Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 PHUNZIRO 14

N’chifukwa Chiyani Mulungu Ali ndi Gulu?

N’chifukwa Chiyani Mulungu Ali ndi Gulu?

1. N’chifukwa chiyani Mulungu anakonza zoti Aisiraeli akale akhale gulu la anthu ake?

Mulungu anakonza zoti mbadwa za Abulahamu zikhale mtundu waukulu wa anthu ndipo anawapatsa malamulo osiyanasiyana. Mtunduwo anaupatsa dzina lakuti “Isiraeli” ndipo anausankha kuti uzimulambira m’njira yovomerezeka ndiponso kuti uzitsatira mawu ake. (Salimo 147:19, 20) Ndipo anthu ena ochokera m’mitundu yonse akanatha kupeza madalitso kuchokera mumtundu wa Isiraeli.​—Werengani Genesis 22:18.

Mulungu anasankha Aisiraeli kuti akhale mboni zake. Mbiri yawo yakale imasonyeza bwino mfundo yakuti, zinthu zimawayendera bwino anthu akamamvera malamulo a Mulungu. (Deuteronomo 4:6) Motero kudzera mwa Aisiraeli, anthu enanso anali ndi mwayi wodziwa Mulungu woona.​—Werengani Yesaya 43:10, 12.

2. N’chifukwa chiyani Akhristu enieni ndi gulu lochita zinthu mwadongosolo?

Patapita nthawi, Aisiraeli anasiya kumvera Mulungu ndipo iye anasiyanso kuwakonda. Choncho, Yehova anakonza zoti pakhale mpingo wachikhristu womwe unawalowa m’malo. (Mateyu 21:43; 23:37, 38) Masiku ano, m’malo mwa Aisiraeli, Akhristu oona amatumikira Yehova monga mboni zake.​—Werengani Machitidwe 15:14, 17.

Yesu anakonza zoti otsatira ake akhale gulu limene lizilalikira ndi kuphunzitsa anthu a mitundu yonse kuti akhale ophunzira ake. (Mateyu 10:7, 11; 24:14; 28:19, 20) Masiku ano, pamene tili m’nyengo ya mapeto a nthawi ino, ntchitoyi ikufika pachimake. Ndipo kwa nthawi yoyamba m’mbiri yonse, Yehova wasankha anthu mamiliyoni ambiri ochokera m’mitundu yonse kuti agwirizane n’kukhala olambira ake oona. (Chivumbulutso 7:9, 10) Akhristu oona ndi gulu logwirizana ndipo anthu ake amalimbikitsana ndiponso amathandizana. Padziko lonse, iwo amakhala ndi pulogalamu yofanana yophunzirira Baibulo pamisonkhano yawo.​—Werengani Aheberi 10:24, 25.

 3. Kodi gulu la masiku ano la Mboni za Yehova linayamba bwanji?

Gulu la m’nthawi yathu ino la Mboni za Yehova linayamba m’zaka za m’ma 1870. Pa nthawiyo, kagulu ka anthu ochepa omwe ankaphunzira Baibulo kanatulukira mfundo za m’Baibulo za choonadi zomwe zinali zitabisika kwa nthawi yaitali. Anthu a m’kaguluko anadziwa zoti Yesu anakhazikitsa mpingo wachikhristu monga gulu loti lizilalikira. Choncho iwo anayamba ntchito yapadera yolalikira za Ufumu padziko lonse. Mu 1931, iwo anatenga dzina lakuti Mboni za Yehova.​—Werengani Machitidwe 1:8; 2:1, 4; 5:42.

4. Kodi gulu la Mboni za Yehova limayenda bwanji?

M’nthawi ya atumwi, mipingo yachikhristu yomwe inali m’mayiko ambiri inkapindula ndi malangizo ochokera ku bungwe lolamulira limene linkachita zinthu mozindikira kuti Yesu ndi Mutu wa mpingo. (Machitidwe 16:4, 5) Masiku anonso anthu a Mboni za Yehova padziko lonse amapindula ndi malangizo ochokera ku Bungwe Lolamulira, lomwe lapangidwa ndi akulu amene akhala akutumikira Mulungu kwa nthawi yaitali. Bungwe Lolamulira limayang’anira ntchito imene ikuchitika m’maofesi a nthambi a Mboni za Yehova. Anthu omwe akutumikira m’maofesi amenewa amagwira ntchito monga yomasulira mabuku ophunzirira Baibulo, kuwasindikiza ndiponso kuwatumiza m’mipingo yosiyanasiyana, ndipo mabuku amenewa akumasuliridwa m’zinenero zoposa 600. Choncho, ntchito imeneyi imathandiza kuti Bungwe Lolamulira lizitha kulimbikitsa ndiponso kupereka malangizo a m’Malemba kumipingo yoposa 100,000 padziko lonse. Ndipo mumpingo uliwonse, amuna oyenerera amatumikira monga akulu kapena kuti oyang’anira. Amuna amenewa amasamalira nkhosa za Mulungu mwachikondi.​—Werengani 1 Petulo 5:2, 3.

Mboni za Yehova ndi gulu limene limalalikira uthenga wabwino ndiponso limaphunzitsa anthu kuti akhale ophunzira a Yesu. Mofanana ndi zimene atumwi ankachita, ifenso timalalikira kunyumba ndi nyumba. (Machitidwe 20:20) Komanso timadzipereka kuphunzira Baibulo ndi anthu amene amakonda choonadi. Komatu ife a Mboni za Yehova sikuti tangokhala gulu basi. Ndife banja ndipo Atate wathu ndi wachikondi. Ndife abale ndi alongo amene timakondana ndi kusamalirana. (2 Atesalonika 1:3) Popeza anthu a Yehova ndi gulu limene limachita zinthu zokondweretsa Mulungu ndiponso limathandiza ena, iwo apanga banja losangalala kwambiri padziko lonse.​—Werengani Salimo 33:12; Machitidwe 20:35.