Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Munapitako ku Malo Osungira Nyama?

Kodi Munapitako ku Malo Osungira Nyama?

ZAKA 3,000 zapitazo, wolamulira wina wa ku China anakhazikitsa malo enaake osungira nyama. Malowo anali aakulu maekala 1,500, ndipo panali nyama zamitundu yosiyanasiyana. Nthawi imeneyo, kunalibe malo ambiri osungira nyama.

Koma masiku ano, kuli malo ambiri omwe anthu amakaonako nyama. Buku lina linanena kuti: “Chifukwa cha kuchuluka kwa anthu, malo ambiri okhala zinyama akutha ndipo malo okha amene anthu angathe kuona nyama zakutchire ndi malo osungira nyama.”—Zoos in the 21st Century.

Kodi Kumapezeka Nyama Zotani?

Anthu amakhala ndi mwayi wokaona zina mwa nyama zokongola komanso zochititsa chidwi padziko lonse kumalo osungirako nyama. Nyamazi zimakhala ngati mmene zimakhalira kutchire. Anthu akapita kumalowa amatha kuona agulugufe okongola akuulukauluka m’maluwa kapena anyani akudumphadumpha m’mitengo ngati mmene amachitira akakhala kutchire.

Munthu akapita kumalo amenewo amakhala ngati ali kutchire kwenikweni ndipo amaona nyama ndi mbalame zosiyanasiyana. Kumalo ena osungira nyama kumakhalanso nyama zimene zimayenda usiku wokhawokha, pomwe kumalo ena anthu amatha kuona mbalame zikusaka ngati mmene zimasakira zikakhala kuthengo. Kale nyama zoopsa kwambiri ankazitsekera mukhola la zitsulo ndi mawaya koma masiku ano akumazisiya pamtetete ndipo amangokumba ngalande n’kuikamo madzi kuti nyamazo zisawolokere kumene anthu akudutsa.

 Kusagwirizana pa Nkhani ya Malo Osungira Nyama

Anthu ena oona za ufulu wa nyama amanena kuti nyama siziyenera kuchotsedwa kutchire n’kukaziika kumalo osungira nyama chifukwa sizikhala motakasuka komanso zimalephera kuchita zinthu ngati mmene zimachitira zikakhala kutchire.

Koma anthu amene amayang’anira malo osungirako nyama amanena kuti zimenezo sizoona, chifukwa ntchito yawo imathandiza kuti nyama zitetezeke komanso kuti anthu aphunzire zinthu zosiyanasiyana zokhudza nyama. Munthu wina, dzina lake Jaime Rull, yemwe amagwira ntchito kumalo osungirako nyama a Faunia ku Madrid, m’dziko la Spain, ananena kuti: “Cholinga chathu ndi kuphunzitsa anthu kuti aziteteza nyama zakutchire komanso malo amene zimakhala. Zimenezi zingathandize kuti nyamazi zisatheretu.” Kafukufuku amasonyeza kuti malo osungira nyama amathandizadi anthu kudziwa kufunika koteteza nyama zomwe zatsala pang’ono kutheratu.

Pali mtundu winawake wa nyama zotchedwa Panda, zomwe sizipezeka kawirikawiri moti anthu amasangalala kwambiri akamaona nyama zimenezi kumalo osungirako nyama. Mkulu wa dipatimenti yoona za maphunziro pamalo osungira nyama a Madrid Zoo Aquarium, dzina lake Noelia Benito, ananena kuti: “Tili ndi ma Panda awiri ndipo  aliyense akabwera amafuna kuona nyama zimenezi. Nyama zimenezi zimatikumbutsa udindo umene tili nawo woteteza nyama zimene zatsala pang’ono kutheratu. Tikukhulupirira kuti nyama zimenezi ziswana ngakhale kuti zimatenga nthawi yaitali kuti ziswane.”

Mosiyana ndi nyama zimenezi, nyama zina zimaswana kwambiri zikakhala kumalo amene amazisungira chifukwa chakuti amazisamalira bwino kwambiri. Ngakhale anthu ena sagwirizana ndi zoti nyama zizisungidwa kumalo osungirako nyama, njira zothandizira kuti nyama ziziswana zathandiza kuti mitundu ina ya nyama zimene zinatsala pang’ono kutheratu izipezeka. Komanso, anthu osamalira malo osungira nyama amagwiritsa ntchito njira zothandizira kuti nyama ziziswana n’cholinga choti nyama zimene zatsala pang’ono kutheratu zikachulukana azikazisiya kutchire komwe zimayenera kukhala.

Nyama zambiri zikutha chifukwa zilibe malo okhala. Choncho, mabungwe ena osamalira malo osungira nyama amapereka ndalama ku mabungwe enanso oteteza nyama zakutchire, zoti ziwathandize kuteteza malo amene nyamazi zimakhala. *

Kuona Zachilengedwe Kumasangalatsa

Ana ambiri amasangalala akamaona nyama zakutchire. Choncho, ngati nthawi zina makolo atatengera ana awo kumalo osungira nyama, akhoza kugwiritsa ntchito mpata umenewo kuwaphunzitsa anawo za zimene Mulungu analenga. Banja likhoza kusangalala kwambiri kuonera limodzi zinthu zachilengedwe.

Kuyambira kale kwambiri, anthu akhala akuchita chidwi ndi nyama zakutchire. Tiyenera kuthandiza ana athu kuti azikonda zinthu zachilengedwe chifukwa zimatiphunzitsa zambiri zokhudza Mlengi wathu. Komanso kupita kumalo osungira nyama kungatithandize kuti tidziwe nyama zosiyanasiyana komanso kuti tiziziteteza.

^ ndime 12 Mwachitsanzo, mabungwe ena osamalira malo osungira nyama athandizapo pa ntchito yoteteza akambuku a ku Asia, apusi ang’onoang’ono a ku Madagascar ndi anyani a ku Africa.