano ndi ku Turkey), analembera kalata Mfumu Trajan. M’kalatayo iye analemba kuti, Chikhristu “chafalikira kwambiri m’matauni, m’midzi komanso m’madera a zaulimi.” Poikirapo ndemanga mfundo imeneyi, wolemba mbiri wina ananena kuti: “Pasanathe zaka 100 atumwi onse atamwalira, m’mizinda yambiri ya mu Ufumu wa Roma munali mutamangidwa malo ambiri omwe Akhristu ankakalambirira.”

  • Buku lina limene pulofesa Henry Chadwick analemba linati: “Chikhristu chinafalikira modabwitsa kwambiri. Poyamba zinkaoneka ngati Chikhristu sichipita patali koma zinali zodabwitsa kuti pasanapite nthawi yaitali chinafalikira m’madera ambiri.”—The Early Church

Ena Adzafuna Kulepheretsa Kuti Uthenga Wabwino Usafalikire

Ulosi:

“Anthu adzakuperekani kumakhoti aang’ono, ndipo adzakukwapulani m’masunagoge ndi kukuimikani pamaso pa abwanamkubwa ndi mafumu chifukwa cha ine, kuti ukhale umboni kwa iwo.”Maliko 13:9.

Kukwaniritsidwa kwake: Akhristu ankazunzidwa ndi Ayuda komanso Aroma. Ankawatsekera m’ndende, kuwamenya komanso kuwapha.

Zimene mbiri imasonyeza:

  • Katswiri wina wachiyuda wa mbiri yakale, dzina lake Flavius Josephus, analemba kuti Yakobo, yemwe anali m’bale wake wa Yesu, anaphedwa ndi atsogoleri achipembedzo achiyuda. Baibulo limanena kuti pa nthawi ina otsatira a Yesu ankazengedwa mlandu ku Khoti Lalikulu la Ayuda. M’khotilo munali Gamaliyeli, yemwe anali mmodzi mwa akuluakulu, ndipo anachenjeza anzake kuti achite zinthu mosamala poweruza mlanduwo. (Machitidwe 5:34-39) Mabuku ena amasonyeza kuti kunalidi Gamaliyeli ndiponso kuti ankanena maganizo ake mosabisa mawu.

  • Akatswiri ena a mbiri yakale amanena kuti kuyambira mu ulamuliro wa mfumu Nero mu 64 C.E., mafumu ambiri Achiroma ankazunza Akhristu. Kalata imene Pliny Wamng’ono analembera Mfumu Trajan imasonyezanso kuti ankakambirana za chilango chimene angapatse Akhristu omwe sankafuna kusiya chikhulupiriro chawo.

  • Pulofesa Henry Chadwick ananenanso kuti: “Anthu ankaganiza kuti Akhristu azilambira mwamseri chifukwa chozunzidwa, koma zimene zinachitika zinali zosiyana ndi zimenezo. Pamene Akhristuwo amathawa kuzunzidwa, anayamba kulalikiranso uthenga wabwino m’madera amene anathawirawo. (Machitidwe 8:1) Iwo sanasiye kulalikira ngakhale kuti anzawo komanso abale awo ankawazunza. Zimenezi zinali zochititsa chidwi chifukwa otsatira a Yesu anali “osaphunzira ndiponso anthu wamba,” komanso sankathandizidwa ndi andale. (Machitidwe 4:13) Akatswiri a mbiri yakale amanena kuti “anthu wamba ngati ogulitsa malonda komanso amisiri a zinthu zosiyanasiyana, . . . analabadira Uthenga Wabwino mosavuta.”

Akamafufuza mbiri ya Akhristu, akatswiri amagoma ndi mmene kagulu kakang’ono ka anthu wamba kameneka kanafalitsira Chikhristu mofulumira ngakhale kuti ankazunzidwa kwambiri. Yesu anali ataneneratu kuti zimenezi zidzachitika. Malembanso anali ataneneratu kuti anthu ena adzayesa kulepheretsa ntchito yolalikira.

 Kudzabwera Akhristu Onyenga

Maulosi:

“Mimbulu yopondereza idzafika pakati panu ndipo sidzasamalira gulu la nkhosa mwachikondi. Ndipo pakati panu anthu ena adzayamba kulankhula zinthu zopotoka kuti apatutse ophunzira aziwatsatira.” (Machitidwe 20:29, 30) “Padzakhala aphunzitsi onyenga pakati panu. Amenewa adzabweretsa mwakachetechete timagulu tampatuko towononga . . . , ndipo chifukwa cha amenewa, anthu adzalankhula monyoza njira ya choonadi.”—2 Petulo 2:1, 2.

Kukwaniritsidwa kwake: Anthu ankhanza, achinyengo komanso odzikonda anaipitsa mpingo wachikhristu.

Zimene mbiri imasonyeza:

  • Otsatira oyambirira a Yesu atamwalira, anthu ena otchuka mu mpingo wachikhristu anasokoneza Chikhristu ndi nzeru za Agiriki. Pasanapite nthawi, anthuwa anayamba kudzipatsa maudindo ndipo anayamba kuchita zinthu ngati anthu andale. Akatswiri a mbiri yakale amanena kuti, pa nthawi imene akuluakulu a boma analamula kuti Chikhristu chikhale chipembedzo cha ufumu wa Roma, n’kuti anthuwa atasinthiratu zimene Akhristu oyambirira ankaphunzitsa.

  • Kuyambira nthawi imeneyo, Akhristu onyenga amenewa akhala akulimbikitsa chiwawa komanso kuchita zinthu modzikonda. M’malo mochita zimene Yesu analamula, atsogoleri achipembedzo anayamba kuzunza anthu amene ankayesetsa kuchita zimene Yesu analamula monga kulalikira. Iwo ankazunzanso anthu amene ankamasulira Baibulo m’chinenero chimene anthu angamve.

Pa zaka zonse zimene Akhristu onyenga amenewa anakhala akulamulira, zinkaoneka ngati ntchito yolalikira uthenga wabwino yaima. Komabe Yesu anali atanena kuti ntchito yolalikirayi idzayambiranso m’nthawi yamapeto. Iye anayerekezera nthawi imeneyi ndi nthawi yokolola, ndipo Akhristu onyenga omwe ali ngati namsongole adzasiyanitsidwa ndi Akhristu oona, omwe ali ngati tirigu. (Mateyu 13:24-30, 36-43) Pa nthawi imeneyi, uthenga wabwino udzakhala utalalikidwa padziko lonse mogwirizana ndi ulosi. (Mateyu 24:14) Gawo 6 la nkhanizi lidzafotokoza zambiri za ulosi umenewu.