Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

PHUNZIRO 7

Kodi Ufumu wa Mulungu N’chiyani?

Kodi Ufumu wa Mulungu N’chiyani?

1. Kodi Ufumu wa Mulungu n’chiyani?

Kodi n’chiyani chimene chimachititsa kuti Yesu akhale Mfumu yoyenerera?​—MALIKO 1:40-42.

Ufumu wa Mulungu ndi boma lakumwamba. Boma limeneli lidzalowa m’malo mwa maboma onse ndipo Mulungu adzagwiritsa ntchito boma limeneli pokwaniritsa chifuniro chake kumwamba ndi padziko lapansi. Uthenga wonena za Ufumu wa Mulungu ndi wabwino. Anthu akufunikira boma labwino, ndipo posachedwapa Ufumu wa Mulungu, womwe ndi boma labwino uyamba kulamulira. Bomali lidzagwirizanitsa anthu onse okhala padziko lapansi.​—Werengani Danieli 2:44; Mateyu 6:9, 10; 24:14.

Ufumu uliwonse umakhala ndi mfumu yake. Choncho, Yehova anaika Mwana wake, Yesu Khristu, kuti akhale Mfumu ya Ufumu wake.​—Werengani Chivumbulutso 11:15.

Onerani vidiyo yakuti Kodi Ufumu wa Mulungu N’chiyani?

2. N’chifukwa chiyani Yesu ali Mfumu yoyenerera?

Mwana wa Mulungu ndi Mfumu yoyenerera chifukwa chakuti ndi wachifundo ndipo amachita zabwino nthawi zonse. (Mateyu 11:28-30) Komanso ali ndi mphamvu zambiri moti angathe kuthandiza anthu. Izi zili choncho chifukwa chakuti azidzalamulira dziko lapansi ali kumwamba. Iye ataukitsidwa, anapita kumwamba n’kukakhala kudzanja lamanja la Yehova poyembekezera kuti amupatse ufumu. (Aheberi 10:12, 13) Kenako Mulungu anapatsa Yesu mphamvu kuti ayambe kulamulira.​—Werengani Danieli 7:13, 14.

3. Kodi ndani amene azidzalamulira limodzi ndi Yesu?

Pali gulu lina la “oyera” amene azidzalamulira limodzi ndi Yesu kumwamba. (Danieli 7:27) Oyera oyambirira kusankhidwa anali atumwi okhulupirika a Yesu. Mpaka pano Yehova akusankhabe amuna ndi akazi okhulupirika kuti akhale m’gulu la oyera limeneli. Mofanana ndi Yesu, anthu amenewa amaukitsidwa ndi matupi auzimu.​—Werengani Yohane 14:1-3; 1 Akorinto 15:42-44.

Kodi ndi anthu angati amene adzapite kumwamba? Yesu ananena kuti anthu opita kumwambawa ndi “kagulu ka nkhosa.” (Luka 12:32) Onse pamodzi adzakwana 144,000, ndipo adzalamulira dziko lapansi limodzi ndi Yesu.​—Werengani Chivumbulutso 14:1.

4. Kodi chinachitika n’chiyani Yesu atayamba kulamulira?

Ufumu wa Mulungu unayamba kulamulira m’chaka cha 1914. * Chinthu choyamba chimene Yesu anachita atakhala Mfumu chinali kuchotsa Satana ndi ziwanda zake kumwamba n’kuwaponyera padziko lapansi. Zitatero Satana anakwiya kwambiri ndipo anayamba kubweretsa mavuto kwa anthu padziko lonse lapansi. (Chivumbulutso 12:7-10, 12) Kungoyambira pa nthawi imeneyo, mavuto amene anthu akukumana nawo akhala akuwonjezereka kwambiri. Choncho, nkhondo, njala, miliri komanso zivomezi, zonsezi ndi mbali ya “chizindikiro” chosonyeza kuti posachedwapa Ufumu wa Mulungu uyamba kulamulira dziko lapansi.​—Werengani Luka 21:7, 10, 11, 31.

5. Kodi Ufumu wa Mulungu udzachita zinthu zotani?

Kudzera m’ntchito yolalikira imene ikuchitika padziko lonse, Ufumu wa Mulungu wayamba kale kugwirizanitsa khamu lalikulu la anthu ochokera m’mitundu yonse. Anthu ofatsa mamiliyoni ambiri akubwera kumbali ya Ufumu wa Mulungu, womwe wolamulira wake ndi Yesu. Ufumu umenewu udzateteza anthuwo pamene dziko loipali lizidzawonongedwa. Choncho aliyense amene akufuna kupeza madalitso mu Ufumu wa Mulungu, ayenera kumvera Yesu monga wolamulira wake.​—Werengani Chivumbulutso 7:9, 14, 16, 17.

Mkati mwa zaka 1,000, Ufumu umenewu udzakwaniritsa cholinga choyambirira cha Mulungu chokhudza anthu. Dziko lonse lapansi lidzakhala paradaiso, ndipo pamapeto pake Yesu adzabwezera Ufumuwo m’manja mwa Atate wake. (1 Akorinto 15:24-26) Kodi pali winawake amene mungakonde kumuuza za Ufumu wa Mulungu?​—Werengani Salimo 37:10, 11, 29.

 

^ ndime 6 Kuti mumve zambiri zokhudza ulosi wa m’Baibulo wonena za chaka cha 1914, werengani tsamba 217 mpaka 220 m’buku lakuti Zimene Baibulo Limaphunzitsa.