Uthenga Wabwino Wochokera kwa Mulungu

Kodi uthenga wabwino wochokera kwa Mulungu n’chiyani? Kodi tingaukhulupirire? Kabuku kano kali ndi mayankho a mafunso ambiri a m’Baibulo.

Zimene Mungachite Kuti Mupindule ndi Kabukuka

Kabukuka kakuthandizani kuti muziphunzira mosavuta Mawu a Mulungu, Baibulo. Tayeserani kufufuza m’Baibulo lanu malemba amene ali m’kabukuka.

PHUNZIRO

Kodi Uthenga Wabwino N’chiyani?

Dziwani uthenga wabwino wochokera kwa Mulungu, chifukwa chake ukufunika kulengezedwa mwamsanga, ndiponso zimene inuyo muyenera kuchita.

PHUNZIRO

Kodi Mulungu Ndani?

Kodi Mulungu ali ndi dzina, nanga amasamala za ife?

PHUNZIRO

Kodi Uthenga Wabwino ndi Wochokeradi kwa Mulungu?

Kodi tingatsimikize bwanji kuti Baibulo limanena zoona?

PHUNZIRO

Kodi Yesu Khristu Ndani?

Dziwani chifukwa chake Yesu anafa, tanthauzo la mawu akuti dipo, komanso zimene Yesu akuchita panopa.

PHUNZIRO

Kodi Mulungu Ali ndi Cholinga Chotani Chokhudza Dziko Lapansili?

Baibulo limafotokoza chifukwa chake Mulungu analenga dzikoli, nthawi imene mavuto adzathe, mmene zinthu zidzakhalire padzikoli komanso anthu amene adzakhale m’dziko la paradaiso.

PHUNZIRO

Kodi Pali Chiyembekezo Chotani Chokhudza Anthu Amene Anamwalira?

Kodi chimachitika n’chiyani munthu akamwalira? Kodi abale athu amene anamwalira tidzawaonanso?

PHUNZIRO

Kodi Ufumu wa Mulungu N’chiyani?

Kodi Mfumu ya Ufumu wa Mulungu ndani, ndipo Ufumuwo udzachita zotani?

PHUNZIRO

N’chifukwa Chiyani Mulungu Walola Zinthu Zoipa Komanso Kuti Anthu Azivutika?

Kodi zinthu zoipa zinayamba bwanji, ndipo n’chifukwa chiyani Mulungu walola kuti zoipazo zipitirirebe mpaka pano? Kodi mavuto amenewa adzatha?

PHUNZIRO

Kodi Mungatani Kuti Banja Lanu Likhale Losangalala?

Yehova, Mulungu wachimwemwe, amafuna kuti mabanja azikhala osangalala. Werengani nkhaniyi kuti mudziwe malangizo othandiza a m’Baibulo opita kwa amuna, akazi, makolo, ndiponso ana.

PHUNZIRO

Kodi Chipembedzo Choona Mungachidziwe Bwanji?

Kodi chipembedzo choona chilipo chimodzi chokha? Taonani zinthu 5 zomwe zingakuthandizeni kudziwa chipembedzo choona.

PHUNZIRO

Kodi Timapindula Bwanji ndi Mfundo za M’Baibulo?

Yesu anafotokoza chifukwa chake timafunikira malangizo komanso anatchula mfundo ziwiri za m’Baibulo zomwe ndi zofunika kwambiri pa moyo wathu.

PHUNZIRO

Kodi Mungatani Kuti Muyandikire Mulungu?

Werengani nkhaniyi kuti mudziwe ngati Mulungu amamvetsera mapemphero onse, mmene tiyenera kupempherera, komanso zinthu zina zimene tingachite kuti tiyandikire Mulungu.

PHUNZIRO

Kodi Pali Uthenga Wabwino Wotani Wokhudza Zipembedzo?

Kodi idzafika nthawi imene anthu onse adzagwirizana n’kumalambira Mulungu woona yekha?

PHUNZIRO

N’chifukwa Chiyani Mulungu Ali ndi Gulu?

Baibulo limatiuza chifukwa chake Akhristu oona ayenera kuchita zinthu monga gulu.

PHUNZIRO

N’chifukwa Chiyani Muyenera Kupitiriza Kuphunzira za Yehova?

Kodi mungatani kuti zimene mukudziwa zokhudza Mulungu ndiponso Mawu ake zithandizenso anthu ena? Kodi mungakhale pa ubwenzi wotani ndi Mulungu?