Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Zimene Mungachite Kuti Mupindule ndi Kabukuka

Zimene Mungachite Kuti Mupindule ndi Kabukuka

Kabuku kano kakuthandizani kuti muzisangalala mukamaphunzira Mawu a Mulungu, Baibulo. Kumapeto kwa ndime iliyonse kuli malemba a m’Baibulo omwe angakuthandizeni kudziwa yankho la funso limene lalembedwa ndi mawu akuda kwambiri lomwe lili pamwamba pa ndimeyo.

Pamene mukuwerenga malemba a m’Baibulo, ganizirani mmene malembawo akuyankhira mafunsowo. Aliyense wa Mboni za Yehova ndi wokonzeka kukuthandizani kumvetsa bwino Malembawo.​—Werengani Luka 24:32, 45.

Dziwani izi: Mabuku omwe atchulidwa m’kabuku kano ndi ofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.