Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Dziko Silidzatha Ngati Mmene Anthu Amaganizira

Dziko Silidzatha Ngati Mmene Anthu Amaganizira

NKHANI zapitazi zasonyeza kuti anthu amachita mantha kwambiri akaganizira za kutha kwa dziko. Nkhanizi zikufanana zinthu zitatu. Choyamba, nkhanizi ndi zongopeka ndipo anthu pawokha amalephera kudziwa bwinobwino zimene zidzachitike m’tsogolo. Chachiwiri, zikusonyeza kuti ngati anthu adzapulumuke ndiye kuti udzangokhala mwayi basi. Ndipo chachitatu, anthu amene adzapulumuke adzakumana ndi mavuto ambiri.

Koma mosiyana ndi zimenezi, Baibulo limanena zoona zenizeni zimene zidzachitike. N’zoona kuti Baibulo limanena kuti kutsogoloku kudzachitika zinthu zoopsa kwambiri koma silinena kuti anthu onse padziko lapansi adzafa. M’malomwake limanena kuti amene adzapulumuke ndi okhawo amene amachita chifuniro cha Mulungu. Komanso Baibulo silinena kuti dzikoli lidzaphulika kapena kuwonongeka mwanjira inayake, koma limanena kuti lidzasintha n’kukhala Paradaiso.

Anthu ambiri savomereza zimene Baibulo limanena. Iwo amatsutsa mfundo yakuti kudzachitika chisautso chachikulu, nkhondo ya Aramagedo, Yesu adzalamulira kwa zaka 1,000 komanso kuti dziko lapansi lidzakhala Paradaiso. Akatswiri a maphunziro achipembedzo akhala akukambirana komanso kunena maganizo osiyanasiyana pa nkhaniyi. Mwachitsanzo munthu wina wolemba mabuku, dzina lake Bruce A. Robinson, ananena kuti: “Anthu akhala akulemba mfundo zovuta kumvetsa pa nkhani ya kutha kwadziko kuposa nkhani ina iliyonse imene matchalitchi alembapo m’mbuyo monsemu.” Nkhani zimenezi zimangosokoneza anthu.

Koma zimene Malemba amanena sizosokoneza. Baibulo, lomwe ndi Mawu a Mulungu, limatiuza zimene zidzachitike mtsogolo. Taonani ena mwa mafunso amene anthu ambiri amakonda kufunsa komanso zimene Baibulo limanena. Ngati mukufuna kudziwa zambiri pa nkhani imeneyi, mukhoza kuitanitsa buku lakuti, Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

Kodi anthu komanso dziko lapansi lidzawonongedwa?

“Olungama adzalandira dziko lapansi, ndipo adzakhala mmenemo kwamuyaya.”—Salimo 37:29.

Kodi pali anthu amene adzapulumuke?

“Pakuti owongoka mtima ndi amene adzakhale m’dziko lapansi, ndipo opanda cholakwa ndi amene adzatsalemo. Koma oipa adzachotsedwa padziko lapansi ndipo achinyengo adzazulidwamo.”—Miyambo 2:21, 22.

Kodi Mulungu anawonongapo anthu oipa m’mbuyomu?

Mulungu “anaperekanso chilango padziko lakale lija ndipo sanalilekerere, koma anasunga Nowa, mlaliki wa chilungamo, pomupulumutsa pamodzi ndi anthu ena 7, pamene anabweretsa chigumula padziko la anthu osaopa Mulungu. Anaweruzanso mizinda ya Sodomu ndi Gomora mwa kuinyeketsa ndi moto, kuti chikhale chitsanzo cha zinthu zimene zidzachitikire anthu osaopa Mulungu m’tsogolo.”—2 Petulo 2:5, 6.

Kodi n’zotheka kudziwa tsiku lenileni limene Mulungu adzawononge anthu oipa?

“Kunena za tsikulo ndi ola lake, palibe amene akudziwa, ngakhale angelo akumwamba kapenanso Mwana, koma Atate yekha. Pakuti monga mmene analili masiku a Nowa, ndi mmenenso kukhalapo kwa Mwana wa munthu kudzakhalire. M’masiku amenewo chigumula chisanafike, anthu anali kudya ndi kumwa. Amuna anali kukwatira ndipo akazi anali kukwatiwa, kufikira tsiku limene Nowa analowa m’chingalawa. Anthu ananyalanyaza zimene zinali kuchitika mpaka chigumula chinafika n’kuwaseseratu onsewo. Zidzateronso ndi kukhalapo kwa Mwana wa munthu.”—Mateyu 24:36-39.

Kodi pali umboni uliwonse wosonyeza kuti Mulungu watsala pang’ono kuwononga anthu oipa?

“Masiku otsiriza adzakhala nthawi yapadera komanso yovuta. Pakuti anthu adzakhala odzikonda, okonda ndalama, odzimva, odzikweza, onyoza, osamvera makolo, osayamika, osakhulupirika, osakonda achibale awo, osafuna kugwirizana ndi anzawo, onenera anzawo zoipa, osadziletsa, oopsa, osakonda zabwino, achiwembu, osamva za ena, odzitukumula ndiponso onyada, okonda zosangalatsa, m’malo mokonda Mulungu, ndiponso ooneka ngati odzipereka kwa Mulungu koma amakana kuti mphamvu ya kudziperekako iwasinthe.”—2 Timoteyo 3:1-5.

Kodi anthu adzakhala ndi moyo wotani mtsogolo?

Mulungu “adzapukuta misozi yonse m’maso mwawo, ndipo imfa sidzakhalaponso. Sipadzakhalanso kulira, kapena kubuula, ngakhale kupweteka. Zakalezo zapita.”—Chivumbulutso 21:4.

Mulungu “adzapukuta misozi yonse m’maso mwawo”

Ngakhale kuti Baibulo silimanena zonse zimene zidzachitike mtsogolo, limasonyeza kuti anthu omvera adzapeza madalitso. Mtsogolomu mudzachitika zinthu zabwino kwambiri moti patokha sitingathe kumvetsa zonse mmene zidzakhalire. Musakayikire kuti Yehova Mulungu adzakwaniritsadi zimene watilonjeza.