Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 PHUNZIRO 3

Kodi Uthenga Wabwino ndi Wochokeradi kwa Mulungu?

Kodi Uthenga Wabwino ndi Wochokeradi kwa Mulungu?

1. Kodi Mlembi Wamkulu wa Baibulo ndani?

Uthenga wabwino wakuti anthu adzakhala kwamuyaya padziko lapansi ukupezeka m’Baibulo. (Salimo 37:29) M’Baibulo muli mabuku ang’onoang’ono okwana 66, ndipo polemba mabuku amenewa, Mulungu anagwiritsa ntchito amuna okhulupirika okwana 40. Mabuku asanu oyambirira analembedwa ndi Mose zaka pafupifupi 3,500 zapitazo. Ndipo buku lomaliza linalembedwa ndi mtumwi Yohane zaka zoposa 1,900 zapitazo. Kodi anthu olemba Baibulowo ankalemba maganizo a ndani? Mulungu ankalankhula ndi anthu amene analemba Baibulowo kudzera mwa mzimu woyera. (2 Samueli 23:2) Choncho, iwo analemba maganizo a Mulungu, osati maganizo awo. Pa chifukwa chimenechi, Yehova ndiye Mlembi Wamkulu wa Baibulo.​—Werengani 2 Timoteyo 3:16; 2 Petulo 1:20, 21.

Onerani vidiyo yakuti Kodi Analemba Baibulo Ndi Ndani?

2. Kodi tingatsimikize bwanji kuti Baibulo limanena zoona?

Tikudziwa kuti Baibulo ndi lochokera kwa Mulungu chifukwa chakuti limalosera za m’tsogolo molondola komanso mwatsatanetsatane. Palibe munthu aliyense amene angachite zimenezi. (Yoswa 23:14) Ndi Mulungu Wamphamvuyonse yekha amene amatha kudziwiratu zimene zidzachitikire anthu m’tsogolo.​—Werengani Yesaya 42:9; 46:10.

Choncho n’zosadabwitsa kuti buku lochokera kwa Mulungu ndi lapadera kwambiri. Mabaibulo mabiliyoni ochuluka afalitsidwa m’zinenero mahandiredi ambiri. Ngakhale kuti Baibulo ndi lakale kwambiri, limagwirizana ndi mfundo zolondola za sayansi. Komanso anthu 40 amene analemba Baibuloli sanalembe mfundo zotsutsana. * Kuwonjezera pamenepo, zimene Baibulo limanena pa nkhani ya chikondi n’zapadera kwambiri, ndipo sizingachokere kwa wina aliyense koma kwa Mulungu woona yekha,  yemwe ndi Mulungu wachikondi. Ndipotu Baibulo lidakali ndi mphamvu yosintha moyo wa anthu kuti ukhale wabwino. Poganizira mfundo zimenezi, anthu mamiliyoni ambiri sakayikira kuti Baibulo ndi Mawu a Mulungu.​—Werengani 1 Atesalonika 2:13.

Onerani vidiyo yakuti Kodi Tingadziwe Bwanji Kuti Baibulo Limanena Zoona?

3. Kodi m’Baibulo muli nkhani zotani?

Imodzi mwa mfundo zikuluzikulu za m’Baibulo ndi yakuti Mulungu ali ndi cholinga chapadera chokhudza anthu. Malemba amafotokoza mmene anthu anatayira mwayi wokhala m’paradaiso padziko lapansi pano kalelo, komanso amafotokoza mmene Mulungu adzabwezeretsere paradaiso ameneyo.​—Werengani Chivumbulutso 21:4, 5.

M’Mawu a Mulungu mulinso malamulo, mfundo za makhalidwe abwino komanso malangizo. Kuwonjezera pamenepo, m’Baibulo muli nkhani zokhudza zimene Mulungu ankachitira anthu, ndipo tikamawerenga nkhanizi timaona makhalidwe amene Mulungu ali nawo. Choncho Baibulo lingakuthandizeni kuti mum’dziwe bwino Mulungu. Limafotokoza zimene mungachite kuti mukhale bwenzi lake.​—Werengani Salimo 19:7, 11; Yakobo 2:23; 4:8.

4. Kodi mungatani kuti muzilimvetsa bwino Baibulo?

Kabuku kano kakuthandizani kuti mulimvetse bwino Baibulo, ndipo kakufotokoza malemba potsatira njira imene Yesu ankagwiritsa ntchito. Nthawi zonse, Yesu ankagwiritsa ntchito malemba pophunzitsa, ndipo ankafotokoza ‘tanthauzo la Malembawo.’​—Werengani Luka 24:27, 45.

Palibe chinthu chosangalatsa kuposa uthenga wabwino wochokera kwa Mulungu. Komabe, anthu ena safuna kumva uthenga umenewu, ndipo ena amakwiya chifukwa cha uthengawu. Koma zimenezi zisakufooketseni, chifukwa ngati mukufuna kudzapeza moyo wosatha mukuyenera kuphunzira kuti mum’dziwe bwino Mulungu.​—Werengani Yohane 17:3.

 

^ ndime 3 Onani kabuku kakuti Buku la Anthu Onse.