Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

PHUNZIRO 6

Kodi Pali Chiyembekezo Chotani Chokhudza Anthu Amene Anamwalira?

Kodi Pali Chiyembekezo Chotani Chokhudza Anthu Amene Anamwalira?

1. Kodi pali uthenga wabwino wotani wokhudza anthu amene anamwalira?

Pamene Yesu ankafika m’tauni ya Betaniya, yomwe inali pafupi ndi mzinda wa Yerusalemu, panali patadutsa masiku anayi mnzake Lazaro atamwalira. Kenako Yesu pamodzi ndi Malita ndi Mariya, omwe anali azichemwali ake a Lazaro, anapita kumanda kumene mchimwene wawoyo anaikidwa. Posapita nthawi, kumandako kunadzaza anthu. Kenako Yesu anaukitsa Lazaro, ndipo mukhoza kuona m’maganizo mwanu chisangalalo chimene Malita ndi Mariya anali nacho ataona kuti m’bale wawo waukitsidwa.​—Werengani Yohane 11:21-24, 38-44.

Malita anali akudziwa kale za uthenga wabwino wokhudza anthu amene anamwalira. Iye ankadziwa kuti Yehova adzaukitsa akufa ndipo adzakhalanso ndi moyo padziko lapansili.​—Werengani Yobu 14:14, 15.

2. Kodi chimachitika n’chiyani munthu akamwalira?

Mulungu anauza Adamu kuti: “Popeza ndiwe fumbi, kufumbiko udzabwerera.”—GENESIS 3:19.

Anthu anapangidwa kuchokera kufumbi. (Genesis 2:7; 3:19) Anthufe si mizimu imene ikukhala m’matupi okhala ndi minofu. Koma ndife zolengedwa zooneka, zokhala ndi thupi, ndipo mkati mwathu mulibe chinthu chomwe chimapitirizabe kukhala ndi moyo tikamwalira. Munthu akamwalira, ubongo wake umafanso, ndipo zinthu zonse zimene ankaganiza zimathera pomwepo. N’chifukwa chaketu Lazaro sananene chilichonse chokhudza zimene zinkamuchitikira pa nthawi imene anamwalira, popeza munthu akafa sadziwa chilichonse.​—Werengani Salimo 146:4; Mlaliki 9:5, 6, 10.

Kodi anthu oipa akamwalira, Mulungu amawawotcha ndi moto? Popeza Baibulo limasonyeza momveka bwino kuti munthu akafa sadziwa chilichonse, mfundo yakuti Mulungu amawotcha anthu ndi yabodza, ndipo imangochititsa kuti anthu aziimba Mulungu mlandu wa zinthu zimene iye sachita n’komwe. Ndipotu Mulungu amanyansidwa kwambiri anthu akamazunza anzawo powawotcha ndi moto kapena akamamunamizira kuti iye amachita zimenezi.​—Werengani Yeremiya 7:⁠31.

Onerani vidiyo yakuti Kodi Chimachitika N’chiyani Munthu Akamwalira?

3. Kodi anthu amene anamwalira angathe kulankhula nafe?

Anthu akufa sangalankhule kapena kumva. (Salimo 115:17) Komabe pali angelo ena oipa ndipo amalankhula ndi anthu ponamizira kuti ndi anthu amene anamwalira. (2 Petulo 2:4) Ndipotu Yehova amaletsa kulankhula ndi anthu akufa.​—Werengani Deuteronomo 18:10, 11.

4. Kodi ndi anthu ati amene adzaukitsidwe?

Anthu mamiliyoni ambirimbiri amene ali m’manda adzauka n’kukhalanso ndi moyo padziko lapansi. Ngakhalenso anthu ena amene sankamudziwa Mulungu ndipo ankachita zoipa adzaukitsidwa.​—Werengani Luka 23:43; Machitidwe 24:15.

Anthu amene adzaukitsidwe adzakhala ndi mwayi woti aphunzire za Mulungu ndi kusonyeza kuti akukhulupirira Yesu pomumvera. (Chivumbulutso 20:11-13) Oukitsidwawo akamadzachita zinthu zabwino adzakhala ndi mwayi wokhala ndi moyo wosatha padziko lapansi.​—Werengani Yohane 5:28, 29.

5. Kodi mfundo yakuti akufa adzaukitsidwa ikutiuza chiyani za Yehova?

N’zotheka kuti akufa adzaukitsidwe chifukwa Mulungu anatumiza Mwana wake kudzatifera. Choncho tikaganizira mfundo imeneyi timaona kuti Yehova ndi wachikondi komanso kukoma mtima kwake n’kwakukulu. Kodi akufa akadzauka, inuyo mukufunitsitsa kudzaonana ndi ndani?​—Werengani Yohane 3:16; Aroma 6:23.